Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Sankhani Kucilikiza Ufumu wa Mulungu Palipano!

Sankhani Kucilikiza Ufumu wa Mulungu Palipano!

Yelekezani kuti kubwela cimvula camphamvu cimene cidzapangitsa madzi kusefukila. Ndiyeno anthu a boma akupeleka cenjezo kuti mucitepo kanthu mwamsanga. Iwo afuula kuti: “THAŴANI! THAŴILANI KU MTUNDA MWAMSANGA!” Kodi cinthu canzelu cimene mungacite n’ciani? Mosakaikila, mungathaŵile ku mtunda.

Mofananamo, tonsefe tiyembekezela cocitika coopsa cimene cili monga “cimvula camphamvu copangitsa madzi kusefukila,” cimene Yesu anachula kuti “cisautso cacikulu.” (Mateyu 24:21) Sitingacithaŵe cocitika coopsa cimeneci. Koma pali cimene tingacite kuti tidziteteze. Kodi tingacite ciani?

Paulaliki wake wa pa phili, Yesu Khristu anapeleka malangizo aya: “Pitilizani kufunafuna Ufumu [wa Mulungu] coyamba ndi cilungamo cake.” (Mateyu 6:33) Kodi tingacite bwanji zimenezo?

Funa-funani Ufumu wa Mulungu coyamba. Izi zitanthauza kuti tiyenela kuona Ufumu wa Mulungu kukhala wofunika kwambili kuposa cina ciliconse. (Mateyu 6:25, 32, 33) N’cifukwa ciani tiyenela kuuona conco? Cifukwa anthu sangakwanitse kucotsapo mavuto a anthu. Ni Ufumu wa Mulungu cabe umene ungakwanitse kugwila nchito yovuta imeneyi.

Funa-funani cilungamo cake. Tiyenela kuyesetsa kukhala umoyo woyendela malamulo olungama a Mulungu na mfundo zake. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati tidzisankhila tekha cabwino na coipa, zotulukapo zake zidzakhala zoipa. (Miyambo 16:25) Koma ngati titsatila miyezo ya Mulungu zinthu zimatiyendela bwino, komanso timakondweletsa Mulungu.—Yesaya 48:17, 18.

Pitilizani kufuna-funa Ufumu wa Mulungu coyamba na cilungamo cake. Yesu anacenjeza kuti ena adzabwelela m’mbuyo cifukwa coganiza kuti adzakhala otetezeka mwa kupanga ndalama zambili. Ndipo ena adzalola nkhawa za umoyo kuwatangwanitsa, cakuti sadzakhala na nthawi yofuna-funa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 6:19-21, 25-32.

Komabe, Yesu analonjeza kuti amene amacilikiza Ufumu wa Mulungu adzakhala na zofunikila palipano, komanso adzakondwela na madalitso osatha kutsogolo.—Mateyu 6:33.

Ngakhale kuti ophunzila a Yesu m’nthawi ya atumwi anali kufuna-funa Ufumu wa Mulungu na cilungamo cake, sanaone kutha kwa zoŵaŵa zonse na mavuto m’nthawi yawo. Komabe iwo anali otetezeka. Motani?

Cifukwa coyendela miyezo yolungama ya Mulungu, iwo anatetezeka ku mavuto amene anthu onyalanyaza zimene Mulungu anakamba anali kukumana nawo. Cikhulupililo cawo colimba cakuti Ufumu wa Mulungu udzabwela, cinaŵathandiza kupilila mavuto aakulu kwambili. Ndiponso Mulungu anaŵapatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti apilile.—2 Akorinto 4:7-9.

KODI MUDZAFUNA-FUNA UFUMU WA MULUNGU COYAMBA?

Akhristu m’nthawi ya atumwi anamvela lamulo la Yesu la kufuna-funa Ufumu coyamba. Iwo analalikila uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu onse. (Akolose 1:23) Kodi alipo amene akucita zimenezi masiku ano?

Inde! Mboni za Yehova zimadziŵa kuti nthawi yotsala kuti Ufumu wa Mulungu ucotsepo dongosolo lino la zinthu ni yaifupi. Conco, amacita zonse zotheka kuti agwile nchito imene Yesu anakamba. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.

Kodi mudzacita ciani mukamvetsela uthenga wabwino umenewo? Tikulimbikitsani kutengela citsanzo ca anthu a m’nthawi ya atumwi amene anali kukhala mu mzinda wa Makedoniya ku Bereya. Anthuwo atamva uthenga wabwino wa Ufumu kucokela kwa mtumwi Paulo, analandila uthengawo “ndi cidwi cacikulu kwambili.” Iwo “anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizile ngati zimene anamvazo zinali zoona,” ndipo anacitapo kanthu pa zimene anaphunzila.—Machitidwe 17:11, 12.

Mungacitenso cimodzi-modzi. Mwa kufuna-funa Ufumu wa Mulungu coyamba na cilungamo cake, mudzakhala otetezeka palipano, ndipo kutsogolo mudzakondwela na mtendele wosatha komanso citetezo.