Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 40

Tizitumikira Yehova Mwakhama Kumapeto kwa ‘Masiku Otsirizawa’

Tizitumikira Yehova Mwakhama Kumapeto kwa ‘Masiku Otsirizawa’

“Khalani olimba, osasunthika, okhala ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.”​1 AKOR. 15:58.

NYIMBO NA. 58 Kufufuza Anthu Okonda Mtendere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi timadziwa bwanji kuti tikukhala “m’masiku otsiriza”?

KODI munabadwa pambuyo pa chaka cha 1914? Ngati zili choncho, moyo wanu wonse mwakhala ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Tim. 3:1) Tonsefe tamvapo za zinthu zimene Yesu ananeneratu kuti zidzachitika m’masiku otsirizawa. Zinthu zake ndi monga nkhondo, njala, zivomezi, miliri, kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo komanso kuzunzidwa kwa anthu a Yehova. (Mat. 24:3, 7-9, 12; Luka 21:10-12) Taonanso kuti anthu ali ndi makhalidwe amene mtumwi Paulo anafotokoza. (Onani bokosi lakuti “ Mmene Anthu Alili Masiku Ano.”) Choncho atumiki a Yehovafe sitikayikira ngakhale pang’ono kuti tikukhala “m’masiku otsiriza.”​—Mika 4:1.

2. Kodi tiyenera kudziwa mayankho a mafunso ati?

2 Popeza zaka zambiri zadutsa kuchokera mu 1914, n’zosakayikitsa kuti panopa tili kumapeto kwa ‘masiku otsiriza.’ Choncho tiyenera kudziwa mayankho a mafunso ofunika awa: Kodi n’chiyani chidzachitike kumapeto kwa ‘masiku otsiriza’? Nanga Yehova amafuna kuti tizichita chiyani panopa?

N’CHIYANI CHIDZACHITIKE KUMAPETO KWA ‘MASIKU OTSIRIZA’?

3. Malinga ndi ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:1-3, kodi maboma adzalengeza kuti chiyani?

3 Werengani 1 Atesalonika 5:1-3. Palembali, Paulo ananena za “tsiku la Yehova.” Apa ankanena za nthawi imene idzayambe ndi kuukiridwa kwa “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga, ndipo idzatha ndi nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16; 17:5) Koma tsikuli likadzangotsala pang’ono kuyamba, maboma adzalengeza kuti kuli “bata ndi mtendere.” (Mabaibulo ena amanena kuti: “Mtendere ndi Chitetezo.”) N’zoona kuti atsogoleri a mayiko nthawi zina amagwiritsa ntchito mawu ngati amenewa polimbikitsa mgwirizano wapadziko lonse. * Koma kulengeza za “bata ndi mtendere” kumene Baibulo limafotokoza kudzakhala kosiyana. Tikutero chifukwa chakuti akadzalengeza, anthu ambiri adzaganiza kuti maboma akwanitsadi kubweretsa mtendere ndi chitetezo padziko lonse. Koma zoona zake n’zakuti akadzangolengeza, “chisautso chachikulu” chidzayamba ndipo “chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika.”​—Mat. 24:21.

Tisadzapusitsidwe maboma akadzalengeza za “bata ndi mtendere” (Onani ndime 3-6) *

4. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene sitikudziwa zokhudza kulengezedwa kwa “bata ndi mtendere”? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene tikudziwa kale pa nkhaniyi?

4 Tikudziwa kale zinthu zina zokhudza kulengezedwa kwa “bata ndi mtendere.” Koma pali zinthu zina zimene sitikuzidziwa. Mwachitsanzo, sitikudziwa zimene zidzachititse kuti alengeze komanso mmene angalengezere. Sitikudziwanso ngati adzalengeze maulendo angapo kapena ulendo umodzi wokha. Kaya zidzakhala bwanji, chomwe tikudziwa n’chakuti: Sitiyenera kutengeka nazo n’kumaganiza kuti atsogoleri a mayiko angakwanitsedi kubweretsa mtendere padzikoli. Paja Baibulo limatiuza kuti chilengezo chimenechi chidzasonyeza kuti “tsiku la Yehova” latsala pang’ono kwambiri kuti liyambe.

