Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 47

Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko

Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko

“Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.​”—2 TIM. 3:16.

NYIMBO 98 Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. N’cifukwa ciani ife Akhristu tiyenela kucita cidwi na buku la Levitiko masiku ano?

MTUMWI Paulo anakumbutsa bwenzi lake lacicepele Timoteyo kuti “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Tim. 3:16) Malembawo aphatikizapo buku la Levitiko. Kodi buku limeneli mumaliona bwanji? Ena amaona kuti ni buku lokhala na malamulo ambili-mbili amene sagwilanso nchito masiku ano. Koma Akhristu oona saliona conco.

2 Buku la Levitiko linalembedwa zaka 3,500 zapitazo. Komabe, Yehova analola kuti bukuli lisungidwe cifukwa zimene zinalembedwa mmenemo “zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Popeza bukuli limatithandiza kudziŵa bwino mmene Yehova amaonela zinthu, tiyenela kukhala na cidwi coliphunzila. Ndipo m’buku louzilidwa limeneli, muli mfundo zambili zimene tingaphunzile. Tiyeni lomba tikambilane zinayi mwa mfundo zimenezi.

ZIMENE TINGACITE KUTI YEHOVA AZIKONDWELA NAFE

3. N’cifukwa ciani Aisiraeli anali kupeleka nsembe pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo?

3 Mfundo yoyamba: Tifunika kucita zinthu zokondweletsa Yehova kuti iye alandile nsembe zathu. Caka ciliconse, pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, mtundu wa Isiraeli unali kusonkhana pamodzi na kupeleka nsembe za nyama. Nsembe zimenezo zinakumbutsa Aisiraeli kuti anafunika kuyeletsedwa ku macimo awo. Pa tsikulo, mkulu wa ansembe anali kutenga magazi a nyama zopelekela nsembe, na kukaloŵa nawo m’Malo Oyela Koposa kuti ayeletse mtunduwo. Koma asanacite zimenezo, coyamba anali kucita cinthu cina cofunika kwambili.

(Onani ndime 4) *

4. Malinga na Levitiko 16:12, 13, kodi wansembe anali kucita ciani akaloŵa koyamba m’Malo Oyela Koposa pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo? (Onani cithunzi pa cikuto.)

4 Ŵelengani Levitiko 16:12, 13. Yelekezelani kuti mukuona zimene zinali kucitika pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo. Mkulu wa nsembe akuloŵa m’cihema. Ndipo aka ni koyamba pa nthawi zitatu zimene afunika kuloŵa m’Malo Oyela Koposa pa tsikuli. Pamene akuloŵa, dzanja lina wanyamula ciwiya codzala na zofukiza zonunkhila, ndipo dzanja linalo wanyamula ciwiya ca golide cofukizila cimene n’codzala na makala amoto. Atafika pa nsalu yochinga khomo loloŵela ku Malo Oyela Koposa, iye akuima pang’ono. Ndiyeno mwaulemu kwambili, akuloŵa m’cipinda ca Malo Oyela Koposa na kuima pafupi na likasa la pangano. Mophiphilitsa, iye waima pamaso peni-peni pa Yehova Mulungu! Ndiyeno, mosamala wansembeyo akuthila zofukiza zopatulika zija pa makala amoto, ndipo fungo lonunkhila bwino likudzala m’cipinda conse. * Iye akutuluka m’cipindaco. Koma pambuyo pake, adzaloŵanso m’Malo Oyela Koposa atanyamula magazi a nsembe zophimba macimo. Onani kuti mkulu wa ansembe coyamba anali kufukiza zofukiza asanapeleke magazi a nsembe zophimba macimo.

