Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 10

Cikuniletsa Kubatizika N’ciani?

Cikuniletsa Kubatizika N’ciani?

“Filipo ndi nduna ija, anatsika ndi kulowa m’madzimo ndipo anaibatiza.”—MAC. 8:38.

NYIMBO 52 Kudzipeleka Monga Mkhristu

ZA M’NKHANI INO *

1. Kodi Adamu na Hava anataya ciani? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

KODI muganiza kuti n’ndani ayenela kutiikila miyezo ya cabwino na coipa? Pamene Adamu na Hava anadya cipatso ca mtengo wodziŵitsa cabwino na coipa, anaonetselatu kuti sanali kudalila Yehova na miyezo yake. Iwo anasankha kudziikila miyezo yawo ya cabwino na coipa. (Gen. 3:22) Koma ganizilani cabe zimene iwo anataya. Anataya mwayi wokhala paubwenzi na Yehova. Anatayanso mwayi wokhala na moyo wosatha. Ndipo anapatsila ana awo ucimo na imfa. (Aroma 5:12) Zimene Adamu na Hava anasankha, zinabweletsa mavuto osaneneka.

Nduna ya ku Itiyopiya itakhulupilila mwa Yesu, siinazengeleze kubatizika (Onani ndime 2-3)

2-3. (a) Kodi nduna ya ku Itiyopiya inacita ciani pambuyo polalikidwa na Filipo? (b) Ni madalitso ati amene timapeza tikabatizika? Nanga tidzakambilana mafunso ati?

2 Zimene Adamu na Hava anasankha kucita n’zosiyana kwambili na zimene nduna ya ku Itiyopiya inacita pambuyo polalikidwa na Filipo. Ndunayo inayamikila kwambili itamva zimene Yehova na Yesu anaticitila, cakuti nthawi yomweyo inabatizika. (Mac. 8:34-38) Tikadzipatulila kwa Mulungu na kubatizika monga mmene nduna ya ku Itiyopiya inacitila, timaonetsa poyela kuti timayamikila zimene Yehova na Yesu anaticitila. Timaonetsanso kuti timadalila Yehova, na kuzindikila kuti iye ndiye woyenela kutiikila miyezo ya cabwino na coipa.

3 Ganizilani cabe kuculuka kwa madalitso amene timalandila cifukwa cotumikila Yehova. Mwacitsanzo, tili na ciyembekezo cakuti posacedwa, Yehova adzatipatsa zonse zimene Adamu na Hava anataya, kuphatikizapo moyo wosatha. Ndipo cifukwa cokhulupilila mwa Yesu Khristu, Yehova amatikhululukila macimo athu na kutipatsa cikumbumtima coyela. (Mat. 20:28; Mac. 10:43) Timakhalanso mbali ya banja la Yehova la atumiki ake amene iye wawalonjeza tsogolo labwino. (Yoh. 10:14-16; Aroma 8:20, 21) Ngakhale kuti pali madalitso amenewa, anthu ena akaphunzila za Yehova, amawayawaya kutengela citsanzo ca nduna ya ku Itiyopiya. Kodi ni zopinga ziti zimene zimawapangitsa kuwayawaya kubatizika? Nanga angagonjetse bwanji zopinga zimenezo?

ZOPINGA ZIMENE ZIMALEPHELETSA ENA KUBATIZIKA

Zopinga zimene zimalepheletsa ena kubatizika

Kudzikayikila (Onani ndime 4-5) *

4-5. Kodi Avery na Hannah anali na zopinga zotani?

4 Kudzikayikila. M’nyamata wina dzina lake Avery, makolo ake ni Mboni. Atate ake ni m’bale wa citsanzo cabwino. Iwo ni mkulu waluso komanso kholo lacikondi. Koma Avery anali kuwayawaya kubatizika. Cifukwa ciani? Avery anati: “N’nali kuona kuti siningakwanitse kukhala wacitsanzo cabwino monga atate.” Avery analinso kudzikayikila kuti sadzakwanitsa kusamalila maudindo amene angadzalandile kutsogolo. Iye anati: “N’nali kuyopa kuti tsiku lina adzaniuza kupemphela pagulu, kukamba nkhani, kapena kutsogolela kagulu ka ulaliki.”

