Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 28

Musaleke Kulambila Yehova pa Nthawi ya Ciletso

Musaleke Kulambila Yehova pa Nthawi ya Ciletso

“Ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”—MAC. 4:19, 20.

NYIMBO 122 Cilimikani, Musasunthike!

ZA M’NKHANI INO *

1-2. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kudabwa ngati taletsedwa kulambila Mulungu? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

MU 2018, ciŵelengelo ca ofalitsa uthenga wabwino okhala m’maiko amene munali ciletso, kapena mmene abale athu sanali kulambila mwaufulu cinali coposa 223,000. Izi n’zosadabwitsa. Monga tinaphunzilila m’nkhani yapita, Akhristu oona amadziŵa kuti adzazunzidwa. (2 Tim. 3:12) Mosasamala kanthu za kumene tikhala, mosayembekezeleka boma lingatiletse kulambila Mulungu wathu wacikondi, Yehova.

2 Ngati boma m’dziko lanu lakuletsani kulambila Yehova, mungakhale na mafunso monga aya: ‘Kodi tikamazunzidwa, ndiye kuti Mulungu waleka kutikonda? Kodi tidzaleka kulambila Yehova ngati kuli ciletso? Kodi niyenela kusamukila ku dziko lina, kumene ningakalambile Mulungu mwaufulu?’ Tidzakambilana mafunso amenewa m’nkhani ino. Tidzakambilananso zimene tingacite kuti tipitilize kulambila Yehova ngati m’dziko muli ciletso, komanso misampha imene tidzafunika kupewa pa nthawi imeneyo.

KODI TIKAMAZUNZIDWA, NDIYE KUTI YEHOVA WALEKA KUTIKONDA?

3. Malinga na 2 Akorinto 11:23-27, ni cizunzo cotani cimene mtumwi Paulo anakumana naco? Nanga tiphunzilapo ciani pa citsanzo cake?

3 Ngati boma latiletsa kulambila Mulungu, tingaganize kuti Mulungu waleka kutikonda. Koma kumbukilani kuti kuzunzidwa si cizindikilo cakuti Yehova sakukondwela nafe. Mwacitsanzo, ganizilani za mtumwi Paulo. N’zacidziŵikile kuti Mulungu anali kum’konda. Iye anali na mwayi wolemba makalata 14 a Malemba Acigiliki Acikristu, ndiponso anali mtumwi wotumidwa ku mitundu ina. Ngakhale n’telo, iye anakumana na cizunzo coopsa. (Ŵelengani 2 Akorinto 11:23-27.) Zimene zinacitikila mtumwi Paulo zitiphunzitsa kuti nthawi zina Yehova amalola atumiki ake okhulupilika kuzunzidwa.

4. N’cifukwa ciani dziko limatizonda?

4 Yesu anafotokoza cifukwa cake timazunzidwa. Anakamba kuti tidzazondewa cifukwa cakuti sitili mbali ya dziko. (Yoh. 15:18, 19) Conco, cizunzo si cizindikilo cakuti Yehova waleka kutidalitsa. M’malomwake, ni cizindikilo cakuti zimene timacita n’zabwino.

KODI TIDZALEKA KULAMBILA YEHOVA CIFUKWA CA CILETSO?

5. Kodi anthu angakwanitse kuthetsa kulambila Yehova? Fotokozani citsanzo.

5 Anthu sangakwanitse kuthetsa kulambila koona—sangathe kutiletsa kulambila Mulungu wathu wamphamvuzonse, Yehova. Ambili ayesapo, koma alephela. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika m’nthawi ya Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse. Pa nthawiyo, maboma m’maiko ambili anazunza anthu a Mulungu kwambili. Nchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa pa nthawi ya ulamulilo wa cipani ca Nazi ku Germany. Inalinso yoletsedwa ku Australia, ku Canada, na ku maiko ena. Koma onani zimene zinacitika. Mu 1939, pamene nkhondo inali kuyamba, pa dziko lonse panali ofalitsa 72,475. Koma lipoti inaonetsa kuti pamene nkhondo inali kutha mu 1945, mwa dalitso la Yehova, ciŵelengelo ca ofalitsa cinali citakwela kufika pa 156,299. Ciŵelengelo cinawonjezeka kuposa kuŵilikiza kaŵili!

