Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 34

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Utumiki Wanu Watha

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Utumiki Wanu Watha

“Mulungu si wosalungama woti angaiwale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.”—AHEB. 6:10.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-3. N’zinthu zina ziti zimene zingacititse kuti utumiki wanthawi zonse wa abale na alongo ena uthe?

M’BALE Robert na mkazi wake Mary Jo, anati: “Titatumikila mwacimwemwe kwa zaka 21 mu utumiki wa umishonale, makolo anga na makolo a mkazi wanga, onse anayamba kudwala. Tinali okondwela kuwasamalila. Komabe, cinatiŵaŵa kucoka ku dela limene tinali kulikonda kwambili.”

2 M’bale William na mkazi wake Terrie, anati: “Pamene tinazindikila kuti sitingayambenso utumiki wathu cifukwa ca matenda, tinalila. Mwayi wokatumikila Yehova ku dziko lina unathela pomwepo.”

3 M’bale Aleksey, anati: “Tinadziŵa kuti adani athu afuna kutseka ofesi yathu ya nthambi imene n’nali kutumikilako. Koma zitacitika, sitinakhulupilile. Cinatiŵaŵa kwambili kudziŵa kuti tifunika kucoka pa Beteli.”

4. Ni mafunso ati amene tikambilane m’nkhani ino?

4 Kuwonjezela pa zitsanzo zimenezi, pali abale na alongo masauzande ambili a mu utumiki wa nthawi zonse, kuphatikizapo a pa Beteli, amene utumiki wawo unatha. * Zimakhala zovuta kwa abale na alongo okhulupilika amenewa, ngati utumiki wawo umene anali kuukonda kwambili watha. Kodi n’ciani cingawathandize kujaila umoyo watsopano zinthu zikasintha? Nanga imwe mungawathandize bwanji? Mayankho pa mafunso amenewa angatithandize tonse pamene zinthu zasintha mu umoyo wathu.

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI NGATI UTUMIKI WANU WATHA

N’cifukwa ciani zingakhale zovuta kwa atumiki a nthawi zonse ngati utumiki wawo watha? (Onani ndime 5) *

5. Kodi kutha kwa utumiki kungatikhudze bwanji?

5 Kaya tikutumikila pa Beteli kapena mu utumiki wina wanthawi zonse, timayamba kukonda kwambili anthu amene tikhala nawo komanso malo amene tikutumikilako. Conco, ngati pa zifukwa zina tifunika kucoka ku delalo, cimatiŵaŵa kwambili mu mtima. Timawayewa kwambili abale na alongo amene tinali kutumikila nawo, ndiponso timawadela nkhawa, maka-maka ngati tacoka cifukwa ca cizunzo. (Mat. 10:23; 2 Akor. 11:28, 29) Kuwonjezela apo, nthawi zambili cimakhala covuta kujaila cikhalidwe ca ku dela latsopano limene tingapite. Zingakhale zovuta ngakhale titabwelela kwathu kumene tinacokela. M’bale Robert na mkazi wake Mary Jo, anati: “Tinafika poiŵala cikhalidwe cathu. Tinaiŵalanso ngakhale kulalikila m’citundu cathu. Popeza tinatumikila ku dziko lina kwa nthawi yaitali, tinayamba kucita cilendo m’dziko lathu.” Abale na alongo ena amene utumiki wawo watha, angakumane na mavuto azacuma mosayembekezeleka. Angayambe kuda nkhawa, ndiponso angafooke. N’ciani cingawathandize?

Kukhala pa ubale wolimba na Yehova komanso kum’dalila n’kofunika kwambili (Onani ndime 6-7) *

6. Tingacite ciani kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba na Yehova?

6 Khalanibe pa ubwenzi wolimba na Yehova. (Yak. 4:8) Tingacite bwanji zimenezi? Tingatelo mwa kum’khulupilila iye, cifukwa ni “Wakumva pemphelo.” (Sal. 65:2) Salimo 62:8 imati: “Mukhuthulileni za mumtima mwanu.” Yehova “angathe kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Inde, iye angaticitile zambili kuposa zimene tingam’pemphe. Angathetse mavuto athu m’njila imene sitinali kuyembekezela.

7. (a) N’ciani cingatithandize kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova? (b) Malinga na Aheberi 6:10-12, cidzacitika n’ciani ngati tipitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika?

7 Kuti mukhalebe pa ubwenzi wolimba na Yehova, muziŵelenga Baibo tsiku lililonse na kusinkha-sinkha zimene mwaŵelengazo. M’bale wina amene kale anali mmishonale, anati: “Pitilizani kucita kulambila kwa pabanja na kukonzekela misonkhano nthawi zonse, monga mmene munali kucitila utumiki wanu usanathe.” Komanso, mu mpingo wanu watsopano, pitilizani kucita zonse zimene mungathe polalikila uthenga wabwino. Yehova saiŵala anthu amene amapitiliza kum’tumikila mokhulupilika, ngakhale amene sakwanitsa kucita zambili monga mmene anali kucitila poyamba.—Ŵelengani Aheberi 6:10-12.

