Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Cikondi ca Mulungu Cosasintha Cimatiteteza ku Mabodza a Satana

Cikondi ca Mulungu Cosasintha Cimatiteteza ku Mabodza a Satana

Satana amafuna kuti anthu azikhulupilila kuti Yehova ndiye amacititsa zinthu zoipa (Yobu 8:4)

Iye amafuna tiziganiza kuti Yehova alibe nazo kanthu zakuti kaya ndife okhulupilika kwa iye kapena ayi (Yobu 9:​20-22; w15 7/1 12 ¶3)

Cikondi ca Yehova cosasintha cimatiteteza kuti tisasoceletsedwe na mabodza a Satana komanso kuti tikhalebe okhulupilika (Yobu 10:12; Sal. 32:​7, 10; w21.11 6 ¶14)

YESANI KUCITA IZI: Kuti mukhalebe wolimba pokumana na mayeso, ganizilani mmene Yehova akuonetsela cikondi cake cosasintha kwa inu. Kenako lembani zimene mwapeza na kumaziŵelenga kaŵili-kaŵili.