Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 40

Khalanibe Acangu mu Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”

Khalanibe Acangu mu Ndime Ino Yothela ya “Masiku Otsiliza”

Khalani olimba, osasunthika, okhala ndi zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye.”​—1 AKOR. 15:58.

NYIMBO 58 Kusakila Anthu Okonda Mtendele

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi timadziŵa bwanji kuti tilidi ‘m’masiku otsiliza’?

KODI munabadwa caka ca 1914 citapita? Ngati n’conco, ndiye kuti kwa moyo wanu wonse mwakhala muli ‘m’masiku otsiliza’ a nthawi ino. (2 Tim. 3:1) Tonsefe tinamvelako zinthu zimene Yesu anakambilatu kuti zidzacitika m’masiku ano otsiliza. Zinthu zimenezi ziphatikizapo nkhondo, njala, zivomezi, milili, kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, komanso kuzunzidwa kwa anthu a Yehova. (Mat. 24:3, 7-9, 12; Luka 21:10-12) Taonanso kuti anthu ali na makhalidwe oipa amene mtumwi Paulo anakambilatu. (Onani kabokosi kakuti “ Makhalidwe a Anthu Masiku Ano.”) Ife Mboni za Yehova, timakhulupilila kuti tikukhaladi “m’masiku otsiliza.”—Mika 4:1.

2. Kodi tifunika kupeza mayankho pa mafunso ati?

2 Popeza kuti papita nthawi yaitali kucokela mu 1914, n’zoonekelatu kuti tsopano tikukhala mu ndime yothela ya “masiku otsiliza.” Pokhala kuti mapeto lomba ali pafupi kwambili, tifunika kudziŵa mayankho pa mafunso ena ofunika kwambili monga akuti: Kodi padzacitika zotani pa mapeto a “masiku otsiliza”? Nanga Yehova afuna kuti tizicita ciani poyembekezela zocitika zimenezo?

N’CIANI CIDZACITIKA PA MAPETO A “MASIKU OTSILIZA”?

3. Malinga na ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:1-3, ni cilengezo cotani cimene atsogoleli a maiko adzalengeza?

3 Ŵelengani 1 Atesalonika 5:1-3. Kodi “tsiku la Yehova” limene Paulo anachula pa lembali n’ciani? Tsiku limeneli ni nyengo ya nthawi yoyambila pa kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu,” ufumu wa pa dziko lonse wa cipembedzo conama, mpaka pa Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16; 17:5) “Tsiku” limeneli likadzatsala pang’ono kuyamba, atsogoleli a maiko adzalengeza “Bata ndi mtendele.” (Ma Baibo ena amati: “Bata ndi citetezo.”) Olamulila a maiko, nthawi zina amaseŵenzetsa mawu amenewa pamene akambilana za kukhazikitsa mtendele pakati pa maiko. * Koma cilengezo ca “bata ndi mtendele” cimene Baibo imakamba cidzakhala capadela. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cilengezoco cikadzapelekedwa, ambili adzaganiza kuti atsogoleli a maiko akwanitsa kupangitsa dzikoli kukhala malo abwino na otetezeka. Koma nthawi yomweyo, “cisautso cacikulu” cidzayamba, ndipo “ciwonongeko codzidzimutsa” cidzafika pa iwo.—Mat. 24:21.

Musakapusitsidwe na cilengezo cabodza ca “bata ndi mtendele” cimene atsogoleli a maiko adzalengeza (Onani ndime 3-6) *

4. (a) Ni zinthu ziti zokhudza cilengezo ca “bata ndi mtendele” zimene sitidziŵa pali pano? (b) Nanga ni ziti zimene tidziŵa?

4 Pali zinthu zina zimene tidziŵa zokhudza cilengezo ca “bata ndi mtendele.” Koma palinso zina zimene sitidziŵa. Mwacitsanzo, sitidziŵa cimene cidzapangitsa atsogoleli a maiko kulengeza zimenezi. Sitidziŵanso mmene adzalengezela. Komanso, sitidziŵa kuti kaya adzalengeza kangapo kapena kamodzi cabe. Mulimonse mmene zidzakhalila, cimene tidziŵa n’cakuti, pa nthawiyo sitidzafunika kupusitsidwa n’kuyamba kuganiza kuti atsogoleli a dziko angakwanitse kukhazikitsa mtendele pa dziko lonse lapansi. M’malomwake, cilengezo ca bata ndi mtendele ni cocitika cimene Baibo imatiuza kuti tiyenela kukhala naco chelu kwambili. Cidzakhala cizindikilo cakuti “tsiku la Yehova” langotsala pang’ono kuyamba.

