NKHANI YOPHUNZIRA 18

Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo Mumpingo

Tizisonyeza Chikondi ndi Chilungamo Mumpingo

“Musaleke kunyamulirana zolemetsa. Mukatero mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.”​AGAL. 6:2.

NYIMBO NA. 12 Yehova Ndi Mulungu Wamkulu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi sitiyenera kukayikira mfundo ziwiri ziti?

YEHOVA MULUNGU amakonda anthu amene amamulambira ndipo sadzasiya kuwakonda. Iye amakondanso chilungamo. (Sal. 33:5) Zimenezi zimatitsimikizira mfundo ziwiri izi: (1) Yehova zimamupweteka kwambiri akaona kuti atumiki ake akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo. (2) Iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika. Munkhani yoyamba, * tinaphunzira kuti Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli kudzera mwa Mose chinapangidwa chifukwa cha chikondi. Chilamulocho chinkalimbikitsa kuti anthu onse, ngakhale anthu amene sankatha kudziteteza, azichitiridwa chilungamo. (Deut. 10:18) Chilamulochi chimasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake.

2. Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Chilamulo cha Mose chinatha mu 33 C.E. pamene mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa. Kodi zimenezi zinatanthauza kuti panalibenso chilamulo cholimbikitsa chikondi ndi chilungamo chomwe Akhristu ankayenera kutsatira? Ayi. Akhristuwo anapatsidwa chilamulo chatsopano. Munkhaniyi, tikambirana mafunso awa: Kodi chilamulochi n’chiyani? N’chifukwa chiyani tinganene kuti chinapangidwa chifukwa cha chikondi? Nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti chimalimbikitsa chilungamo? Kodi anthu audindo amene amatsatira chilamulochi ayenera kuchita chiyani?

KODI “CHILAMULO CHA KHRISTU” N’CHIYANI?

3. Kodi “chilamulo cha Khristu” chotchulidwa pa Agalatiya 6:2 chimaphatikizapo chiyani?

3 Werengani Agalatiya 6:2. Akhristu amatsatira “chilamulo cha Khristu.” Yesu sanalembe mndandanda wa malamulo, komabe anapatsa otsatira ake malangizo, malamulo komanso mfundo zoti azitsatira. “Chilamulo cha Khristu” chimaphatikizapo zinthu zonse zimene Yesu anaphunzitsa. Tiyeni tikambirane mfundo zimene zingatithandize kumvetsa bwino chilamulochi.

4-5. Kodi Yesu ankaphunzitsa m’njira ziti, komanso pa nthawi ziti?

4 Kodi Yesu ankaphunzitsa anthu m’njira ziti? Choyamba, ankawaphunzitsa polankhula nawo. Zimene ankanena zinali zamphamvu chifukwa zinkathandiza anthu kudziwa mfundo zoona zokhudza Mulungu, cholinga cha moyo komanso kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto. (Luka 24:19) Yesu ankaphunzitsanso anthu powapatsa chitsanzo chabwino. Zimene iye ankachita zinkathandiza otsatira ake kudziwa zimene nawonso ayenera kuchita.​—Yoh. 13:15.

5 Nanga kodi ankaphunzitsa pa nthawi ziti? Yesu ankaphunzitsa anthu pamene ankachita utumiki wake padzikoli. (Mat. 4:23) Iye anaphunzitsanso otsatira ake atangoukitsidwa kumene. Mwachitsanzo, anaonekera kwa ophunzira, mwina oposa 500, ndipo anawalamula kuti ‘aziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.’ (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 15:6) Popeza Yesu ndi mutu wa mpingo, anapitiriza kuphunzitsa ophunzira ake ngakhale atabwerera kumwamba. Mwachitsanzo, cha m’ma 96 C.E., Khristu anagwiritsa ntchito mtumwi Yohane kuti alimbikitse Akhristu odzozedwa ndiponso kuwalangiza.​—Akol. 1:18; Chiv. 1:1.

6-7. (a) Kodi tingapeze kuti zimene Yesu anaphunzitsa? (b) Kodi timamvera bwanji chilamulo cha Khristu?

