Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 27

Konzekelani Cizunzo Pali Pano

Konzekelani Cizunzo Pali Pano

“Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.”—2 TIM. 3:12.

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

ZA M’NKHANI INO *

1. N’cifukwa ciani tifunika kukonzekela cizunzo?

MADZULO akuti adzaphedwa maŵa, Ambuye Yesu anakamba kuti onse amene adzasankha kukhala otsatila ake adzazondedwa ndi anthu. (Yoh. 17:14) Kucokela nthawiyo mpaka pano, Mboni za Yehova zokhulupilika zakhala zikuzunzidwa ndi anthu amene amatsutsa kulambila koona. (2 Tim. 3:12) Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, tiyembekezela kutsutsidwa kwambili na adani athu.—Mat. 24:9.

2-3. (a) Kodi tifunika kudziŵa ciani za mantha? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Ni zinthu ziti zimene tingacite pali pano pokonzekela cizunzo? Sikuti tiyenela kumaganizila zinthu zoipa zimene zingakaticitikile pa nthawiyo. Kuganizila izi, kungatipangitse kukhwethemuka na mantha komanso nkhawa. Ndipo tingafike poleka kutumikila Yehova tikalibe kukumana na cizunzo n’komwe. (Miy. 12:25; 17:22) Mantha ni cida camphamvu kwambili cimene “mdani [wathu] Mdyelekezi” amaseŵenzetsa pofuna kutigonjetsa. (1 Pet. 5:8, 9) Nanga tingacite ciani pali pano kuti tikathe kupilila cizunzo?

3 M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingalimbitsile ubwenzi wathu na Yehova, komanso cifukwa cake tifunika kucita zimenezo pali pano. Tidzakambilananso zimene tingacite kuti tikhale olimba mtima kwambili. Cotsiliza, tidzaona zimene tingacite anthu akamatizonda.

MMENE MUNGALIMBITSILE UBWENZI WANU NA YEHOVA

4. Malinga na Aheberi 13:5, 6, kodi sitiyenela kukayikila za ciani? Cifukwa ciani?

4 Musamakayikile kuti Yehova amakukondani na kuti sadzakusiyani ngakhale pang’ono. (Ŵelengani Aheberi 13:5, 6.) Zaka zambili kumbuyoko, magazini ina ya Nsanja ya Mlonda inati: “Munthu amene adziŵa bwino Mulungu, amam’dalila kwambili pa nthawi ya mayeselo.” Izi n’zoona, cifukwa kuti tipilile cizunzo, tifunika kukonda Yehova na kum’dalila na mtima wathu wonse. Ndiponso sitiyenela kukayikila ngakhale pang’ono kuti amatikonda.—Mat. 22:36-38; Yak. 5:11.

5. N’ciani cingakuthandizeni kuona kuti Yehova amakukondani?

5 Muziŵelenga Baibo tsiku lililonse kuti mulimbitse ubwenzi wanu na Yehova. (Yak. 4:8) Pamene muŵelenga, muziganizila kwambili za makhalidwe a Yehova, monga cikondi, cifundo na kukoma mtima. Ganizilani mmene iye waonetsela cikondi cake mwa zokamba na zocita zake. (Eks. 34:6) Ena amakayikila zakuti Mulungu amawakonda cifukwa cakuti anthu sawakonda. Ngati na imwe mumakayikila, yesani kucita izi: Tsiku lililonse, muzilemba zinthu zimene Yehova wakucitilani pokuonetsani cifundo na kukoma mtima kwake. (Sal. 78:38, 39; Aroma 8:32) Ngati muganizila zocitika mu umoyo wanu na kusinkha-sinkha pa zimene mwaŵelenga m’Mawu a Mulungu, mudzaona kuti pali zambili zimene Yehova wakucitilani. Mukayamba kuyamikila kwambili zimene Yehova amakucitilani, m’pamene ubwenzi wanu na iye udzalimba kwambili.—Sal. 116:1, 2.