5. Kodi 1 Atesalonika 5:4-6 imati tiyenela kucita ciani pokonzekela “tsiku la Yehova”?

5 Ŵelengani 1 Atesalonika 5:4-6. Pa lembali, Paulo anafotokoza zimene tiyenela kucita pokonzekela “tsiku la Yehova.” Anakamba kuti sitiyenela “kugona ngati mmene enawo akucitila.” Koma tiyenela ‘kukhalabe maso’ komanso achelu. Mwacitsanzo, tifunika kukhala maso kuti tipewe kutengako mbali m’mikangano ya ndale. Ngati titengako mbali, ndiye kuti tili “mbali ya dziko.” (Yoh. 15:19) Tidziŵa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzabweletsa mtendele padziko lonse lapansi.

6. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tithandize ena? Nanga n’cifukwa ciani?

6 Kuonjezela pa kukhalabe maso, tiyenela kuthandiza ena kuti naonso akhale maso. Tiyenela kuwathandiza kudziŵa zimene Baibo inakamba kuti zidzacitika pa dzikoli. Tiyenela kucita zimenezi pali pano, cifukwa cisautso cacikulu cikadzangoyamba, nthawi yakuti anthu ayambe kutumikila Yehova idzakhala itatha. Ndiye cifukwa cake nchito yathu yolalikila iyenela kucitidwa mwamsanga. *

KHALANIBE ACANGU PA NCHITO YOLALIKILA

Masiku ano, tikamagwila nchito yolalikila, timaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzapangitsa dziko kukhala malo abwino na otetezeka (Onani ndime 7-9)

7. Kodi Yehova afuna kuti tizicita ciani pali pano?

7 Mu nthawi yocepa imene yatsala kuti “tsiku” la Yehova liyambe, Yehova akufuna kuti tigwile nchito yolalikila mwacangu. Tifunika kuonetsetsa kuti ‘tikukhala ndi zocita zambili . . . mu nchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Yesu anakambilatu nchito imene tiyenela kucita. Pamene iye anali kufotokoza zinthu zapadela zimene zidzacitika m’masiku otsiliza, anakambanso kuti: “Komanso, m’mitundu yonse uthenga wabwino uyenela ulalikidwe coyamba.” (Maliko 13:4, 8, 10; Mat. 24:14) Ganizilani cabe, nthawi iliyonse tikapita mu ulaliki, timatengako mbali pokwanilitsa ulosi wa m’Baibo umenewu!

8. Kodi nchito yolalikila za Ufumu ikupitabe patsogolo motani?

8 Kodi nchito yolalikila za Ufumu yapita patsogolo motani? Caka na caka, nchito yolalikila ikupitila-pitila patsogolo. Mwacitsanzo, ganizilani cabe za kuwonjezeka kwa ciŵelengelo ca ofalitsa Ufumu pa dziko lonse m’masiku ano otsiliza. Mu 1914, panali ofalitsa 5,155 m’maiko 43. Koma tsopano, pali ofalitsa oposa 8.5 miliyoni m’maiko 240! Tifunika kupitiliza kuuza anthu kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzathetsa mavuto onse pa dzikoli.—Sal. 145:11-13.

9. N’cifukwa ciani tifunika kupitiliza kulalikila uthenga wa Ufumu?

9 Nchito yathu yolalikila idzapitilizabe kucitika mpaka pamene Yehova adzatiuze kuti kwatha. Kodi kwatsala nthawi yaitali bwanji yothandiza anthu kudziŵa Yehova Mulungu na Yesu Khristu? (Yoh. 17:3) Sitidziŵa nthawi yeni-yeni. Koma cimene tidziŵa n’cakuti cisautso cacikulu cisanayambe, anthu amene ali na ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha’ ali na mwayi wolabadila uthenga wabwino na kusankha kutumikila Yehova. (Mac. 13:48) Kodi tingawathandize bwanji anthu amenewa nthawi isanathe?

10. Kodi Yehova akutithandiza bwanji kuti tikwanitse kuphunzitsa anthu coonadi?

10 Kupitila m’gulu lake, Yehova akutipatsa zonse zofunikila kuti tiphunzitse anthu coonadi. Mwacitsanzo, wiki iliyonse pa misonkhano ya mkati mwa wiki, timaphunzitsidwa mmene tingagwilile nchitoyi. Misonkhanoyi imatithandiza kudziŵa mmene tingakambile na anthu pa ulendo woyamba na pa maulendo obwelelako. Imatiphunzitsanso mmene tingatsogozele maphunzilo a Baibo. Gulu la Yehova latipatsanso Zida Zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu. Zida zimenezi zimatithandiza . . .

