Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Tingadzitetezele ku Msampha wa Satana

Mmene Tingadzitetezele ku Msampha wa Satana

AISIRAELI atatsala pang’ono kuwoloka mtsinje wa Yorodano kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, ku msasa wawo kunabwela akazi acimowabu. Akaziwo anaitanila amuna aciisiraeli ku phwando. Aisiraeliwo ayenela kuti anaona kuti umenewo unali mwayi wosoŵa. Anaona kuti adzakhala na mwayi wopanga mabwenzi atsopano, kuvina, ndiponso kudya zakudya zabwino. Akaziwo anali kutsatila miyambo na mfundo zotsutsana na Cilamulo cimene Mulungu anapatsa Aisiraeli. Ngakhale zinali conco, n’kutheka kuti amuna ena Aciisiraeli anali kuganiza kuti: ‘Tidzapita. Sizingatibweletsele mavuto. Tidzakhala osamala.’

Koma kodi n’ciani cinacitika? Baibo imati: “[Aisiraeli] anayamba kucita ciwelewele ndi akazi a ku Mowabu.” Cimene akazi amenewo anali kufuna maka-maka, n’cakuti Aisiraeli ayambe kulambila mafano. Ndipo n’zimenedi iwo anacita. Conco, m’pomveka kuti “mkwiyo wa Yehova unawayakila.”—Num. 25:1-3.

Aisiraeliwo anaphwanya malamulo aŵili a m’Cilamulo ca Mulungu. Loyamba, analambila mafano ndipo laciŵili, anacita ciwelewele. Mwa ici, Aisiraeli masauzande ambili anaphedwa. (Eks. 20:4, 5, 14; Deut. 13:6-9) N’cifukwa ciani zimene zinacitikazo zinali zomvetsa cisoni kwambili? Cifukwa cakuti zinacitika iwo atatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, moti Aisiraeli masauzande ambili anataya mwayi wokaloŵamo.—Num. 25:5, 9.

Pokamba za nkhani imeneyi, mtumwi Paulo anati: “Zinthu zimenezi zinali kuwagwela monga zitsanzo, ndipo zinalembedwa kuti ziticenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikila.” (1 Akor. 10:7-11) N’zodziŵikilatu kuti Satana anakondwela kwambili pamene Aisiraeli anacita chimo lalikulu na kutaya mwayi wokaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Tifunika kutengelapo phunzilo pa zolakwa zawo. Tisaiŵale kuti Satana amafuna kutilepheletsa kukaloŵa m’dziko latsopano la Mulungu.

MSAMPHA WOOPSA

Masiku ano, Satana amafuna kukola Akhristu. Amacita izi mwa kuseŵenzetsa misampha imene aona kuti imakola anthu ambili. Monga mmene taphunzilila, Satana anaseŵenzetsa msampha wa ciwelewele pofuna kukola Aisiraeli. Masiku ano, ciwelewele cikali msampha woopsa kwambili. Cinthu cimodzi cimene cingatigwetsele mosavuta mu msampha umenewu ni kutamba zamalisece.

Lelolino, anthu angatambe zamalisece, popanda ena kudziŵa. Kale, munthu akafuna kutamba zamalisece anali kupita kumalo otambitsila mafilimu osayenelela. Ena anali kukagula mabuku a zithunzi zamalisece ku mashopu ogulitsa mabuku otelo. Zioneka kuti anthu ambili sanali kupitako kumalo aconco, cifukwa anali kucita manyazi poganiza kuti anthu ena adzawaona. Koma masiku ano, munthu angatambe zamalisece pa intaneti ali kunchito, ngakhale m’motoka. Ndipo m’madela ambili, anthu angathe kutamba zamalisece ngakhale pa nyumba.

Si apo pokha. Mafoni na matabuleti, apangitsa kuti cikhale cosavuta kwa anthu kutamba zamalisece. Kaya munthu akuyenda pa msewu, ali m’basi kapena m’sitima, angatambe zamalisece pa foni kapena pa tabuleti yake.

Masiku ano, n’zosavuta munthu kutamba zamalisece ena osadziŵa. Pa cifukwa ici, mcitidwe wotamba zamalisece wavulaza anthu ambili kuposa kale lonse. Anthu oculuka amene amatamba zamalisece, awononga maukwati awo, adzicotsela ulemu, komanso aipitsa cikumbumtima cawo. Coipa kwambili, iwo aika ubwenzi wawo na Mulungu paciopsezo. Conco, n’zoonekelatu kuti anthu amene amatamba zamalisece amadzivulaza okha. Kutamba zamalisece kumaononga maganizo a munthu, ndipo zimatenga nthawi yaitali kwambili kuti maganizo oipa acoke mu mtima mwake.

Koma n’zokondweletsa kudziŵa kuti Yehova amatiteteza ku msampha wa Satana umenewu. Kuti Yehova atiteteze, tiyenela kucita zimene Aisiraeli analephela kucita. Tiyenela ‘kulabadila’ Mawu a Mulungu. (Eks. 19:5) Tiyenela kuzindikila kuti Mulungu amadana kwambili na mcitidwe wotamba zamalisece. N’cifukwa ciani takamba conco?

