NKHANI YOPHUNZIRA 13

Tizisonyeza Anthu Chifundo Tikakhala mu Utumiki

Tizisonyeza Anthu Chifundo Tikakhala mu Utumiki

“Anawamvera chifundo . . . Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”​MALIKO 6:34.

NYIMBO NA. 70 Fufuzani Anthu Oyenerera

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi khalidwe lina la Yesu losangalatsa ndi liti? Fotokozani.

N’ZOSANGALATSA kudziwa kuti Yesu amamvetsa mavuto amene anthu amakumana nawo. Yesu ali padzikoli ‘ankasangalala ndi anthu amene akusangalala komanso kulira ndi anthu amene akulira.’ (Aroma 12:15) Mwachitsanzo, ophunzira ake 70 atabwera mosangalala chifukwa chakuti zinthu zawayendera bwino kokalalikira, Yesu “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera.” (Luka 10:17-21) Koma ataona anthu ali ndi chisoni chifukwa cha imfa ya Lazaro, Yesu “anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni.”​—Yoh. 11:33.

2. N’chiyani chinathandiza Yesu kuti akhale wachifundo?

2 Yesu anali wangwiro koma pochita zinthu ndi anthu ochimwa ankakhala wokoma mtima komanso wachifundo. Kodi n’chiyani chinkamuthandiza kuchita zimenezi? Choyamba, Yesu ankakonda anthu. Monga tinaonera munkhani yapita ija, zimene zimamusangalatsa kwambiri ndi “zokhudzana ndi ana a anthu.” (Miy. 8:31) Kukonda anthu n’kumene kunamuthandiza kuti azimvetsa maganizo awo. Paja mtumwi Yohane ananena kuti Yesu “anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.” (Yoh. 2:25) Yesu ankaganizira kwambiri anthu ena. Anthu ankachita kuoneratu kuti amawakonda ndipo ankamvetsera uthenga wa Ufumu. Ifenso tikamakonda anthu, ntchito yathu yolalikira iziyenda bwino.​—2 Tim. 4:5.

3-4. (a) Ngati ndife achifundo, kodi tingakhale ndi maganizo ati polalikira? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Mtumwi Paulo ankadziwa kuti ali ndi udindo wolalikira ndipo ndi mmene ifenso timamvera. (1 Akor. 9:16) Koma ngati tili ndi chifundo, sitingagwire ntchito yolalikira chifukwa choti ndi udindo wathu basi. Tingamaigwire m’njira yosonyeza kuti ndife achikondi ndipo tikufuna kuthandiza anthu. Timadziwanso kuti “kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Tikamalalikira tili ndi maganizo amenewa, tikhoza kukhala osangalala kwambiri.

4 Munkhaniyi tikambirana mmene tingasonyezere chifundo mu utumiki. Choyamba tiona zimene tikuphunzira pa chitsanzo cha Yesu. Kenako tikambirana njira 4 zosonyeza mmene tingamutsanzirire.​—1 Pet. 2:21.

YESU ANKASONYEZA ANTHU CHIFUNDO MU UTUMIKI

Chifundo chinathandiza Yesu kuti azilalikira uthenga wolimbikitsa (Onani ndime 5-6)

5-6. (a) Kodi Yesu ankasonyeza chifundo kwa ndani? (b) Mogwirizana ndi ulosi wa pa Yesaya 61:1, 2, n’chifukwa chiyani Yesu anamvera chifundo anthu amene ankawalalikira?

5 Tiyeni tikambirane mmene Yesu anasonyezera chifundo mu utumiki. Tsiku lina, Yesu ndi ophunzira ake anagwira ntchito yolalikira mwakhama kwambiri. Iwo analibe nthawi “ngakhale yoti adye chakudya.” Ndiyeno Yesu anauza ophunzira ake kuti apite kwaokhaokha kumalo opanda anthu kuti akapumule pang’ono. Koma khamu lalikulu la anthu linathamangira kumene ankapita moti linayamba ndi khamulo kufika kumalowo. Yesu atafika anangoona kuti khamulo lafika kale. Kodi iye anatani? Yesu “anawamvera chifundo, * chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Choncho anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”​—Maliko 6:30-34.