5. Kodi mkulu wa ansembe anali kuloŵa bwanji m’Malo Oyela Koposa? Ndipo tiphunzilapo ciani?

5 Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene mkulu wa ansembe anali kuseŵenzetsela zofukiza pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo? Baibo imaonetsa kuti mapemphelo a atumiki okhulupilika a Yehova ali ngati zofukiza. (Sal. 141:2; Chiv. 5:8) Kumbukilani kuti mkulu wansembe anali kubweletsa zofukiza pa maso pa Yehova mwaulemu kwambili. Mofananamo, pamene tipemphela kwa Yehova, tiyenela kupemphela mwaulemu kwambili. Timacita zimenezi cifukwa timamulemekeza kwambili. Timayamikila ngako kuti Mlengi wacilengedwe conse, amatilola kukamba naye na kukhala naye pafupi, monga mmene tate amacitila na mwana wake. (Yak. 4:8) Iye watilola kukhala mabwenzi ake. (Sal. 25:14) Timayamikila kwambili mwayi umenewo, ndipo sitifuna kucita ciliconse cimene cingam’khumudwitse.

6. Mkulu wansembe anali kufukiza zofukiza asanapeleke nsembe. Kodi izi zitiphunzitsa ciani?

6 Kumbukilani kuti mkulu wansembe asanapeleke nsembe, coyamba anali kufukiza zofukiza. Anali kucita izi n’colinga cakuti Mulungu akondwele naye pamene apeleka nsembezo. Kodi tiphunzilapo ciani? Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anacita zinazake zofunika kwambili asanapeleke moyo wake monga nsembe. Zimene anacitazo zinali zofunika kwambili kuposa kupulumutsa mtundu wa anthu. Kodi anacita ciani? Anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mu umoyo wake wonse pa dziko lapansi kuti Yehova alandile nsembe yake. Mwa kucita zimenezo, Yesu anaonetsa kuti kutsatila malamulo a Yehova n’kumene kungatithandize kukhala na umoyo wabwino. Iye anakweza ucifumu wa Atate wake. Anaonetsa kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wabwino komanso wacilungamo.

7. N’cifukwa ciani Yehova anakondwela na zonse zimene Yesu anali kucita pano pa dziko lapansi?

7 Pa nthawi yonse imene Yesu anali pano pa dziko lapansi, anali kumvela Yehova pa ciliconse. Ngakhale kuti anakumana na mayeselo, ndipo anadziŵa kuti adzafa imfa yoŵaŵa, Yesu sanasunthike pocilikiza ulamulilo wa Atate wake. (Afil. 2:8) Yesu atakumana na mavuto, anapemphela “mofuula komanso akugwetsa misozi.” (Aheb. 5:7) Mapemphelo ake ocokela pansi pa mtima anaonetsa kuti anali wokhulupilika kwa Yehova, ndiponso anamulimbikitsa kukhalabe womvela kwa iye. Kwa Yehova, mapemphelo a Yesu anali monga fungo lokoma la zofukiza. Zonse zimene Yesu anacita pa dziko lapansi zinakondweletsa kwambili mtima wa Atate wake, komanso zinakweza ucifumu wa Mulungu.

8. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu?

8 Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kuyesetsa kumvela Yehova na kukhalabe okhulupilika kwa iye. Tikakumana na mayeselo, timapempha thandizo kwa Yehova mocokela pansi pa mtima cifukwa timafuna kucita zom’kondweletsa. Tikatelo, timaonetsa kuti tikucilikiza ulamulilo wa Yehova. Timadziŵa kuti iye sangamvele mapemphelo athu ngati timacita zinthu zimene amazonda. Koma tikamatsatila miyezo ya Yehova mu umoyo wathu, tingakhale na cidalilo cakuti mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima adzakhala ngati fungo lokoma la zofukiza kwa iye. Ndiponso, sitikayikila kuti Atate wathu wakumwamba amakondwela poona kuti tili na mtima wamphumphu, ndipo timamumvela mokhulupilika.—Miy. 27:11.

