Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 1

‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’

‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’

LEMBA LA CAKA CA 2020: Pitani mukaphunzitse anthu . . . , kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza.”​—MAT. 28:19.

NYIMBO 79 Aphunzitseni Kucilimika

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi mngelo anawauza ciani azimayi atafika ku manda a Yesu? Nanga Yesu anawapatsa malangizo otani?

YELEKEZELANI kuti mukuona zimene zinacitika m’maŵa pa Nisani 16, m’caka ca 33 C.E. Azimayi oopa Mulungu akupita ku manda kumene anaika mtembo wa Yesu kuti akaudzoleke mafuta onunkhila na zonunkhilitsa. Iwo ali na cisoni cacikulu. Apa n’kuti mtembo wa Ambuye Yesu Khristu wakhala m’manda kwa masiku aŵili. Azimayiwo atafika ku mandako, akudabwa kuona kuti m’mandamo mulibe mtembo wa Yesu. Kenako, mngelo akuwauza kuti Yesu wauka kwa akufa, ndipo akuwauzanso kuti: “Watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona.”—Mat. 28:1-7; Luka 23:56; 24:10.

2 Azimayiwo atacoka ku mandako, Yesu anaonekela kwa iwo na kuwapatsa malangizo akuti: “Pitani, kauzeni abale anga, kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.” (Mat. 28:10) Yesu ataukitsidwa, cinthu coyamba cimene anacita ni kupanga makonzedwe okakumana na ophunzila ake ku Galileya. Conco, iye ayenela kuti anali kufuna kupatsa ophunzilawo malangizo enaake ofunika kwambili.

N’NDANI ANALAMULIDWA KUGWILA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA?

Yesu ataukitsidwa anakumana na atumwi ake na ophunzila ena ku Galileya, ndipo anawalamula kuti “pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzila anga”(Onani ndime 3-4)

3-4. N’cifukwa ciani tikamba kuti lamulo la pa Mateyu 28:19, 20, Yesu sanalipeleke kwa atumwi ake okha? (Onani cithunzi pa cikuto.)

3 Ŵelengani Mateyu 28:16-20. Pa nthawi imene Yesu anasonkhana na ophunzila ake pa phili la ku Galileya, anawafotokozela nchito yofunika kwambili imene iwo anafunika kugwila pa nthawiyo. Nchitoyo ni imenenso ife timacita masiku ano. Yesu anati: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga . . . ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.”

4 Yesu amafuna kuti otsatila ake onse azilalikila. Lamulo limeneli sanalipeleke cabe kwa atumwi ake 11 okhulupilika. Tidziŵa bwanji zimenezi? Cabwino, kodi ni atumwi okha amene analipo pamene Yesu anali kupeleka lamuloli pa phili la ku Galileya? Iyai. Kumbukilani kuti mngelo anauza azimayi aja kuti: Mukamuona  [ku Galileya].” Conco, n’zoonekelatu kuti azimayi ena okhulupilika naonso analipo pa msonkhanowo. Koma palinso umboni wina. Mtumwi Paulo anakamba kuti Yesu “anaonekelanso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.” (1 Akor. 15:6) Kodi anaonekela kuti?

5. Kodi tiphunzilapo ciani pa 1 Akorinto 15:6?

5 Pali zifukwa zomveka zokhulupilila kuti pa 1 Akorinto 15:6, Paulo anali kukamba za msonkhano wa ku Galileya wochulidwa m’caputa 28 ca Mateyu. Kodi zifukwazo ni ziti? Cifukwa coyamba n’cakuti ophunzila ambili a Yesu anali a ku Galileya. Conco, cinali cosavuta kucita msonkhano wa anthu ambili pa phili ku Galileya kusiyana na kucitila m’nyumba ya munthu ku Yerusalemu. Caciŵili, Yesu woukitsidwayo anali ataonekela kale kwa atumwi ake 11 m’nyumba ya munthu wina ku Yerusalemu. Iye akanakhala kuti anali kufuna kupatsa atumwi okha lamulo la kulalikila na kupanga ophunzila, sembe anawauzila ku Yerusalemu komweko m’malo mowauza kuti akakumane naye ku Galileya, pamodzi na azimayi komanso anthu ena.—Luka 24:33, 36.

6. Kodi lemba la Mateyu 28:20 lionetsa bwanji kuti lamulo lopanga ophunzila limagwilanso nchito kwa atumiki a Mulungu masiku ano? Nanga ni anthu oculuka motani amene akumvela lamulo limeneli?

