Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 44

Pezani Anzanu Apamtima Mapeto Asanafike

Pezani Anzanu Apamtima Mapeto Asanafike

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”​—MIY. 17:17.

NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

Tidzafunika kukhala ndi anzathu apamtima pa nthawi ya “chisautso chachikulu” (Onani ndime 2) *

1-2. Mogwirizana ndi 1 Petulo 4:7, 8, kodi n’chiyani chingatithandize zinthu zikavuta?

PAMENE tikuyandikira kwambiri mapeto a “masiku otsiriza,” tikhoza kukumana ndi mavuto aakulu. (2 Tim. 3:1) Mwachitsanzo, chisankho chitachitika m’dziko lina lakumadzulo kwa Africa, ziwawa zinayambika. Kwa miyezi yoposa 6, abale ndi alongo athu sankatha kuyenda momasuka chifukwa anthu ankamenyana m’dera limene ankakhala. Kodi n’chiyani chinawathandiza pa nthawiyi? Ena anakakhala m’nyumba za abale amene m’dera lawo zinthu zinali bwinoko. M’bale wina ananena kuti: “Pa nthawi yovutayi, ndinayamikira kwambiri kukhala ndi anzanga apamtima chifukwa tinkalimbikitsana.”

2 “Chisautso chachikulu” chikadzayamba, tidzasangalala kwambiri kuti tili ndi anzathu abwino omwe amatikonda. (Chiv. 7:14) Choncho tiyenera kuyamba panopa kupeza anzathu apamtima. (Werengani 1 Petulo 4:7, 8.) Tingaphunzire zambiri pa nkhani ya Yeremiya amene anathandizidwa ndi anzake kuti apulumuke Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa. * Kodi tingamutsanzire bwanji?

ZIMENE TINGAPHUNZIRE PA NKHANI YA YEREMIYA

3. (a) N’chiyani chikanachititsa kuti Yeremiya asamacheze ndi anthu? (b) Kodi Yeremiya ankauza Baruki zinthu zotani, nanga zotsatira zake zinali zotani?

3 Kwa zaka zosachepera 40, Yeremiya ankakhala pafupi ndi anthu osakhulupirika ndipo n’kutheka kuti ena anali achibale ake ochokera kwawo ku Anatoti. (Yer. 11:21; 12:6) Koma anapezabe anthu ocheza nawo. Iye ankauza mlembi wake wokhulupirika dzina lake Baruki zamumtima mwake ndipo zinalembedwa kuti ifenso tizidziwe. (Yer. 8:21; 9:1; 20:14-18; 45:1) Pamene Baruki ankalemba zimene zinkachitikira Yeremiya, anthu awiriwa ayenera kuti anayamba kukondana komanso kulemekezana kwambiri.​—Yer. 20:1, 2; 26:7-11.

4. Kodi Yehova anapempha Yeremiya kuti achite chiyani, nanga ntchitoyi inathandiza bwanji kuti Yeremiya ndi Baruki azigwirizana kwambiri?

4 Kwa zaka zambiri, Yeremiya ankachenjeza Aisiraeli molimba mtima zimene zidzachitikire Yerusalemu. (Yer. 25:3) Pofuna kuthandiza anthu kuti alape, Yehova anapempha Yeremiya kuti alembe machenjezowo mumpukutu. (Yer. 36:1-4) Yeremiya ndi Baruki anagwira limodzi ntchito imene Mulungu anawapatsayi ndipo n’kutheka kuti inatenga miyezi yambiri. Pa nthawiyo, ayenera kuti ankakambirana zinthu zolimbitsa chikhulupiriro chawo.

5. Kodi Baruki anasonyeza bwanji kuti anali mnzake wapamtima wa Yeremiya?

5 Iwo atamaliza kulemba machenjezo mumpukutuwu, Yeremiya anafunika kudalira Baruki kuti akapereke uthengawu. (Yer. 36:5, 6) Baruki anachita zimenezi molimba mtima ngakhale kuti zinaika moyo wake pa ngozi. Yeremiya ayenera kuti ananyadira kwambiri pamene Baruki anapita kubwalo la kachisi kukapereka uthengawu. (Yer. 36:8-10) Akalonga a ku Yuda atamva zimene Baruki anachita anamulamula kuti awawerengerenso mpukutuwo mokweza. (Yer. 36:14, 15) Kenako akalongawo anasankha zokauza Mfumu Yehoyakimu zimene Yeremiya ananena. Koma anasonyeza kuti ankamuganizira Baruki pomuuza kuti: “Pita, iweyo ndi Yeremiya mukabisale ndipo munthu aliyense asadziwe kumene mwapita.” (Yer. 36:16-19) Awatu anali malangizo abwino.

