NKHANI YOPHUNZIRA 47

Zimene Tingaphunzire M’buku la Levitiko

Zimene Tingaphunzire M’buku la Levitiko

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”​2 TIM. 3:16.

NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. N’chifukwa chiyani Akhristu amasiku ano ayenera kuphunzira mwakhama buku la Levitiko?

MTUMWI PAULO anakumbutsa Timoteyo kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Tim. 3:16) Malembawo akuphatikizapo buku la Levitiko. Kodi mumaona kuti bukuli ndi lotani? Ena amaona kuti bukuli ndi la malamulo amene sangatithandize masiku ano. Koma Akhristu enieni samaliona choncho.

2 Buku la Levitiko linalembedwa zaka zoposa 3,500 zapitazo, komabe Yehova anaonetsetsa kuti mawu ake asungidwe kuti ‘azitilangiza.’ (Aroma 15:4) Popeza m’bukuli munalembedwa maganizo a Yehova, tiyenera kuliphunzira mwakhama. Ndipotu pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire m’bukuli. Tiyeni tsopano tikambirane zinthu 4 zimene tingaphunzire.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZISANGALATSA MULUNGU

3. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankapereka nsembe pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo?

3 Phunziro Loyamba: Tiyenera kusangalatsa Yehova kuti azilandira nsembe zathu. Chaka chilichonse pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, Aisiraeli onse ankakumana n’cholinga choti apereke nsembe. Nsembe zimenezi zinkathandiza Aisiraeli kukumbukira kuti ndi ochimwa ndipo ankafunika kuyeretsedwa. Koma mkulu wa ansembe asanapite ndi magazi a nsembezi m’Malo Oyera Koposa, ankayenera kuchita chinthu china chofunika kuposa kuthandiza Aisiraeli kuti akhululukidwe machimo awo.

(Onani ndime 4) *

4. Malinga ndi Levitiko 16:12, 13, kodi mkulu wa ansembe ankachita chiyani ku Malo Oyera Koposa pa ulendo woyamba? (Onani chithunzi chapachikuto.)

4 Werengani Levitiko 16:12, 13. Taganizirani zimene zinkachitika pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Pa tsiku limeneli, mkulu wa ansembe ankalowa katatu m’Malo Oyera Koposa. Pa ulendo woyamba, ankanyamula zofukiza zonunkhira m’dzanja limodzi ndipo dzanja lina ankanyamula chofukizira chagolide chokhala ndi makala amoto. Akayandikira nsalu yotchingira Malo Oyera Koposa ankaima kaye. Ndiyeno ankalowa m’malowo mwaulemu kwambiri n’kupita kukaima pafupi ndi likasa la pangano. Akatero zinkakhala ngati waima pamaso pa Yehova Mulungu. Kenako ankathira zonunkhira zopatulika zija pamakala amotowo mosamala kwambiri ndipo m’chipinda chonsecho munkamveka kafungo kabwino. * Ulendo wachiwiri, ankatenga magazi a nsembe zamachimo n’kulowanso m’Malo Oyera Koposa. Mungaone kuti ankafukiza zonunkhira zopatulikazo asanapite ndi magazi a nsembe zamachimo.

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zofukiza zimene zinkagwiritsidwa ntchito pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo?

5 Kodi tikuphunzira chiyani pa zofukiza zimene zinkagwiritsidwa ntchito pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo? Baibulo limasonyeza kuti mapemphero ovomerezeka a atumiki okhulupirika a Yehova ali ngati zofukiza zonunkhira. (Sal. 141:2; Chiv. 5:8) Kumbukirani kuti mkulu wa ansembe ankapita mwaulemu kwambiri kukapereka zonunkhirazo pamaso pa Yehova. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kupereka mapemphero athu kwa Yehova mwaulemu kwambiri. Timalemekeza kwambiri Mlengi wa chilengedwe chonse komanso kuyamikira kuti amatipatsa mwayi woti tizigwirizana naye ngati mmene bambo amachitira ndi mwana wake. (Yak. 4:8) Ndipo iye amalola kuti tikhale anzake. (Sal. 25:14) Timayamikira mwayi wamtengo wapatali umenewu moti sitifuna kumukhumudwitsa ngakhale pang’ono.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo yoti mkulu wa ansembe ankafukiza kaye zonunkhira asanapereke nsembe?