MUZIDANA NA ZAMALISECE MMENE YEHOVA AMACITILA

Malamulo amene Mulungu anapatsa Aisiraeli anali apadela, osiyana ndi a mitundu ina. Malamulo amenewo anali ngati mpanda woteteza Aisiraeli kwa anthu a mitundu ina, komanso ku macita-cita awo oipa. (Deut. 4:6-8) Malamulo a Mulungu anaonetselatu kuti Yehova amadana na khalidwe laciwelewele.

Pambuyo pofotokoza zonyansa zimene anthu a mitundu ina anali kucita, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musakacite zimene amacita m’dziko la Kanani, kumene ndikukulowetsani. . . . Dzikolo n’lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga cifukwa ca kulakwa kwake.” Kwa Mulungu woyela wa Aisiraeli, makhalidwe a Akanani anali onyansa kwambili, cakuti zinacititsa dziko lawo kukhala lodetsedwa.—Lev. 18:3, 25.

Ngakhale kuti Yehova analanga Akanani, anthu ena anapitiliza kucita ciwelewele. Patapita zaka 1,500, Paulo anakamba kuti anthu a mitundu ina m’nthawi yake, anafika ‘posathanso kuzindikila makhalidwe abwino.’ Ndipo “anadzipeleka okha ku khalidwe lotayilila kuti acite conyansa camtundu uliwonse mwadyela.” (Aef. 4:17-19) N’cimodzi-modzinso masiku ano. Anthu ambili ali na khalidwe lotayilila. Conco, olambila oona afunika kucita zonse zotheka kuti apewe kuyang’ana zinthu zaciwelewele zimene anthu a m’dzikoli amacita.

Kutamba zamalisece n’kusalemekeza Mulungu ngakhale pang’ono. Iye anatilenga m’cifanizilo cake, ndipo anatipatsa mtima wofuna kucita zinthu modzilemekeza. Ndiye cifukwa cake, anaika malamulo pa nkhani ya kugonana. Iye anafuna kuti anthu okwatilana okha ndiwo azisangalala na mphatso imeneyi. (Gen. 1:26-28; Miy. 5:18, 19) Koma kodi anthu amene amapanga zamalisece kapena kuzifalitsa amalimbikitsa mzimu wotani? Amalimbikitsa mzimu wonyozela mfundo za Mulungu. Kukamba zoona, anthu amene amafalitsa zamalisece amatonza Yehova. Ndipo iye adzawaweluza.—Aroma 1:24-27.

Nanga bwanji za anthu amene amaŵelenga kapena kutamba zamalisece mwadala? Ena angaganize kuti kucita zimenezi n’kosangalatsa, ndipo kulibe vuto. Koma zoona zake n’zakuti, ngati munthu acita zimenezi, ndiye kuti akucilikiza anthu amene amanyozela mfundo za Yehova. N’kutheka kuti ena anayamba kutamba zamalisece pambuyo poziona mwangozi cabe. Ngakhale n’conco, Malemba amaonetselatu kuti atumiki a Mulungu afunika kunyansidwa na zamalisece. Baibo imati: “Inu okonda Yehova danani naco coipa.”—Sal. 97:10.

Kupewa zamalisece kungakhale kovuta ngakhale kwa anthu amene amafunitsitsa kuzipewa. Zili conco cifukwa ndife opanda ungwilo, ndipo nthawi zina timalimbana na zilako-lako zoipa za kugonana. Cinanso, mtima wathu wopanda ungwilo ungatinyenge kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. (Yer. 17:9) Koma anthu ambili amene poyamba anali kutamba zamalisece, anakwanitsa kuleka atakhala Mboni. Kudziŵa mfundo imeneyi kungakulimbikitseni kwambili, ngati na imwe mulimbana na vuto limeneli. Onani mmene mfundo za m’Mawu a Mulungu zingakuthandizileni kupewa msampha wa Satana wotamba zamalisece.

MUSAMAGANIZILE ZACIWELEWELE

Malinga n’zimene taphunzila, Aisiraeli ambili anatsatila zilako-lako zawo zoipa, ndipo zotulukapo zake zinali zoopsa. Zotelo zingaticitikile na ife masiku ano. M’bale wake wa Yesu, Yakobo anafotokoza ngozi imene imakhalapo ngati munthu atsatila zilako-lako zake zoipa. Iye anati: ‘Aliyense . . . amakopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake. Ndiye cilakolako cikatenga pakati, cimabala chimo.’ (Yak. 1:14, 15) Cilako-lako cikakula mumtima mwa munthu, cimakhala capafupi munthuyo kucita chimo. Conco, tifunika kucotsa maganizo alionse a ciwelewele mumtima mwathu, osati kuwalekelela.