5 Nayenso Hannah, mtsikana wa zaka 18, anali na vuto lalikulu la kudzikayikila. Makolo ake ni Mboni za Yehova. Ngakhale n’conco, iye anali kukayikila zoti angakwanitse kutsatila malamulo a Yehova mu umoyo wake. N’cifukwa ciani anali kukayikila? Cifukwa anali kudziona ngati wacabe-cabe. Nthawi zina, anali kufika mpaka podzivulaza mwadala. Izi zinali kungowonjezela vuto lake. Hannah anati: “Sin’nauzeko aliyense zimene n’nali kucita, ngakhale makolo anga. Ndipo n’nali kuganiza kuti cifukwa ca zimene n’nali kucita, Yehova sangafune olo pang’ono kuti nikhale mtumiki wake.”

Kusonkhezeledwa na Mabwenzi (Onani ndime 6) *

6. N’ciani cinali kulepheletsa Vanessa kubatizika?

6 Kusonkhezeledwa na mabwenzi. Vanessa, mtsikana wa zaka 22, anati: “N’nali na mnzanga wa pamtima amene n’nakhala naye pa ubwenzi kwa zaka pafupi-fupi 10.” Komabe, mnzakeyo sanali Mboni, ndipo sanali kum’limbikitsa kukwanilitsa colinga cake cokabatizika. Izi zinam’khudza kwambili Vanessa. Iye anati: “Zimanivuta kupanga mabwenzi. Conco, n’nali kuyopa kuti nikathetsa ubwenziwo, sinidzakwanitsa kupeza mnzanga wina.”

Kuyopa Kuti Adzacimwa (Onani ndime 7) *

7. Kodi Makayla anali kuyopa ciani? Nanga n’cifukwa ciani anali kuyopa?

7 Kuyopa kuti adzacimwa. Mtsikana wina, dzina lake Makayla, anali na zaka 5 pamene m’bale wake wamkulu anacotsedwa mumpingo. Pamene Makayla anali kukula, anaona kuti zimene m’bale wakeyo anacita zinawakhudza kwambili makolo ake. Makayla anati: “N’nali kuyopa kubatizika cifukwa coganiza kuti na ine nidzacimwa, n’kucotsedwa mumpingo. Ndipo izi zidzawonjezela cisoni ca makolo anga.”

Kuyopa Kutsutsidwa (Onani ndime 8) *

8. Kodi Miles anali kuyopa ciani?

8 Kuyopa kutsutsidwa. Atate ŵake a mnyamata wina, dzina lake Miles komanso amayi ake opeza, onse amatumikila Yehova. Koma amayi ake omubala si Mboni. Miles anati: “Kwa zaka 18, n’nali kukhala na amayi onibala. Pamene atate anakhala Mboni, amayi anayamba kuwatsutsa kwambili. Conco, poganiza kuti na ine adzanitsutsa, n’nali kuyopa kuwauza kuti nifuna kubatizika.”

KODI MUNGAGONJETSE BWANJI ZOPINGA ZIMENEZI?

9. Cingacitike n’ciani mukadziŵa zambili zokhudza kuleza mtima kwa Yehova na cikondi cake?

9 Adamu na Hava anasankha kupandukila Yehova cifukwa sanakulitse cikondi cawo pa iye. Olo zinali conco, Yehova anawalola kukhala na moyo kwa zaka zambili ndithu, n’colinga cakuti abeleke ana na kudziikila okha malangizo olelela anawo. Posapita nthawi, zotulukapo za kusamvela kwa Adamu na Hava, zinaonetsa kuti iwo sanacite zinthu mwa nzelu. Mwana wawo wamkulu anapha mng’ono wake wosalakwa. Ndipo m’kupita kwa nthawi, ciwawa komanso dyela zinaculuka pakati pa anthu. (Gen. 4:8; 6:11-13) Komabe, Yehova anakonza njila yopulumutsila ana onse a Adamu na Hava amene amasankha kum’tumikila. (Yoh. 6:38-40, 57, 58) Pamene muphunzila zambili zokhudza kuleza mtima kwa Yehova na cikondi cake, cikondi canu pa iye cidzakula. Komanso, mudzapewa kutengela zocita za Adamu na Hava. M’malomwake, mudzasankha kudzipatulila kwa Yehova.

