Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 11

Mvelani Mawu a Yehova

Mvelani Mawu a Yehova

“Uyu ndiye Mwana wanga . . . Muzimumvela.”—MAT. 17:5.

NYIMBO 89 Mvela Udalitsike

ZA M’KHANI INO *

1-2. (a) Kodi Yehova wakhala akuseŵenzetsa njila ziti pokamba ndi anthu? (b) Kodi tidzakambila ciani m’nkhani ino?

YEHOVA amakondwela kukamba nafe. Kale, anali kuseŵenzetsa aneneli, angelo, komanso Mwana wake Yesu Khristu pokamba ndi anthu. (Amosi 3:7; Agal. 3:19; Chiv. 1:1) Koma masiku ano, Mulungu amakamba nafe kupitila m’Mawu ake, Baibo. Iye anatipatsa Baibo n’colinga cakuti tidziŵe mmene amaonela zinthu, komanso kuti timvetse njila zake.

2 Pamene Yesu anali padziko lapansi, Yehova anakamba naye maulendo atatu kucokela kumwamba. Tsopano tiyeni tikambilane zimene Yehova anakamba, zimene tiphunzilapo pa mawu akewo, komanso mmene timapindulila na zimene anakambazo.

“IWE NDIWE MWANA WANGA WOKONDEDWA”

3. Malinga na Maliko 1:9-11, kodi Yehova anakamba ciani pa ubatizo wa Yesu? Nanga mawu amenewo anatsimikizila mfundo zofunika ziti?

3 Maliko 1:9-11 imafotokoza cocitika coyamba pamene Yehova anakamba na Yesu kucokela kumwamba. (Ŵelengani) Pa nthawiyo, Yehova anati: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwela nawe.” Yesu ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili kumvela mawu a Atate wake, oonetsa kuti amam’konda na kum’dalila. Mawu amenewa a Yehova anatsimikizila mfundo zitatu zofunika zokhudza Yesu. Yoyamba, ni yakuti Yesu ni Mwana wake. Yaciŵili, ni yakuti Yehova amam’konda Mwana wakeyo. Ndipo yacitatu, ni yakuti amakondwela naye. Tiyeni tsopano tikambilane zambili pa mfundo iliyonse mwa mfundo zitatuzi.

4. Kodi Yesu anakhala Mwana wa Mulungu m’njila yapadela iti pa ubatizo wake?

4 “Iwe ndiwe Mwana wanga.” Pamene Yehova anakamba mawu amenewa, anaonetsa kuti Mwana wake wokondedwa, Yesu, anakhala pa ubale wapadela na iye. Pamene Yesu anali kumwamba, anali kale Mwana wa Mulungu. Koma pa ubatizo wake, iye anakhala Mwana wa Mulungu m’njila yapadela. Panthawiyo, Mulungu anaonetsa kuti Yesu, monga mwana wake wodzozedwa, tsopano ali na ciyembekezo cokakhala Mfumu yodzozedwa ya Ufumu wa Mulungu kumwamba, komanso Mkulu wa Ansembe. (Luka 1:31-33; Aheb. 1:8, 9; 2:17) Conco, m’pomveka kuti pa ubatizo wake, Yehova anamuuza kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga.”—Luka 3:22.

Timapita patsogolo mwauzimu ngati ena atiyamikila na kutilimbikitsa (Onani ndime 5) *

5. Tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani yoonetsa cikondi na kulimbikitsa ena?

5 “Wokondedwa.” Mawu amenewa a Yehova aonetsa kuti iye amakonda Mwana wake na kukondwela naye. Ndipo amatikumbutsa kuti tifunika kusakila mipata yolimbikitsila ena. (Yoh. 5:20) Timalimbikitsidwa ngati munthu amene timakonda waonetsa kuti nayenso amatikonda, komanso watiyamikila pa zabwino zimene timacita. Conco, nafenso tifunika kumalimbikitsa abale na alongo athu na kuwaonetsa cikondi. Tifunika kucita cimodzi-modzi kwa anthu a m’banja lathu. Tikayamikila ena, timalimbitsa cikhulupililo cawo na kuwasonkhezela kupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika. Maka-maka makolo, ayenela kuyesetsa kulimbikitsa ana awo. Ana amapita patsogolo mwauzimu ngati makolo awo amawayamikila mocokela pansi pa mtima na kuwaonetsa cikondi.

6. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala na cidalilo mwa Yesu Khristu?