6 N’chifukwa chiyani Yesu anamvera chifundo anthu aja? Iye anaona kuti anthuwo “anali ngati nkhosa zopanda m’busa.” Mwina Yesu anazindikira kuti ena mwa anthuwo anali osauka ndipo ankagwira ntchito nthawi yaitali kuti apezere mabanja awo zinthu zofunika pa moyo. Mwina ena anali oferedwa. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Yesu ankamvetsa mmene zinthu zinalili pa moyo wawo. Munkhani yapita ija tinakambirana kuti Yesu ayenera kuti anakumanapo ndi ena mwa mavuto amenewa. Yesu ankaganizira anthu ena ndipo ankawachitira chifundo n’kumawauza uthenga wolimbikitsa.​—Werengani Yesaya 61:1, 2.

7. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

7 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yesu? Nafenso timakumana ndi anthu amene ali ngati “nkhosa zopanda m’busa.” Anthuwo amakumana ndi mavuto ambirimbiri. Uthenga wa Ufumu, umene timalalikira, ndi umene ungawathandize kwambiri. (Chiv. 14:6) Choncho mofanana ndi Yesu, tiyenera kulalikira chifukwa ‘chomvera chisoni anthu onyozeka ndi osauka.’ (Sal. 72:13) Mtima wa chifundo umatilimbikitsa kuti tizithandiza anthu.

KODI TINGASONYEZE BWANJI CHIFUNDO?

Tiziganizira mavuto amene munthu aliyense akukumana nawo (Onani ndime 8-9)

8. Kodi tingasonyeze bwanji chifundo mu utumiki? Perekani chitsanzo.

8 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamvera chifundo anthu amene timawalalikira? Tiyenera kuganizira kuti, Kodi ineyo ndikanakhala kuti ndakumana ndi mavuto awowa, ndikanafuna kuti anthu andichitire zotani? Kenako tiziwachitira zimene ifeyo tikanafuna kuchitiridwazo. * (Mat. 7:12) Tiyeni tikambirane njira 4 zosonyeza mmene tingachitire zimenezi. Choyamba, tiziganizira vuto la munthu aliyense. Ntchito yolalikira imafanana ndi ya dokotala. Dokotala wabwino amaganizira vuto la wodwala aliyense. Amafunsa mafunso komanso kumvetsera mwatcheru pamene wodwalayo akufotokoza mmene akumvera. Samangofulumira kupereka mankhwala amene waganiza. Koma amaona bwinobwino zizindikiro zimene wodwalayo ali nazo kenako n’kupereka mankhwala oyenera. Nafenso tikamalalikira tisamangofotokoza zinthu zofanana kwa aliyense amene tingakumane naye. M’malomwake, tiziganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthu aliyense komanso maganizo ake.

9. Kodi tisamafulumire kuganiza kuti tikudziwa chiyani? Fotokozani.

9 Mukakumana ndi munthu mu utumiki, musamaganize kuti mukudziwa za moyo wake, zimene amakhulupirira komanso chifukwa chake amakhulupirira zimenezo. (Miy. 18:13) M’malomwake muzimufunsa mafunso okuthandizani kudziwa maganizo ake. (Miy. 20:5) Ngati n’zotheka m’dera lanu, muziwafunsa zokhudza ntchito yawo, banja lawo, chikhalidwe chawo komanso maganizo awo. Tikamakambirana ndi anthu zinthu zimenezi zimakhala ngati tikuwalola kutiuza chifukwa chake akufunikira uthenga wabwino. Tikadziwa zinthu zimenezi tikhoza kuchitira munthu chifundo n’kumuthandiza m’njira yoyenera ngati mmene Yesu ankachitira.​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:19-23.

Tiziganizira zimene munthu amene tikumulalikira akhoza kukumana nazo (Onani ndime 10-11)

10-11. Malinga ndi 2 Akorinto 4:7, 8, kodi njira ina imene tingasonyezere chifundo ndi iti? Perekani chitsanzo.

10 Chachiwiri, tiziganizira mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Tikatero tikhoza kuzindikira mavuto amene akukumana nawo. Ndipotu anthufe timakumana ndi mavuto ofanana ndithu. (1 Akor. 10:13) Timadziwanso kuti moyo m’dziko loipali ndi wamavuto okhaokha. Yehova ndi amene amatithandiza kupirira. (Werengani 2 Akorinto 4:7, 8.) Ndiye mukuganiza kuti anthu amene sali pa ubwenzi ndi Yehova amapirira bwanji mavuto amene amakumana nawo? Mofanana ndi Yesu, mtima wachifundo umatilimbikitsa kuti tiziwalalikira “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”​—Yes. 52:7.