Ngati mwaona kuti muli na vuto lokonda kuganizila zaciwelewele, citamponi kanthu mwamsanga. Yesu anati: “Ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule ndi kulitaya kutali. . . . Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa ulikolowole n’kulitaya.” (Mat. 18:8, 9) Apa, Yesu sanali kutanthauza kuti tifunika kucotsa ziwalo zeni-zeni za thupi lathu. Koma anali kupeleka fanizo loonetsa kufunika kocitapo kanthu mwamsanga komanso mwamphamvu, kuti ticotse cimene cikutipangitsa kuganizila zinthu zoipa. Kodi tingaseŵenzetse bwanji uphungu umenewu pa nkhani ya kutamba zamalisece?

Mukangoona zamalisece, pewani maganizo akuti, ‘Sizinganibweletsele vuto.’ Yang’anani kumbali mwamsanga. Kaya museŵenzetsa TV, kompyuta, foni kapena tabuleti, zimyani nthawi yomweyo. Ndipo yesetsani kuganizila zinthu zoyenela. Kucita izi kudzakuthandizani kulamulila maganizo anu, m’malo molola cilakolako coipa kukulamulilani.

BWANJI NGATI ZITHUNZI ZOIPA ZIMABWELABE M’MAGANIZO MWANU?

Nanga bwanji ngati munaleka kutamba zamalisece, koma nthawi zina zithunzi zoipa zimabwelabe m’maganizo mwanu? Kumbukilani kuti pamatenga nthawi yaitali kuti munthu aiŵaliletu zinthu zoipa zimene anaona. Conco, zithunzi zoipa zingabwele m’maganizo mwanu nthawi iliyonse. Zikakhala telo, mungayambe kulakalaka kucita zinthu zodetsa, monga kudzipukusa umalisece. Conco, mufunika kudziŵilatu kuti nthawi iliyonse maganizo oipa angabwele mu mtima mwanu. Ndipo khalani okonzeka kulimbana nawo.

Tsimikizani mtima kuganiza na kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Tengelani citsanzo ca mtumwi Paulo, amene anali wokonzeka ‘kumenya thupi lake ndi kulitsogolela ngati kapolo.’ (1 Akor. 9:27) Musalole kukhala kapolo wa zilako-lako zoipa. “Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.” (Aroma 12:2) Kumbukilani kuti kuganiza na kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu, n’kumene kumabweletsa cimwemwe, osati kutsatila zilako-lako zoipa.

Kuganiza na kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu, n’kumene kumabweletsa cimwemwe, osati kutsatila zilako-lako zoipa

Yesetsani kuloŵeza pa mtima Malemba ena a m’Baibo. Ndiyeno, maganizo oipa akabwela mu mtima mwanu, dzikakamizeni kuganizila pa malemba amenewo. Kuganizila malemba monga Salimo 119:37; Yesaya 52:11; Mateyu 5:28; Aefeso 5:3; Akolose 3:5; na 1 Atesalonika 4:4-8, kungakuthandizeni kuyamba kuona zamalisece mmene Yehova amazionela na kudziŵa zimene iye amafuna kuti muzicita.

Kodi mungacite ciani ngati muona kuti cilako-lako cofuna kutamba zamalisece kapena kuziganizila, cafika posalamulilika? Tengelani citsanzo ca Yesu. (1 Pet. 2:21) Iye atabatizika, Satana anamuyesa kuti acite zinthu zolakwika. Kodi Yesu anacita ciani? Anapitiliza kukana. Iye anaseŵenzetsa malemba osiyana-siyana pokana mayeselo a Satana. Yesu anati: “Coka Satana!” Ndipo Satana anamusiya. Yesu sanaleke kukaniza Mdyelekezi. Inunso musaleke. (Mat. 4:1-11) Satana na dziko lake adzapitiliza kukusonkhezelani kuganizila zinthu zoipa. Koma musagonje polimbana naye. Mungakwanitse kuthetsa vuto lotamba zamalisece. Inde, na thandizo la Yehova, mungam’gonjetse Satana.

MUZIPEMPHELA KWA YEHOVA NA KUMUMVELA

Muzidalila kwambili Yehova mwa kupemphela kwa iye. Paulo anati: “Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Mtendele wa Mulungu udzakuthandizani kupewa kucita zoipa. Ngati muyandikila Yehova, nayenso “adzayandikila kwa inu.”—Yak. 4:8.

Kukhala pa ubwenzi wabwino na Mfumu ya cilengedwe conse, ndiye citetezo cacikulu ku msampha uliwonse wa Satana. Yesu anati: “Wolamulila wa dziko, [Satana] akubwela. Iye alibe mphamvu pa ine.” (Yoh. 14:30) N’cifukwa ciani Yesu anakamba motsimikiza conco? Panthawi ina, iye anafotokoza cifukwa cake. Anati: “Amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, cifukwa ndimacita zinthu zomukondweletsa nthawi zonse.” (Yoh. 8:29) Ngati na imwe mucita zinthu zokondweletsa Yehova, iye sadzakusiyani ngakhale pang’ono. Pewani msampha wotamba zamalisece, ndipo Satana sadzakugwilani.