6. Malinga na Salimo 94:17-19, kodi kupemphela mocokela pansi pa mtima kungakuthandizeni bwanji?

6 Muzipemphela nthawi zonse. Yelekezelani kuti tate wanyamula mwana wake wamng’ono. Mwanayo, akuona kuti ni wotetezeka kwambili, cakuti akufotokozela tateyo momasuka zinthu zabwino na zoipa zimene zam’citikila pa tsikulo. Na imwe mungakhale pa ubwenzi wathithithi na Yehova ngati mupemphela kwa iye tsiku lililonse. (Ŵelengani Salimo 94:17-19.) Pamene mupemphela, ‘khuthulani mtima wanu pamaso pa Yehova ngati madzi.’ M’fotokozeleni Tate wanu wacikondi nkhawa zanu. (Maliro 2:19) Kodi padzakhala zotulukapo zotani? Mudzakhala na cimene Baibo imati “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:6, 7) Mukamapemphela mocokela pansi pa mtima nthawi zonse, mudzamuyandikila kwambili Yehova.—Aroma 8:38, 39.

Kukhulupilila kwambili Yehova na Ufumu wake n’kumene kumatithandiza kukhala olimba mtima

M’bale Stanley Jones anakhalabe wolimba cifukwa cokhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu ni weni-weni (Onani ndime 7)

7. N’cifukwa ciani muyenela kukhulupilila na mtima wonse kuti malonjezo a Mulungu okhudza Ufumu wake adzakwanilitsidwa?

7 Limbitsani cikhulupililo canu cakuti malonjezo a Ufumu wa Mulungu adzakwanilitsidwa. (Num. 23:19) Ngati cikhulupililo canu m’malonjezo a Mulungu n’cofooka, cidzakhala capafupi kuti Satana ndi anthu ake akuyofyeni. (Miy. 24:10; Aheb. 2:15) Kodi mungacite ciani pali pano kuti mukhale na cikhulupililo colimba cakuti malonjezo a Ufumu adzakwanilitsidwa? Patulani nthawi yoŵelenga mosamala zimene Mulungu walonjeza kuti Ufumu wake udzacita. Pamene muŵelenga, yesani kupeza maumboni otsimikizila kuti malonjezo amenewo adzakwanilitsidwa. Kodi kucita izi kudzakuthandizani bwanji? Ganizilani za m’bale Stanley Jones, amene anakhala m’ndende zaka 7 cifukwa ca cikhulupililo cake. * Kodi n’ciani cinam’thandiza kupilila mokhulupilika? Iye anati: “Cikhulupililo canga cinali colimba cifukwa n’nali kudziŵa za Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzacita. Ndipo sin’nali kukayikila zimenezo olo pang’ono. Ndiye cifukwa cake sin’nagwedezeke.” Ngati mumakhulupilila na mtima wonse zimene Mulungu analonjeza, mudzam’yandikila kwambili Yehova, ndipo simudzagonja cifukwa ca mantha.—Miy. 3:25, 26.

8. Kodi kupezeka kwathu pa misonkhano ni cizindikilo ca ciani? Fotokozani.

8 Muzipezeka pa misonkhano nthawi zonse. Misonkhano imatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu na Yehova. Kupezeka kwathu pa misonkhano ni cizindikilo cabwino coonetsa mmene tidzacitile pa nthawi ya cizunzo. (Aheb. 10:24, 25) N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa ngati pali pano timalola mavuto aang’ono-ang’ono kutilepheletsa kusonkhana, tidzalephelelatu kusonkhana pa nthawi imene tingafunikile kuika moyo wathu paciwopsezo kuti tikasonkhane. Koma ngati timayesetsa kupezeka ku misonkhano, ndiye kuti sitidzagonja pamene adani athu atiletsa kusonkhana. Conco, ino ndiyo nthawi yokulitsa cizolowezi copezeka pa misonkhano. Ngati timakonda misonkhano, ndiye kuti olo pakakhale citsutso, kapena ciletso ca boma, sitidzaleka kumvela Mulungu kuposa anthu.—Mac. 5:29.