11 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale Sergey. M’baleyu asanaphunzire choonadi anali wamanyazi ndipo sankakonda kunena maganizo ake. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo. Sergey anati: “Nditayamba kuphunzira Baibulo ndinazindikira kuti Mkhristu aliyense ali ndi udindo wouza anthu zimene amakhulupirira. Poyamba ndinkaganiza kuti sindingathe kuchita zimenezi ngakhale pang’ono.” Koma kenako anayamba kuganizira anthu amene sanamvepo choonadi komanso mmene moyo wawo ulili chifukwa chosadziwa Yehova. M’baleyu anati: “Zinthu zatsopano zimene ndinaphunzira zinandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima komanso ndizisangalala. Ndinaona kuti anthu ena afunikanso kuphunzira mfundo za choonadi zimene ndinaphunzira.” Mtima wachifundo utayamba kukula, mantha oopa kulalikira anayamba kuchepa. Sergey anati: “Ndinadabwa kuona kuti nditayamba kuuza ena mfundo za m’Baibulo ndinakhala wolimba mtima kwambiri. Mfundozo zinayambanso kukhazikika mumtima mwanga.” *

Anthu ena amatenga nthawi kuti akule mwauzimu (Onani ndime 12-13)

12-13. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oleza mtima pophunzitsa anthu? Perekani chitsanzo.

12 Chachitatu, tizileza mtima ndi anthu amene timawaphunzitsa. Tizikumbukira kuti anthuwo mwina sanaganizirepo mfundo za m’Baibulo zimene ifeyo timazidziwa bwino. Ndipo ambiri amakonda kwambiri mfundo zimene amakhulupirira. Mwina amaona kuti mfundo zimene amakhulupirirazo zimawathandiza kuti azigwirizana ndi achibale awo, anthu am’dera lawo kapena achikhalidwe chawo. Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

13 Kuti timvetse nkhaniyi, tiyerekezere kuti mlatho ukutha ndipo pakufunika kukonza watsopano. Nthawi zambiri mlatho watsopano umayamba kukonzedwa wakalewo udakalipo komanso ukugwira ntchito. Watsopanowo ukatha m’pamene amagwetsa wakalewo. N’chimodzimodzi ndi ntchito yophunzitsa anthu mfundo za choonadi. Tisanawauze kuti asiye kukhulupirira mfundo zawo tiyenera kuwathandiza kuti amvetse bwino mfundo zatsopano zimene sakuzidziwa bwino. Akamvetsa zatsopanozo m’pamene angathe kusiya zimene ankakhulupirira poyamba. Ndiye kuti zimenezi zichitike pangadutse nthawi yambiri.​—Aroma 12:2.

14-15. Kodi tingathandize bwanji anthu amene amangodziwa zochepa kapena sadziwa n’komwe za moyo wosatha padziko lapansi? Perekani chitsanzo.

14 Ngati ndife oleza mtima, sitidzayembekezera kuti anthu amvetse komanso kuvomereza mfundo za m’Baibulo pa ulendo woyamba. Mtima wachifundo ungatithandize kuti tizikambirana nawo Malemba kwa nthawi yaitali ndithu. Tiyerekeze kuti tikukambirana ndi munthu za moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Anthu ambiri amangodziwa zochepa pa nkhaniyi ndipo ena sadziwa chilichonse. Mwina amakhulupirira kuti munthu akafa zonse zimathera pomwepo. Apo ayi amakhulupirira kuti anthu abwino onse amapita kumwamba. Ndiye kodi tingawathandize bwanji?

15 M’bale wina anafotokoza zimene zimamuthandiza. Choyamba, amawerengera munthu lemba la Genesis 1:28. Kenako amamufunsa kuti, “Kodi Mulungu ankafuna kuti anthu azikhala kuti, nanga azikhala motani?” Ambiri amayankha kuti, “Padziko lapansi mosangalala.” Kenako m’baleyo amawerenga Yesaya 55:11 n’kufunsa munthuyo ngati cholinga cha Mulungu chinasintha. Nthawi zambiri anthu amayankha kuti sichinasinthe. Pomaliza, m’baleyo amawerenga Salimo 37:10, 11 n’kufunsa munthuyo kuti, “Malinga ndi vesili, kodi n’chiyani chidzachitike m’tsogolo?” Malemba ngati amenewa amathandiza anthu ambiri kumvetsa mfundo yoti Mulungu akufunabe kuti anthu akhale m’Paradaiso padziko lapansi.