8. Kodi mawu a pa 1 Yohane 2:15-17 angatithandize bwanji kukhala na umoyo wosalila zambili?

8 Khalani na umoyo wosalila zambili. Musalole kuti nkhaŵa za m’dziko la Satanali ‘zikulepheletseni’ kupitiliza kutumikila Yehova. (Mat. 13:22) Nthawi zina, anthu osatumikila Yehova, anzanu, kapena acibululu anu angakuuzeni kuti mufunika kupeza ndalama zambili kuti mukhale na umoyo wabwino. Koma musamvele malangizo awo. (Ŵelengani 1 Yohane 2:15-17.) Khulupililani Yehova. Iye analonjeza kuti adzatipatsa zinthu zofunikila, “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” Adzatisamalila mwauzimu, mwakuthupi, ndiponso adzatilimbikitsa.—Aheb. 4:16; 13:5, 6.

9. Mogwilizana na Miyambo 22:3, 7, n’cifukwa ciani tifunika kupewa nkhongole zosafunikila? Nanga n’ciani cingatithandize kupanga cosankha mwanzelu?

9 Pewani nkhongole zosafunikila. (Ŵelengani Miyambo 22:3, 7.) Utumiki ukatha, mungafunike kusamuka. Koma kusamuka kumawonongetsa ndalama zambili, ndipo ngati sitingasamale kungatigwetsele mu nkhongole. Conco, pewani kugula zinthu zosafunikila kweni-kweni pa nkhongole. Pamene tili na nkhawa, mwina cifukwa cakuti wokondedwa wathu akudwala, cingakhale covuta kusankha mwanzelu kukula kwa nkhongole imene tingatenge. Zikakhala conco, ni bwino kukumbukila kuti “pemphelo ndi pembedzelo” zingatithandize kupanga cosankha mwanzelu. Yehova angayankhe mapemphelo athu mwa kutipatsa mtendele umene ‘udzateteza mitima yathu ndi maganizo athu.’ Izi zingatithandize kupanga zosankha mwanzelu.—Afil. 4:6, 7; 1 Pet. 5:7.

10. Tingacite ciani kuti tipeze mabwenzi atsopano?

10 Khalanibe pa ubwenzi wabwino na ena. Muzifotokozelako ena mmene mumvelela komanso zovuta zimene mukukumana nazo, maka-maka aja amene anakumanapo na zinthu monga zimene imwe mukumana nazo. Mukatelo, mudzalimbikitsidwa. (Mlal. 4:9, 10) Mabwenzi amene munapeza ku malo kumene munali kutumikila poyamba, adzakhalabe mabwenzi anu. Koma ku mpingo wanu watsopano, muyenelanso kupeza mabwenzi ena. Ndipo kumbukilani mfundo iyi: Kuti mupeze bwenzi, muyenelanso kukhala waubwenzi. Kodi mungacite ciani kuti mupeze mabwenzi atsopano? Muzifotokozelako ena zinthu zabwino zimene Yehova wakucitilani mu utumiki wanu. Ndipo muzionetsa kuti mumakondwela potumikila Yehova. Olo kuti ena mu mpingo wanu sangamvetsetse cifukwa cake mumaukonda kwambili utumiki wanthawi zonse, ena angakopeke na citsanzo canu n’kukhala mabwenzi anu abwino. Komabe, pewani kudzionetsela, kapena kusumika maganizo anu pa zinthu zofooketsa.

11. Mungacite ciani kuti banja lanu likhalebe lacimwemwe pamene utumiki wanu watha?

11 Ngati munasiya utumiki wanu cifukwa ca kudwala kwa mkazi kapena mwamuna wanu, pewani kumuimba mlandu. Kumbali ina, ngati ndimwe munali kudwala, musadziimbe mlandu poganiza kuti munalepheletsa mkazi kapena mwamuna wanu kutumikila. Kumbukilani kuti ndimwe “thupi limodzi,” ndipo munalonjeza pa maso pa Yehova kuti mudzasamalana zivute zitani. (Mat. 19:5, 6) Ngati munasiya utumiki cifukwa ca mimba yosakonzekela, muuzeni mwana wanu kuti mumam’konda kwambili kuposa utumiki umene munali nawo. Musamuimbe mlandu kuti iye ndiye anapangitsa kuti utumiki wanu uthe. M’malo mwake, m’tsimikizileni kuti mumamuona kuti ni “mphoto”yocokela kwa Mulungu. (Sal. 127:3-5) Kuwonjezela apo, muuzeni madalitso amene munapeza mu utumiki wanu. Kucita izi, kungam’sonkhezele mwanayo kukhala na colinga cokatumikila Yehova mu utumiki wanthawi zonse, monga mmene imwe munacitila.