Kuloŵeza pa mtima malemba na nyimbo za Ufumu pali pano kudzakuthandizani kupilila pa nthawi ya cizunzo (Onani ndime 9) *

9. N’cifukwa ciani kuloŵeza Malemba pa mtima ni njila yabwino yokonzekelela cizunzo?

9 Muziloŵeza pa mtima malemba amene mumakonda. (Mat. 13:52) N’zoona kuti tonse timaiŵala. Koma Yehova angaseŵenzetse mzimu wake wamphamvu kuti utikumbutse Malemba amene tinaloweza pa mtima. (Yoh. 14:26) Ganizilani zimene m’bale wina amene anaikidwa m’cipinda cayekha ca ndende ku East Germany anakamba. Iye anati: “N’nali wokondwela kwambili cifukwa pa nthawiyo n’nali n’taloweza pa mtima Malemba oposa 200. Cotelo, nthawi imene n’nali nekha m’ndende, sin’nali kusoŵa zocita. N’nali kusinkha-sinkha pa nkhani zosiyana-siyana za m’Baibo.” Kusinkha-sinkha nkhani zimenezo kunathandiza m’baleyo kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova, komanso kupilila mokhulupilika.

(Onani ndime 10) *

10. N’cifukwa ciani tiyenela kuloŵeza pamtima nyimbo?

10 Muziloŵeza pa mtima nyimbo zotamanda Yehova na kuziimba. Pamene Paulo na Sila anali m’ndende ku Filipi, anali kuimba nyimbo zauzimu zimene analoŵeza pa mtima. (Mac. 16:25) Kuimba nyimbo n’kumenenso kunalimbikitsa abale athu amene anawathamangitsila ku Siberia, mu ulamulilo wa Soviet Union. Mlongo Mariya Fedun, anati: “Tinali kuimba nyimbo zonse za m’buku la nyimbo zimene tinali kudziŵa.” Mlongoyo anakamba kuti nyimbo zimenezo zinali kuwalimbikitsa onse, na kuwathandiza kuyandikila kwambili Yehova. Kodi na imwe mumalimbikitsidwa pamene muimba nyimbo zauzimu zimene m’makonda? Ngati n’conco, ino ndiyo nthawi yoyenela kuloŵeza pa mtima nyimbo zimenezo.—Onani bokosi yakuti “ Nilimbitseni Mtima.”

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUKHALE WOLIMBA MTIMA KWAMBILI

11-12. (a) Malinga na 1 Samueli 17:37, 45-47, n’cifukwa ciani Davide anali wolimba mtima? (b) Tiphunzilapo mfundo yofunika iti pa citsanzo cake?

11 Kupilila cizunzo kumafuna kulimba mtima. Ngati muona kuti sindinu wolimba mtima, kodi mungacite ciani? Kumbukilani kuti kulimba mtima kweni-kweni sikudalila msinkhu, mphamvu, kapena luso. Ganizilani mmene Davide anaonetsela kulimba mtima ali wacinyamata, pamene anayang’anizana na Goliyati. Poyelekezela na ciphona cimeneco, Davide anali wamng’ono kwambili, wopanda mphamvu, komanso analibe zida zokwanila. Davide analibe ngakhale lupanga. Koma anali wolimba mtima kwambili. Ndiye cifukwa cake, mopanda mantha, iye anathamanga kukamenyana na ciphona codzikuza cimeneco.

12 N’cifukwa ciani Davide anali wolimba mtima kwambili? Cifukwa anali na cikhulupililo camphamvu cakuti Yehova ali naye. (Ŵelengani 1 Samueli 17:37, 45-47.) Davide sanasumike maganizo ake pa kukula thupi kwa Goliyati. M’malomwake, anasumika maganizo ake pa ukulu wa Yehova poyelekezela na Goliyati. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tiphunzilapo kuti tingakhale olimba mtima ngati tili na cikhulupililo camphamvu cakuti Yehova ali nafe, komanso ngati tidziŵa kuti amene amatitsutsa sali kanthu poyelekezela na Mulungu Wamphamvuzonse. (2 Mbiri 20:15; Sal. 16:8) Kodi tingacite ciani kuti tikhale olimba mtima kwambili pali pano, tikalibe kukumana na cizunzo?