6. M’malo motipangitsa kuopa kutumikila Yehova, kodi cizunzo cingatisonkhezele kucita ciani? Pelekani citsanzo.

6 Cizunzo cikayamba, mwacibadwa timakhala na mantha. Koma cizunzo cimakhalanso na zotulukapo zabwino. Cingatisonkhezele kuyamba kutumikila Yehova mwakhama komanso mopanda mantha. Mwacitsanzo, m’bale wina na mkazi wake amene anali na mwana wamng’ono, anali kukhala m’dziko limene boma linaletsa kulambila kwathu. Iwo sanabwelele m’mbuyo pa kulambila kwawo. M’malomwake, anayamba kucita upainiya wa nthawi zonse. Mkazi wake anacita kuleka nchito ya ndalama zambili kuti ayambe upainiya. M’baleyo anakamba kuti ciletsoco cinacititsa kuti anthu ambili ayambe kucita cidwi na Mboni za Yehova, moti sicinali covuta kuyambitsa maphunzilo a Baibo. Ciletso cimeneco cinalinso na zotulukapo zina zabwino. Mkulu wina m’dziko limodzi-modzilo anakamba kuti, anthu ambili amene anali ataleka kutumikila Yehova anayambanso kupezeka ku misonkhano na kulalikila.

7. (a) Kodi tiphunzilapo ciani pa Levitiko 26:36, 37? (b) Kodi inu mudzacita ciani pa nthawi ya ciletso?

7 Adani athu akatiletsa kulambila Yehova, amaganiza kuti tidzacita mantha n’kuleka kum’tumikila. Kuphatikiza pa ciletso, iwo angafalitse mabodza ponena za ife, angatumize apolisi kuti akasece m’nyumba zathu, angatitengele ku khoti, ngakhale kutiponya m’ndende kumene. Iwo amafuna kuti tikamva kuti ena mwa abale athu aponyedwa m’ndende, ticite mantha. Ngati tingacitedi mantha na zimenezi, tingabwelele m’mbuyo pa kulambila kwathu, mwina mpaka kulekelatu kutumikila Yehova. Koma sitifunika kucita zinthu ngati anthu amene akufotokozedwa pa Levitiko 26:36, 37. (Ŵelengani.) Tisalole mantha kutibweza m’mbuyo pa kulambila kwathu, kapena kutipangitsa kuleka kutumikila Yehova. Tidalile Yehova na mtima wonse, ndipo tisakhwethemuke na mantha. (Yes. 28:16) Tiyenela kupemphela kwa Yehova kuti atitsogolele. Popeza iye ali ku mbali yathu, ngakhale maboma amphamvu kwambili pa dzikoli sangathe kutilepheletsa kulambila Mulungu wathu mokhulupilika.—Aheb. 13:6.

KODI NIFUNIKA KUSAMUKILA KU DZIKO LINA?

8-9. (a) N’cosankha cotani cimene mutu wa banja kapena munthu aliyense payekha afunika kupanga? (b) N’ciani cingathandize munthu kupanga cosankha mwanzelu pa nkhaniyi?

8 Ngati m’dziko lanu, boma lakuletsani kulambila Yehova, mwina mungaganize zosamukila ku dziko lina kumene mungakam’tumikile mwaufulu. Ici ni cosankha caumwini. Akhristu ena asanapange cosankha pa nkhaniyi, amaganizila zimene Akhristu a m’nthawi ya atumwi anacita pamene anakumana na cizunzo. Adani atapha Sitefano mwa kum’ponya miyala, ophunzila ku Yerusalemu anathaŵila ku Yudeya na ku Samariya. Ndipo ena anakafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro, na ku Antiokeya. (Mat. 10:23; Mac. 8:1; 11:19) Komabe, ena angaganizile zotengela citsanzo ca mtumwi Paulo. Pa nthawi imene Akhristu a m’nthawi yake anakumananso na cizunzo cina, iye sanacoke m’madela amene nchito yolalikila inali yoletsedwa. M’malomwake, Paulo anaika moyo wake paciopsezo, mwa kupita kukalalikila uthenga wabwino na kukalimbikitsa abale m’mizinda imene munali cizunzo coopsa.—Mac. 14:19-23.

