Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 45

Mmene Mzimu Woyela Umatithandizila

Mmene Mzimu Woyela Umatithandizila

“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—AFIL. 4:13.

NYIMBO 104 Mphatso ya Mzimu Woyela

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. (a) N’ciani cimatithandiza kupilila mavuto a tsiku na tsiku? Fotokozani. (b) Tikambilane ciani m’nkhani ino?

“NIKAGANIZILA mavuto amene napitamo, nidziŵa kuti panekha sembe sin’nakwanitse kuwapilila.” Kodi na imwe munakambako mawu aconco pa nthawi ina? Ambili a ife tinakambako. Mwina munakamba izi pambuyo popilila matenda aakulu amene munali kudwala, kapena imfa ya munthu amene munali kukonda. Ndipo mukaganizila zimene zinacitikazo, mumaona kuti munakwanitsa kupilila tsiku na tsiku cabe cifukwa mzimu woyela wa Yehova unakupatsani “mphamvu yoposa yacibadwa.”—2 Akor. 4:7-9.

2 Timafunikilanso mzimu woyela kuti utithandize kukaniza mzimu woipa wa dziko. (1 Yoh. 5:19) Kuwonjezela apo, timalimbana na “makamu a mizimu yoipa.” (Aef. 6:12) Tsopano, tiyeni tikambilane njila ziŵili zimene mzimu woyela umatithandizila polimbana na zovuta zimenezi. Tikambilananso zimene tingacite kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela.

MZIMU WOYELA UMATIPATSA MPHAMVU

3. Kodi njila imodzi imene Yehova amatithandizila kupilila mavuto ni iti?

3 Mzimu woyela wa Yehova umatithandiza mwa kutipatsa mphamvu kuti tipitilize kum’tumikila ngakhale tikukumana na mavuto. Mtumwi Paulo anazindikila kuti, kudalila “mphamvu ya Khristu” n’kumene kunamuthandiza kuti apitilize kutumikila Yehova, olo kuti anali kukumana na mavuto. (2 Akor. 12:9) Pa ulendo wake waciŵili waumishonale, Paulo anagwila nchito yolalikila mwacangu. Koma pa nthawi imodzimodziyo, anali kugwilanso nchito yomuthandiza kupeza zofunikila mu umoyo. Pamene anafika ku Korinto, anali kukhala ku nyumba ya Akula na Purisikila. Iwo anali amisili opanga matenti. Popeza Paulo nayenso anali mmisili wopanga matenti, nthawi zina anali kuseŵenzela nawo pamodzi. (Mac. 18:1-4) Mzimu woyela unam’patsa mphamvu Paulo kuti akwanitse kugwila nchito zonse ziŵili, yakuthupi komanso yolalikila.

4. Malinga na 2 Akorinto 12:7b-9, kodi Paulo anali kulimbana na vuto lanji?

4 Ŵelengani 2 Akorinto 12:7b-9. Pa mavesi amenewa, kodi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti anali kulimbana na “munga m’thupi”? Ngati mwalasiwa na minga, mumamvela kupweteka kwambili. Conco, Paulo anatanthauza kuti anali kulimbana na vuto linalake mu umoyo wake, limene linali kumusautsa kwambili. Iye anakamba kuti vutolo linali ngati “mngelo wa Satana,” amene anali ‘kumumenya’ nthawi zonse. Mwina Satana na ziwanda zake si ndiwo anacititsa vuto limenelo mwacindunji. Kucita zimenezo kukanakhala ngati kum’lasa Paulo na munga kapena kuti minga. Koma n’kutheka kuti mizimu yoipayo itaona kuti Paulo ali na “munga” m’thupi, inayamba kuukankhila mkati, titelo kukamba kwake, n’colinga cakuti iye amvele ululu kwambili. Kodi Paulo anacita ciani?

