Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Makolo—Thandizani Ana Anu Kupeza Nzelu ya Umulungu

Makolo—Thandizani Ana Anu Kupeza Nzelu ya Umulungu

Imodzi mwa njila zabwino zimene makolo angathandizile ana awo kupeza nzelu za umulungu ni kuwathandiza kupindula na misonkhano yacikhristu. Zimene acicepele amaona, kumva, komanso kukamba m’ndemanga zawo pa misonkhano, zimawathandiza kuphunzila za Yehova komanso kukhala bwenzi lake la pamtima. (Deut. 31:​12, 13) Ngati ndinu kholo, mungam’thandize bwanji mwana wanu kuti azipindula kwambili na misonkhano?

  • Muziyesetsa kupezeka pa misonkhano ya pamaso-mpamaso.—Sal. 22:22

  • Pezani nthawi yokhala na maceza olimbikitsa pa Nyumba ya Ufumu misonkhano isanayambe kapena pambuyo pake.—Aheb. 10:25

  • Onetsetsani kuti aliyense m’banja ali naco cofalitsa cimene cikuphunzilidwa pa misonkhano, kaya ca pacipangizo kapena copulintidwa

  • Thandizani mwana wanu kukonzekela ndemanga m’mawu ake-ake.—Mat. 21:​15, 16

  • Muzikamba zinthu zolimbikitsa ponena za misonkhano komanso zimene timaphunzila

  • Thandizani ana anu kugwilako nchito yoyeletsa Nyumba ya Ufumu komanso kuceza na acikulile a mumpingo mwanu

• Kuthandiza ana kuyandikila Yehova ni nchito yaikulu, ndipo nthawi zina ingaoneke yolemetsa kwambili. Komabe, dziŵani kuti Yehova adzakuthandizani.—Yes. 40:29.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI MAKOLO, DALILANI YEHOVA NA MPHAMVU ZAKE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi kukhala olema kunam’khudza bwanji Zack na mkazi wake Leah?

  • N’cifukwa ciyani makolo ayenela kuyang’ana kwa Yehova kuti awapatse mphamvu?

  • Kodi Zack na Leah anadalila Yehova m’njila ziti kuti awathandize?