Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mudziŵa?

Kodi Mudziŵa?

M’nthawi yamakedzana, kodi munthu anali kupeza bwanji ngalawa akafuna kuyenda ulendo wapanyanja?

NGALAWA zonyamula anthu sizinali kupezeka kweni-kweni m’nthawi ya Paulo. Conco, munthu akafuna kuyenda ulendo wa panyanja, anali kufunsa ena ngati adziŵako ngalawa ina yake yonyamula katundu, imene inali kuloŵela kumene iye anali kupita. Anali kufunsanso ngati eni ngalawayo angalole kukwezeka anthu a paulendo. (Mac. 21:2, 3) Ngakhale kuti ngalawa siikupita kumalo eni-eni amene munthu wapaulendo akufuna, nthawi zina iye anali kukwelabe ngalawayo. Ndipo akafika pa doko lina mkati mwa ulendowo, anali kufuna-funa ngalawa ina yoti ikam’fikitse kufupi kwambili na kumene anali kupita.—Mac. 27:1-6.

Maulendo a panyanja anali na nyengo yake. Koma ngalawa zinalibe masiku oikika onyamukila. Nthawi zina, ngalawa zinali kucedwa kuyamba ulendo cifukwa ca kuipa kwa nyengo. Koma nthawi zinanso oyendetsa ngalawa ena okhulupilila malodza anali kusintha tsiku lonyamuka akaona zizindikilo zina monga, kulila kwa khwangwala pa nthambo za ngalawa yawo kapena akaona zidutsa za ngalawa yosweka m’mbali mwa nyanja. Oyendetsa ngalawa anali kuganizilanso mmene mphepo ikuyendela. Akaona kuti mphepo yayamba kuyenda bwino, anali kunyamuka ulendo wawo. Munthu wapaulendo akapeza ngalawa yoloŵela kumene afuna kupita, anali kukatenga katundu wake na kupita kumalo a kufupi na doko limene kunali ngalawayo. Kumeneko, anali kuyembekeza cilengezo cakuti ngalawayo ili pafupi kunyamuka.

Wolemba mbili wina dzina lake Lionel Casson, anati: “Mumzinda wa Roma, maulendo a panyanja anali kucitika mwadongosolo, cakuti anthu sanali kuvutika kusakila okha ngalawa zapaulendo. Doko la mumzindawo linali pamalo amene mtsinje wa Tiber unakathila m’nyanja. Cakufupi na dokolo kunali tauni yochedwa Ostia. M’tauniyo munali malo ena ake amene panali maofesi osiyana-siyana. Ambili mwa maofesiwo anali a eni ake ngalawa zopita kumadoko osiyana-siyana: Mwacitsanzo, eni ake ngalawa zopita ku Narbonne [m’dziko limene tsopano ni France] anali na ofesi yawo, eni ake ngalawa zopita ku Carthage [m’dziko limene tsopano ni Tunisia] anali na ofesi yawo, . . . ndi maofesi ena ambili. Motelo, munthu akafuna kuyenda ulendo wapanyanja, anali kungopita ku maofesi a ngalawa zoloŵela kumene afuna kupita.”

Ulendo wapanyanja unali wofulumila, koma unali na zovuta zake. Mwacitsanzo, Paulo pamaulendo ake aumishonale, ngalawa inamuswekelapo kangapo.—2 Akor. 11:25.