5. Kodi lemba la 1 Atesalonika 5:4-6 lingatithandize bwanji kukonzekera “tsiku la Yehova”?

5 Werengani 1 Atesalonika 5:4-6. Paulo anatchula zinthu zina zimene zingatithandize kukonzekera “tsiku la Yehova.” Ananena kuti “tisapitirize kugona ngati mmene enawo akuchitira.” Koma ananena kuti “tikhalebe maso.” Mwachitsanzo, tiyenera kukhala maso kuti tisayambe kukopeka ndi nkhani zandale. Ngati tingayambe kuchita nawo zandale, ndiye kuti tikhoza kukhala “mbali ya dzikoli.” (Yoh. 15:19) Tizikumbukira kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungabweretse mtendere padziko lonse.

6. Kodi tiyenera kuthandiza anthu ena kuti achite chiyani? Perekani chifukwa.

6 Koma tiyeneranso kuthandiza anthu ena kuti akhale maso n’kumadziwa zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika padzikoli. Tisaiwale kuti chisautso chachikulu chikangoyamba, mwayi woti anthu ayambe kutumikira Yehova udzakhala utatha. N’chifukwa chake tiyenera kulalikira mwakhama. *

TIZILALIKIRABE MWAKHAMA

Tikamalalikira timasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungabweretse mtendere ndi chitetezo (Onani ndime 7-9)

7. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?

7 Yehova akufuna kuti tizilalikira mwakhama pa nthawi yochepa imene yatsalayi “tsiku” lake lisanafike. Choncho tiyenera kuonetsetsa kuti tikuchita ‘zambiri mu ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Yesu ananeneratu ntchito imene tidzagwire m’masiku otsirizawa. Pofotokoza zinthu zapadera zimene zidzachitike m’masiku otsiriza, ananenanso kuti: “M’mitundu yonse uthenga wabwino uyenera ulalikidwe choyamba.” (Maliko 13:4, 8, 10; Mat. 24:14) Tangoganizani, nthawi iliyonse imene mwalowa mu utumiki mumathandiza kukwaniritsa ulosi umenewu.

8. Kodi ntchito yolalikira za Ufumu ikuyenda bwanji?

8 Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti ntchito yolalikira ikuyenda bwino kwambiri? Chaka chilichonse anthu ambiri akumvetsera uthenga wabwino. Mwachitsanzo, chiwerengero cha ofalitsa chakhala chikuwonjezeka m’masiku otsirizawa. Mu 1914, panali ofalitsa 5,155 m’mayiko 43. Panopa pali ofalitsa oposa 8.5 miliyoni m’mayiko 240. Koma ntchito yathu sinathe. Choncho tiyenera kulalikirabe kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene ungathetse mavuto a anthu.​—Sal. 145:11-13.

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikirabe uthenga wa Ufumu?

9 Ntchito yathu yolalikira idzatha pokhapokha Yehova atanena kuti tamaliza. Sitikudziwa kuti kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti anthu aphunzire za Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu. (Yoh. 17:3) Koma chomwe tikudziwa n’chakuti anthu a “maganizo abwino” adakali ndi mwayi womvetsera uthenga wabwino mpaka pamene chisautso chachikulu chidzayambe. (Mac. 13:48) Ndiye kodi tingathandize bwanji anthu amenewa?

10. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti tiziphunzitsa anthu choonadi?

10 Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake kuti azitipatsa zinthu zonse zofunika kuti tiziphunzitsa choonadi. Mwachitsanzo, timaphunzira zambiri pamsonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Timaphunzira zimene tinganene mu utumiki pa ulendo woyamba komanso wobwereza. Timaphunziranso zimene tingachite pophunzitsa anthu Baibulo. Gulu la Yehova latipatsanso Zinthu Zophunzitsira. Zinthu zimenezi zimatithandiza . . .