Mmene mungagonjetsele zopinga zimenezi (Onani ndime 9-10) *

10. Kodi kusinkha-sinkha Salimo 19:7 kungakuthandizeni bwanji kutumikila Yehova?

10 Pitilizani kuphunzila za Yehova. Mukaphunzila zambili zokhudza Yehova, m’pamenenso mumakhala na cidalilo cakuti mungakwanitse kum’tumikila. Avery, amene tam’chula kuciyambi, anati: “Cidalilo canga cinakula pamene n’naŵelenga na kusinkha-sinkha mawu a pa Salimo 19:7.” (Ŵelengani.) Pamene Avery anaona mmene Yehova amakwanilitsila mawu a pa lembali, akuti ‘amapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu,’ cikondi cake pa Mulungu cinalimbilako. Kuwonjezela potithandiza kukhala na cidalilo, cikondi cimatithandizanso kukhala na cikhumbo cotumikila Yehova na kupewa kucita zinthu zom’khumudwitsa. Hannah, amene tam’tomola kuciyambi, anati: “Kucita phunzilo laumwini, kwanithandiza kuzindikila kuti ngati nidzivulaza, Yehova sakondwela nazo.” (1 Pet. 5:7) Hannah anayamba ‘kucita zimene mawu’ a Mulungu amanena. (Yak. 1:22) Kodi panakhala zotulukapo zanji? Iye anati: “N’taona mmene kumvela Yehova kwanithandizila, n’nayamba kum’konda kwambili. Tsopano nili na cidalilo cakuti nikakumana na vuto, Yehova nthawi zonse adzanithandiza.” Hannah anagonjetsa vuto lake lodzivulaza. Ndipo anadzipatulila kwa Yehova na kubatizika.

(Onani ndime 11) *

11. N’ciani cimene Vanessa anacita kuti apeze mabwenzi abwino? Nanga tiphunzilaponji?

11 Sankhani mabwenzi anu mwanzelu. Vanessa, amene tam’chula kuciyambi, anazindikila kuti mnzake anali kumulepheletsa kutumikila Yehova. Conco, iye anathetsa ubwenzi wawo. Kuwonjezela apo, anayesetsa kupeza mabwenzi atsopano mumpingo. Iye anakamba kuti citsanzo ca Nowa na banja lake n’cimene cinam’limbikitsa. Vanessa anati: “Nowa na banja lake anali kukhala pakati pa anthu osakonda Yehova. Koma iwo monga banja, anali kukhala na mayanjano abwino pakati pawo.” Vanessa atabatizika, anayamba upainiya. Iye anati: “Upainiya wanithandiza kupeza mabwenzi abwino mumpingo mwathu, ngakhale m’mipingo ina.” Na imwe mungapeze mabwenzi abwino ngati mumatangwanika kwambili pa nchito yolalikila imene Yehova watipatsa.—Mat. 24:14.

(Onani ndime 12-15) *

12. Kodi Adamu na Hava analibe mantha abwanji? Nanga panakhala zotulukapo zanji?

12 Khalani na mantha oyenelela. Mantha ena amakhala oyenelela. Mwacitsanzo, tifunika kukhala na mantha oyenelela oopa kukhumudwitsa Yehova. (Sal. 111:10) Adamu na Hava akanakhala na mantha aconco, sembe sanam’pandukile Yehova. Koma anam’pandukila. Atam’pandukila, maso awo anatseguka, kutanthauza kuti anazindikila kuti ni ocimwa. Anazindikilanso kuti adzapatsila ana awo ucimo na imfa. Ataona kapena kuti kuzindikila kuti ni ocimwa, anacita manyazi na umalisece wawo, cakuti anadzipangila zovala zamasamba.—Gen. 3:7, 21.