6 Kodi tingapeze kuti mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa? Mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza zinthu zambiri zimene Yesu ananena komanso kuchita ali padzikoli. Mabuku ena a Malemba Achigiriki amatithandizanso kumvetsa maganizo a Yesu. Zili choncho chifukwa analembedwa ndi anthu omwe ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera komanso anali ndi “maganizo a Khristu.”​—1 Akor. 2:16.

7 Zimene tikuphunzirapo: Zimene Yesu ankaphunzitsa zimatithandiza pa zinthu zonse zimene timachita pa moyo wathu. Choncho chilamulo cha Khristu chimatithandiza tikakhala kunyumba, kuntchito, kusukulu kapena mumpingo. Tingadziwe bwino chilamulochi tikamawerenga komanso kusinkhasinkha Malemba Achigiriki. Timamvera chilamulochi tikamasintha moyo wathu kuti uzigwirizana ndi malangizo, malamulo ndiponso mfundo za m’Malembawa. Tikamamvera chilamulo cha Khristu timakhala tikumveranso Mulungu wathu wachikondi chifukwa zonse zimene Yesu anaphunzitsa zimachokera kwa iyeyo.​—Yoh. 8:28.

CHILAMULO CHA KHRISTU CHINAPANGIDWA CHIFUKWA CHA CHIKONDI

8. Kodi maziko a chilamulo cha Khristu n’chiyani?

8 Anthu akakhala m’nyumba yabwino yokhala ndi maziko olimba amaona kuti ndi otetezeka. N’chimodzimodzi ndi malamulo. Lamulo likakhala ndi maziko abwino limathandiza anthu amene amalitsatira kumva kuti ndi otetezeka. Chilamulo cha Khristu chili ndi maziko abwino kwambiri omwe ndi chikondi. N’chifukwa chiyani tikutero?

Tikamachita zinthu mwachikondi komanso mosakondera timakhala tikutsatira “chilamulo cha Khristu” (Onani ndime 9-14) *

9-10. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankachita zinthu zonse chifukwa cha chikondi, nanga tingamutsanzire bwanji?

9 Choyamba, Yesu ankachita zinthu zonse chifukwa cha chikondi. Munthu akamamvera anthu chisoni kapena kuwachitira chifundo amasonyeza kuti ndi wachikondi. Yesu ankamvera ena chisoni choncho ankaphunzitsa anthu, kuchiritsa odwala, kudyetsa anjala komanso kuukitsa akufa. (Mat. 14:14; 15:32-38; Maliko 6:34; Luka 7:11-15) Kuchita zimenezi kunkafuna nthawi komanso mphamvu. Koma Yesu ankaika zofuna za ena pamalo oyamba osati zake. Iye anasonyeza chikondi chachikulu kwambiri pamene anapereka moyo wake chifukwa cha anthufe.​—Yoh. 15:13.

10 Zimene tikuphunzirapo: Tingatsanzire Yesu tikamaika zofuna za anthu ena pamalo oyamba osati zathu. Tingamutsanzirenso tikamayesetsa kumvera chisoni anthu a m’gawo lathu. Tikamawalalikira ndiponso kuwaphunzitsa chifukwa chowamvera chisoni timakhala kuti tikutsatira chilamulo cha Khristu.

11-12. (a) N’chiyani chimasonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri? (b) Kodi tingatsanzire bwanji chikondi cha Yehova?

11 Chachiwiri, Yesu anasonyeza kuti Atate ake ndi achikondi. Pa utumiki wake, Yesu anasonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake. Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa mfundo izi: Aliyense wa ife ndi wamtengo wapatali kwambiri kwa Atate athu akumwamba. (Mat. 10:31) Yehova amafunitsitsa kulandira munthu yemwe anali ngati nkhosa yotayika amene wabwerera mumpingo. (Luka 15:7, 10) Iye anasonyeza kuti amatikonda kwambiri pamene anapereka Mwana wake nsembe kuti atiwombole.​—Yoh. 3:16.