9 Kodi tiphunzilapo ciani pa zitsanzo zimenezi? Tiphunzilapo kuti aliyense amene ni mutu wa banja ali na udindo wopanga cosankha pa nkhani yosamuka. Koma asanapange cosankha, afunika kupemphela na kuganizila mosamala mmene zinthu zilili pa banja lake. Afunika kuganizilanso mmene kusamukako kungakhudzile banjalo. Pa nkhani imeneyi, Mkhristu aliyense ayenela “kunyamula katundu wake.” (Agal. 6:5) Ndipo sitiyenela kuweluza ena pa cosankha cawo.

KODI TIDZAM’LAMBILA BWANJI YEHOVA PA NTHAWI YA CILETSO?

10. Kodi ofesi ya nthambi komanso akulu adzapeleka malangizo otani?

10 Kodi mungacite ciani kuti mupitilize kulambila Yehova pa nthawi ya ciletso? Ofesi yanu ya nthambi idzapeleka malangizo kwa akulu a mu mpingo wanu okhudza mmene mungalandilile cakudya cauzimu, kusonkhana pamodzi, na kulalikila uthenga wabwino. Ngati ofesi ya nthambi siinakwanitse kukambilana na akulu, ndiye kuti akuluwo adzapeleka malangizo othandiza kuti mupitilize kulambila Yehova. Iwo adzapeleka malangizo mogwilizana na zimene Baibo imakamba komanso zofalitsa zathu.—Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29; Aheb. 10:24, 25.

11. N’cifukwa ciani tifunika kukhala na cikhulupililo cakuti tidzadyetsedwa mwauzimu pa nthawi ya ciletso? Nanga tidzafunika kucita ciani kuti titeteze Baibo na zofalitsa zathu?

11 Yehova analonjeza kuti atumiki ake adzakhala odyetsedwa bwino mwauzimu. (Yes. 65:13, 14; Luka 12:42-44) Conco, tiyenela kukhala na cikhulupililo cakuti, pa nthawi ya ciletso, gulu lake lidzacita zilizonse zotheka kuti tidzakhalebe olimba mwauzimu. Nanga ife tidzafunika kucita ciani? Tidzafunika kupeza malo abwino obisapo Baibo yathu na mabuku ena amene tingakhale nawo. Mabuku amenewo ni amtengo wapatali. Conco, kaya ali pa foni kapena ni opulintiwa, tisakawaike pa malo amene anthu angawatulukile mosavuta. Aliyense wa ife afunika kucita zonse zotheka kuti ateteze cikhulupililo cake.

Na thandizo la Yehova, sitidzayopa kusonkhana kuti timulambile (Onani ndime 12) *

12. Kodi akulu angalinganize bwanji misonkhano m’njila yakuti anthu otsutsa asadziŵe?

12 Nanga bwanji za misonkhano ya mpingo? Akulu adzapanga makonzedwe akuti muzisonkhana m’njila yakuti otsutsa asazindikile zimenezo. Mwina adzalinganiza zakuti muzisonkhana m’tumagulu tung’ono-tung’ono, ndiponso kuti muzisintha-sintha nthawi na malo osonkhanako. Kuti aliyense adzakhale wotetezeka ku misonkhanoyo, mudzayenela kupewa kukamba mokweza mawu popita na pocoka pa malo amene mucitila misonkhano. Mudzafunikanso kuvala m’njila yakuti anthu asadziŵe kuti mupita ku misonkhano.