6 “Ndimakondwela nawe.” Mawu amenewa aonetsa kuti Yehova anali na cidalilo cakuti Yesu adzacita cifunilo ca Atate wake mokhulupilika. Yehova amam’dalila kwambili mwana wake. Conco, nafenso sitiyenela kukayikila olo pang’ono kuti Yesu adzakwanilitsa zonse zimene Yehova anatilonjeza. (2 Akor. 1:20) Ngati tiganizila citsanzo ca Yesu, timakhala ofunitsitsa kuphunzila kwa iye na kutsatila citsanzo cake. Yehova alinso na cidalilo cakuti atumiki ake monga gulu, adzapitiliza kutsatila mapazi a Mwana wake.—1 Pet. 2:21.

“MUZIMUMVELA”

7. Malinga na Mateyu 17:1-5, ni pa cocitika cina citi pamene Yehova anakamba kucokela kumwamba? Nanga anakamba ciani?

7 Ŵelengani Mateyu 17:1-5. Pa cocitika caciŵili pamene Yehova anakamba kucokela kumwamba, ni panthawi imene Yesu “anasandulika.” Tsiku lina Yesu anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane n’kukwela nawo m’phili lalitali. Ali kumeneko, anaona masomphenya ocititsa cidwi. Nkhope ya Yesu na malaya ake zinawala kwambili. Kenako panaonekela anthu ena aŵili, Mose na Eliya. Iwo anayamba kukambilana na Yesu za imfa yake na kuukitsidwa kwake. Atumwiwo anali “atatopa ndi tulo,” koma atagalamuka anaona masomphenya ocititsa cidwi amenewa. (Luka 9:29-32) Ndiyeno, mtambo woyela unawaphimba. Kenako anamvela mawu a Mulungu kucokela mumtambowo. Mofanana na pa ubatizo wa Yesu, panthawiyi Yehova anakambanso mawu oonetsa kuti amakonda Mwana wake na kukondwela naye. Anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye.” Koma panthawiyi, Yehova anawonjezela mawu akuti: “Muzimumvela.”

8. Kodi masomphenya a kusandulika analimbikitsa bwanji Yesu na atumwi ake?

8 Masomphenyawa, anaonetsa ulemelelo komanso mphamvu zimene Yesu adzakhala nazo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Mwacionekele, izi zinam’limbikitsa Khristu na kum’patsa mphamvu yopilila mazunzo na imfa yoŵaŵa. Masomphenyawa analimbitsanso cikhulupililo ca atumwi ake. Ndipo izi zinawakonzekeletsa kaamba ka mayeselo amene anali kudzakumana nawo, komanso nchito yaikulu imene anali kudzagwila kutsogolo. Patapita zaka pafupi-fupi 30, mtumwi Petulo anakambapo za masomphenya a kusandulika kwa Yesu, kuonetsa kuti anali kuwakumbukilabe bwino masomphenyawo.—2 Pet. 1:16-18.

9. Ni malangizo othandiza ati amene Yesu anapatsa ophunzila ake?

9 “Muzimumvela.” Pamene Yehova anakamba mawu amenewa, anaonetselatu kuti amafuna kuti tizimvela mawu a Mwana wake. Kodi Yesu anakamba ciani pamene anali padziko lapansi? Anakamba zinthu zambili zofunika kuzimvela. Mwacitsanzo, mwacikondi anaphunzitsa otsatila ake mmene angalalikilile uthenga wabwino, komanso anawakumbutsa mobweleza-bweleza kuti afunika kukhala maso. (Mat. 24:42; 28:19, 20) Cinanso, anawalangiza kuti afunika ‘kuyesetsa mwamphamvu kuloŵa pakhomo lopapatiza,’ ndiponso anawalimbikitsa kuti sayenela kubwelela m’mbuyo. (Luka 13:24) Kuwonjezela apo, Yesu anauzanso otsatila ake kuti afunika kukondana wina na mnzake, kukhalabe ogwilizana, na kusunga malamulo ake. (Yoh. 15:10, 12, 13) Ndithudi, malangizo amenewa anali othandiza kwambili kwa atumwi ake! Ndipo malangizowa ni ofunikanso kwambili kwa ife monga mmene analili pa nthawi imene Yesu anawapeleka.

10-11. Tingaonetse bwanji kuti timamvela Yesu?

10 Yesu anati: “Aliyense amene ali kumbali ya coonadi amamvela mawu anga.” (Yoh. 18:37) Timaonetsa kuti timamvela mawu ake pamene ‘tipitiliza kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse.’ (Akol. 3:13; Luka 17:3, 4) Timaonetsanso kuti timamvela mawu ake, mwa kulalikila uthenga wabwino mokangalika “m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.” —2 Tim. 4:2.