6 Kumbukirani kuti mkulu wa ansembe ankafunika kufukiza zonunkhira asanapereke nsembe. Zimenezi zinkathandiza kuti Mulungu asangalale naye pamene akupereka nsembezo. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Yesu ali padzikoli, ankafunika kuchita chinthu china chofunika kwambiri kuposa kupulumutsa anthu. Ndipo ankayenera kuchita chinthucho asanapereke moyo wake nsembe. Iye ankafunika kukhala wokhulupirika pa moyo wake n’cholinga choti nsembe yake ikhale yovomerezeka kwa Yehova. Pochita zimenezi, Yesu anasonyeza kuti munthu akamamvera Yehova zinthu zimamuyendera bwino kwambiri. Anasonyezanso kuti Atate wake ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse.

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zonse zimene Yesu ankachita zinkasangalatsa Yehova?

7 Pa nthawi yonse imene Yesu anakhala padziko lapansi, ankatsatira mfundo za Yehova mokhulupirika. Sanalole kuti mayesero, imfa yopweteka kwambiri kapena chinthu china chilichonse chimulepheretse kusonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. (Afil. 2:8) Akakumana ndi mayesero, Yesu ankapemphera “mofuula komanso akugwetsa misozi.” (Aheb. 5:7) Mapemphero akewa anali ochokera pansi pa mtima ndipo anamuthandiza kuti akhalebe womvera. Yehova ankaona kuti mapemphero a Yesu anali ngati kafungo kabwino ka zofukiza. Zonse zimene Yesu ankachita pa moyo wake zinkasangalatsa Yehova komanso kusonyeza kuti Yehovayo ndi woyenera kulamulira.

8. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu?

8 Tikhoza kutsanzira Yesu tikamayesetsa kumvera Yehova mokhulupirika. Tikakumana ndi mayesero tiyenera kumachonderera Yehova kuti atithandize kukhalabe okhulupirika kwa iye. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Timadziwa kuti Yehova sangayankhe mapemphero athu ngati timachita zinthu zosemphana ndi zimene iye amafuna. Koma tikamachita zinthu zimene amasangalala nazo sitikayikira kuti iye amaona kuti mapemphero athu ali ngati zofukiza zonunkhira. Sitikayikiranso kuti kumvera ndi kukhulupirika kwathu kumasangalatsa Atate wathu wakumwamba.​—Miy. 27:11.

TIMATUMIKIRA MULUNGU CHIFUKWA CHOMUYAMIKIRA NDIPONSO KUMUKONDA

(Onani ndime 9) *

9. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankapereka nsembe zachiyanjano?

9 Phunziro lachiwiri: Timatumikira Yehova chifukwa chomuyamikira. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tikambirane za nsembe zachiyanjano zomwe zinali zofunikanso kwa Aisiraeli pa nkhani yolambira. * M’buku la Levitiko timaphunzira kuti Aisiraeli ankatha kupereka nsembe zachiyanjano “posonyeza kuyamikira.” (Lev. 7:11-13, 16-18) Iwo ankapereka nsembezi mwa kufuna kwawo osati chifukwa chotsatira lamulo linalake. Choncho munthu ankasankha yekha kupereka nsembeyi chifukwa chokonda Yehova Mulungu. Munthuyo ankadya nyama imene wapereka nsembeyo limodzi ndi banja lake komanso ansembe. Koma mbali zina za nyamayo ankazipereka kwa Yehova basi. Kodi mbali zake zinali ziti?

(Onani ndime 10) *

10. Kodi nsembe zachiyanjano zotchulidwa pa Levitiko 3:6, 12, 14-16 zimafanana bwanji ndi zimene Yesu ankachita potumikira Atate wake?

10 Phunziro lachitatu: Timachita zonse zimene tingathe potumikira Yehova chifukwa chomukonda. Yehova ankaona kuti mafuta ndi mbali yabwino kwambiri ya nyama. Ananenanso kuti ziwalo zina monga impso zinali zamtengo wapatali. (Werengani Levitiko 3:6, 12, 14-16.) Choncho Yehova ankasangalala kwambiri Aisiraeli akapereka mwa kufuna kwawo mafuta kapena ziwalo ngati zimenezi. Ndipo munthu amene wapereka zimenezi ankasonyeza kuti akufunitsitsa kupatsa Mulungu zinthu zake zamtengo wapatali. Nayenso Yesu anapereka zinthu zake zabwino kwambiri kwa Yehova. Anachita zimenezi pomutumikira ndi mtima wake wonse chifukwa chomukonda. (Yoh. 14:31) Yesu ankasangalala kuchita zimene Mulungu ankafuna ndipo ankakonda kwambiri malamulo ake. (Sal. 40:8) Yehova ayenera kuti ankasangalala kwambiri kuona Yesu akumutumikira ndi mtima wonse.