Zinthu zochepa monga kulemba kalata zingalimbikitse kwambiri munthu (Onani ndime 16-17)

16-17. Mogwirizana ndi Miyambo 3:27, kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere chifundo? Perekani chitsanzo.

16 Cha nambala 4, tizifufuza njira zosonyezera chifundo. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mwapeza munthu kunyumba kwake koma pa nthawi imene iyeyo akuona kuti si yabwino? Ndi bwino kungopepesa n’kulonjeza kuti tibweranso nthawi yabwino. Nanga mungatani ngati pakhomo lina pali kantchito kenakake koti mungathandize? Tiyerekezenso kuti mwapeza munthu amene ali ndi vuto loti sangachoke pakhomo koma angafunike kumuthandiza zinthu zina monga kumugulira zinazake? Pa nthawi ngati imeneyi, zingakhale bwino kuwathandiza.​—Werengani Miyambo 3:27.

17 Mlongo wina atangosonyeza chifundo pochita zinthu zochepa, zotsatira zake zinali zabwino kwambiri. Mwana wa m’banja lina atamwalira, iye analembera banjalo kalata yowapepesa. M’kalatayo anaikamo malemba olimbikitsa. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mayi woferedwayo analemba kuti: “Ine dzulo sizimandiyendera ngakhale pang’ono. Mwina simungamvetse mmene kalata yanu inatithandizira. Dzulo ndinawerenga kalata yanu maulendo oposa 20. Kunena zoona, inasonyezeratu kuti ndinu wokoma mtima, wachikondi komanso wolimbikitsa. Ndikukuthokozani kuchokera pansi pa mtima.” Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti tikamaganizira mavuto amene anzathu akukumana nawo n’kuwathandiza, zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri.

TIZIDZIWA MALIRE ATHU

18. Malinga ndi 1 Akorinto 3:6, 7, kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamalalikira?

18 Koma tiyenera kudziwa malire athu tikamalalikira. Tizikumbukira kuti mbali yathu pa ntchito yothandiza anthu kuti aphunzire za Mulungu ndi yochepa kwambiri. (Werengani 1 Akorinto 3:6, 7.) Yehova ndi amene amakokera anthu m’gulu lake. (Yoh. 6:44) Ndipo pamapeto pake, munthu aliyense amalandira kapena kukana uthenga wabwino malinga ndi mmene mtima wake ulili. (Mat. 13:4-8) Tizikumbukira kuti Yesu anali Mphunzitsi wabwino kwambiri koma anthu ambiri sanalandire uthenga wake. Choncho tisamakhumudwe ngati anthu ena sanatilandire bwino.

19. Kodi chimachitika n’chiyani tikamasonyeza chifundo mu utumiki?

19 Tikamasonyeza chifundo mu utumiki zotsatira zake zimakhala zabwino ndipo utumikiwo umakhala wosangalatsa. Paja Baibulo limanena kuti munthu amakhala ndi chimwemwe kwambiri ngati ali wopatsa. Tikamalalikira timapereka uthenga wabwino kwa anthu amene ali ndi maganizo oyenera moyo wosatha. (Mac. 13:48) Choncho “ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino.” (Agal. 6:10) Tikatero tidzakhala osangalala podziwa kuti tikulemekeza Atate wathu wakumwamba.​—Mat. 5:16.

NYIMBO NA. 64 Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala

^ ndime 5 N’chifukwa chiyani tinganene kuti tikamasonyeza chifundo, tikhoza kumasangalala mu utumiki ndipo zinthu zingamatiyendere bwino? Munkhaniyi tikambirana chitsanzo cha Yesu pa nkhani yosonyeza chifundo. Kenako tiona mmene ifeyo tingasonyezere chifundo kwa anthu amene timawalalikira.

^ ndime 5 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Munkhaniyi, mawu oti chifundo akutanthauza kuganizira mmene munthu wina akumvera chifukwa cha mavuto kapena kuzunzidwa. Chifundo choterechi chimapangitsa munthu kuchita chilichonse chimene angathe kuti athandize anthu.

^ ndime 8 Onani nkhani yakuti “Muzichitira Anthu Zimene Mungafune Kuti Akuchitireni” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2014.

^ ndime 11 Onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 2011, tsamba 21-22.