  • kuyambitsa makambilano,

  • kudzutsa cidwi ca anthu,

  • kusonkhezela anthu kuti aphunzile zambili za m’Baibo,

  • kuphunzitsa coonadi anthu amene timaphunzila nawo Baibo, komanso

  • kudziŵitsa anthu acidwi za webusaiti yathu na kuwaitanila ku Nyumba ya Ufumu.

Koma kungokhala na zida zimenezi si kokwanila. Tifunika kuziseŵenzetsa. * Mwacitsanzo, ngati pambuyo polalikila munthu wacidwi, mwamusiyila kathirakiti kapena magazini, iye angapitilize kuŵelenga cofalitsaco mpaka pamene mukakambilanenso naye. Ni udindo wa aliyense wa ife kugwila nchito yolalikila za Ufumu mwacangu mwezi ulionse.

11. Kodi colinga ca mbali yakuti Maphunzilo a Baibo a pa Intaneti n’ciani?

11 Palinso citsanzo cina cimene cionetsa mmene Yehova akuthandizila anthu kuphunzila coonadi. Ganizilani cabe za mbali ya pa jw.org® yakuti, Maphunzilo a Baibo a pa Intaneti. (Pitani ku Cizungu pa BIBLE TEACHINGS > ONLINE LESSONS.) Kodi colinga ca maphunzilo amenewa n’ciani? Mwezi uliwonse, anthu masauzande ambili pa dziko lonse amafufuza pa Intaneti kuti aphunzile zambili za Baibo. Conco, maphunzilo a Baibo amenewa a pa jw.org angalimbikitse anthuwo kuyamba kuphunzila coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Anthu ena amene timawalalikila, amawaya-waya kuti tiyambe kuphunzila nawo Baibo. Anthu otelo mungawaonetse mbali imeneyi pa webusaiti yathu, kapena mungawatumizile linki yopitila pa mbali imeneyi. Ngati n’zotheka, mungawaonetse mbaliyi m’citundu cimene amamvetsetsa. *

12. Kodi Maphunzilo a Baibo a pa Intaneti angathandize munthu kudziŵa ciani?

12 Maphunzilo a Baibo amenewa a pa webusaiti yathu, amafotokoza nkhani izi: “Baibo na Mlembi Wake,” “Anthu Ochulidwa Kwambili M’Baibo,” na “Uthenga wa M’Baibo Wopatsa Ciyembekezo.” Maphunzilowa angathandize munthu kudziŵa:

  • Mmene Baibo imathandizila

  • kuti Yehova, Yesu, na angelo n’ndani

  • Cifukwa cake Mulungu analenga anthu

  • Cifukwa cake pali mavuto na kuipa

Maphunzilo a Baibo amenewa afotokozanso kuti Yehova . . .

  • adzathetsa mavuto na imfa,

  • adzaukitsa akufa, komanso

  • adzathetsa maboma a anthu, omwe ni olephela, na kubweletsa Ufumu wa Mulungu.

13. Kodi mbali ya maphunzilo a Baibo a pa Intaneti inaloŵa m’malo makonzedwe otsogoza maphunzilo a Baibo a pa nyumba? Fotokozani.

13 Mbali ya maphunzilo a Baibo a pa Intaneti, siinaloŵe m’malo makonzedwe otsogoza maphunzilo a Baibo a pa nyumba. Yesu anatipatsa mwayi wogwila nchito yopanga ophunzila. Colinga ca maphunzilo a pa intaneti ni kuthandiza anthu acidwi amene angaŵelenge mbali imeneyi. Tili na cikhulupililo cakuti anthu acidwi adzakondwela na zimene adzaŵelenga, ndipo adzafuna kuphunzila zambili. Mwina ena mwa iwo angalole kuyamba kuphunzila nafe Baibo. Kumapeto kwa phunzilo lililonse, kuli mawu olimbikitsa woŵelengayo kutumiza fomu ya pa intaneti yopempha munthu woti aziphunzila naye Baibo. Ndipo kupitila pa webusaiti yathu, pa avaleji anthu oposa 230 padziko lonse, amapempha phunzilo la Baibo tsiku lililonse! Kuphunzila Baibo mwacindunji na mmodzi wa Mboni za Yehova n’kofunika kwambili.