6. Kodi Yeremiya ndi Baruki anachita chiyani ataopsezedwa?

6 Mfumu Yehoyakimu anakwiya kwambiri atamva uthengawo moti anawotcha mpukutuwo n’kulamula kuti Yeremiya ndi Baruki amangidwe. Koma Yeremiya sanachite mantha. Iye anangotenga mpukutu wina n’kupatsa Baruki ndipo anayamba kumuuzanso uthenga wa Yehova woti alembe. Ndiye Baruki analemba “mawu onse amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha.”​—Yer. 36:26-28, 32.

7. Kodi mwina n’chiyani chinachitika pamene Yeremiya ndi Baruki ankagwira ntchito limodzi?

7 Anthu amene apirira mavuto limodzi, nthawi zambiri amayamba kugwirizana. N’kutheka kuti zimenezi n’zimene zinachitika pamene Yeremiya ndi Baruki ankagwira ntchito limodzi yolembanso mpukutu umene Mfumu Yehoyakimu anawotcha. Aliyense ayenera kuti ankayamikira makhalidwe abwino a mnzake. Kodi chitsanzo cha anthu okhulupirikawa chingatithandize bwanji?

MUZIUZANA ZAMUMTIMA

8. N’chiyani chingatilepheretse kupeza anzathu apamtima, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsabe?

8 Mwina timaopa kuuza anthu zamumtima mwathu chifukwa choti munthu wina anatikhumudwitsapo m’mbuyomo. (Miy. 18:19, 24) Apo ayi, timaona kuti sitingapeze anzathu apamtima chifukwa choti timasowa nthawi. Komatu n’zotheka kupeza anzathu. Ngati tikufuna kuti abale athu adzatithandize pa nthawi ya mayesero, tiyenera kusonyeza panopa kuti timawadalira powauza zimene zili mumtima mwathu. Zimenezi zimathandiza kwambiri kuti anthu ayambe kugwirizana.​—1 Pet. 1:22.

9. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankadalira anzake? (b) Kodi kukambirana momasuka ndi anthu kungathandize bwanji kuti muzigwirizana nawo? Perekani chitsanzo.

9 Yesu anasonyeza kuti ankadalira anzake powauza zimene zinali mumtima mwake. (Yoh. 15:15) Tingamutsanzire pofotokozera anzathu zimene zatisangalatsa, zimene zikutidetsa nkhawa komanso zimene zatikhumudwitsa. Munthu wina akamakufotokozerani zinthu, muzimvetsera mwachidwi. Mukhoza kuzindikira kuti zambiri zimene amaganiza, zimene zili mumtima mwake komanso zolinga zake zikufanana ndi zanu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wazaka za m’ma 20 dzina lake Cindy. Iye anayamba kugwirizana ndi mpainiya wina wazaka za m’ma 60 dzina lake Marie-Louise. Alongo awiriwa amalalikira limodzi Lachinayi lililonse m’mawa ndipo amakambirana momasuka nkhani zosiyanasiyana. Cindy anati: “Ndimasangalala kukambirana ndi anzanga momasuka chifukwa zimandithandiza kuti ndiwadziwe bwino.” Anthu amagwirizana kwambiri ngati amalankhulana momasuka. Inunso mukamayesetsa kulankhula ndi anthu momasuka zidzakuthandizani kuti muzigwirizana nawo kwambiri.​—Miy. 27:9.

MUZIGWIRA NTCHITO LIMODZI

Anthu amene amagwirizana amagwira ntchito limodzi mu utumiki (Onani ndime 10)

10. Malinga ndi Miyambo 27:17, kodi chingachitike n’chiyani tikamagwira ntchito ndi Akhristu anzathu?

10 Mofanana ndi Yeremiya ndi Baruki, nafenso tikamagwira ntchito limodzi ndi Akhristu anzathu, timaona makhalidwe awo abwino, timaphunzira zinthu zina komanso timayamba kugwirizana nawo kwambiri. (Werengani Miyambo 27:17.) Mwachitsanzo, kodi mumamva bwanji mukaona mnzanu mu utumiki akulankhula molimba mtima za chikhulupiriro chake komanso zokhudza Yehova ndi zolinga zake? Mungafune kuti muzigwirizana naye kwambiri.