6 Palinso mfundo ina yofunika kwambili imene tiyenela kuiganizila. Yesu sanapeleke lamulo lopanga ophunzila kwa Akhristu a m’nthawi yake okha. N’cifukwa ciani takamba zimenezi? Cifukwa Yesu anatsiliza kupeleka malangizo kwa otsatila ake na mawu akuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Mogwilizana na zimene Yesu anakamba, masiku ano pali anthu ambili amene akugwila nchito yopanga ophunzila. Ganizilani cabe, caka ciliconse anthu pafupi-fupi 300,000 amabatizika kukhala Mboni za Yehova komanso ophunzila a Yesu Khristu!

7. Kodi tsopano tidzakambilana ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

7 Anthu ambili amene timaphunzila nawo Baibo amapita patsogolo mpaka kubatizika. Koma anthu ena amene timaphunzila nawo amayopa kukhala ophunzila a Khristu. Amakondwela tikamaphunzila nawo, koma sapita patsogolo kuti akabatizike. Ngati imwe mumaphunzila Baibo na winawake, tikhulupilila kuti mumafuna kuthandiza wophunzilayo kuseŵenzetsa zimene amaphunzila, komanso kukhala wophunzila wa Khristu. M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingam’fikile pamtima wophunzila na mmene tingam’thandizile kuti apite patsogolo mwauzimu. N’cifukwa ciani tifunika kukambilana zimenezi? Cifukwa cakuti pa nthawi ina tingafunike kusankha kupitiliza kuphunzila Baibo na munthu kapena kuleka.

YESETSANI KUWAFIKA PA MTIMA OPHUNZILA

8. N’cifukwa ciani nthawi zina zimavuta kuthandiza wophunzila Baibo kuyamba kukonda Yehova?

8 Yehova amafuna kuti anthu azimutumikila cifukwa comukonda. Conco, colinga cathu ni kuthandiza wophunzila kudziŵa kuti Yehova amam’dela nkhawa ndiponso kuti amam’konda kwambili. Timafuna kum’thandiza kuti aziona Yehova monga “tate wa ana amasiye ndi woweluzila akazi amasiye milandu.” (Sal. 68:5) Ophunzila Baibo akazindikila kuti Mulungu amawakonda, nawonso amayamba kum’konda ngako. Koma ophunzila ena cingawavute kuti ayambe kuona Yehova monga Tate wawo wacikondi cifukwa atate awo akuthupi sanali kuwaonetsa cikondi na cifundo. (2 Tim. 3:1, 3) Conco, pamene mutsogoza phunzilo, muzigogomeza kwambili pa makhalidwe ocititsa cidwi a Yehova. Thandizani wophunzila Baibo kuzindikila kuti Mulungu wathu wacikondi amafuna kuti iye akapeze moyo wamuyaya, ndipo ni wofunitsitsa kum’thandiza kuti akaupeze. N’ciani cinanso cimene tingacite kuti timufike pa mtima wophunzila?

9-10. Kodi tiyenela kuseŵenzetsa mabuku ati pophunzila Baibo ndi anthu? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuseŵenzetsa mabuku amenewa?

9 Seŵenzetsani mabuku akuti, “Zimene Baibulo Ingatiphunzitse” na “Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu.” Mabuku amenewa anapangidwa na colinga cakuti azitithandiza kuwafika pa mtima ophunzila Baibo. Mwacitsanzo, nkhani 1 m’buku yakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse iyankha mafunso aya: Kodi Mulungu amatidela nkhawa kapena ni wankhanza?, Kodi Mulungu amamvela bwanji ngati anthu avutika?, komanso lakuti Kodi inu mungakhale bwenzi la Yehova? Nanga bwanji za buku lakuti Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu? Buku limeneli lidzathandiza wophunzila kuzindikila kuti kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo kungamuthandize kukhala na umoyo wabwino na kulimbitsa ubwenzi wake na Yehova. Ngakhale kuti mwina tinaseŵenzetsapo kale bukuli pophunzila Baibo na ophunzila ena, tifunikabe kukonzekela bwino phunzilo lililonse. Ndipo pokonzekela, tiziganizila zosoŵa za wophunzila aliyense.