MMENE TINGAWATHANDIZILE

12. (a) Kodi tingawathandize bwanji amene ali mu utumiki wanthawi zonse kupitiliza utumiki wawo? (b) Nanga tingawathandize bwanji kujaila mwamsanga umoyo wawo watsopano?

12 Abale na alongo m’mipingo yambili amayesetsa kuthandiza Akhristu amene ali mu utumiki wanthawi zonse, kuti apitilize utumiki wawo. Amacita izi mwa kuwalimbikitsa, kuwapatsa thandizo la ndalama kapena thandizo lina lakuthupi, kapenanso kuwathandiza kusamalila abululu awo amene ali ku nyumba. (Agal. 6:2) Ngati abale na alongo ena amene utumiki wawo unatha asamukila mu mpingo wanu, pewani kuganiza kuti utumikiwo unatha cifukwa cakuti analephela kucita zinazake, kapena kuti anacita colakwa cinacake. * M’malomwake, athandizeni kujaila mwamsanga umoyo wawo watsopano. Alandileni na manja aŵili. Ayamikileni cifukwa cotumikila mwakhama, olo kuti mwina lomba sacita zambili cifukwa ca thanzi lofooka. Adziŵeni bwino. Phunzilani zinthu kwa iwo, cifukwa amadziŵa zambili komanso anaphunzila zambili.

13. Tingawathandize bwanji abale na alongo amene utumiki wawo unatha?

13 Abale na alongo amene utumiki wawo unatha akangofika mu mpingo wanu, mungafunike kuwathandiza kupeza nyumba, nchito, mayendedwe, na zinthu zina zofunikila mu umoyo wa tsiku na tsiku. Angafunikenso kuuzidwa mmene zinthu zilili pa nkhani zina, monga ya kukhoma misonkho na kutenga inshuwalansi. Ndipo cacikulu cimene amafuna si kuwamvela cisoni, koma kumvetsetsa mmene zinthu zilili mu umoyo wawo. Iwo angakhale kuti akudwala kapena akudwazika wacibululu wawo. N’kuthekanso kuti anataikilidwa munthu amene anali kum’konda kwambili, ndipo akali na cisoni cacikulu. * Komanso akhoza kumayewa abale na alongo a ku malo kumene anali kutumikila poyamba. Izi zingapangitse kuti azikhala na cisoni, ngakhale kuti mwina sangacite kutiuza. Cifukwa ca zinthu ngati zimenezi, pangatenge nthawi kuti maganizo awo akhale m’malo.

14. Kodi ofalitsa a mu mpingo wina anam’thandiza bwanji mlongo amene anasamukila mu mpingo wawo?

14 Mungathandize Akhristu amenewa kujaila umoyo wawo watsopano mwa kulalikila nawo pamodzi, ndiponso mwa citsanzo canu cabwino. Mlongo wina amene anatumikila ku dziko lina kwa zaka zambili, anati: “Kumene n’nali kutumikila poyamba, n’nali kutsogoza maphunzilo a Baibo tsiku lililonse. Koma kumene nitumikila manje, poyamba zinali zovuta ngakhale kuŵelengela munthu Baibo mu ulaliki, kapena kumutambitsa vidiyo. Koma ofalitsa a kuno anali kunitenga popita ku maulendo awo obwelelako na ku maphunzilo. Kuona ofalitsa olimba mtima komanso okangalika amenewo akutsogoza maphunzilo a Baibo opita patsogolo, kunanithandiza kuti niziona anthu a m’gawo moyenelela. N’naphunzila moyambila makambilano ndi anthu m’gawo la mpingo wanga watsopano. Izi zinanithandiza kukhalanso na cimwemwe.”

MUSABWELELE M’MBUYO!

Pezani njila zowonjezela utumiki m’gawo la mpingo wanu (Onani ndime 15-16) *

15. Mungacite ciani kuti utumiki uzikuyendelani bwino olo pamene zinthu zasintha mu utumiki wanu?

15 Mungacitebe zambili ngakhale pamene zinthu zasintha mu utumiki wanu. Musaone kusintha kumeneku monga cizindikilo cakuti ndimwe wolephela kapena wosafunika. Yesetsani kuona mmene Yehova akukudalitsilani mu umoyo wanu, ndipo musaleke kulalikila. Tengelani citsanzo ca Akhristu okhulupilika a m’nthawi ya atumwi. Kulikonse kumene anapita, iwo anali ‘kulengeza uthenga wabwino wa mawu opatulika.’ (Mac. 8:1, 4) Ngati mupitiliza kugwila nchito yolalikila, pangakhale zotulukapo zabwino. Mwacitsanzo, apainiya ena atawathamangitsa m’dziko lina, anapita kukakhala ku dziko linanso lapafupi, kumene kunali gawo losoŵa la anthu okamba citundu cawo. Patapita miyezi yocepa, panapangidwa tumagulu twatsopano twa citundu cimeneco.