13. Tingacite ciani kuti tikhale olimba mtima kwambili? Fotokozani.

13 Cina cimene cingatithandize kukhala olimba mtima kwambili ni kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa kulalikila kumatiphunzitsa kudalila Yehova. Kumatithandizanso kuti tisamaope anthu. (Miy. 29:25) Kulalikila tingakuyelekezele na maseŵela olimbitsa thupi. Ngati munthu amacita maseŵela olimbitsa thupi, amakhala na thupi lolimba. Mofananamo, tikamacita ulaliki wa ku nyumba na nyumba, wapoyela, wamwayi, komanso wa m’gawo la malonda, timakhala olimba mtima kwambili. Ngati tiphunzila kulalikila molimba mtima pali pano, ndiye kuti cidzakhala cosavuta kupitiliza kulalikila ngakhale pa nthawi imene nchito yathu idzaletsedwa.—1 Ates. 2:1, 2.

Mlongo Nancy Yuen anakana kusiya kulalikila uthenga wabwino (Onani ndime 14)

14-15. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Nancy Yuen na Valentina Garnovskaya?

14 Tingaphunzile zambili pa citsanzo ca alongo aŵili okhulupilika amene anali olimba mtima kwambili. Woyamba ni mlongo Nancy Yuen. Iye anali wamfupi kwambili; mamita 1.5 cabe. Koma anali wopanda mantha. * Mlongoyu anakana kuleka kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Izi zinapangitsa kuti akhale m’ndende kwa zaka zoposa 20, ku China. Apolisi amene anali kumufunsa mafunso, anafika pokamba kuti mlongoyo “anali munthu wovuta kwambili” m’dziko lawo!

15 Nayenso mlongo Valentina Garnovskaya anaikidwa m’ndende maulendo atatu mu ulamulilo wa Soviet Union. Ndipo zaka zonse zimene anakhala m’ndende zinakwana 21. * N’cifukwa ciani anamuika m’ndende? Cifukwa anakanilatu zoleka kulalikila, cakuti apolisi anakamba kuti anali “munthu wophwanya malamulo woopsa.” N’ciani cinathandiza alongo okhulupilika amenewa kukhala olimba mtima conco? Iwo anali kukhulupilila kuti Yehova anali nawo.

Mlongo Valentina Garnovskaya anali kukhulupilila na mtima wonse kuti Yehova anali naye (Onani ndime 15)

16. Kodi cisinsi ca kulimba mtima kweni-kweni n’ciani?

16 Monga takambila, kuti tikhale olimba mtima kwambili, sitiyenela kudalila mphamvu na maluso athu. M’malomwake, tiyenela kukhulupilila kuti Yehova ali nafe, ndiponso kuti adzatiteteza. (Deut. 1:29, 30; Zek. 4:6) Ici ndiye cisinsi ca kulimba mtima kweni-kweni.

ZIMENE TINGACITE NGATI ANTHU AMATIZONDA

17-18. Kodi Yesu anaticenjeza za ciani pa Yohane 15:18-21? Fotokozani.

17 Timamvela bwino anthu akamatilemekeza. Koma sitiyenela kuganiza kuti ngati anthu satilemekeza, ndiye kuti ndife osafunika. Yesu anati: “Ndinu odala anthu akamadana nanu, kukusalani, kukunyozani ndi kukana dzina lanu n’kumanena kuti ndi loipa, cifukwa ca Mwana wa munthu.” (Luka 6:22) Kodi Yesu anatanthauzanji pamenepa?

