Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Akuti “Ame” Ndi Amtengo Wapatali kwa Yehova

Mawu Akuti “Ame” Ndi Amtengo Wapatali kwa Yehova

YEHOVA amayamikira tikamamulambira. Paja Baibulo limanena kuti ‘amatchera khutu ndi kumvetsera’ chilichonse chimene atumiki ake akuchita pomutamanda ngakhale chitakhala chaching’ono kwambiri. (Mal. 3:16) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mawu ena amene timawatchula kambirimbiri. Mawu ake ndi akuti “ame.” Kodi Yehova amaona kuti mawu amenewa ndi amtengo wapatali? Inde. Tiyeni tikambirane chifukwa chake tikunena zimenezi komanso mmene amawagwiritsira ntchito m’Baibulo.

‘ANTHU ONSE ADZANENA KUTI, “AME”’

Mawu amene anamasuliridwa kuti “ame” amatanthauza “zikhale momwemo” kapena kuti “ndithudi.” Mawuwa anachokera ku mawu achiheberi omwe amatanthauza “kukhala wokhulupirika” kapena “kukhala wodalirika.” Mawuwa ankagwiritsidwa ntchito pa nkhani za milandu. Munthu akamaliza malumbiro ankanena kuti “ame” pofuna kutsimikizira kuti zimene wanenazo ndi zoona komanso adzavomereza zotsatira zake. (Num. 5:22) Munthu akanena mawuwo pagulu amasonyeza kuti adzakwaniritsadi zimene walonjeza.​—Neh. 5:13.

M’Baibulo, mawu oti “ame” anagwiritsidwa ntchito kwambiri mu Deuteronomo chaputala 27. Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa anasonkhanitsidwa pakati pa phiri la Ebala ndi phiri la Gerizimu kuti amve Chilamulo chikuwerengedwanso. Iwo anafunika kumvetsera komanso kuvomereza kuti adzatsatira Chilamulocho. Ndiye zotsatira za kusamvera zikawerengedwa, iwo ankayankha kuti “Ame,” kutanthauza kuti “zikhale momwemo.” (Deut. 27:15-26) Kodi mukuganiza kuti ame wonenedwa ndi anthu masauzande ambiri, kuphatikizapo amuna, akazi ndi ana, ankamveka bwanji? (Yos. 8:30-35) N’kutheka kuti aliyense amene analipo sanaiwale zimene zinachitika. Aisiraeliwo anachitadi zimene analonjeza chifukwa Baibulo limanena kuti: “Aisiraeli anapitiriza kutumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akulu amene anapitiriza kukhalabe ndi moyo Yoswa atamwalira, omwe ankadziwa ntchito zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli.”​—Yos. 24:31.

Yesu anagwiritsanso ntchito mawu oti ame potsimikizira kuti zimene zanenedwa n’zoona, koma anachita zimenezi m’njira yapadera. M’malo mogwiritsa ntchito mawuwa povomereza zimene zanenedwa kale, iye ankatchula mawuwa akamayamba chiganizo. Nthawi zina mawuwa ankamasuliridwa kuti “ndithu” kapena “ndithudi.” (Mat. 5:18; Yoh. 1:51) Polankhula chonchi, iye ankatsimikizira anthu kuti zimene akunena ndi zoona zokhazokha. Yesu ankalankhula motsimikiza chonchi chifukwa chakuti iye ndi amene anapatsidwa udindo wochititsa kuti malonjezo onse a Yehova akwaniritsidwe.​—2 Akor. 1:20; Chiv. 3:14.

‘ANTHU ANANENA KUTI, “AME” NDIPO ANATAMANDA YEHOVA’

Aisiraeli ankagwiritsanso ntchito mawu oti “ame” popemphera kwa Yehova kapena pomutamanda. (Neh. 8:6; Sal. 41:13) Anthu akanena mawuwa pamapeto pa pemphero, ankasonyeza kuti akugwirizana ndi zonse zimene zanenedwa m’pempherolo ngati kuti apempha ndi iwowo. Zimenezi zinkawalimbikitsa mwauzimu chifukwa zinali ngati aliyense wanena nawo pempherolo. Izi n’zimene zinachitika pa nthawi imene Davide anabweretsa Likasa la Yehova ku Yerusalemu. Pa nthawi ya chikondwerero, Davide anapereka pemphero lomwe linali ngati nyimbo ndipo linalembedwa pa 1 Mbiri 16:8-36. Anthu onse amene analipo anakhudzidwa kwambiri ndi mawu ake moti “ananena kuti, ‘Ame!’ n’kutamanda Yehova.” Kuyankha onse pamodzi kuti ame kunali kosangalatsa kwambiri.

Akhristu oyambirira ankagwiritsanso ntchito mawu oti “ame” potamanda Yehova. Anthu ambiri amene analemba Baibulo anaikamo mawu amenewa. (Aroma 1:25; 16:27; 1 Pet. 4:11) Buku la Chivumbulutso limafotokozanso za angelo akulemekeza Yehova ponena kuti “Ame! Tamandani Ya, anthu inu.” (Chiv. 19:1, 4) Akhristu oyambirirawa ankanena kuti ame pambuyo pa mapemphero operekedwa kumisonkhano. (1 Akor. 14:16) Koma sikuti ankangonena mawuwa mwamwambo ayi.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUNENA KUTI “AME” N’KOFUNIKA?

Malinga ndi zimene takambiranazi, tinganene kuti mawu oti “ame” ndi oyeneradi kuwatchula pamapeto pa pemphero. Tikawatchula timasonyeza kutsimikizira zimene tanena m’pemphero. Ndipo tikanena mawuwa ngakhale chamumtima pambuyo pa pemphero lapagulu timasonyeza kuti tikuvomereza zonse zimene zanenedwa. Koma kodi mawu amenewa ndi ofunikanso m’njira ziti?

Timakhala atcheru polambira Yehova. Zimene timalankhula komanso kuchita pa nthawi ya pemphero zimasonyeza kuti tikulambiradi Yehova. Ngati tikufuna kuti “ame” wathu asakhale wamwambo, tiyenera kukhala aulemu komanso atcheru munthu wina akamapereka pemphero.

Timalambira Mulungu mogwirizana. Pemphero limatithandiza kuti aliyense mumpingo azimvetsera zinthu zofanana pa nthawi imodzi. (Mac. 1:14; 12:5) Tikamayankha kuti ame limodzi ndi abale ndi alongo zimathandiza kuti tizigwirizana kwambiri. Ndipo tikanena mawuwa mokweza kapena chamumtima, zimathandiza kuti Yehova ayankhe zimene tonse tazivomerezazo.

Mawu athu akuti “ame” amathandiza kuti Yehova atamandike

Timatamanda Yehova. Yehova amaona chilichonse chimene timachita pomulambira ngakhale chitakhala chaching’ono. (Luka 21:2, 3) Iye amaona zolinga zathu komanso zonse zimene zili mumtima mwathu. Ngakhale titachita kumvetsera misonkhano pa foni, Yehova amamva tikanena kuti “ame.” Zimenezi zimathandiza kuti timutamande limodzi ndi abale ndi alongo amene asonkhana.

Mawu oti “ame” amaoneka ngati achabechabe koma ndi ofunika kwambiri kwa Yehova. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti: “Tikanena mawu amenewa, timasonyeza kutsimikiza ndi mtima wonse, kuvomereza mwamphamvu komanso kukhala ndi chiyembekezo chenicheni mumtima mwathu.” Tiyeni tonse tiziyesetsa kuti “ame” wathu azikhala wosangalatsa kwa Yehova.—Sal. 19:14.