Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Thandizani Anthu Osapembedza Kudziŵa Mlengi Wawo

Thandizani Anthu Osapembedza Kudziŵa Mlengi Wawo

Kodi mumazengeleza kulalikila anthu osapembedza poganiza kuti sadzamvetsela uthenga wanu? Ngati n’conco, kumbukilani kuti anthu ambili osapembedza, kuphatikizapo osakhulupilila Mulungu, afika pokhala Mboni za Yehova. Nthawi zambili, iwo anali kungofunika kuwathandiza kupeza umboni wakuti Mulungu aliko.—Aroma 1:20; 10:14.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUMBUKILANI—ANTHU OPANDA CIKHULUPILILO ANGAPEZE CIKHULUPILILO!—ANTHU OSAPEMBEDZA, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

Kodi cocitika ca Tommaso cakuthandizani bwanji kukhala na maganizo oyenela pa nkhani yolalikila anthu osapembedza?