5. Kodi Yehova anayankha bwanji mapemphelo a Paulo?

5 Poyamba, Paulo anali kufuna kuti Yehova amucotsele ‘mungawo’ m’thupi mwake. Iye anati: “Katatu konse ndinacondelela Ambuye [Yehova] kuti mungawu undicoke.” Ngakhale kuti Paulo anaipemphelela nkhaniyi, Yehova sanacotse mungawo. Kodi izi zitanthauza kuti Yehova sanayankhe mapemphelo a Paulo? Kutali-tali. Yehova anayankha. Ngakhale kuti sanathetse vutolo, anam’patsa mphamvu kuti apilile. Yehova anati: “Mphamvu yanga imakhala yokwanila iweyo ukakhala wofooka.” (2 Akor. 12:8, 9) Ndipo mwa thandizo la Mulungu, Paulo anakwanitsa kupilila ali na cimwemwe komanso mtendele wa m’maganizo.—Afil. 4:4-7.

6. (a) Kodi Yehova angayankhe bwanji mapemphelo athu? (b) Ni mawu ati opezeka m’malemba osagwila mawu m’ndime ino amene amakulimbikitsani?

6 Mofanana na Paulo, kodi na imwe munapemphapo Yehova kuti athetse vuto lina lake limene munali kukumana nalo? N’kutheka kuti munacondelela Yehova mocokela pansi pa mtima za vutolo, koma silinathe kapena linangokulila-kulila. Kodi izi zinakupangitsani kuganiza kuti Yehova sakondwela namwe? Ngati n’conco, kumbukilani citsanzo ca Paulo. Yehova anayankha mapemphelo a Paulo, ndipo sadzalephela kuyankha mapemphelo anu. Mwina sangathetse vuto lanu. Koma poseŵenzetsa mzimu woyela, adzakupatsani mphamvu kuti mupilile mayeselowo. (Sal. 61:3, 4) ‘Mungagwetsedwe pansi,’ koma Yehova sadzakusiyani.—2 Akor. 4:8, 9; Afil. 4:13.

MZIMU WOYELA UMATITHANDIZA KUPITILIZA KUTUMIKILA YEHOVA

7-8. (a) Kodi mzimu woyela uli ngati mphepo m’lingalilo lotani? (b) Kodi Petulo anaseŵenzetsa mawu otani pofotokoza mmene mzimu woyela umagwilila nchito?

7 Kodi njila ina imene mzimu woyela umatithandizila ni iti? Tingayelekezele mzimu woyela na mphepo ya pa nyanja. Mphepo imene ikuwombela kumene boti ikupita, ingathandize botiyo kukafika kumene ikupitako olo kuti pa nyanjapo pali cimphepo. Mofananamo, mzimu woyela umatithandiza kupitiliza kutumikila Yehova ngakhale kuti tikukumana na mavuto, kufikila tikaloŵe m’dziko latsopano lolonjezedwa.

8 Monga msodzi, mtumwi Petulo anali kuidziŵa bwino nchito yoyendetsa boti. Conco, n’zosadabwitsa kuti pofotokoza za mzimu woyela, anaseŵenzetsa mawu amene aoneka kuti ni ogwilizana na nchito yoyendetsa boti. Iye analemba kuti: “Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.” Mawu a Cigiriki omasulidwa kuti “motsogoleledwa,” kweni-kweni amatanthauza “kutengedwa” kapena “kukankhidwa.”—2 Pet. 1:21.