16. N’ciani cingakuthandizeni kukhalabe na cimwemwe ngati zinthu zasintha mu utumiki wanu?

16 Nehemiya anauza Ayuda kuti “cimwemwe cimene Yehova amapeleka” ndico cinali malo awo acitetezo, kapena kuti mphamvu zawo. (Neh. 8:10) Izi zionetsa kuti cimwemwe cathu ciyenela kudalila pa ubale wathu na Yehova, osati pa utumiki wathu, olo kuti timaukonda kwambili utumikiwo. Conco, khalanibe pa ubale wolimba na Yehova, ndipo pitilizani kum’dalila kuti akutsogoleleni, kukuthandizani, na kukupatsani nzelu. Kumbukilani kuti munayamba kukonda utumiki wanu wakale cifukwa munali kuyesetsa na mtima wanu wonse kuthandiza anthu. Mofananamo, mukaika mtima wanu wonse pa utumiki umene mucita pali pano, Yehova adzakuthandizani kuyambanso kuukonda.—Mlal. 7:10.

17. Kodi tiyenela kukumbukila ciani za utumiki umene tikucita pali pano?

17 Tifunika kukumbukila kuti kutumikila Yehova sikudzatha, koma zimene ticita pom’tumikila zimasintha-sintha. Ndipo utumiki umene ticita pali pano, mwina si umene tidzacita m’dziko latsopano. M’bale Aleksey, amene tam’chula kuciyambi, anakamba kuti amaona kuti kusintha kwa zinthu pa utumiki wake kukumuthandiza kukonzekela masinthidwe a kutsogolo. Iye anati: “Nakhala nikukhulupilila kuti Yehova ni weni-weni, komanso kuti dziko latsopano lili pafupi. Koma lomba m’pamene nili pa ubwenzi wolimba kwambili na Yehova, ndipo nimaona kuti dziko latsopano lili pafupi kwambili.” (Mac. 2:25) Mosasamala kanthu za utumiki umene tili nawo, tiyeni tipitilize kuyenda na Yehova. Iye sadzatisiya, koma adzatithandiza kupeza cimwemwe pamene ticita zonse zimene tingathe pom’tumikila, kulikonse kumene tingakhale.—Yes. 41:13.

NYIMBO 90 Tilimbikitsane Wina na Mnzake

^ ndime 5 Nthawi zina, abale na alongo amene ali mu utumiki wanthawi zonse wapadela, angafunike kusiya utumiki wawo, kapena angapatsidwe utumiki wina. M’nkhani ino, tikambilane mavuto amene iwo amakumana nawo, na zimene zingawathandize kujaila umoyo watsopano. Tikambilanenso zimene ena angacite kuti awalimbikitse na kuwathandiza, komanso mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize tonse pamene zinthu zasintha mu umoyo wathu.

^ ndime 4 Mofananamo, abale ambili a maudindo akafika pa msinkhu winawake, amasiyila abale acicepele maudindo awo. Onani nkhani yakuti, “Akhristu Acikulile—Yehova Amayamikila Kukhulupilika Kwanu,” mu Nsanja ya Mlonda ya September 2018, ndiponso yakuti “Khalanibe na Mtendele wa mu Mtima Olo Pamene Zinthu Zasintha,” mu Nsanja ya Mlonda ya October 2018.

^ ndime 12 Akulu a mu mpingo umene abale na alongowo anali kutumikila, ayenela kulemba mwamsanga kalata yodziŵikitsa mlendo, n’colinga cakuti iwo apitilize kutumikila monga apainiya, akulu kapena atumiki othandiza.

^ ndime 13 Onani Galamuka! ya Na. 3 2018, ya mutu wakuti: “Thandizo Kwa Ofedwa.”

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale na mkazi wake amene anali kutumikila ku dziko lina monga amishonale, akulailana na abale na alongo a mu mpingo wawo, ndipo nkhope zawo zioneka zacisoni.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Atabwelela ku dziko lawo, m’baleyo na mkazi wake akupemphela mosalekeza kwa Yehova kuti awathandize kupilila mavuto amene akumana nawo.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwa thandizo la Yehova, iwo akuyambanso utumiki wanthawi zonse. Poseŵenzetsa citundu cimene anaphunzila pamene anali amishonale, iwo akulalikila uthenga wabwino kwa anthu ocokela ku dziko lina m’gawo la mpingo wawo.