TIMATUMIKILA YEHOVA CIFUKWA COMUYAMIKILA NA KUM’KONDA

(Onani ndime 9) *

9. N’cifukwa ciani Aisiraeli anali kupeleka nsembe zaciyanjano?

9 Mfundo yaciŵili: Timatumikila Yehova cifukwa comuyamikila. Kuti timvetsetse mfundoyi, tiyeni tikambilane za nsembe zaciyanjano. Kupeleka nsembe zimenezi, inali mbali inanso yofunika kwambili pa kulambila koona mu Isiraeli wakale. * Buku la Levitiko limakamba kuti Aisiraeli anali kupeleka nsembe zaciyanjano “posonyeza kuyamikila.” (Lev. 7:11-13, 16-18) Aisiraeli anali kupeleka nsembe zimenezi, osati mocita kulamulidwa, koma mwa kufuna kwawo. Anali kucita izi cifukwa cokonda Mulungu wawo Yehova. Munthu wopeleka nsembeyo, banja lake, na wansembe, anali kudya nyama ya nsembeyo. Koma ziwalo zina za nyamayo zinali kupelekedwa kokha kwa Yehova. Kodi ziwalo zimenezo ni ziti?

(Onani ndime 10) *

10. Kodi nsembe zaciyanjano zochulidwa pa Levitiko 3:6, 12, 14-16, zionetsa kuti n’ciani cinasonkhezela Yesu kucita cifunilo ca Atate wake?

10 Mfundo yacitatu: Timapatsa Yehova zabwino koposa cifukwa timam’konda. Yehova anali kuona mafuta kukhala mbali yabwino koposa ya nyama. Iye anafotokozanso kuti ziwalo zina za nyama, kuphatikizapo impso zinali zofunika kwambili. (Ŵelengani Levitiko 3:6, 12, 14-16.) Conco, Yehova anali kukondwela ngako Mwisiraeli akapeleka modzifunila ziwalo zofunika kwambili za nyama komanso mafuta. Mwisiraeli akapeleka nsembe imeneyo, anali kuonetsa kuti akufunitsitsa kupatsa Mulungu zabwino koposa. Yesu anacita zofanana na zimenezi. Modzifunila, anapatsa Yehova zabwino koposa mwa kum’tumikila na mtima wonse cifukwa com’konda. (Yoh. 14:31) Yesu anali kukondwela kucita cifunilo ca Mulungu, ndipo anali kukonda kwambili cilamulo cake. (Sal. 40:8) Ndithudi, Yehova anakondwela kwambili kuona kuti Yesu akum’tumikila na mtima wonse!

Kukonda Yehova kumatisonkhezela kum’patsa zabwino koposa (Onani ndime 9-12) *

11. Kodi utumiki wathu umafanana bwanji na nsembe zaciyanjano? Nanga izi zingatilimbikitse bwanji?

11 Utumiki wathu kwa Yehova uli ngati nsembe zaciyanjano. Pamene tim’tumikila, timaonetsa kuti timam’konda. Timapatsa Yehova zabwino koposa, ndipo timacita zimenezi cifukwa timam’konda na mtima wonse. Kukamba zoona, Yehova amakondwela kwambili akaona olambila ake ofika m’mamiliyoni, akumutumikila na mtima wonse cifukwa comukonda kwambili, komanso cifukwa cokonda miyezo yake! Tidziŵa kuti Yehova saona cabe zimene timacita pom’tumikila, koma amaonanso cimene cimatisonkhezela kucita zimenezo. Izi zimatitonthoza kwambili. Mwacitsanzo, ngati ndimwe okalamba ndipo simukwanitsa kucita zambili monga mmene mumafunila, dziŵani kuti Yehova amakumvetsetsani. Mwina mumaona kuti simucita zambili. Koma Yehova amaona cikondi canu cacikulu cimene cimakusonkhezelani kucita zimene mungathe pom’tumikila, ndipo amakondwela ngati mucita zimenezo.

12. Kodi Yehova anali kuziona bwanji nsembe zaciyanjano? Nanga n’cifukwa ciani zimenezi n’zolimbikitsa?

12 Tiphunzilapo ciani tikaganizila nsembe zaciyanjano zimene Aisiraeli anali kupeleka? Pamene moto unali kunyeketsa mbali zabwino koposa za nyama, utsi unali kukwela m’mwamba ndipo Yehova anali kukondwela. Conco, na imwe musakayikile kuti Yehova amakondwela akaona kuti mumadzipeleka kucita zimene mungathe pom’tumikila. (Akol. 3:23) Ndithudi, iye amakondwela namwe kwambili. Kaya mumacita zambili pom’tumikila kapena ayi, iye sadzaiŵala nchito zanu, ndipo amaziona kukhala zamtengo wapatali.—Mat. 6:20; Aheb. 6:10.