11 Yesu anati: “Nkhosa zanga zimamva mawu anga.” (Yoh. 10:27) Otsatila a Khristu amaonetsa kuti amamvela mawu a Yesu mwa kucita zinthu mogwilizana ndi mawu ake. Iwo satangwanika na “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) M’malomwake, amaona kuti kumvela malamulo a Yesu n’kofunika kwambili, olo zinthu zivute bwanji mu umoyo wawo. Ambili mwa abale athu akukumana na mayeselo aakulu, monga kuzunzidwa ndi anthu otsutsa, umphawi, komanso masoka acilengedwe. Mosasamala kanthu za mavutowa, iwo akhalabe okhulupilika kwa Yehova. Ponena za Akhristu amenewa, Yesu anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso.”—Yoh. 14:21.

Nchito yathu yolalikila imatithandiza kupitiliza kumvela mawu a Yesu (Onani ndime 12) *

12. Ni njila ina iti imene tingaonetsele kuti timamvela Yesu?

12 Njila ina imene tingaonetsele kuti timamvela Yesu ni mwa kumvela na kugonjela anthu amene iye wawaika kukhala otsogolela pakati pathu. (Aheb. 13:7, 17) Gulu la Mulungu lapanga masinthidwe ambili m’zaka zaposacedwa. Ena mwa masinthidwe amenewa ni okhudza zida na njila zolalikilila, kacitidwe ka misonkhano ya mkati mwa wiki, komanso njila zomangila na kukonzanso Nyumba za Ufumu. Kukamba zoona, kusintha kumeneku kumatipindulitsa, ndipo kumaonetsa kuti gulu la Mulungu limatikonda. Timayamikila kwambili citsogozo cimeneci. Yehova adzatidalitsa kwambili ngati tiyesetsa kutsatila malangizo a panthawi yake, amene gulu lake limapeleka.

13. Kodi timapindula bwanji ngati timvela Yesu?

13 Timapindula ngati timvetsela zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa. Yesu analonjeza ophunzila ake kuti zimene anali kuphunzitsa zidzawatsitsimula. Iye anati: “Mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Mawu a Mulungu, amene amaphatikizapo mabuku anayi a Uthenga Wabwino wofotokoza umoyo na utumiki wa Yesu, amatitsitsimula, kutilimbikitsa mwauzimu, na kutipatsa nzelu. (Sal. 19:7; 23:3) Yesu anati: “Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28.

‘NDIDZALEMEKEZA DZINA LANGA’

14-15. (a) Kodi Yohane 12:27, 28 imafotokoza cocitika citi cacitatu pamene Yehova anakamba kucokela kumwamba? (b) N’cifukwa ciani tikamba kuti mawu a Yehova anam’limbikitsa Yesu?

14 Ŵelengani Yohane 12:27, 28. Buku la Uthenga Wabwino wa Yohane limafotokoza cocitika cacitatu pamene Yehova anakamba kucokela kumwamba. Pa nthawi ina, Yesu anapita ku Yerusalemu kukacita cikondwelelo ca Pasika. Apa n’kuti kwatsala masiku ocepa cabe kuti aphedwe. Ali kumeneko, Yesu anati: “Moyo wanga ukusautsika.” Kenako anapemphela kuti: “Atate lemekezani dzina lanu.” Ndiyeno, Atate wake anayankha kucokela kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”

15 Yesu anasautsika mtima cifukwa coganizila udindo waukulu umene anali nawo wokhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Iye anali kudziŵa kuti adzakwapulidwa mwankhanza, komanso kuti adzafa imfa yoŵaŵa. (Mat. 26:38) Ngakhale n’telo, anali kufunitsitsa kulemekeza dzina la Atate wake. Yesu anaimbidwa mlandu wonyoza Mulungu, ndipo anali kudela nkhawa kuti imfa yake idzabweletsa citonzo pa dzina la Mulungu. Conco, n’zoonekelatu kuti mawu amene Yehova anakamba anam’limbikitsa ngako! Izi zinam’thandiza kukhala na cidalilo cakuti zivute zitani, dzina la Yehova lidzalemekezedwa. Mawu a Atate wake anam’limbikitsa kwambili Yesu na kum’patsa mphamvu yopilila mayeselo amene anali kudzakumana nawo. Cioneka kuti Yesu yekha ndiye anamva mawu amene Atate wake anakamba pa nthawiyo. Ngakhale n’conco, Yehova anaonetsetsa kuti mawu akewo alembedwa kuti adzatilimbikitse tonsefe.—Yoh. 12:29, 30.