  • kuyamba kukambirana ndi anthu,

  • kuthandiza anthu kuti achite chidwi,

  • kuthandiza anthu kuti afune kuphunzira zambiri,

  • kuphunzitsa anthu Baibulo komanso

  • kuthandiza anthu kuti apite pawebusaiti yathu kapena kufika kumisonkhano.

Koma kungokhala ndi zinthu zophunzitsirazi si kokwanira. Tiyenera kuzigwiritsa ntchito. * Mwachitsanzo, ngati mutasiyira munthu amene wasonyeza chidwi kapepala kapena magazini, akhoza kupitiriza kuwerenga mpaka pa nthawi imene mudzakumane nayenso. Ndi udindo wa Mkhristu aliyense kuti azichita zonse zimene angathe polalikira mwezi uliwonse.

11. N’chifukwa chiyani Phunziro la Baibulo la pa Intaneti laikidwa pawebusaiti yathu?

11 Chinthu china chosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu kuti aziphunzira choonadi ndi Phunziro la Baibulo la pa Intaneti lopezeka pa jw.org®. (Pitani pamene alemba kuti BIBLE TEACHINGS > ONLINE LESSONS.) Kodi n’chifukwa chiyani phunziroli laikidwa pawebusaiti yathu? Mwezi uliwonse, anthu masauzande ambiri amafufuza pa intaneti kuti aphunzire Baibulo. Ndiye phunziroli laikidwa pawebusaiti yathu n’cholinga choti lizithandiza anthu amenewa kuti aphunzire mfundo zoona za m’Mawu a Mulungu. Komanso anthu ena amene timakumana nawo sangavomere kuti aziphunzira nafe Baibulo. Zikatero, tingawasonyeze phunziroli pawebusaiti yathu kapena kuwatumizira linki yake. *

12. Kodi munthu angaphunzire zotani pa Phunziro la Baibulo la pa Intaneti?

12 Phunziro la Baibulo la pa Intaneti lili ndi nkhani zokhudza amene analemba Baibulo, anthu otchulidwa m’Baibulo komanso uthenga wa m’Baibulo. Nkhanizi zimayankha mafunso akuti:

  • Kodi Baibulo lingathandize bwanji munthu?

  • Kodi Yehova, Yesu komanso angelo ndi ndani?

  • N’chifukwa chiyani Mulungu analenga anthu?

  • N’chifukwa chiyani zinthu zoipa zimachitika?

Maphunziro ake amafotokozanso zimene Yehova adzachite kuti . . .

  • athetse mavuto ndi imfa,

  • aukitse akufa komanso kuti

  • Ufumu wa Mulungu ulowe m’malo mwa maboma a anthu.

13. Kodi Phunziro la Baibulo la pa Intaneti likulowa m’malo mwa kuphunzitsa anthu Baibulo? Fotokozani.

13 Phunziro la Baibulo la pa Intaneti silikulowa m’malo mwa kuphunzitsa anthu Baibulo. Paja Yesu watipatsa mwayi woti tizithandiza anthu kuti akhale ophunzira ake. Timakhulupirira kuti anthu akawerenga phunziro la Baibulo limeneli, adzakonda zimene angaphunzire ndipo angafune kuti aziphunzira zambiri. Akatero, mwina adzavomera kuti aziphunzira nafe Baibulo. Pamapeto pa phunziro lililonse, munthu amauzidwa kuti akhoza kupempha kuti munthu wina aziphunzira naye. Tsiku lililonse anthu pafupifupi 230 amapempha pawebusaiti yathu kuti aziphunzira Baibulo. Ndipotu kuphunzira ndi munthu wina n’kofunika kusiyana ndi kungophunzira pawekha.