12 Zimene tikuphunzirapo: Kodi tingatsanzire bwanji chikondi cha Yehova? (Aef. 5:1, 2) Tiyenera kuona kuti Mkhristu aliyense ndi wamtengo wapatali kwambiri. Komanso tiyenera kulandira bwino aliyense amene anali ngati “nkhosa yosochera” yemwe wabwerera kwa Yehova. (Sal. 119:176) Timasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo athu tikamachita khama kuti tiwathandize akavutika. (1 Yoh. 3:17) Tikamachita zinthu mwachikondi ndi anthu ena, timakhala tikumvera chilamulo cha Khristu.

13-14. (a) Kodi Yesu anapereka lamulo liti pa Yohane 13:34, 35, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti ndi lamulo latsopano? (b) Kodi tingatsatire bwanji lamulo latsopanoli?

13 Chachitatu, Yesu analamula otsatira ake kuti azisonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. (Werengani Yohane 13:34, 35.) Lamulo la Yesuli linali latsopano chifukwa linkafuna kuti anthu azisonyeza chikondi chosiyana ndi chimene ankalamulidwa kusonyeza m’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Tikutero chifukwa chakuti lamuloli linawalamula kukonda anzawo ngati mmene Yesu anawakondera. Izi zikutanthauza kuti ankafunika kusonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. * Choncho tiyenera kukonda abale ndi alongo athu kuposa mmene timadzikondera tokha. Tiyenera kuwakonda kwambiri mpaka kukhala okonzeka kuwafera ngati mmene Yesu anachitira.

14 Zimene tikuphunzirapo: Kodi tingamvere bwanji lamulo latsopanoli? Mwachidule, tikhoza kumvera tikamayesetsa kuthandiza abale ndi alongo athu. N’zoona kuti tiyenera kukhala okonzeka kuwafera, koma tiyenera kuwathandizanso pa zinthu zing’onozing’ono. Mwachitsanzo, tikhoza kumathandiza m’bale kapena mlongo wachikulire kuti azipezeka kumisonkhano, tingadzimane zinthu zina kuti tisangalatse mnzathu kapenanso kutenga tchuthi kuti tikathandize kumene kwachitika ngozi zadzidzidzi. Tikamachita zinthu ngati zimenezi timakhala tikutsatira chilamulo cha Khristu. Timathandizanso kuti aliyense mumpingo azimva kuti ndi wotetezeka.

CHILAMULO CHA KHRISTU CHIMALIMBIKITSA CHILUNGAMO

15-17. (a) Kodi zochita za Yesu zinkasonyeza bwanji kuti amakonda chilungamo? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

15 M’Baibulo, mawu akuti “chilungamo” amatanthauza kuchita zinthu zimene Mulungu amaziona kuti ndi zabwino, komanso kuzichita mosakondera. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chilamulo cha Khristu chimalimbikitsa chilungamo?

Yesu ankachita zinthu mwaulemu komanso mokoma mtima ndi akazi, ngakhale akazi amene anthu ena ankawanyoza (Onani ndime 16) *

16 Choyamba, taganizirani mmene zochita za Yesu zimasonyezera kuti amakonda chilungamo. Pa nthawi imene iye anali padzikoli, atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankadana ndi anthu amitundu ina, ankanyoza Ayuda wamba komanso sankalemekeza akazi. Koma Yesu ankachita zinthu ndi anthu onse mwachilungamo komanso mosakondera. Iye ankalandira anthu omwe sanali Ayuda amene ankamukhulupirira. (Mat. 8:5-10, 13) Ankalalikira mosakondera kwa anthu onse, kaya achuma kapena osauka. (Mat. 11:5; Luka 19:2, 9) Iye sankachitira nkhanza akazi, koma ankachita nawo zinthu mwaulemu ndiponso mokoma mtima. Ankachita zimenezi ngakhale kwa akazi amene anthu ena ankawanyoza.​—Luka 7:37-39, 44-50.