9. Kodi Petulo anafuna kuti anthu aganize za ciani pamene anaseŵenzetsa mawu akuti “motsogoleledwa”?

9 Kodi Petulo anafuna kuti anthu aganize za ciani pamene anaseŵenzetsa mawu akuti “motsogoleledwa”? Luka, amene analemba buku la Machitidwe, anaseŵenzetsa liwu lina la Cigiriki lofanana na liwu limene linamasulidwa kuti “motsogoleledwa,” pofotokoza za boti imene ‘ikutengedwa’ na mphepo. (Mac. 27:15) Conco, pamene Petulo anakamba kuti olemba Baibo ‘anatsogoleledwa’ na mzimu woyela, anagwilitsila nchito mawu amene katswili wina wa Baibo anati ali monga “fanizo locititsa cidwi lokamba za ulendo wapanyanja.” Petulo anali kukamba kuti monga mmene mphepo imakankhila boti pa nyanja kuti ikafike kumene ikupita, mzimu woyela unatsogolela olemba Baibo kuti agwile nchito imeneyi. Katswiliyo anakambanso kuti olemba Baibo anali monga maboti amene “nsalu zake zoyendetsela zatambasulidwa.” Iwo anali okonzeka kucita zimene mzimu woyela unawalamula. Yehova anacita mbali yake. Anapeleka “mphepo,” kapena kuti mzimu woyela. Nawonso olemba Baibo anacita mbali yawo. Anatsatila citsogozo ca mzimu woyela.

SITEPU 1: Muzicita zinthu zauzimu nthawi zonse

SITEPU 2: Muzicita zinthu zauzimu zimenezi mwakhama mmene mungathele (Onani ndime 11) *

10-11. N’zinthu ziŵili ziti zimene tiyenela kucita kuti mzimu woyela uzititsogolela? Fotokozani citsanzo.

10 N’zoona kuti masiku ano Yehova sagwilitsilanso nchito mzimu wake woyela pouzila anthu kuti alembe mawu ake. Komabe, iye akali kuseŵenzetsa mzimu woyela potsogolela atumiki ake. Yehova akali kucita mbali yake. Nanga ife tiyenela kucita ciani kuti mzimu woyela uzititsogolela? Tiyenela kuyesetsa nthawi zonse kucita mbali yathu. Tingacite bwanji zimenezo?

11 Kuti tipeze yankho, tiyeni tiganizile citsanzo ca woyendetsa boti. Kuti mphepo ya pa nyanja imuthandize kuyendetsa boti, pali zinthu ziŵili zimene amafunika kucita. Coyamba, amafunika kukankhila boti yake pa malo amene papita mphepo. Ngati angaisiye botiyo pa doko, pamene palibe mphepo, ndiye kuti singayende kulikonse. Caciŵili, amafunika kukweza na kutambasula mokwanila nsalu zoyendetsela botiyo. Ndipo olo mphepo ikuwomba, botiyo ingayambe kuyenda kokha ngati nsaluzo zagwila mphepo. Mofanana na zimenezi, timafunika thandizo la mzimu woyela kuti tipitilize kutumikila Yehova. Kuti mzimuwo uzititsogolela, pali zinthu ziŵili zimene timafunika kucita. Coyamba, tiyenela kucita zinthu zimene zingapangitse kuti mzimu wa Mulungu uzititsogolela. Caciŵili, tifunika kucita zinthu zimenezi mwakhama mmene tingathele. Kucita izi kuli ngati kukweza nsalu zoyendetsela boti m’mwamba kwambili na kuzitambasula mokwanila. (Sal. 119:32) Tikatelo, mzimu woyela udzatipatsa mphamvu kuti tipilile zitsutso na mayeselo, komanso kuti tipitilize kutumikila Yehova mokhulupilika mpaka m’dziko latsopano la Mulungu.

12. Kodi tidzakambilana ciani lomba?

12 Takambilana njila ziŵili za mmene mzimu woyela umatithandizila. Yoyamba, umatipatsa mphamvu na kutithandiza kukhalabe wokhulupilika pamene tikumana na mayeselo. Yaciŵili, umatitsogolela na kutithandiza kupitiliza kuyenda pa njila ya ku moyo wosatha. Tiyeni lomba tikambilane zinthu zinayi zimene tifunika kucita kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela.