10 Koma bwanji ngati wophunzila afuna kumvetsetsa nkhani inayake, koma nkhaniyo siipezeka mu zofalitsa zophunzitsila anthu Baibo? Mwina mungamulimbikitse kuti akaŵelenge payekha nkhaniyo mu cofalitsaco, n’colinga cakuti mupitilize kutsogoza phunzilo pogwilitsila nchito zofalitsa zoyenelela zimene tachula m’ndime yapita.

Yambani phunzilo na pemphelo (Onani ndime 11)

11. Ni liti pamene tingayambe kupemphela pa phunzilo la Baibo? Nanga mungayambe bwanji kukambilana nkhaniyi na wophunzila?

11 Yambani phunzilo na pemphelo. Nthawi zambili, ngati taphunzila na munthu kangapo ndipo taona kuti phunzilo lidzapitiliza, cimakhala bwino kuyamba mwamsanga kupemphela pa phunzilolo. Tifunika kuthandiza wophunzila kuzindikila kuti tingathe kumvetsetsa Mawu a Mulungu kokha mothandizidwa na mzimu woyela wa Mulungu. Ofalitsa ena pofuna kuthandiza wophunzila Baibo kuona kufunika koyamba phunzilo na pemphelo, amaŵelenga Yakobo 1:5, imene imati: “Ngati wina akusowa nzelu, azipempha kwa Mulungu.” Kenako wofalitsayo amafunsa wophunzilayo kuti, “Kodi tingapemphe bwanji nzelu kwa Mulungu?” Mwacidziwikile, wophunzilayo adzayankha kuti tifunika kupemphela kwa Mulungu.

12. Mungaseŵenzetse bwanji Salimo 139:2-4 pothandiza wophunzila kuti azipeleka mapemphelo ocokela pansi pa mtima?

12 Phunzitsani wophunzila Baibo kupemphela. M’tsimikizileni wophunzila kuti Yehova amafuna kumvetsela mapemphelo ake ocokela pansi pa mtima. Mufotokozeleni kuti m’mapemphelo athu aumwini, tingamuuze Yehova za mu mtima mwathu, ngakhale zinthu zimene mwina sitingafune kuuza wina aliyense. Ndipo kumbukilani kuti Yehova amadziŵa za mu mtima mwathu. (Ŵelengani Salimo 139:2-4.) Cina, tingamulimbikitse kuti azipempha Mulungu kuti amuthandize kusintha maganizo olakwika na zizoloŵezi zoipa. Mwacitsanzo, wophunzilayo angakhale kuti amakonda cikondwelelo cinacake cosagwilizana na Malemba. Iye amadziŵa kuti n’kulakwa kucitako cikondweleloco. Koma amakondabe zinthu zina zimene zimacitika pa cikondweleloco. Ngati n’conco, m’limbikitseni kuti azipemphela kwa Yehova na kumuuza mosapita m’mbali mmene amamvelela, komanso kumupempha kuti amuthandize kukonda cabe zinthu zimene Mulungu amaona kuti n’zabwino.—Sal. 97:10.

Itanilani wophunzila Baibo ku misonkhano (Onani ndime 13)

13. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuyamba mwamsanga kuitanila wophunzila Baibo ku misonkhano? (b) Nanga tingathandize bwanji wophunzila kukhala womasuka pa Nyumba ya Ufumu?

13 Musacedwe kuitanila wophunzila Baibo ku misonkhano. Zimene wophunzila angaone na kumvetsela pa misonkhano zingamuthandize kuti apite patsogolo na kuyamba kutumikila Yehova. M’tambitseni vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? ndipo mulimbikitseni kuti mukapitile naye pamodzi ku misonkhano. Ngati n’zotheka, muuzeni kuti mudzamukonzela mayendedwe. Cinanso, mungacite bwino kwambili kutengako ofalitsa osiyana-siyana pamene mupita kukatsogoza phunzilo. Izi zidzathandiza wophunzilayo kudziŵana na abale na alongo mu mpingo, ndipo adzakhala womasuka akapezeka pa misonkhano.

THANDIZANI WOPHUNZILA KUKULA MWAUZIMU

14. N’ciani cingasonkhezele wophunzila kukula mwauzimu?

14 Colinga cathu n’kuthandiza wophunzila Baibo kukula mwauzimu. (Aef. 4:13) Munthu akavomeleza kuphunzila nafe Baibo, kaŵili-kaŵili amaganizila kwambili za mmene iye payekha adzapindulila na phunzilolo. Koma cikondi cake pa Yehova cikamakula, amayamba kuganizila mmene angathandizile ena, kuphatikizapo abale na alongo mu mpingo. (Mat. 22:37-39) Pa nthawi imene muona kuti ni yoyenela, musalephele kumudziŵitsa za mwayi wocilikiza nchito yolalikila za Ufumu mwa kupeleka zopeleka.