Timachita zonse zimene tingathe potumikira Yehova chifukwa chomukonda (Onani ndime 11-12) *

11. Kodi zimene timachita potumikira Yehova zimafanana bwanji ndi nsembe zachiyanjano, nanga zimenezi zimatilimbikitsa bwanji?

11 Nafenso timatumikira Yehova mwa kufuna kwathu pofuna kusonyeza kuti timamukonda. Timapatsa Yehova zinthu zathu zabwino kwambiri chifukwa chomukonda ndi mtima wathu wonse. Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona atumiki ake mamiliyoni akumutumikira chifukwa choti amamukonda komanso amakonda njira zake. Timalimbikitsidwa tikakumbukira kuti Yehova amaona zimene timachita komanso chifukwa chimene timachitira zinthuzo ndipo amayamikira. Mwachitsanzo, ngati ndinu achikulire ndipo simungakwanitse kuchita zonse zimene mumafuna, dziwani kuti Yehova amakumvetsani. Mwina mumaona kuti mumachita zochepa, koma Yehova amadziwa kuti mumachita zimene mungathe chifukwa chomukonda kwambiri. Iye amasangalala kulandira zimene mungakwanitse kumupatsa.

12. Kodi tikuphunzira chiyani pa nsembe zachiyanjano?

12 Kodi tikuphunzira chiyani pa nsembe zachiyanjano? Pamene mbali zabwino za nyama zinkapsa, utsi wake unkakwera kumwamba ndipo Yehova ankasangalala. Choncho musamakayikire kuti Yehova amasangalala mukamamutumikira mwa kufuna kwanu komanso ndi mtima wonse. (Akol. 3:23) Iye amayamikira kwambiri zimene mukuchita, kaya zazikulu kapena zazing’ono. Amaona kuti ndi zamtengo wapatali ndipo sadzaziiwala mpaka kalekale.​—Mat. 6:20; Aheb. 6:10.

YEHOVA AKUDALITSA GULU LAKE

13. Malinga ndi Levitiko 9:23, 24, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankasangalala ndi ansembe atsopano?

13 Phunziro la nambala 4: Yehova akudalitsa mbali yapadziko lapansi ya gulu lake. Taganizirani zimene zinachitika mu 1512 B.C.E. pamene Aisiraeli anaimika chihema m’mphepete mwa phiri la Sinai. (Eks. 40:17) Mose anatsogolera pa mwambo woika Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe. Aisiraeli anasonkhana kuti aone ansembe akupereka nsembe za nyama zoyamba. (Lev. 9:1-5) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti akusangalala ndi ansembe atsopanowo? Pamene Aroni ndi Mose ankadalitsa anthu, Yehova anatumiza moto umene unapsereza nsembe zomwe zinatsala paguwa.​—Werengani Levitiko 9:23, 24.

14. Kodi zimene zinachitika poika ansembe a m’banja la Aroni zikutikhudza bwanji masiku ano?

14 Kodi zimene zinachitika pa nthawi yoika ansembe atsopano zinasonyeza chiyani? Zinasonyeza kuti Yehova ankasangalala kwambiri ndi ansembe a m’banja la Aroni. Aisiraeli ataona kuti Yehova akusangalala ndi ansembewo anazindikira kuti ndi bwino kuchita zinthu mogwirizana nawo. Kodi nkhani imeneyi ikutikhudza bwanji masiku ano? Ansembe a ku Isiraeli ankaimira ansembe ena abwino komanso ofunika kwambiri. Yesu ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba kwambiri ndipo pali anthu 144,000 amene adzatumikira naye limodzi kumwamba ngati mafumu ndi ansembe.​—Aheb. 4:14; 8:3-5; 10:1.

Yehova akudalitsa komanso kutsogolera gulu lake. Timayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi gululi (Onani ndime 15-17) *

15-16. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti akugwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?

