Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufufuza Choonadi

Kufufuza Choonadi

Kudziwa zoona kungapulumutse moyo. Mwachitsanzo, taganizirani mmene kudziwa yankho lolondola la funso ili kwakhudzira moyo wathu: Kodi matenda opatsirana amafalikira bwanji?

Kwa zaka zambiri palibe amene ankadziwa yankho la funsoli ndipo miliri inapulula miyoyo ya anthu ambiri. Koma m’kupita kwa nthawi asayansi anadziwa zoona pa nkhaniyi. Anatulukira kuti matenda ambiri amayambitsidwa ndi majeremusi monga mabakiteriya ndi mavailasi, tomwe ndi tizilombo tating’ono kwambiri. Kudziwa mfundo yolondola imeneyi kwathandiza anthu kuti azitha kupewa komanso kuchiza matenda ambiri. Zimenezi zachititsa kuti anthu ambiri azikhala athanzi komanso azikhala ndi moyo wotalikirapo.

Koma pali mafunso enanso ofunika kwambiri. Kodi mukuganiza kuti kudziwa zolondola pa mafunso otsatirawa kungakuthandizeni bwanji?

  • Kodi Mulungu ndi ndani?

  • Kodi Yesu Khristu ndi ndani?

  • Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

  • Kodi m’tsogolomu muchitika zotani?

Pali anthu ambiri amene anapeza mayankho olondola a mafunso amenewa ndipo zimenezi zasintha kwambiri moyo wawo. Kudziwa mayankho a mafunsowa kungakuthandizeninso inuyo.

KODI N’ZOTHEKA KUDZIWA CHOONADI?

Mwina mungafunse kuti, ‘Kodi n’zotheka kudziwa zolondola pa nkhani inayake?’ Ndipotu masiku ano pali zinthu zambiri zomwe kudziwa zoona zake kumakhala kovuta kwambiri. N’chifukwa chiyani zili choncho?

Anthu ambiri sakhulupirira kuti boma, amalonda komanso ofalitsa nkhani angawauze zoona. Amaona kuti zimakhala zovuta kusiyanitsa ngati zimene munthu akunena zili zoona kapena akungonena maganizo ake, ngati waphatikizamo bodza, kapenanso ngati lonselo ndi bodza lankunkhuniza. Popeza masiku ano anthu ambiri sakhulupirirana komanso mfundo zambiri zimakhala zabodza, anthu ena ngakhale atauzidwa mfundo zoona komanso mmene zingawathandizire, amatsutsabe.

Ngakhale kuti pali mavuto onsewa, n’zotheka kupeza mayankho olondola a mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Zingatheke ngati mutatsatira zimene mumachita tsiku ndi tsiku mukafuna kudziwa zoona pa nkhani inayake.

MMENE MUNGAFUFUZIRE KUTI MUDZIWE CHOONADI

Tingati anthufe tsiku lililonse timafufuza kuti tidziwe zoona pa nkhani inayake. Taganizirani chitsanzo cha mayi wina dzina lake Jessica. Iye anati: “Mwana wanga amadana kwambiri ndi mtedza, moti atati adye chakudya chimene muli mapulotini ochokera ku mtedza, ngakhale ochepa kwambiri, akhoza kufa.” Jessica amafunika kudziwa kuti chakudya chimene akugula sichingabweretse mavuto kwa mwana wake. Iye anati: “Choyamba ndimawerenga zimene alemba papaketi yake kuti ndidziwe zinthu zimene anagwiritsa ntchito popanga chakudyacho. Kenako ndimafufuzanso zambiri ndipo mpaka pena ndimafunsa amene anapanga chakudyacho kuti anditsimikizire ngati sichingabweretse mavuto kwa mwana wanga. Ndimafufuzanso kwa anthu odalirika kuti ndidziwe ngati kampaniyo ili ndi mbiri yoti imapanga zakudya zabwino.”

Mwina sikuti inuyo mumafunika kufufuza zinthu zovuta ngati mmene amachitira Jessica. Komabe mofanana ndi mayi ameneyu mungachite zinthu zotsatirazi kuti mudziwe zolondola pa nkhani inayake.

  • Pezani mfundo zokhudza nkhaniyo.

  • Fufuzani kuti mudziwe zambiri.

  • Onetsetsani kuti mukufufuza kwa anthu kapena zinthu zodalirika.

Mukhoza kugwiritsanso ntchito njira yomweyi kuti mupeze mayankho a mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

BUKU LIMENE LIMANENA ZOONA

Pofufuza choonadi cha m’Baibulo, Jessica anagwiritsanso ntchito njira imene amagwiritsa ntchito akamafufuza zokhudza chakudya cha mwana wake. Iye anati: “Kuwerenga mosamala komanso kufufuza mwakhama kunandithandiza kuti ndipeze choonadi cha m’Baibulo.” Mofanana ndi Jessica, anthu ambiri adziwa zimene Baibulo limanena pa mafunso otsatirawa:

  • Kodi cholinga cha moyo n’chiyani?

  • N’chiyani chimachitika munthu akamwalira?

  • N’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto?

  • Kodi Mulungu akuchita chiyani kuti athetse mavuto padzikoli?

  • Kodi tingatani kuti tikhale ndi banja losangalala?

Mungathe kupeza mayankho olondola a mafunso amenewa ndi enanso ambiri ngati mutawerenga Baibulo komanso kufufuza zambiri pa webusaiti ya www.pr418.com.