Thandizani wophunzila Baibo kudziŵa zimene angacite akakumana na mavuto (Onani ndime 15)

15. Tingam’thandize bwanji wophunzila Baibo kudziŵa zoyenela kucita pakabuka mavuto?

15 Thandizani wophunzila Baibo kudziŵa zimene angacite pakabuka mavuto. Mwacitsanzo, tiyelekeze kuti wophunzila Baibo wanu, amene ni wofalitsa wosabatizika, wakuuzani kuti winawake mu mpingo wamukhumudwitsa. M’malo moikila kumbuyo mmodzi wa iwo, bwanji osamufotokozela wophunzilayo zimene angacite mogwilizana na Malemba? Wophunzilayo angasankhe kum’khululukila m’baleyo na kuiŵalako za nkhaniyo. Kapena ngati n’zovuta kungonyalanyaza nkhaniyo, angakambilane na m’bale amene wamulakwilayo mokoma mtima ndi mwacikondi, n’colinga cakuti ‘abweze m’bale wakeyo.’ (Yelekezelani na Mateyu 18:15.) Thandizani wophunzilayo kukonzekela zimene akakambe. M’phunzitseni mmene angaseŵenzetsele JW Library®, Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, na jw.org® kuti adziŵe zimene angacite kuti athetse nkhaniyo. Wophunzila akadziŵa mothetsela mavuto asanabatizike, ndiye kuti akakabatizika cidzakhala cosavuta kugwilizana na abale na alongo mu mpingo.

16. N’cifukwa ciani zili bwino kupempha ofalitsa ena kuti apite nanu pokatsogoza phunzilo?

16 Pemphani ena mu mpingo kapena woyang’anila dela pamene acezela mpingo wanu kuti apite nanu ku phunzilo. Cifukwa ciani? Kuonjezela pa zifukwa zimene tachula kale, kucita izi n’kofunika cifukwa ofalitsa ena angapeleke thandizo kwa wophunzilayo, limene mwina imwe simungakwanitse kupeleka. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti wophunzilayo wakhala akuyesetsa kuti aleke kupepa fwaka, koma zakhala zikumuvuta. Zikakhala telo, mungapite ku phunzilolo na wofalitsa amene kale anali na cizoloŵezi coipaci koma anakwanitsa kuleka, olo kuti poyamba zinali kumuvuta. Wofalitsa winayo angapeleke malangizo othandiza kwa wophunzilayo. Ngati simumasuka kutsogoza phunzilo pa maso pa m’bale waluso komanso wodziŵa zambili, mungapemphe m’baleyo kuti atsogoze phunzilo pa nthawiyo. Mukamapempha ena kupita nanu ku phunzilo, wophunzilayo adzapindula kwambili na malangizo awo. Kumbukilani kuti colinga cathu ni kuthandiza wophunzila kukula mwauzimu.

KODI MUYENELA KULEKA KUTSOGOZA PHUNZILO?

17-18. Ni zinthu ziti zimene muyenela kuganizila kuti mudziŵe ngati muyenela kuleka kutsogoza phunzilo?

17 Ngati wophunzila Baibo sapita patsogolo, pa nthawi ina mungafunike kudzifunsa kuti, ‘Kodi nileke kutsogoza phunziloli?’ Musanapange cosankha pa nkhaniyi, coyamba muyenela kuganizila luso la wophunzilayo. Anthu ena amatenga nthawi yaitali kuti apite patsogolo, pamene ena satenga nthawi. Conco, dzifunseni kuti: ‘Kodi wophunzilayu akupita patsogolo pa mlingo woyenela malinga na mmene zinthu zili mu umoyo wake?’ ‘Kodi wayamba “kusunga” kapena kuti kuseŵenzetsa zimene amaphunzila?’ (Mat. 28:20) N’zoona kuti nthawi zina zimatenga nthawi yaitali kuti wophunzila Baibo apite patsogolo. Ngakhale n’telo, iye afunika kumasintha umoyo wake pang’ono-pang’ono.