17 Zimene tikuphunzirapo: Tingatsanzire Yesu tikamachita zinthu mosakondera. Tiyenera kulalikiranso munthu aliyense amene akufuna kumvetsera ndipo sitiyenera kuganizira za chuma chake kapena chipembedzo chake. Amuna achikhristu amatsatira chitsanzo cha Yesu akamachita zinthu mwaulemu ndi akazi. Tikamachita zinthu ngati zimenezi timakhala tikutsatira chilamulo cha Khristu.

18-19. Kodi Yesu anaphunzitsa mfundo ziti zokhudza chilungamo, nanga tikuphunzirapo chiyani?

18 Chachiwiri, taganizirani zimene Yesu ankaphunzitsa pa nkhani ya chilungamo. Iye ankaphunzitsa mfundo zimene zinkathandiza otsatira ake kuti azichita zinthu mwachilungamo. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo ya pa Mateyu 7:12. Tonsefe timafuna kuti anthu azitichitira zinthu mwachilungamo. Choncho nafenso tiyenera kuwachitira zinthu mwachilungamo. Tikatero, nawonso akhoza kutichitira zomwezo. Koma kodi tingatani ngati tachitiridwa zinthu mopanda chilungamo? Yesu anaphunzitsanso kuti tisamakayikire kuti Yehova ‘adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene amafuulira kwa iye usana ndi usiku.’ (Luka 18:6, 7) Tingati mawu amenewa akulonjeza kuti: Mulungu wathu wachilungamo amadziwa mavuto amene tikukumana nawo m’masiku otsirizawa ndipo adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nthawi yoyenera.​—2 Ates. 1:6.

19 Zimene tikuphunzirapo: Tikamatsatira mfundo zimene Yesu anaphunzitsa tidzayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Komanso ngati tachitiridwa zinthu mopanda chilungamo m’dziko la Satanali, tizikumbukira kuti Yehova adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.

KODI ANTHU AMENE ALI NDI UDINDO AYENERA KUCHITA CHIYANI?

20-21. (a) Kodi anthu amene ali ndi udindo ayenera kuchita chiyani? (b) Kodi amuna angasonyeze bwanji chikondi chololera kuvutikira ena, nanga abambo ayenera kuchita bwanji zinthu ndi ana awo?

20 Kodi anthu amene ali ndi udindo angatsatire bwanji chilamulo cha Khristu? Popeza maziko a chilamulochi ndi chikondi, anthu amene ali ndi udindo ayenera kulemekeza anthu komanso kuwayang’anira mwachikondi. Ayenera kukumbukira kuti Yesu amafuna kuti tizisonyeza chikondi pa zonse zimene timachita.

21 M’banja. Mwamuna ayenera kukonda mkazi wake ngati “mmene Khristu anakondera mpingo.” (Aef. 5:25, 28, 29) Ayenera kutsanzira chikondi cha Khristu poika zofuna za mkazi wake patsogolo osati zake. Amuna ena zimawavuta kusonyeza chikondi choterechi, mwina chifukwa choti analeredwa m’banja limene anthu sankachitirana zinthu mwachilungamo komanso mwachikondi. Zikhoza kuwavuta kusintha makhalidwe oipa amene anatengera, koma ayenera kuyesetsa kusintha n’cholinga choti azimvera chilamulo cha Khristu. Mwamuna amene amasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena amalemekezedwa ndi mkazi wake. Bambo amene amakonda ana ake sangawachitire nkhanza kapena kuwalankhula mawu opweteka. (Aef. 4:31) M’malomwake, amayamikira ana ake komanso kuwakonda ndipo izi zimachititsa anawo kumva kuti ndi otetezeka. Bambo akamachita zimenezi ana ake amamukonda komanso kumudalira.

22. Kodi lemba la 1 Petulo 5:1-3 limasonyeza kuti nkhosa ndi za ndani, nanga akulu ayenera kuchita chiyani?

22 Mumpingo. Akulu ayenera kukumbukira kuti “nkhosa” zimene akuyang’anira si zawo. (Yoh. 10:16; werengani 1 Petulo 5:1-3.) Mawu oti “gulu la nkhosa za Mulungu” komanso “cholowa chochokera kwa Mulungu” ayenera kukumbutsa akulu kuti nkhosazo ndi za Yehova. Iye amafuna kuti akuluwo azisamalira nkhosa zake mwachikondi. (1 Ates. 2:7, 8) Choncho akulu amene amayang’anira nkhosa mwachikondi amasangalatsa Yehova. Ndipo abale ndi alongo mumpingo amawakonda komanso kuwalemekeza.

