Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 24

Tizichotsa Maganizo Alionse Otsutsana ndi Kudziwa Mulungu

Tizichotsa Maganizo Alionse Otsutsana ndi Kudziwa Mulungu

“Pakuti tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu.”​—2 AKOR. 10:5.

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Paulo anapereka chenjezo liti kwa Akhristu odzozedwa?

MTUMWI PAULO analembera Akhristu oyambirira kuti: “Musamatengere nzeru za nthawi ino.” (Aroma 12:2) N’chifukwa chiyani analemba zimenezi kwa Akhristu amene anali atadzipereka kwa Mulungu komanso anali odzozedwa ndi mzimu woyera?​—Aroma 1:7.

2-3. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito zinthu ziti pofuna kuti tisiye kutumikira Yehova? (b) N’chiyani chingatithandize kuchotsa zinthu zolakwika zimene zinazikika molimba m’maganizo athu?

2 Paulo anali ndi nkhawa chifukwa zikuoneka kuti Akhristu ena ankatengera maganizo komanso nzeru zosathandiza zam’dziko la Satanali. (Aef. 4:17-19) Zimenezi zikhoza kutichitikiranso ifeyo. Satana, yemwe ndi Mulungu wa nthawi ino, ali ndi zinthu zambiri zimene amagwiritsa ntchito pofuna kuti tisiye kutumikira Yehova. Mwachitsanzo, iye akhoza kupezerapo mwayi ngati tili ndi kamtima kodziona kuti ndife ofunika kwambiri. Akhozanso kugwiritsa ntchito zinthu zina zokhudza kumene tinakulira, chikhalidwe chathu kapena maphunziro athu kuti tiziyendera maganizo ake.

3 Koma kodi n’zotheka kuchotsa ‘zinthu zimene zinazikika molimba’ m’maganizo athu? (2 Akor. 10:4) Inde n’zotheka chifukwa Paulo analemba kuti: “Tikugubuduza maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu, ndipo tikugonjetsa ganizo lililonse n’kulimanga ngati mkaidi kuti lizimvera Khristu.” (2 Akor. 10:5) Yehova akhoza kutithandiza kuchita zimenezi. Mofanana ndi mankhwala amene amachotsa mphamvu ya poizoni, Mawu a Mulungu angatithandize kuchotsa maganizo olakwika amene tatengera m’dziko la Satanali.

‘SINTHANI MAGANIZO ANU’

4. Kodi ambirife tinafunika kusintha zinthu ziti titayamba kuphunzira choonadi?

4 Kodi ndi zinthu ziti zimene munafunika kusintha mutaphunzira Mawu a Mulungu n’kusankha zoti muyambe kutumikira Yehova? Ambirife tinafunika kusintha makhalidwe ena oipa. (1 Akor. 6:9-11) Ndipo timayamikira kuti Yehova anatithandiza kusintha makhalidwewo.

5. Malinga ndi Aroma 12:2, kodi tiyenera kuchita zinthu ziwiri ziti?

5 Komabe sitiyenera kukhutira ndi zimene tinasintha basi. N’zoona kuti tasiya kuchita machimo akuluakulu amene tinkachita tisanabatizidwe. Koma tiyenera kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingatichititse kuyambiranso khalidwe loipalo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Paulo ananena kuti: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” (Aroma 12:2) Malinga ndi lembali, tifunika kuchita zinthu ziwiri. Choyamba, tiyenera kupewa ‘kutengera nzeru’ za dzikoli. Chachiwiri, tiyenera “kusandulika” mwa kusintha maganizo athu.

6. Kodi mfundo yaikulu pa mawu a Yesu a pa Mateyu 12:43-45 ndi yotani?

6 Mawu a Paulo akuti kusandulika amatanthauza zambiri osati kungosintha maonekedwe. Amatanthauza kusintha mbali zonse za moyo wathu. (Onani bokosi lakuti “Kusandulika Kapena Kudzisandutsa?”) Kusintha maganizo kumatanthauza kusintha mtima wathu, zimene timalakalaka komanso mmene timaonera zinthu. Choncho aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi munthune ndangosintha pamwambamwamba kapena ndasinthadi kuchokera mumtima?’ Funso limeneli ndi lofunika kwambiri. Yesu ananena zimene tiyenera kuchita pa Mateyu 12:43-45. (Werengani.) Mfundo yaikulu palembali ndi yakuti: Tikachotsa zinthu zolakwika m’maganizo athu, tiyenera kuikamo maganizo a Mulungu.

“MUKHALE ATSOPANO MU MPHAMVU YOYENDETSA MAGANIZO ANU”

7. Kodi tingatani kuti tisinthe kuchokera mumtima?

7 Kodi n’zothekadi kusintha kuchokera mumtima? Mawu a Mulungu amanena kuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aef. 4:23, 24) Apa zikuoneka kuti n’zotheka kusintha kuchokera mumtima koma si zophweka. Kungodziletsa kuti tisachite kapena kulakalaka zinthu zina si kokwanira. Tiyenera kusintha “mphamvu yoyendetsa maganizo” athu. Apa tikutanthauza kuti tiyenera kusintha mtima wathu, zimene timalakalaka komanso zimene tinazolowera kuchita. Kuti zimenezi zitheke, pamafunika kuchita khama nthawi zonse.