YEHOVA AKUDALITSA GULU LAKE

13. Malinga na Levitiko 9:23, 24, kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anavomeleza kuti Aroni ndi ana ake akhale ansembe?

13 Mfundo yacinayi: Yehova akudalitsa gawo la pa dziko lapansi la gulu lake. Ganizilani zimene zinacitika mu 1512 B.C.E. pamene Aisiraeli anamanga cihema m’mbali mwa Phili la Sinai. (Eks. 40:17) Mose anatsogolela pa mwambo woika Aroni ndi ana ake kukhala ansembe. Mtundu wa Isiraeli unasonkhana kuti uonelele pamene ansembewo anali kupeleka nsembe zoyamba za nyama. (Lev. 9:1-5) Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anavomeleza Aroni ndi ana ake amene anali atangoikidwa kumene kukhala ansembe? Pamene Mose na Aroni anali kudalitsa Aisiraeli, Yehova anagwetsa moto umene unanyeketsa nsembe yotsala imene inali pa guwa la nsembe.—Ŵelengani Levitiko 9:23, 24.

14. N’cifukwa ciani zimene Yehova anacita povomeleza Aroni ndi ana ake kukhala ansembe zikutikhudza ife masiku ano?

14 Kodi moto wocokela kumwamba umene unaonekela pa mwambo umenewo unaonetsa ciani? Unaonetsa kuti Yehova anavomeleza Aroni ndi ana ake kukhala ansembe, komanso kuti adzawacilikiza pa utumiki wawo. Aisiraeli ataona umboni umenewu wakuti Yehova akucilikiza Aroni ndi ana ake, anazindikila kuti naonso anafunika kuwacilikiza. Kodi zimenezi zikutikhudza masiku ano? Inde, cifukwa gulu la ansembe a m’nthawi ya Aisiraeli linali kuimila gulu lina la ansembe abwino komanso ofunika kwambili. Khristu, ndiye Mkulu wa Ansembe wapamwamba, ndipo ali na gulu la ansembe okhulupilika okwana 144,000, amene adzatumikila naye limodzi kumwamba.—Aheb. 4:14; 8:3-5; 10:1.

Yehova akutsogolela na kudalitsa gulu lake. Ndipo ife timalicilikiza na mtima wonse (Onani ndime 15-17) *

15-16. N’ciani cionetsa kuti Yehova akutsogolela “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”?

15 Mu 1919, Yesu anaika kagulu kocepa ka abale odzozedwa kukhala “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Kapolo ameneyu amatsogolela pa nchito yolalikila, ndiponso amapeleka “cakudya pa nthawi yoyenela” kwa otsatila a Khristu. (Mat. 24:45) Kodi mumauona umboni wakuti Mulungu akutsogolela kapolo wokhulupilika ndi wanzelu?

16 Satana na dziko lake akucita zonse zotheka kuti asokoneze kapena kuletselatu nchito ya kapolo wokhulupilika. Koma cifukwa ca thandizo la Yehova, kapoloyu wapitilizabe kupeleka cakudya cauzimu kwa otsatila a Khristu pa dziko lapansi. Wacita izi olo kuti pacitikapo nkhondo ziŵili za padziko lonse, mavuto aakulu a zacuma, ndiponso anthu a Mulungu akhala akuzunzidwa na kucitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Ganizilani cabe za cakudya cauzimu coculuka komanso caulele cimene tili naco masiku ano m’vitundu voposa 900! Uwu ni umboni wosatsutsika wakuti Mulungu akucilikiza kapolo wokhulupilika. Nchito yolalikila ni umboni winanso woonetsa kuti Yehova akudalitsa gulu lake. Ndithudi, uthenga wabwino tsopano ukulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) N’zoonekelatu kuti Yehova akutsogolela na kudalitsa gulu lake masiku ano.

