CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzithandiza Ena Kuti Azichita Zambiri

Muzithandiza Ena Kuti Azichita Zambiri

Moredekai anapereka chitsanzo chabwino cha kukhala wolimba mtima komanso wokhulupirika kwa Yehova (Est 3:​2-4; it-2 431:7)

Anathandiza Esitere kuona kuti akhoza kuchita zabwino (Est 4:​7, 8; it-2 431:9)

Analimbikitsa Esitere kuti akhale wolimba mtima komanso azidalira Yehova (Est 4:​12-14; ia 16:22-23)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi zolankhula komanso zochita zanga zimathandiza ena mumpingo kuti azichita zambiri potumikira Yehova?’