18 Koma bwanji ngati mwakhala mukuphunzila na winawake kwa nthawi ndithu koma amacita zinthu zoonetsa kuti saona phunzilo kukhala lofunika? Tiyelekezele kuti munatsiliza kuphunzila naye buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, mwina ngakhale kuyamba buku lakuti Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu. Koma sanapezekeko pa msonkhano uliwonse wa mpingo, ngakhale pa Cikumbutso! Ndipo nthawi zambili amapeleka zifukwa zosamveka zokanila kuphunzila. Zikakhala conco, mungafunike kukambilana naye mosapita m’mbali. *

19. Kodi munthu amene saona phunzilo kukhala lofunika mungamufunse funso lotani? Nanga zimene angayankhe zingakuthandizeni bwanji?

19 Mungayambe kukambilana na wophunzilayo mwa kumufunsa kuti, ‘Kodi vuto lalikulu limene muona kuti lingakulepheletseni kukhala Mboni ya Yehova ni liti?’ Mwina wophunzilayo angayankhe kuti, ‘Nimakondwela kuphunzila Baibo, koma kukhala Mboni siningayese!’ Ngati ali na maganizo otelo, olo kuti mwaphunzila naye kwa kanthawi, kodi muona kuti pali cifukwa comveka copitilizila kuphunzila naye? Koma mosiyana na zimenezi, wophunzilayo tikamufunsa funso limeneli, mwina angamasuke na kutiuza cimene cikum’lepheletsa kupita patsogolo. Mwacitsanzo, mwina angakambe kuti sangakwanitse kulalikila ku nyumba na nyumba. Mukadziŵa vuto lake, mudzapeza njila yabwino yom’thandizila.

Musataye nthawi kuphunzila ndi anthu amene sapita patsogolo (Onani ndime 20)

20. Kodi kumvetsetsa lemba la Machitidwe 13:48 kungatithandize bwanji kudziŵa ngati tifunika kuleka kutsogoza phunzilo kapena ayi?

20 N’zacisoni kuti ophunzila ena ali monga Aisiraeli a m’nthawi ya Ezekieli. Onani zimene Yehova anakamba kwa Ezekieli ponena za Aisiraeli amenewo. Anati: “Kwa iwo uli ngati munthu woimba nyimbo zacikondi. Uli ngati munthu wa mawu anthetemya komanso wodziwa kuimba coimbila ca zingwe. Iwo adzamva ndithu mawu ako, koma palibe amene adzawatsatile.” (Ezek. 33:32) Nthawi zina, cingativute kuuza wophunzila Baibo kuti tidzaleka kuphunzila naye. Komabe, tiyenela kukumbukila kuti “nthawi yotsalayi yafupika.” (1 Akor. 7:29) M’malo motaya nthawi kutsogoza phunzilo la Baibo losapita patsogolo, tiyenela kusakila anthu amene amaonetsa kuti ali na ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Ŵelengani Machitidwe 13:48.

Pangakhale anthu ena m’gawo lanu amene akupemphela kuti adziŵe coonadi (Onani ndime 20)

21. Kodi lemba la caka ca 2020 ni liti? Nanga lidzatithandiza kucita ciani?

21 Lemba la caka ca 2020 lidzatithandiza kuganizila mmene tingakulitsile luso pa nchito yathu yopanga ophunzila. Lembali ni mbali ya mawu amene Yesu anakamba pa msonkhano wosaiŵalika, umene unacitikila pa phili ku Galileya. Iye anati: “Conco pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza.”Mat. 28:19.

Tiyeni tiyesetse kukulitsa luso lathu pa nchito yopanga ophunzila na kuthandiza ophunzila Baibo kupita patsogolo mpaka kukabatizika (Onani ndime 21)

NYIMBO 70 Funa-funani Oyenelela

^ ndime 5 Lemba la caka ca 2020 litilimbikitsa kupanga “ophunzila.” Ife tonse atumiki a Yehova tifunika kumvela lamulo limeneli. Kodi tingawathandize bwanji anthu amene timaphunzila nawo Baibo kuti apite patsogolo mpaka kukhala ophunzil a a Khristu? M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingathandizile ophunzila Baibo kukhala pa ubwenzi na Yehova. Tidzakambilananso zimene zingatithandize kudziŵa ngati tifunika kuleka kuphunzila Baibo na munthu kapena ayi.

^ ndime 18 Tambani vidiyo yakuti Kuleka Kutsogoza Maphunzilo a Baibo Osapita Patsogolo, imene ili pa JW Broadcasting®.