23-24. (a) Kodi udindo wa akulu ndi wotani ngati munthu wachita tchimo lalikulu? (b) Kodi akulu amaganizira mafunso ati akamasamalira nkhani ngati zimenezi?

23 Ngati munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu, kodi udindo wa akulu umakhala wotani? Udindo wawo umakhala wosiyana ndi wa oweruza komanso akulu a ku Isiraeli amene ankatsatira Chilamulo cha Mose. Amuna achiisiraeliwo ankakhala ndi udindo wosamalira nkhani zokhudza kulambira komanso milandu ina. Koma udindo wa akulu amene amatsatira chilamulo cha Khristu ndi wongosamalira nkhani zokhudza kulambira basi. Iwo amazindikira kuti akuluakulu a boma ndi amene apatsidwa udindo ndi Mulungu kuti azisamalira milandu ina yosakhudza kulambira. Iwo ali ndi udindo wopatsa munthu chilango monga kumulipiritsa kapena kumumanga.​—Aroma 13:1-4.

24 Kodi akulu amachita chiyani ngati munthu wina mumpingo wachita tchimo lalikulu? Iwo amagwiritsa ntchito Malemba posankha zochita pa nkhani zimenezi. Amakumbukiranso kuti maziko a chilamulo cha Khristu ndi chikondi. Zimenezi zimawachititsa kuganizira funso lakuti: Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tithandize anthu mumpingo amene alakwiridwa? Pothandiza munthu wolakwayo, akulu achikondi amaganizira mafunso akuti: Kodi munthuyu ali ndi mtima wolapa? Nanga kodi tingamuthandize bwanji kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova?

25. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

25 Timayamikira kwambiri kuti tapatsidwa chilamulo cha Khristu. Tonsefe tikamayesetsa kutsatira chilamulochi timathandiza kuti munthu aliyense mumpingo azimva kuti amakondedwa, ndi wamtengo wapatali ndiponso wotetezeka. Koma tikukhala m’dziko limene ‘anthu oipa akungoipiraipira.’ (2 Tim. 3:13) Choncho nthawi zonse tiyenera kukhala osamala. Ndiye kodi akulu angatsanzire bwanji chilungamo cha Mulungu posamalira nkhani zokhudza kugwirira mwana? Tidzakambirana yankho la funsoli munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

^ ndime 5 Nkhaniyi komanso nkhani ziwiri zotsatira zifotokoza mfundo zotitsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi komanso wachilungamo. Iye amafuna kuti anthu ake azichitiridwa zinthu zachilungamo ndipo amalimbikitsa anthu amene achitiridwa zinthu zopanda chilungamo m’dziko loipali.

^ ndime 1 Onani nkhani yakuti, “Aisiraeli Ankafunika Kusonyeza Chikondi ndi Chilungamo” mu Nsanja ya Olonda ya February 2019.

^ ndime 13 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Tikakhala ndi chikondi chololera kuvutikira ena timaika patsogolo zofuna za ena osati zathu. Timalolera kudzimana kapena kuluza zinthu zina n’cholinga choti tithandize anthu ena.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akuyang’ana mkazi wamasiye yemwe mwana wake wamwalira. Kenako iye anamumvera chisoni ndipo anaukitsa mwana wakeyo.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu akudya kunyumba ya Mfarisi wina dzina lake Simoni. Mzimayi wina, yemwe mwina ndi hule, wasambitsa mapazi a Yesu ndi misozi yake ndipo wawapukuta ndi tsitsi lake n’kuwapaka mafuta. Simoni sakusangalala ndi zimene mzimayiyo wachita koma Yesu akumuikira kumbuyo.