11-12. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kulalikira limodzi kungatithandize kuti tizigwirizana kwambiri.

11 Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri zimene zikusonyeza kuti kulalikira limodzi kungatithandize kuti tizigwirizana. Mlongo wina wazaka 23 dzina lake Adeline anapempha mnzake dzina lake Candice kuti akalalikire limodzi m’gawo limene sililalikidwa kawirikawiri. Iye ananena kuti: “Tinkaona kuti zimenezi zikhoza kutilimbikitsa mwauzimu komanso kutithandiza kuti tizikonda kwambiri utumiki.” Kodi kugwira ntchito limodzi kunawathandiza bwanji? Adeline anati: “Tikaweruka mu utumiki, tinkakambirana mmene tinkamvera, zimene zinatilimbikitsa pokambirana ndi anthu komanso mmene Yehova anatithandizira. Tonse tinkasangalala pokambirana mochokera pansi pa mtima ndipo zinkatithandiza kuti tidziwane bwino kwambiri.”

12 Chitsanzo china ndi cha alongo awiri osakwatiwa omwe amachokera ku France. Mayina awo ndi Laïla ndi Marianne. Iwo anakalalikira kwa milungu 5 mumzinda wa Bangui, womwe ndi likulu la dziko la Central African Republic. Laïla anafotokoza kuti: “Ine ndi Marianne tinkakumana ndi mavuto koma tinkagwirizana kwambiri chifukwa choti tinkauzana zamumtima komanso kuyesetsa kuchita zinthu mwachikondi. Ndinayamba kumulemekeza kwambiri Marianne nditaona kuti sachedwa kuzolowera zinthu zatsopano, amakonda anthu komanso ndi wakhama mu utumiki.” Sikuti munthu amafunika kuchita kusamukira kudziko lina kuti ayambe kugwirizana kwambiri ndi anthu ena. Nthawi iliyonse imene mukulalikira ndi m’bale kapena mlongo m’gawo lanu, mumakhala ndi mwayi wodziwana bwino komanso kuyamba kugwirizana kwambiri.

MUZIGANIZIRA MAKHALIDWE ABWINO A ANZANU KOMANSO KUWAKHULULUKIRA

13. Kodi tingakumane ndi vuto lotani tikamagwira ntchito kwambiri ndi anzathu?

13 Nthawi zina tikamagwira ntchito kwambiri ndi anzathu timaona makhalidwe awo abwino komanso zimene amalakwitsa. Ndiye kodi tingatani kuti tizigwirizana nawobe? Tiyeni tionenso chitsanzo cha Yeremiya. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti aziona zinthu zabwino zimene ena ankachita komanso kuwakhululukira zimene ankalakwitsa?

14. Kodi Yeremiya anaphunzira chiyani zokhudza Yehova, nanga zimenezi zinamuthandiza bwanji?

14 Yeremiya analemba buku la m’Baibulo la Yeremiya komanso ayenera kuti analembanso mabuku a 1 Mafumu ndi 2 Mafumu. Polemba mabukuwa, ayenera kuti anazindikira kuti Yehova amasonyeza chifundo kwa anthu ochimwafe. Mwachitsanzo, anadziwa kuti Mfumu Ahabu atalapa, Yehova anasankha kuti asawononge anthu a m’banja lake onse pa nthawi imene iye anali moyo. (1 Maf. 21:27-29) Yeremiya anadziwanso kuti Manase anachita zinthu zoipa kwambiri kuposa Ahabu. Koma Yehova anamukhululukira chifukwa choti analapa. (2 Maf. 21:16, 17; 2 Mbiri 33:10-13) Nkhani zimenezi ziyenera kuti zinathandiza Yeremiya kuti azitsanzira Yehova pokhala woleza mtima komanso wachifundo kwa anzake apamtima.​—Sal. 103:8, 9.

15. Baruki atayamba kusokonezeka ndi zinthu zina, kodi Yeremiya anatsanzira bwanji kuleza mtima kwa Yehova?

15 Tiyeni tione zimene Yeremiya anachita Baruki atayamba kusokonezeka ndi zinthu zina. Iye sanafulumire kusiya kugwirizana ndi mnzakeyo. M’malomwake, anamuthandiza pomuuza uthenga wochokera kwa Mulungu womwe unali wachikondi koma wosapita m’mbali. (Yer. 45:1-5) Kodi tikuphunzirapo chiyani?