15 Mu 1919, Yesu anasankha kagulu ka abale odzozedwa kuti kakhale “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Kapolo ameneyu amatsogolera pa ntchito yolalikira ndipo amapereka “chakudya pa nthawi yoyenera” kwa otsatira a Khristu. (Mat. 24:45) Kodi timaona umboni wakuti Yehova akugwiritsa ntchito kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?

16 Satana ndi dziko lakeli akhala akuyesetsa kuti asokoneze kapena kulepheretseratu ntchito imene kapoloyu amagwira. Mwachitsanzo, pachitika mavuto monga nkhondo ziwiri zapadziko lonse, kuzunzidwa kwa anthu a Yehova, mavuto azachuma komanso zinthu zopanda chilungamo. Ngakhale zili choncho, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wakhala akuperekabe chakudya chauzimu kwa otsatira a Khristu. Masiku ano, chakudya chauzimuchi ndi chambiri, chaulere ndipo chikupezeka m’zilankhulo zoposa 900. Umenewu ndi umboni wosatsutsika wakuti Mulungu akugwiritsa ntchito kapoloyu. Umboni wina ndi wakuti ntchito yolalikira ikuyenda bwino kwambiri moti uthenga wabwino ukulalikidwa “padziko lonse lapansi.” (Mat. 24:14) N’zosachita kufunsa kuti Yehova akutsogolera komanso kudalitsa gulu lake masiku ano.

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timachita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova?

17 Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndimayamikira kukhala m’gulu la Yehova?’ M’masiku a Mose ndi Aroni, Yehova anasonyeza kuti akusangalala ndi ansembe atsopano potumiza moto kuchokera kumwamba. Masiku anonso watipatsa umboni woonekeratu wakuti akutsogolera gulu lake. Tiyenera kuyamikira kwambiri zinthu zonse zimene Yehova watipatsa. (1 Ates. 5:18, 19) Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti timachita zinthu mogwirizana ndi gulu limeneli? Tiyenera kutsatira malangizo ochokera m’Malemba amene timalandira m’mabuku athu, kumisonkhano yampingo, yadera komanso yachigawo. Tiyeneranso kugwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu.​—1 Akor. 15:58.

18. Kodi inuyo muziyesetsa kuchita chiyani?

18 Tiyeni tiziyesetsa kutsatira mfundo zimene tikuphunzira m’buku la Levitiko. Tiziyesetsa kusangalatsa Yehova kuti azilandira nsembe zathu. Tizimutumikira chifukwa choyamikira zimene watichitira. Tizichita zonse zimene tingathe potumikira Yehova chifukwa chomukonda ndi mtima wonse. Ndipo tizichita zinthu mogwirizana ndi gulu limene akuligwiritsa ntchito. Tikamachita zonsezi, tidzasonyeza Yehova kuti timayamikira kwambiri mwayi womutumikira komanso wokhala Mboni zake.

NYIMBO NA. 96 Buku la Mulungu Ndi Chuma

^ ndime 5 M’buku la Levitiko muli malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli. N’zoona kuti Akhristufe sitiyendera malamulo amenewo, koma angatithandizebe masiku ano. Munkhaniyi, tikambirana zimene tingaphunzire m’buku la Levitiko.

^ ndime 4 Zonunkhira zimene ankafukiza m’chihema zinali zopatulika kwambiri ndipo Aisiraeli ankazigwiritsa ntchito polambira Yehova basi. (Eks. 30:34-38) Palibe umboni wosonyeza kuti Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito zonunkhirazi polambira Mulungu.

^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri zokhudza nsembe zachiyanjano, onani Nsanja ya Olonda ya January 15, 2012, tsamba 19, ndime 11 komanso buku lakuti Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 526.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, mkulu wa ansembe ankalowa m’Malo Oyera Koposa atatenga zofukiza ndi makala a moto

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Munthu wa ku Isiraeli akupereka nkhosa kwa wansembe kuti ikhale nsembe yachiyanjano posonyeza kuti banja lake lonse limayamikira Yehova.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Yesu ali padzikoli, anasonyeza kuti amakonda kwambiri Yehova potsatira malamulo ake komanso kuthandiza anthu ena kuti aziwatsatira.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo wachikulire sakutha kuchita zambiri koma akupatsa Yehova zimene angathe pogwiritsa ntchito makalata kuti azilalikira.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mu February 2019, M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso m’Chijeremani ndipo anthu anasangalala kwambiri. Masiku ano, ofalitsa ambiri, ngati alongo awiriwa, amasangalala kuligwiritsa ntchito mu utumiki.