Ngakhale olamulila a boma ataletsa nchito yathu, sitidzaleka kulalikila (Onani ndime 13) *

13. Kodi tiphunzilapo ciani pa zimene abale athu anacita m’nthawi ya ulamulilo wa Soviet Union?

13 Nanga bwanji za kulalikila? Pa nkhani imeneyi, mikhalidwe idzakhala yosiyana-siyana malinga na madela. Koma mulimonse mmene zingakhalile, tidzayesetsa kupeza njila yolalikilila, cifukwa timakonda Yehova komanso timakonda kuuzako anthu za Ufumu wake. (Luka 8:1; Mac. 4:29) Pokamba za nchito yolalikila ya Mboni za Yehova mu ulamulilo wa Soviet Union, katswili wa mbili yakale dzina lake Emily B. Baran anati: “Pamene boma linalamula a Mboni kuti aleke kulalikila, iwo anayamba kukambilana Mawu a Mulungu na maneba awo, anzawo a ku nchito, na mabwenzi awo. Atawaika m’ndende cifukwa ca zimenezi, iwo anayamba kulalikila akaidi anzawo.” Inde, mosasamala kanthu za ciletso, abale athu mu ulamulilo wa Soviet Union sanaleke kulalikila. Conco, ngati nchito yolalikila yaletsedwa m’dziko lanu, mungacite bwino kutengela citsanzo cawo.

MISAMPHA IMENE TIFUNIKA KUPEWA

Tifunika kudziŵa nthawi yokhala cete (Onani ndime 14) *

14. Kodi lemba la Salimo 39:1 limatilimbikitsa kupewa kucita ciani?

14 Tisamale na zimene timauza anthu ena. Pa nthawi ya ciletso, tifunika kuzindikila “nthawi yokhala cete.” (Mlal. 3:7) Sitiyenela kuulula zinthu zimene zingatiikitse m’mavuto, monga maina a abale na alongo athu, malo amene timacitilako misonkhano, mmene timalalikilila, kapena mmene timalandilila cakudya cauzimu. Sitiyenela kuulula zimenezi kwa anthu oimila boma, kapena kwa anzathu kapena acibululu, kaya amene akhala m’dziko lathu kapena ku dziko lina. Ngati tingacite zimenezi, tingaike miyoyo ya abale athu pa ciwopsezo.—Ŵelengani Salimo 39:1.

15. Kodi Satana adzayesetsa kucita ciani? Nanga tingapewe bwanji kugwela mu msampha wake?

15 Tisalole mavuto ocepa kuyambitsa magaŵano pakati pathu. Satana amadziŵa kuti nyumba yogaŵikana singakhale. (Maliko 3:24, 25) Conco, sadzaleka kuyesa kuyambitsa magaŵano pakati pathu. Satana amacita izi n’colinga cakuti tiyambe kulimbana tekha-tekha m’malo molimbana na iye.

16. N’citsanzo cabwino citi cimene mlongo Gertrud Poetzinger anapeleka?

16 Ngakhale Akhristu okhwima mwauzimu afunika kusamala kuti asagwele mu msampha umenewu. Mwacitsanzo, ganizilani za alongo aŵili odzozedwa, mlongo Gertrud Poetzinger na mlongo Elfriede Löhr. Iwo anaikiwa m’ndende yacibalo pamodzi na alongo ena mu ulamulilo wa Nazi ku Germany. Mlongo Poetzinger anayamba kucita nsanje na mlongo Elfriede, cifukwa mlongoyo anali kukamba bwino nkhani zolimbikitsa alongo anzake m’ndendemo. Pambuyo pake, mlongo Poetzinger anayamba kuvutitsidwa na cikumbumtima cifukwa ca khalidwe lake, ndipo anacondelela Yehova kuti am’thandize. Iye analemba kuti, “Tifunika kuphunzila kukhala odzicepetsa ngati anzathu ali na maluso ena amene ife tilibe, kapena ngati ali na maudindo ambili kuposa ife.” Kodi mlongo Poetzinger anathetsa bwanji nsanje imene anali nayo? Iye anayamba kuyang’ana kwambili pa makhalidwe abwino amene mlongo Elfriede anali nawo, kuphatikizapo mtima wake waubwenzi. Izi zinam’thandiza kuti ayambenso kugwilizana na mnzakeyo. Onse aŵili atatulutsidwa m’ndende, anapitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika mpaka pamene anatsiliza moyo wawo wa pa dziko lapansi. Conco, ngati tiyesetsa kuthetsa kusamvana na abale athu, tidzapewa msampha wa magaŵano.—Akol. 3:13, 14.