PITILIZANI KUYESETSA KUPANGA OPHUNZILA

14. Malinga na malangizo a Yesu pa Mateyu 28:19, 20, kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

14 Ŵelengani Mateyu 28:19, 20. Pamene titsogoza maphunzilo a Baibo, tiyenela kuyesetsa kuwathandiza kuti akhale “ophunzila,” komanso ‘kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene [Yesu] anatilamula.’ Tiyenela kuwathandiza kuona kufunika kosankha kutumikila Yehova na kucilikiza Ufumu wake. Izi zitanthauza kuwathandiza kukonda coonadi mwa kuseŵenzetsa zimene aphunzila, kudzipatulila kwa Yehova, na kubatizika. Popanda kucita zimenezi, iwo sangapulumuke tsiku la Yehova.—1 Pet. 3:21.

15. Kodi sitifuna kutaya nthawi na ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

15 Monga takambila kale, kwatsala nthawi yocepa kwambili kuti mapeto a nthawi ino afike. Pa cifukwa cimeneci, sitifuna kutaya nthawi mwa kupitiliza kuphunzila ndi anthu amene safuna kusintha kuti akhale ophunzila a Khristu. (1 Akor. 9:26) Nchito yathu ni yofunika kuigwila mwamsanga! Pakali anthu ambili amene afunika kumvela uthenga wa Ufumu mapeto asanafike.

PEWANI CILICONSE COGWILIZANA NA CIPEMBEDZO CONAMA

16. Malinga na Chivumbulutso 18:2, 4, 5, 8, kodi tonse tifunika kucita ciani? (Onaninso mawu amunsi.)

16 Ŵelengani Chivumbulutso 18:2, 4, 5, 8. Mavesi amenewa achula cinthu cina cimene Yehova amafuna kuti atumiki ake azicita. Iye amafuna kuti Akhristu onse oona azipewa ciliconse cogwilizana na Babulo Wamkulu. Asanaphunzile coonadi, ophunzila Baibo ena anali mamembala a cipembedzo conama. Anali kupezeka ku misonkhano ya cipembedzoco na kutengako mbali pa zocitika zina za m’cipembedzoco. N’kuthekanso kuti anali kupeleka ndalama zocilikizila cipembedzo cimeneco. Conco, wophunzila Baibo asanavomelezedwe kuti akhale wofalitsa wosabatizika, afunika kuthetselatu mgwilizano uliwonse na cipembedzo conama. Angacite izi mwa kulemba kalata yolaila ku chechi kwawo, kapena kufafanizitsa dzina lake ku chechiyo, komanso ku bungwe lililonse logwilizana na Babulo Wamkulu limene analimo. *

17. Ni nchito ziti zimene Mkhristu sangalole kugwila? Nanga n’cifukwa ciani?

17 Mkhristu woona afunika kuonetsetsa kuti nchito imene amaseŵenza si yogwilizana na Babulo Wamkulu. (2 Akor. 6:14-17) Mwacitsanzo, sangalole kulembedwa nchito na cipembedzo. Ndipo ngati Mkhristu analembedwa nchito na kampani, sangalole kukagwila nchito yaikulu pa malo olambilila a cipembedzo conama. Cinanso, Mkhristu amene ali na bizinesi yake, sangasakile nchito kapena kulola kugwila nchito yocilikiza mbali iliyonse ya Babulo Wamkulu. N’cifukwa ciani nkhani yopewa kucilikiza Babulo Wamkulu sitiitenga mopepuka? Cifukwa sitifuna kugaŵanamo mu nchito zoipa komanso macimo a zipembedzo zonama, zimene n’zodetsedwa pa maso pa Mulungu.—Yes. 52:11. *

18. Kodi m’bale wina anaonetsa bwanji kuti sanafune kunyalanyaza mfundo za m’Baibo pa nkhani yosankha nchito?

18 Zaka zapitazo, m’bale wina amene ni mkulu ndipo anali kudziseŵenzela, anapemphedwa na munthu wina kuti akagwile nchito yocepa ya ukalipentala pa chechi ina yake m’tauni yawo. Munthuyo anali kudziŵa kuti m’baleyo nthawi zonse anali kukana kuti sangaseŵenze pa chechi. Koma pa nthawiyo, iye anasoŵelatu munthu woti n’kukagwila nchitoyo. Ngakhale zinali conco, m’baleyo anakanabe cifukwa cotsatila mfundo za m’Baibo. Wiki yotsatila, m’nyuzipepala ya m’tauniyo munatuluka cithunzi ca kalipentala winawake amene anali kukhoma mtanda m’chechiyo. M’baleyo akananyalanyaza mfundo za m’Baibo na kulola kukagwila nchitoyo, sembe iye ndiye anawonekela pa cithunzipo. Ganizilani cabe mmene zimenezo zikanakhudzila mbili yake pakati pa Akhristu anzake! Ganizilaninso mmene Yehova akanamvelela.

