Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu

Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu

Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Kodi palipano ucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kupemphela kuti ubwele?

Yesu Ndiye Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.

Luka 1:31-33: “Udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzachedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wacifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulila monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti Ufumu wake sudzatha konse.”

Ufumu wa Mulungu ndiye inali nkhani yaikulu ya ulaliki wa Yesu.

Mateyu 9:35: “Yesu anayamba ulendo woyendela mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikila uthenga wabwino wa ufumu ndi kucilitsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.”

Yesu anapatsa ophunzila ake cizindikilo coŵathandiza kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwela.

Mateyu 24:7: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”

Ophunzila a Yesu palipano akulalikila za Ufumu wa Mulungu pa dziko lonse lapansi.

Mateyu 24:14: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”