Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRITU

Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvela Cisoni Mumtima Mwawo

Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvela Cisoni Mumtima Mwawo

Aliyense wa ife amamva cisoni nthawi zina. Ndipo kumva cisoni si cizindikilo cakuti ndife ofooka mwauzimu. Malemba amaonetsa kuti ngakhale Yehova amene, amamva cisoni nthawi zina. (Gen. 6:​5, 6) Koma bwanji ngati timakhala na cisoni cacikulu kaŵili-kaŵili kapena nthawi zonse?

Pemphani thandizo kwa Yehova. Yehova amacita cidwi kwambili na mmene timamvela. Amadziŵa ngati ndife osangalala kapena acisoni. Komanso amadziŵa cifukwa cake timamva mwanjila imeneyo. (Sal. 7:9b) Coposa zonse, Yehova amasamala za ife, ndipo angatithandize tikakhala na cisoni ngakhale tikapsinjika maganizo.—Sal. 34:18.

Tetezani maganizo anu. Maganizo olefula angatilande cimwemwe komanso angasokoneze kulambila kwathu. Ndiye cifukwa cake tiyenela kuteteza mtima wathu, kapena kuti umunthu wathu wamkati.—Miy. 4:23.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MMENE ABALE AKUKHALILABE PA MTENDELE OLO KUTI ALI NA VUTO LA KUPSINJIKA MAGANIZO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Ni zinthu ziti zimene Nikki anacita polimbana na vuto lake la kupsinjika maganizo?

  • N’cifukwa ciyani Nikki anaona kuti ayenela kulandila thandizo la ku cipatala?—Mat. 9:12

  • Kodi Nikki anaonetsa m’njila ziti kuti anali kudalila thandizo la Yehova?