MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kupeza Nzeru Zochokera kwa Mulungu

Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kupeza Nzeru Zochokera kwa Mulungu

Njira imodzi imene makolo angathandizire ana awo kupeza nzeru zochokera kwa Mulungu, ndi kuwathandiza kuti azipindula ndi misonkhano ya Chikhristu. Zomwe ana amaona, kumva komanso kufotokoza mu ndemanga zimene amapereka pamisonkhano zimawathandiza kudziwa zokhudza Yehova komanso kukhala anzake apamtima. (De 31:​12, 13) Ngati ndinu kholo, kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti azipindula kwambiri ndi misonkhano?

  • Muziyesetsa kupezeka pa misonkhano ya mpingo pamasom’pamaso ku Nyumba ya Ufumu.—Sl 22:22

  • Muzikhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi abale ndi alongo pa Nyumba ya Ufumu misonkhano isanayambe kapena ikatha.—Ahe 10:25

  • Muzionetsetsa kuti aliyense m’banja lanu ali ndi mabuku kapena magazini ophunzirira pamisonkhano, kaya a pazipangizo zamakono kapena osindikizidwa

  • Muzithandiza mwana wanu kukonzekera kukapereka ndemanga m’mawu akeake.—Mt 21:​15, 16

  • Muzilankhula zinthu zabwino zokhudza misonkhano komanso zimene timaphunzirako

  • Muzithandiza ana anu kuti azichita nawo zinthu zosiyanasiyana monga kuyeretsa pa Nyumba ya Ufumu kapena kucheza ndi abale ndi alongo achikulire a mumpingo mwanu

Kuthandiza ana anu kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova kumafuna khama, ndipo nthawi zina kungaoneke ngati kovuta kwambiri. Komabe mukhoza kukhala otsimikiza kuti Yehova akuthandizani.—Yes 40:29.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MAKOLO, MUZIDALIRA YEHOVA KUTI AZIKUPATSANI MPHAMVU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi kutopa chifukwa chosamalira mwana, kunakhudza bwanji Zack ndi Leah?

  • N’chifukwa chiyani makolo ayenera kudalira Yehova kuti awapatse mphamvu?

  • Kodi Zack ndi Leah anasonyeza bwanji kuti amadalira Yehova kuti awathandize?