TIZITHANDIZABE ANTHU KUTI AKHALE OPHUNZIRA A YESU

14. Malinga ndi malangizo a Yesu pa Mateyu 28:19, 20, kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

14 Werengani Mateyu 28:19, 20. Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti ‘akhale ophunzira komanso kuwaphunzitsa kuti asunge zinthu zonse zimene Yesu analamula.’ Tiyenera kuthandiza anthu kuti adziwe kufunika kokhala kumbali ya Yehova komanso Ufumu wake. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kulimbikitsa anthu kuti azitsatira mfundo zimene amaphunzira m’Baibulo, adzipereke kwa Yehova ndiponso abatizidwe. Zimenezi n’zimene zingawathandize kuti adzapulumuke pa tsiku la Yehova.​—1 Pet. 3:21.

15. Kodi tilibe nthawi yochita chiyani? Perekani chifukwa.

15 Tanena kale kuti nthawi imene yatsala ndi yochepa kwambiri. Choncho tilibe nthawi yoti tiziphunzira ndi anthu amene sakusonyeza kuti akufuna kukhala ophunzira a Khristu. (1 Akor. 9:26) Ntchito yathu ndi yofunika kuigwira mwamsanga. Ndipo pali anthu ambiri amene akufunika kumva uthenga wa Ufumu nthawi isanathe.

TIZIPEWA CHILICHONSE CHOKHUDZA ZIPEMBEDZO ZONYENGA

16. Malinga ndi Chivumbulutso 18:2, 4, 5, 8, kodi tonsefe tiyenera kuchita chiyani? (Onaninso mawu am’munsi.)

16 Werengani Chivumbulutso 18:2, 4, 5, 8. Mavesiwa akusonyeza zinthu zina zimene Yehova amafuna kuti atumiki ake azichita. Akhristu onse oona ayenera kupeweratu chilichonse chogwirizana ndi Babulo Wamkulu. Zingachitike kuti munthu asanayambe kuphunzira Baibulo anali m’chipembedzo chonyenga. Pa nthawiyo, mwina ankachita nawo zinthu zina kapena kupereka ndalama zothandiza chipembedzo chimenecho. Choncho asanavomerezedwe kuti akhale wofalitsa wosabatizidwa, ayenera kusiya chilichonse chokhudzana ndi zipembedzo zonyenga. Ayenera kulemba kalata kapena kudziwitsa chipembedzo chake chakale m’njira inayake kuti wachokamo. Ayeneranso kuchita zimenezi ndi gulu lililonse limene limagwirizana ndi Babulo Wamkulu. *

17. Kodi Mkhristu ayenera kupewa ntchito yotani? Perekani chifukwa.

17 Mkhristu aliyense ayenera kuonetsetsa kuti ntchito yake sikukhudzana ndi Babulo Wamkulu. (2 Akor. 6:14-17) Mwachitsanzo, sangalole kulembedwa ntchito ndi tchalitchi. Ngakhale Mkhristu amene walembedwa ntchito kwina, sangalole kuti azigwira ntchito yambiri kumalo amene amalimbikitsa kulambira konyenga. Ndipo ngati ntchito imene amagwira ndi yakeyake sangavomere kugwira ganyu kapena kontrakiti yokhudzana ndi Babulo Wamkulu. N’chifukwa chiyani tiyenera kupeweratu chonchi? Chifukwa chakuti sitifuna kuthandiza nawo pa ntchito kapena machimo a zipembedzo zomwe ndi zodetsedwa pamaso pa Yehova.​—Yes. 52:11. *