Yehova adzalemekeza dzina lake na kupulumutsa anthu ake (Onani ndime 16) *

16. N’zinthu ziti zingatipangitse kudela nkhawa citonzo cimene adani a Mulungu abweletsa pa dzina lake?

16 Mofanana ndi Yesu, nafenso tingadele nkhawa cifukwa ca kutonzedwa kwa dzina la Yehova. N’kuthekanso kuti monga mmene zinalili kwa Yesu, nafenso tikucitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Kapena tili na nkhawa cifukwa ca mabodza amene otsutsa amafalitsa ponena za ife. Tingadelenso nkhawa poganizila citonzo cimene mabodza amenewa abweletsa pa dzina la Yehova komanso gulu lake. Ngati tili na nkhawa cifukwa ca zimenezi, mawu a Yehova angatilimbikitse kwambili. Sitiyenela kutaya mtima, cifukwa “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Yehova sadzalephela kulemekeza dzina lake. Poseŵenzetsa Ufumu wake, iye adzathetsa mavuto onse amene Satana na dziko lake abweletsa pakati pa atumiki ake okhulupilika.—Sal. 94:22, 23; Yes. 65:17.

TIDZAPINDULA TIKAMAMVELA MAWU A YEHOVA

17. Mogwilizana na Yesaya 30:21, kodi Yehova amakamba nafe bwanji masiku ano?

17 Yehova akali kukamba ndi atumiki ake masiku ano. (Ŵelengani Yesaya 30:21.) N’zoona kuti Mulungu sakamba nafe kucokela kumwamba. Komabe, amatipatsa malangizo kupitila m’Mawu ake olembedwa, Baibo. Kuwonjezela apo, pogwilitsila nchito mzimu wake, Yehova amalimbikitsa “mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika” kupitiliza kupeleka cakudya cauzimu kwa atumiki ake. (Luka 12:42) Kukamba zoona, masiku ano timalandila cakudya cauzimu ca mwana alilenji, kupitila m’mabuku na zofalitsa zina za pa webusaiti yathu, monga mavidiyo na zomvetsela.

18. Kodi mawu a Yehova amalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu na kutithandiza kukhala olimba mtima?

18 Tiyeni tizikumbukila mawu amene Yehova anakamba pamene Mwana wake anali padziko lapansi. Lolani kuti Mawu a Mulungu, olembedwa m’Baibo, alimbitse cikhulupililo canu cakuti Yehova akuona zonse, ndipo adzathetsa mavuto onse amene Satana na dziko lake abweletsa pakati pathu. Conco, tikhale na colinga comvetsela mwachelu Mawu a Yehova. Tikatelo, tidzatha kupilila mavuto alionse amene tikumana nawo pali pano, komanso a kutsogolo. Baibo imati: “Mukufunika kupilila, kuti mutacita cifunilo ca Mulungu, mudzalandile zimene Mulungu walonjeza.”—Aheb. 10:36.

NYIMBO 4 ‘Yehova ni M’busa Wanga’

^ ndime 5 Pamene Yesu anali padziko lapansi, Yehova anakamba naye nthawi zitatu kucokela kumwamba. Pa nthawi imodzi mwa nthawi zitatuzo, Yehova analimbikitsa ophunzila ake kuti azimvela Mwana wake ameneyu. Masiku ano, Yehova amakamba nafe kupitila m’Mawu ake, amene aphatikizapo ziphunzitso za Yesu. Amatiphunzitsanso kupitila m’gulu lake. M’nkhani ino, tidzakambilana mmene timapindulila pamene timvela Yehova na Yesu.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mkulu akuyang’ana mtumiki wothandiza pamene akuyeletsa pa Nyumba ya Ufumu, komanso pamene akutumikila pa malo opelekela mabuku. Ndiyeno, akum’yamikila mocokela pansi pa mtima.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: M’bale na mkazi wake ku Sierra Leone akugaŵila kapepa koitanila anthu ku misonkhano kwa msodzi wa nsomba.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Abale na alongo ku dziko limene nchito yathu ni yoletsedwa akucita misonkhano m’nyumba ya m’bale. Iwo sanavale monga akupita kumisonkhano kuti anthu asazindikile kuti akucita misonkhano.