ZOYENELA KUCITA KUTI MUPINDULE MOKWANILA NA THANDIZO LA MZIMU WOYELA

13. Malinga na 2 Timoteyo 3:16, 17, kodi Malemba angatisonkhezele kucita ciani? Ndipo ife tiyenela kucita ciani?

13 Coyamba, muziŵelenga Mawu a Mulungu. (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:16, 17.) Mulungu anaika maganizo ake m’mitima ya anthu amene analemba Baibo. Iye anacita izi poseŵenzetsa mzimu wake. Pamene tiŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha pa zimene taŵelenga, malangizo a Mulungu amaloŵa m’maganizo na mu mtima mwathu. Mawu ouzilidwa amenewo amatisonkhezela kusintha umoyo wathu, kuti ukhale wogwilizana na cifunilo ca Mulungu. (Aheb. 4:12) Koma kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela, tifunika kupatula nthawi yoŵelenga Baibo tsiku lililonse na kuganizila mozama pa zimene taŵelengazo. Tikatelo, Mawu a Mulungu adzayamba kutitsogolela pa zokamba na zocita zathu zonse.

14. (a) N’cifukwa ciani tingakambe kuti misonkhano yathu ili ngati malo amene “mphepo ikuwomba”? (b) Tingacite ciani kuti pamene tili pa misonkhano tikhale monga boti imene “nsalu zake zoyendetsela zatambasulidwa”?

14 Caciŵili, muzilambila Mulungu pamodzi na Akhristu anzanu. (Sal. 22:22) Mogwilizana na citsanzo cija ca boti, misonkhano yathu ili ngati malo amene “mphepo ikuwomba.” Takamba conco cifukwa pa misonkhanoyi, pamakhala mzimu wa Yehova. (Chiv. 2:29) Tidziŵa bwanji zimenezi? Tidziŵa cifukwa tikasonkhana na Akhristu anzathu, timapempha mzimu woyela, timaimba nyimbo za Ufumu zozikidwa pa Mawu a Mulungu, ndiponso timalandila malangizo ozikidwa pa Baibo amene abale oikidwa na mzimu woyela amapeleka. Kuwonjezela apo, mzimu woyela umathandizanso alongo athu kuti akonzekele na kukamba bwino mbali zawo. Komabe, kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela, tifunika kukonzekela kukapelekapo ndemanga pa misonkhano. Tikatelo, timakhala ngati boti imene “nsalu zake zoyendetsela zatambasulidwa.”

15. Kodi mzimu woyela umatithandiza bwanji pa nchito yolalikila?

15 Cacitatu, muzilalikila. Pamene tiseŵenzetsa Baibo polalikila na kuphunzitsa, timalola mzimu woyela kutitsogolela mu ulaliki. (Aroma 15:18, 19) Komabe, kuti tipindule mokwanila na mzimu wa Mulungu, tiyenela kulalikila nthawi zonse. Tiyenelanso kuseŵenzetsa Baibo nthawi zonse pamene kuli kotheka. Cina cimene tingacite kuti ulaliki uzitiyendela bwino, ni kuseŵenzetsa maulaliki acitsanzo a m’Kabuku ka Misonkhano ya Umoyo na Utumiki.

16. N’ciani cacindunji cimene tingacite kuti tilandile mzimu woyela?

16 Cacinayi, muzipemphela kwa Yehova. (Mat. 7:7-11; Luka 11:13) Cinthu cacindunji cimene tingacite kuti tilandile mzimu woyela ni kupempha mzimuwo kwa Yehova. Palibe cimene cingaletse mapemphelo athu kufika kwa Yehova, kapena kutilepheletsa kulandila mphatso yabwino ya Mulungu ya mzimu woyela. Olo tili m’ndende tingalandile mphamvu ya mzimu woyela, ndipo palibe cimene Satana angacite kuti atilepheletse kulandila mzimuwo. (Yak. 1:17) Koma kodi tiyenela kupemphela bwanji kuti tilandile mzimu woyela? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane mozama za pemphelo, mwa kupenda fanizo la m’buku la Uthenga Wabwino la Luka. *