Anthu amene amagwirizana amakhululukirana (Onani ndime 16)

16. Malinga ndi Miyambo 17:9, kodi tiyenera kutani kuti tipitirize kugwirizana ndi anzathu?

16 Tisamayembekezere kuti abale ndi alongo athu azichita zinthu zonse popanda kulakwitsa. Ndiye tikapeza anzathu apamtima, timafunika kuchita khama kuti tipitirizebe kugwirizana nawo. Anzathu akalakwitsa, tingafunike kuwapatsa malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu mwachikondi koma mosapita m’mbali. (Sal. 141:5) Ndipo akatikhumudwitsa tiyenera kuwakhululukira. Tikatero, tiyenera kupewa kukumbutsanso nkhaniyo. (Werengani Miyambo 17:9.) Masiku otsiriza ano, tiyenera kumaganizira kwambiri zinthu zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita osati zomwe amalakwitsa. Zimenezi zimathandiza kuti tizigwirizana kwambiri. Ndipo kugwirizana n’kofunika kwambiri chifukwa pa nthawi ya chisautso chachikulu tidzafunikira kukhala ndi anzathu apamtima.

MUZISONYEZA CHIKONDI CHOSATHA

17. Kodi Yeremiya anathandiza bwanji mnzake atakumana ndi mavuto?

17 Mneneri Yeremiya ankathandiza anzake akakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, Ebedi-meleki, yemwe anali nduna ya m’nyumba ya mfumu, anapulumutsa Yeremiya ataponyedwa m’chitsime koma kenako ankaopa zimene akalonga angamuchitire. Yeremiya atamva zimenezi, sanangokhala n’kumaganiza kuti mnzakeyo adziwa zochita. Ngakhale kuti Yeremiya anali m’ndende, anachita zimene akanatha ndipo anauza mnzakeyo zinthu zolimbikitsa zimene Yehova analonjeza.​—Yer. 38:7-13; 39:15-18.

Anthu amene amagwirizana amathandizana pa nthawi yamavuto (Onani ndime 18)

18. Malinga ndi Miyambo 17:17, kodi tiyenera kuchita chiyani anzathu akakumana ndi mavuto?

18 Masiku ano, abale ndi alongo athu amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, amakumana ndi ngozi zachilengedwe komanso zoyambitsidwa ndi anthu. Zimenezi zikachitika, mwina tingalolere kuti abale athuwo adzakhale kunyumba kwathu. Apo ayi, tingawathandize ndi ndalama. Koma aliyense angapemphe Yehova kuti azithandiza abale ndi alongowo. Tikamva kuti m’bale kapena mlongo wina akuvutika maganizo, tikhoza kusowa chonena kapena chochita. Koma mfundo ndi yakuti aliyense wa ife angathandize anzake m’njira inayake. Mwachitsanzo, tingapeze mpata wocheza nawo ndipo akamalankhula, tiziwamvetsera mwachifundo. Tingawauzenso malemba amene amatilimbikitsa kwambiri. (Yes. 50:4) Chofunika kwambiri ndi kukhala limodzi ndi anzathu pamene akukumana ndi mavuto.​—Werengani Miyambo 17:17.

19. Kodi kukhala ndi anzathu apamtima panopa kungadzatithandize bwanji m’tsogolo?

19 Tiyenera kuyesetsa panopa kuti tizigwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo athu. Tikutero chifukwa chakuti adani athu azidzayesetsa kusokoneza mgwirizano wathu pogwiritsa ntchito mabodza. Adzayesetsanso kuti tiyambe kudana koma zonse zimene adzachitezi sizidzaphula kanthu. Iwo sadzatha kusokoneza mgwirizano wathu kapena kutilepheretsa kukondana. Ndipo sitidzasiya kugwirizana komanso kukondana mpaka kalekale.

NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova

^ ndime 5 Pamene mapeto akuyandikira, tikufunika kumagwirizana kwambiri ndi Akhristu anzathu. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingaphunzire pa nkhani ya Yeremiya. Tikambirananso mmene kupeza anzathu apamtima panopa kungatithandizire pa nthawi yamavuto.

^ ndime 2 Zinthu za m’buku la Yeremiya sizinalembedwe motsatira nthawi imene zinachitikira.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Chithunzichi chikusonyeza zimene zingadzachitike pa “chisautso chachikulu.” Abale ndi alongo angapo akubisala m’chipinda cham’mwamba. Popeza amagwirizana, akulimbikitsana kwambiri pa nthawi yovutayo. Abale ndi alongowa anali atayamba kale kugwirizana chisautso chachikulu chisanayambe.