18. Kodi m’bale wina anatsatira bwanji mfundo za m’Baibulo pa nkhani ya ntchito?

18 M’mbuyomo, m’bale wina, yemwe ndi mkulu, anapemphedwa ndi munthu wina kuti akagwire kantchito kenakake patchalitchi cham’tauni imene m’baleyo ankakhala. Munthuyo ankadziwa kuti m’baleyo amakana kugwira ntchito kumatchalitchi. Koma pa nthawiyi, munthuyo anazingwa ndipo anapemphabe m’baleyo kuti amuthandize. Ngakhale zinali choncho, m’baleyo anatsatirabe mfundo za m’Baibulo n’kukana. Mlungu wotsatira, munyuzipepala munapezeka chithunzi cha kalipentala wina akukhomerera mtanda patchalitchicho. M’bale uja akanalolera, ndiye kuti chithunzi chake n’chimene chikanapezeka munyuzipepalayo. Zimenezitu zikanaipitsa kwambiri mbiri yake mumpingo. Ndiye mukuganiza kuti Yehova akanamva bwanji?

KODI TAPHUNZIRA CHIYANI?

19-20. (a) Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi? (b) Kodi tidzaphunzira chiyani munkhani yotsatira?

19 Mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo, chinthu chachikulu chimene chichitike posachedwapa n’chakuti maboma adzalengeza za “bata ndi mtendere.” Koma Yehova watithandiza kudziwa kuti maboma sangakwanitse kubweretsa mtendere weniweni. Kodi tiyenera kuchita chiyani zimenezi zisanachitike komanso chiwonongeko chodzidzimutsa chisanafike? Yehova amafuna kuti tizigwirabe mwakhama ntchito yolalikira n’kumayesetsa kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Tiyeneranso kupeweratu chilichonse chokhudza zipembedzo zonyenga. Choncho tiyenera kuchoka m’chipembedzo kapena gulu lililonse lokhudzana ndi Babulo Wamkulu komanso kupewa ntchito iliyonse yokhudzana ndi zipembedzozo.

20 Koma pali zinthu zina zimene zidzachitike kumapeto kwa ‘masiku otsirizawa.’ Palinso zinthu zina zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Kodi zinthu zake ndi ziti, nanga tingakonzekere bwanji zonse zimene zidzachitike posachedwapa? Tidzakambirana zimenezi munkhani yotsatira.

NYIMBO NA. 71 Ndife Gulu Lankhondo la Yehova

^ ndime 5 Posachedwapa maboma adzalengeza kuti akwanitsa kubweretsa “bata ndi mtendere.” Zimenezi zidzasonyeza kuti chisautso chachikulu chatsala pang’ono kwambiri kuyamba. Koma kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani panopa? Nkhaniyi iyankha funso limeneli.

^ ndime 3 Mwachitsanzo, bungwe la United Nations limanena pawebusaiti yake kuti “limathandiza kuti padzikoli pakhale mtendere ndi chitetezo.”

^ ndime 23 Kuti mudziwe mmene mungagwiritsire ntchito Zinthu Zophunzitsira, onani nkhani yakuti “Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi” mu Nsanja ya Olonda ya October 2018.

^ ndime 11 Panopa phunziroli likupezeka m’Chingelezi ndi Chipwitikizi. Koma liyamba kupezeka m’zilankhulo zina.

^ ndime 16 Tiyeneranso kupewa magulu monga a achinyamata kapena a masewera amene amakhudzana ndi zipembedzo zonyenga. Mwachitsanzo, tiyenera kupewa kukhala m’mabungwe a achinyamata monga a YMCA (Young Men’s Christian Association) kapena YWCA (Young Women’s Christian Association) omwe amanena kuti zochita zawo si zachipembedzo kwenikweni. Koma zoona zake n’zakuti mabungwe amenewa anayambitsidwa ndi zipembedzo komanso amalimbikitsa mfundo zachipembedzo.

^ ndime 17 Kuti mumvetse zimene Malemba amanena pa nkhani yogwira ntchito zokhudza chipembedzo, onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999.

^ ndime 83 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Anthu amene ali kulesitilanti akudabwa kuti pa TV akulengeza za “bata ndi mtendere.” Kulinso banja la Mboni limene silikutengeka nazo.