LIMBIKILANI KUPEMPHELA

17. Kodi fanizo la Yesu la pa Luka 11:5-9, 13, litiphunzitsa ciani pa nkhani ya pemphelo?

17 Ŵelengani Luka 11:5-9, 13. Fanizo la Yesu limeneli lionetsa mmene tiyenela kupemphela mzimu woyela. Mwamuna wa m’fanizoli analandila thandizo “cifukwa ca kukakamila kwake.” Iye sanacite mantha kukapempha thandizo kwa bwenzi lake olo kuti unali usiku kwambili. * Kodi Yesu anakamba kuti fanizo limeneli litiphunzitsa ciani pa nkhani ya pemphelo? Iye anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani.” Conco, mfundo imene tiphunzilapo ni yakuti, kuti tilandile thandizo la mzimu woyela, tifunika kulimbikila kupempha Yehova kuti atipatse mzimuwo.

18. Mogwilizana na fanizo la Yesu, n’cifukwa ciani sitiyenela kukayikila kuti Yehova adzatipatsa mzimu wake woyela?

18 Fanizo la Yesu litithandizanso kuona cifukwa cake Yehova amatipatsa mzimu woyela. Munthu wa m’fanizo lija anafuna kumulandila bwino mlendo amene anabwela ku nyumba kwake usiku. Anaona kuti kunali kofunika kumupatsa cakudya mlendoyo, koma analibe cakudya ciliconse. Yesu anakamba kuti mnzake uja anamupatsa cakudya cifukwa cakuti analimbikila kwambili kumupempha. Kodi mfundo ya Yesu pamenepa inali yotani? Inali yakuti, ngati munthu wopanda ungwilo amalolela kuthandiza mnzake amene walimbikila kupempha cinthu, Atate wathu wacikondi wakumwamba sangalephele kuthandiza anthu amene amalimbikila kupempha mzimu woyela kwa iye. Motelo, tisakayikile kuti Yehova adzayankha mapemphelo athu opempha mzimu woyela.—Sal. 10:17; 66:19.

19. Tidziŵa bwanji kuti tingakwanitse kupilila?

19 Tili na cikhulupililo cakuti tidzakwanitsa kupilila olo kuti Satana saleka kulimbana nafe. Cifukwa ciani? Cifukwa mzimu woyela umatithandiza m’njila ziŵili. Njila yoyamba, umatipatsa mphamvu kuti tikwanitse kupilila mayeselo. Yaciŵili, umatipatsa mphamvu kuti tipitilize kutumikila Yehova mpaka tikaloŵe m’dziko latsopano la Mulungu. Cotelo, tiyeni ticite zonse zotheka kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela.

NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde

^ ndime 5 Nkhani ino ifotokoze mmene mzimu wa Mulungu umatithandizila kupilila mavuto. Ifotokozenso zimene tingacite kuti tipindule mokwanila na thandizo la mzimu woyela.

^ ndime 16 Pa onse amene analemba mabuku a Uthenga Wabwino, Luka ndiye anaonetsa bwino kwambili kuti Yesu anali kukonda kwambili kupemphela.—Luka 3:21; 5:16; 6:12; 9:18, 28, 29; 18:1; 22:41, 44.

^ ndime 17 Onani mfundo younikila pa mawu akuti “kukakamila,” pa peji 4 mu Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu, ka July 2018.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: SITEPU 1: M’bale na mlongo afika pa Nyumba ya Ufumu kuti asonkhane pamodzi na Akhristu anzawo. Pa misonkhano imeneyi pamapezeka mzimu wa Yehova. SITEPU 2: Iwo anakonzekela kupelekapo ndemanga pa msonkhanowo. Tifunikanso kutsatila masitepu aŵili amenewa pocita zinthu zina zauzimu zimene takambilana m’nkhani ino, zomwe ni kuŵelenga Mawu a Mulungu, kulalikila, na kupemphela kwa Yehova.