Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani

Muzidalira Yehova Anzanu Akamakuvutitsani

Kuvutitsidwa ndi anthu ena kungachititse kuti tizimva kupweteka komanso tisamasangalale. Kungachititsenso kuti ubwenzi wathu ndi Yehova usokonekere ngati tikuopsezedwa chifukwa cha chikhulupiriro chathu. Kodi mungatani kuti anzanu asamakuvutitseni?

Kudalira Yehova kwathandiza atumiki ambiri kuti akwanitse kupirira pamene anzawo akuwavutitsa. (Sl 18:17) Mwachitsanzo, Esitere analankhulapo kuti aulule mapulani oipa a Hamani. (Est 7:​1-6) Asanachite zimenezi anasala kudya posonyeza kuti ankadalira Yehova. (Est 4:​14-16) Yehova anamudalitsa komanso anamuteteza limodzi ndi anthu a mtundu wake.

Achinyamatanu, ngati anthu ena amakuvutitsani, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni ndipo muziuza munthu wina wachikulire, mwachitsanzo makolo anu. Mungakhale otsimikiza kuti Yehova akuthandizani ngati mmene anathandizira Esitere. Kodi mungachitenso chiyani anzanu akamakuvutitsani?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MOYO WANGA WACHINYAMATA—NDINGATANI NGATI ANZANGA AMANDIVUTITSA?, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi achinyamata angaphunzirepo chiyani kwa Charlie ndi Ferin?

  • Kodi makolo angaphunzire chiyani zokhudza kuthandiza ana awo kuchokera pa zimene Charlie ndi Ferin ananena?