18 Yesu sanatanthauze kuti Akhristu adzayamba kukondwela cifukwa codedwa ndi anthu. M’malomwake, anali kuticenjeza za mavuto amene tidzakumana nawo. Sitili mbali ya dziko. Timatsatila ziphunzitso za Yesu mu umoyo wathu, ndiponso timalalikila uthenga umene iye analalikila. Zotulukapo zake n’zakuti, dziko limatizonda. (Ŵelengani Yohane 15:18-21.) Ife timafuna kukondweletsa Yehova. Conco, cifukwa cakuti timakonda Atate wathu, sitikwiya anthu akamatizonda.

19. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca atumwi?

19 Tisacite manyazi kudzidziŵikitsa kuti ndife Mboni ya Yehova poopa zimene anthu angakambe kapena kuticitila. (Mika 4:5) Nanga n’ciani cingatithandize kuti tisamayope anthu? Tingacite bwino kuganizila mmene atumwi ku Yerusalemu anaonetsela kulimba mtima Yesu ataphedwa. Iwo anali kudziŵa kuti atsogoleli acipembedzo aciyuda anali kuwazonda. (Mac. 5:17, 18, 27, 28) Ngakhale n’conco, tsiku lililonse anali kupita kukacisi, ndipo anapitiliza kuonetsa poyela kuti anali ophunzila a Yesu mwa kulalikila. (Mac. 5:42) Iwo sanalole mantha kuwalepheletsa kucita zimenezo. Nafenso tingagonjetse mantha oopa anthu mwa kudzidziŵikitsa kuti ndife Mboni ya Yehova, kaya ni ku nchito, ku sukulu, kapena kumene tikhala.—Mac. 4:29; Aroma 1:16.

20. N’cifukwa ciani atumwi anali okondwela olo kuti anali kuzondewa?

20 Ngakhale kuti atumwi anali kuzondewa, iwo anakhalabe okondwela. Cifukwa ciani? Cifukwa anaona kuti unali mwayi kucitilidwa cipongwe cifukwa cocita cifunilo ca Yehova. (Luka 6:23; Mac. 5:41) Pambuyo pake, mtumwi Petulo analemba kuti: “Ngakhale mutavutika cifukwa ca cilungamo, mudzakhalabe odala.” (1 Pet. 2:19-21; 3:14) Tikadziŵa kuti timazondewa cifukwa cocita zinthu zoyenela, sitidzaleka kutumikila Yehova cifukwa coopa anthu.

MUKAKONZEKELA, MUDZAKWANITSA KUPILILA

21-22. (a) Kodi imwe mwatsimikiza mtima kucita ciani pokonzekela cizunzo? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

21 Sitidziŵa nthawi pamene cizunzo cingayambe, kapena pamene boma lingatiletse kulambila Yehova. Komabe, tifunika kukonzekela pali pano mwa kulimbitsa ubale wathu na Yehova, kukulitsa khalidwe la kulimba mtima, na kudziŵa zimene tingacite ngati anthu akutizonda. Kukonzekela pali pano, kudzatithandiza kupilila pa nthawi ya cizunzo.

22 Koma bwanji ngati boma laika ciletso pa kulambila kwathu? M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize kupitiliza kutumikila Yehova pa nthawi ya ciletso.

NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”

^ ndime 5 Sitifuna kuzondedwa ndi anthu. Ngakhale n’conco, tonsefe pa nthawi ina, tidzakumana na cizunzo kapena citsutso. Nkhani ino idzatithandiza kukonzekela cizunzo komanso kukhala olimba mtima.

^ ndime 7 Onani Nsanja ya Mlonda ya cizungu ya December 15, 1965, peji 756-767.

^ ndime 14 Onani Nsanja ya Mlonda ya Cizungu ya July 15, 1979, peji 4-7.

^ ndime 15 Onani Nsanja ya Olonda ya 09 4/15 peji 9, pal. 10, 11.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa kulambila kwa pabanja, makolo akuseŵenzetsa tumakadi twa malemba pothandiza ana awo kuloŵeza malemba pa mtima.

^ ndime 70 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene banja lili m’motoka popita ku misonkhano, likuphunzila nyimbo za Ufumu.