8-9. Kodi nkhani ya m’bale wina ikusonyeza bwanji kuti tiyenera kusintha kuchokera mumtima?

8 Chitsanzo ndi m’bale wina amene kale anali wachiwawa. Iye anasiya kumwa mowa komanso kuchita ndewu ndipo anabatizidwa. Anthu am’dera lawo ankaoneratu kuti munthuyo wasintha kwambiri. Koma pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anabatizidwa, panachitika zinthu zina. Munthu woledzera anafika kunyumba kwake n’kumamuputa n’cholinga choti amenyane. Poyamba, m’baleyo anadziletsa kwambiri. Koma munthuyo atayamba kunyoza dzina la Yehova, m’baleyo analephera kudzigwira. Anatuluka n’kukamumenya munthuyo. Kodi pamenepa vuto linali chiyani? Ngakhale kuti kuphunzira Baibulo kunamuthandiza kuti azidziletsa akafuna kuchita zachiwawa, m’baleyo anali asanasinthe mphamvu yoyendetsa maganizo ake. M’mawu ena tingati anali asanasinthe kuchokera mumtima.

9 Chosangalatsa n’chakuti m’baleyu sanataye mtima. (Miy. 24:16) Mothandizidwa ndi akulu, anapitiriza kusintha mpaka nayenso anakhala mkulu. Tsiku lina madzulo ali ku Nyumba ya Ufumu, panachitikanso zinthu zina zofanana ndi zoyamba zija. Munthu woledzera anafika ndipo anatsala pang’ono kumenya mkulu wina. Kodi m’baleyu anatani? Iye anapita n’kukakambirana modekha komanso modzichepetsa ndi munthu woledzerayo ndipo anamuthandiza kuti akafike kunyumba kwake. Kodi n’chiyani chinamuthandiza pa nthawiyi? M’baleyu anali atasintha mphamvu yoyendetsa maganizo ake. Iye anali atasinthiratu mtima wake n’kukhala wodzichepetsa komanso wokonda mtendere. Izi zinathandiza kuti Yehova alemekezeke.

10. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tisinthe kuchokera mumtima?

10 Kuti munthu asinthe chonchi, zimatenga nthawi ndipo sizimangochitika zokha. Pangafunike ‘kuyesetsa mwakhama’ kwa zaka zambiri. (2 Pet. 1:5) Komanso sikuti munthu amasintha chifukwa cha kuchuluka kwa zaka zimene wakhala m’choonadi. Chofunika ndi kuyesetsa mmene tingathere kuti tisinthe kuchokera mumtima. Kuti zimenezi zitheke, pali zinthu zingapo zimene tiyenera kuchita. Tiyeni tsopano tikambirane zina mwa zinthu zimenezi.

KODI TINGASINTHE BWANJI MPHAMVU YOYENDETSA MAGANIZO ATHU?

11. Kodi kupemphera kungatithandize bwanji kuti tisinthe mphamvu yoyendetsa maganizo athu?

11 Chinthu choyamba komanso chofunika kwambiri ndi kupemphera. Tiyenera kupemphera ngati mmene anachitira wolemba masalimo amene ananena kuti: “Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10) Tiyenera kuzindikira kuti tikufunika kusintha mphamvu zoyendetsa maganizo athu ndipo tizipempha Yehova kuti atithandize. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova angatithandize kusintha? Tikhoza kulimba mtima tikaganizira zimene iye analonjeza Aisiraeli m’masiku a Ezekieli. Iye ananena kuti: ‘Ndidzawapatsa mtima umodzi ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzawapatsa mtima wamnofu, [kutanthauza mtima womvera malangizo a Mulungu].’ (Ezek. 11:19) Ngati Yehova ankafunitsitsa kuthandiza Aisiraeliwo kuti asinthe, ndiye kuti angatithandizenso ifeyo.

12-13. (a) Malinga ndi Salimo 119:59, kodi tiyenera kuganizira mozama zinthu ziti? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

12 Chinthu chachiwiri chofunika ndi kusinkhasinkha. Tikamawerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse tiziganizira mozama zimene tiyenera kusintha m’maganizo ndi mumtima mwathu. (Werengani Salimo 119:59; Aheb. 4:12; Yak. 1:25) Tiyenera kuganizira zinthu zimene timachita chifukwa chotengera nzeru zam’dzikoli. Tizizindikira zimene timalakwitsa n’kumayesetsa kusintha.