17. Kodi tingacilikize bwanji gulu limene Yehova akuligwilitsila nchito?

17 Aliyense wa ife angacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimayamikila kukhala m’gawo la pa dziko lapansi la gulu la Yehova?’ M’nthawi ya Mose, Yehova anagwetsa moto kucokela kumwamba poonetsa kuti anavomeleza Aroni ndi ana ake kukhala ansembe. Monga taonela, masiku anonso Yehova watipatsa umboni wooneka bwino wakuti akutsogolela gulu lake. Ndipo kukamba zoona, tili na zifukwa zambili zokhalila oyamikila. (1 Ates. 5:18, 19) Kodi tingacilikize bwanji gulu limene Yehova akuligwilitsila nchito? Tifunika kutsatila malangizo a m’Baibo amene timalandila m’zofalitsa zathu, pa misonkhano yampingo, yadela, na yacigawo. Tingacilikizenso gulu la Mulungu mwa kuyesetsa mmene tingathele kugwila nchito yolalikila na kuphunzitsa.—1 Akor. 15:58.

18. Kodi imwe mwatsimikiza mtima kucita ciani?

18 Tiyeni tiyesetse kutsatila mfundo zimene taphunzila m’buku la Levitiko. Timafuna kuti Yehova alandile nsembe zathu. Timatumikila Yehova cifukwa comuyamikila. Timapitiliza kum’patsa zabwino koposa cifukwa timam’konda na mtima wonse. Ndipo timacilikiza na mtima wonse gulu limene Yehova akuligwilitsila nchito masiku ano. Pamene ticita zimenezi, timaonetsa kuti timayamikila ngako mwayi umene Yehova watipatsa wotumikila monga Mboni zake.

NYIMBO 96 Buku lake la Mulungu ni Cuma

^ ndime 5 M’buku la Levitiko muli malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli akale. Popeza ndife Akhristu, sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Ngakhale n’telo, tingapindule na malamulo a m’bukuli. M’nkhani ino, tidzakambilana mfundo zofunika kwambili zimene tingaphunzile m’buku la Levitiko.

^ ndime 4 Zofukiza zimene zinali kufukizidwa pa cihema zinali kukhala zopatulika, ndipo Aisiraeli akale anali kuzigwilitsila nchito kokha pa kulambila Yehova. (Eks. 30:34-38) Koma palibe umboni uliwonse woonetsa kuti Akhristu a m’nthawi ya Atumwi anali kufukiza zofukiza pa kulambila kwawo.

^ ndime 9 Kuti mudziŵe zambili za nsembe zaciyanjano, onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, peji 526 na Nsanja ya Olonda ya January 15, 2012, peji 19 ndime 11.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI:Pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, mkulu wa ansembe waciisiraeli anali kuloŵa m’Malo Oyela Koposa atanyamula zofukiza na makala amoto kuti anunkhilitse m’cipindamo na fungo lokoma. Pambuyo pake, anali kuloŵanso m’Malo Oyela Koposa atanyamula magazi a nsembe zophimba macimo.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwisiraeli wapeleka nkhosa kwa wansembe kuti ikhale nsembe yaciyanjano, poonetsa kuti iye na banja lake amayamikila Yehova.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI:Pa utumiki wake wa pa dziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti anali kukonda kwambili Yehova mwa kusunga malamulo ake, ndiponso kuthandiza otsatila ake kusunga malamulowo.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI:Olo kuti sakwanitsa kucita zambili, mlongo wokalamba akupatsa Yehova zabwino koposa mwa kucita ulaliki wa m’makalata.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI:Mu February 2019, M’bale  Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulila, anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso la Cijelemani. Masiku ano, ofalitsa ku Germany, monga alongo aŵiliwa, amakondwela kuseŵenzetsa Baibo yokonzedwanso mu ulaliki.