13-14. (a) Malinga na 1 Petulo 3:21, n’cifukwa ciani sitifunika kuopa kwambili imfa? (b) Kodi tili na zifukwa zanji zom’kondela Yehova?

13 Kukhala na mantha oyenelela oopa kukhumudwitsa Yehova n’kofunika. Koma bwanji ponena za imfa. Kodi tiyenela kuiopa kwambili? Iyai, cifukwa Yehova anakonza njila yotithandiza kuti tikapeze moyo wosatha. Ndipo ngati tacimwa, koma n’kulapa mocokela pansi pamtima, iye amatikhululukila. Yehova amatikhululukila cifukwa timakhulupilila nsembe ya dipo la Mwana wake. Njila imodzi yaikulu imene timaonetsela kuti tili na cikhulupililo ni mwa kudzipatulila kwa Mulungu na kubatizika.—Ŵelengani 1 Petulo 3:21.

14 Tili na zifukwa zambili zotipangitsa kum’konda Yehova. Mulungu amatipatsa zinthu zabwino zimene timakondwela nazo tsiku lililonse. Komanso, amatiphunzitsa coonadi ponena za iye na colinga cake. (Yoh. 8:31, 32) Yehova watipatsa mpingo wacikhristu kuti uzititsogolela na kutithandiza. Iye amatithandizanso kupilila mavuto athu, komanso watipatsa ciyembekezo cokakhala na moyo wamuyaya kutsogolo tili angwilo. (Sal. 68:19; Chiv. 21:3, 4) Tikamaganizila zinthu zambili zimene Yehova waticitila cifukwa ca cikondi cake, timayamba kum’konda kwambili. Ndipo cikondi cimeneco, cimatithandiza kukhala na mantha oyenelela. Timayopa kum’khumudwitsa, cifukwa tim’konda kwambili.

15. Kodi Makayla anagonjetsa bwanji vuto lake loyopa kuti adzacita chimo?

15 Makayla amene tam’chula kuciyambi, anagonjetsa vuto lake loyopa kulakwa, pamene anadziŵa kuti Yehova amakhululukila. Makayla anati: “N’naphunzila kuti tonse ndife anthu opanda ungwilo na kuti timalakwitsa. N’naphunzilanso kuti Yehova amatikonda, ndipo amatikhululukila pa maziko ansembe ya dipo.” Cikondi cimene Makayla ali naco pa Yehova cinam’sonkhezela kudzipatulila kwa iye na kubatizika.

(Onani ndime 16) *

16. N’ciani cinathandiza Miles kugonjetsa vuto lake loyopa kutsutsidwa?

16 Miles, amene anali kuyopa kuti amayi ake adzamutsutsa akasankha kubatizika, anapempha malangizo kwa woyang’anila dela wina. Miles anati: “Mofanana na ine, woyang’anila delayo anabadwila m’banja la makolo osiyana zikhulupililo. Iye ananithandiza kupeza njila yabwino yofotokozela amayi kuti n’nasankha nekha kubatizika, osati kuti atate ndiwo anali kunikakamiza kutelo.” Miles atawafotokozela amayi ake za cosankha cake, iwo anakhumudwa. M’kupita kwa nthawi, amayi ake anam’cotsa panyumba pawo. Koma iye sanasinthe maganizo ake. Miles anati: “Pamene n’naphunzila na kuona zinthu zabwino zimene Yehova wanicitila, n’nakhudzika mtima kwambili. N’taganizila mozama za nsembe ya dipo ya Yesu, n’nazindikila kuti Yehova amanikonda kwambili. Izi zinanisonkhezela kudzipatulila kwa iye na kubatizika.”