13 Mwachitsanzo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ineyo ndili ndi kamtima ka nsanje?’ (1 Pet. 2:1) ‘Kodi ndili ndi kamtima konyada chifukwa cha kumene ndinakulira, maphunziro anga kapena chuma changa?’ (Miy. 16:5) ‘Kodi anthu amene alibe zinthu zimene ndili nazo kapena amene ndikusiyana nawo mtundu ndimawaona kuti ndi otsika?’ (Yak. 2:2-4) ‘Kodi ndimakopeka ndi zinthu zam’dziko la Satanali?’ (1 Yoh. 2:15-17) ‘Kodi ndimakonda zosangalatsa zokhudza chiwawa kapena chiwerewere?’ (Sal. 97:10; 101:3; Amosi 5:15) Mayankho a mafunso amenewa angatithandize kudziwa zimene tiyenera kusintha. Yehova amasangalala kwambiri tikamayesetsa kuchotsa ‘zinthu zimene zinazikika molimba’ mumtima mwathu.​—Sal. 19:14.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha bwino anthu ocheza nawo?

14 Chinthu chachitatu chimene tiyenera kuchita ndi kusankha bwino anthu ocheza nawo. Anthufe timatengera zochita za anthu amene timacheza nawo. (Miy. 13:20) Kusukulu kapena kuntchito timakhala ndi anthu amene sangatithandize kukhala ndi maganizo a Mulungu. Koma tikhoza kupeza anthu abwino kumisonkhano yathu. Ndipo tikapita kumisonkhanoyi tikhoza kulimbikitsidwa “pa chikondi ndi ntchito zabwino.”​—Aheb. 10:24, 25.

‘MUKHAZIKIKE M’CHIKHULUPIRIRO’

15-16. Kodi Satana amachita zotani kuti asinthe maganizo athu?

15 Tisaiwale kuti cholinga cha Satana ndi kusintha maganizo athu. Iye amagwiritsa ntchito maganizo alionse olakwika kuti tisiye kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu.

16 Njira imene amagwiritsa ntchito ndi imene anaigwiritsa ntchito polankhula ndi Hava m’munda wa Edeni. Paja anamufunsa kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati . . . ?” (Gen. 3:1) M’dziko la Satanali, nthawi zambiri timakumana ndi mafunso ngati akuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu amadana ndi ukwati wa amuna kapena akazi okhaokha? N’zoona kuti Mulungu safuna kuti muzikondwerera khirisimasi ndi tsiku lobadwa? N’zoona kuti Mulungu wanu safuna kuti muziikidwa magazi kuchipatala? N’zoona kuti Mulungu wachikondi angakuletseni kucheza ndi anzanu amene achotsedwa?’

17 (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati sitinapeze yankho la funso linalake lokhudza zimene timakhulupirira? (b) Malinga ndi Akolose 2:6, 7, kodi chingachitike n’chiyani tikamaphunzira mwakhama?

17 Kuti zitiyendere bwino, tiyenera kutsimikizira kuti zimene timakhulupirira n’zoona. Ngati sitinapeze mayankho abwino pa mafunso amene timakhala nawo mumtima, tikhoza kuyamba kukayikira. Mtima wokayikirawo ukhoza kusokoneza maganizo athu komanso kuwononga chikhulupiriro chathu. Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani? Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tizisintha maganizo athu n’kufika pozindikira “chifuniro cha Mulungu chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Tikamaphunzira mwakhama tikhoza kutsimikizira kuti mfundo zimene timaphunzira m’Baibulo n’zoona. Izi zingathandize kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti mfundo za Yehova ndi zachilungamo. Mofanana ndi mtengo umene uli ndi mizu yolimba, tikhoza ‘kukhazikika m’chikhulupiriro.’​—Werengani Akolose 2:6, 7.

18. Kodi n’chiyani chingatithandize kuchotsa maganizo olakwika alionse amene tatengera m’dziko la Satanali?

18 Munthu wina sangatilimbitsire chikhulupiriro chathu. Choncho tiyenera kupitiriza kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu. Tizipemphera pafupipafupi n’kumachonderera Yehova kuti atipatse mzimu wake. Tiziganizira mozama zimene zili mumtima ndi m’maganizo athu. Tizicheza ndi anthu amene angatithandize kuti tisinthe maganizo athu n’kukhala abwino. Tikamatero tidzachotsa maganizo olakwika alionse amene tatengera m’dziko la Satanali. Tidzakwanitsa kugubuduza “maganizo komanso chotchinga chilichonse chotsutsana ndi kudziwa Mulungu.”​—2 Akor. 10:5.

NYIMBO NA. 50 Pemphero Langa Losonyeza Kudzipereka

^ ndime 5 Tonsefe maganizo athu amakhala ogwirizana ndi kumene tinakulira, chikhalidwe chathu komanso maphunziro athu. Ndipo tikhoza kuzindikira kuti maganizo ena olakwika anatilowerera kwambiri. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tichotse maganizo olakwika alionse amene tili nawo.