KODI TAPHUNZILA CIANI?

19-20. (a) Kodi taphunzila ciani? (b) Nanga tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila?

19 Malinga na ulosi wa m’Baibo, cinthu capadela cimene tikuyembekezela kucitika pa dziko lapansi posacedwapa, ni kulengezedwa kwa “bata ndi mtendele.” Ndipo atsogoleli a maiko ndiwo adzalengeza zimenezi. Cifukwa cakuti taphunzitsidwa na Yehova, tidziŵa kuti atsogoleli a maiko sadzakwanitsa kubweletsa mtendele weni-weni na wosatha. Kodi tiyenela kucita ciani cilengezo cimeneci cisanapelekedwe, komanso ciwonongeko codzidzimutsa cisanafike? Yehova afuna kuti tizigwila nchito yolalikila uthenga wa Ufumu mwacangu, na kuyesetsa kupanga ophunzila. Panthawi imodzi-modzi, tiyenela kupewelatu kucilikiza zipembedzo zonama mwa njila ina iliyonse. Izi ziphatikizapo kukafafanizitsa dzina lathu ku mabungwe ogwilizana na cipembedzo conama, komanso kupewa kugwila nchito iliyonse yocilikiza Babulo Wamkulu.

20 Palinso zocitika zina zapadela zimene zidzacitika m’ndime yothela ya “masiku otsiliza.” Komanso pali zinthu zina zimene Yehova afuna kuti tizicita poyembekezela nthawiyo. Kodi zinthu zimenezo n’ziti? Nanga tingakonzekele bwanji pamene tikuyembekezela zonse zimene zicitike posacedwapa? Tidzaphunzila zimenezi m’nkhani yotsatila.

NYIMBO 71 Ndife Asilikali a Yehova!

^ ndime 5 Posacedwa, atsogoleli a maiko adzalengeza kuti akwanitsa kukhazikitsa “bata ndi mtendele” pa dziko. Cilengezo cimeneco cidzakhala cizindikilo cakuti cisautso cacikulu cangotsala pang’ono kuyamba. Koma kodi Yehova afuna kuti tizicita ciani nthawi imeneyo isanafike? Nkhani ino, idzatithandiza kupeza yankho.

^ ndime 3 Mwacitsanzo, pa webusaiti yawo, a United Nations amakamba kuti colinga ca bungweli ni “kusungitsa bata na mtendele pakati pa maiko.”

^ ndime 6 Onani nkhani ya m’Magazini ino, ya mutu wakuti, “Mulungu Asanapeleke Ciweluzo—Kodi Nthawi Zonse Amacenjeza Anthu Mokwanila?

^ ndime 10 Kuti mudziŵe moseŵenzetsela “Zida Zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu,” onani nkhani yakuti “Kuphunzitsa Coonadi,” mu Nsanja ya Mlonda ya October 2018.

^ ndime 11 Mbali imeneyi ya pa jw.org, pali pano ipezeka cabe m’Cizungu na m’Cipwitikizi, koma idzayamba kupezekanso m’vitundu vina.

^ ndime 16 Tifunikanso kupewa kuseŵenzetsa malo a zosangalatsa ocilikizidwa na cipembedzo conama, kapena kugwilizana na mabungwe monga ma youth camps, amene ni ogwilizana na cipembedzo conama. Mabungwe amenewo angaphatikizepo la YMCA (Young Men’s Christian Association), komanso la YWCA (Young Women’s Christian Association). Anthu a m’mabungwe amenewa angakambe kuti zocita zawo si zacipembedzo. Koma zoona zake n’zakuti, mabungwewa amalimbikitsa mfundo na zolinga zacipembedzo.

^ ndime 17 Kuti mumvetsetse malangizo na mfundo za m’Malemba pa nkhani ya kugwila nchito yokhudzana na cipembedzo conama, onani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999.

^ ndime 83 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pa Nkhani Zongocitika Kumene pa TV papelekedwa cilengezo ca “bata ndi mtendele,” ndipo makasitomala mu lesitilanti acita cidwi kwambili na cilengezo cimeneco. M’bale na mkazi wake akupumula mu lesitilantiyo pamene ali mu ulaliki, ndipo sakupusitsidwa na cilengezo cimeneco.