PITILIZANI KUCITA ZINTHU MOGWILIZANA NA COSANKHA CANU

Tingaonetse kuti timayamikila zimene Mulungu waticitila mwa kubatizika (Onani ndime 17)

17. Kodi tonse tili na mwayi wotani?

17 Zimene Hava anacita, za kudya cipatso ca mtengo wa m’munda wa Edeni, zinaonetsa kuti wakana Atate wake wakumwamba. Komanso pamene Adamu anamvela Hava mwa kudya cipatso coletsedwa, anaonetsa kusayamikila zabwino zonse zimene Yehova anam’citila. Conco, tonsefe tili na mwayi woonetsa kuti, mosiyana na Adamu na Hava, tili na mtima woyamikila. Tikabatizika, timaonetsa kuti timakhulupilila kuti Atate wathu wakumwamba Yehova, ndiye ali na udindo wotiikila miyezo ya cabwino na coipa. Timaonetsanso kuti timam’konda komanso timam’dalila.

18. Mungacite ciani kuti zinthu zizikuyendelani bwino potumikila Yehova?

18 Tikabatizika, timakhala na udindo wotsatila miyezo ya Yehova tsiku lililonse, osati yathu. Izi n’zimene atumiki a Mulungu mamiliyoni ambili amacita. Na imwe mungakwanitse kucita zimenezi ngati mupitiliza kukulitsa cidziŵitso canu ca Mawu a Mulungu Baibo, kupezeka pa misonkhano nthawi zonse, komanso kuuzako ena mwakhama zimene mumaphunzila zokhudza Atate wanu wacikondi, Yehova. (Aheb. 10:24, 25) Popanga zosankha, muzitsatila malangizo amene Yehova amapeleka kupitila m’Baibo na gulu lake. (Yes. 30:21) Mukatelo, zocita zanu zonse zidzakuyendelani bwino.—Miy. 16:3, 20.

19. Kodi mufunika kumaganizila ciani nthawi zonse? Nanga n’cifukwa ciani muyenela kutelo?

19 Pamene mupitiliza kuganizila ubwino wotsatila malangizo a Yehova, mumayamba kum’konda kwambili na kukondanso malamulo ake. Zikakhala conco, Satana sangakwanitse kukukopani kuti muleke kutumikila Yehova. Tangoyelekezani kuti muli na moyo zaka 1000 kutsogolo. Ndithudi, mudzakondwela ngako pokumbukila cosankha cabwino kwambili cobatizidwa cimene munapanga!

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova

^ ndime 5 Cosankha cofunika kwambili cimene mungapange mu umoyo wanu ni ca kubatizika. N’cifukwa ciani kubatizika n’kofunika kwambili? Nkhani ino idzayankha funso limeneli. Idzathandizanso anthu amene akuganizila zobatizika kugonjetsa zopinga zina zimene zingawapangitse kuzengeleza kubatizika.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kudzikayikila: M’bale wacinyamata akucita mantha kuyankhapo pa misonkhano.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mabwenzi: Mlongo wacicepele amene ali na mnzake wa khalidwe loipa akucita manyazi ataona alongo ena akulalikila.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kuyopa kuti adzacimwa: Pamene m’bale wacotsedwa mu mpingo na kucoka panyumba, mlongosi wake wacicepele akucita mantha poganiza kuti nayenso adzacimwa na kucotsedwa mu mpingo.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kutsutsidwa: Mnyamata akucita mantha kupemphela pamaso pa amayi ake amene si Mboni.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kudzikayikila: Conco, wayamba kukonzekela misonkhano mwakhama pa phunzilo lake laumwini.

^ ndime 66 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mabwenzi: Pambuyo pake, wayamba kunyadila mwayi wake wokhala Mboni.

^ ndime 68 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kuyopa kuti adzacimwa: Koma pambuyo pake, akulimbitsa ubwenzi wake na Yehova, ndipo kenako akubatizika.

^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Kutsutsidwa: Patapita nthawi, akufotokozela amayi ake molimba mtima zimene amakhulupilila.