17. N’cifukwa ciani tifunika kupewa kunyalanyaza malangizo?

17 Pewani kunyalanyaza malangizo. Ngati timvela malangizo amene timalandila kwa abale audindo, tidzapewa kudzigwetsela m’mavuto. (1 Pet. 5:5) Mwacitsanzo, m’dziko lina limene nchito yathu ni yoletsedwa, abale audindo analangiza ofalitsa kuti sayenela kugaŵila zofalitsa mu ulaliki. Koma m’bale wina amene ni mpainiya ananyalanyaza malangizo amenewa na kugaŵila zofalitsa. Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Atangotsiliza ulaliki wamwayi pamodzi na anzake, kunabwela apolisi n’kuyamba kuwafunsa mafunso. Cioneka kuti apolisiwo anali kuwatsatila ndipo anapita kukalanda zofalitsa kwa anthu amene anawagaŵilawo. Tiphunzilapo ciani pa cocitika cimeneci? Tifunika kutsatila malangizo, ngakhale amene sitikugwilizana nawo. Nthawi zonse, Yehova amatidalitsa ngati tigwilizana na abale amene anawaika kuti azititsogolela.—Aheb. 13:7, 17.

18. N’cifukwa ciani tifunika kupewa kuika malamulo osafunikila?

18 Pewani kuika malamulo osafunikila. Ngati akulu aika malamulo osafunikila, amasenzetsa abale mtolo wolema. M’bale Juraj Kaminský anafotokoza zimene zinacitika pa nthawi ya ciletso ku dziko limene kale linali kuchedwa Czechoslovakia: “Akulu ambili na abale ena apaudindo atamangidwa, ena mwa abale amene anali kutsogolela m’mipingo na m’madela anayamba kuika malamulo awo-awo. Ndipo anali kuuza abale na alongo zocita pa nkhani iliyonse.” Yehova sanatipatse mphamvu yopangila ena zosankha pa nkhani zaumwini. Ngati akulu aika malamulo osafunikila, ndiye kuti sakuteteza abale, koma akulamulila cikhulupililo cawo.—2 Akor. 1:24.

MUSALEKE KULAMBILA YEHOVA

19. Malinga na 2 Mbiri 32:7, 8, n’cifukwa ciani sitiyenela kucita mantha na zimene Satana angacite?

19 Mdani wathu wamkulu, Satana Mdyelekezi, sadzaleka kuzunza atumiki a Yehova okhulupilika. (1 Pet. 5:8; Chiv. 2:10) Satana ndi anthu amene ali kumbali yake adzayesa kutiletsa kulambila Yehova. Koma tisakhwethemuke na mantha! (Deut. 7:21) Yehova ali ku mbali yathu, ndipo adzapitiliza kutithandiza ngakhale pa nthawi ya ciletso.—Ŵelengani 2 Mbiri 32:7, 8.

20. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?

20 Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kupitiliza kutumikila Yehova monga mmene abale athu anacitila m’nthawi ya atumwi. Iwo anauza olamulila a pa nthawiyo kuti, “Weluzani nokha, ngati n’koyenela pamaso pa Mulungu kumvela inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”—Mac. 4:19, 20.

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

^ ndime 5 Kodi tiyenela kucita ciani ngati boma latiletsa kulambila Yehova? Nkhani ino idzafotokoza zimene tingacite, na zimene tiyenela kupewa n’colinga cakuti tisaleke kulambila Mulungu wathu.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Zithunzi zonse zionetsa Mboni zimene zikutumikila m’maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa. Pa Cithuzi ici kagulu ka abale na alongo kakucita msonkhano m’cipinda cosungila katundu m’nyumba ya m’bale.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Zithunzi zonse zionetsa Mboni zimene zikutumikila m’maiko amene nchito Mlongo (kumanzele) aceza na mzimayi, ndipo pamene akuceza, afunafuna mpata wakuti akambilane naye za Yehova.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Zithunzi zonse zionetsa Mboni zimene zikutumikila m’maiko amene nchito M’bale amene akufunsidwa mafunso na apolisi akukana kuulula zinthu zokhudza mpingo.