Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 3

Yehova Mulungu Wathu Amationa Kuti Ndife Ofunika

Yehova Mulungu Wathu Amationa Kuti Ndife Ofunika

Iye amene amatikumbukila pamene tili ofooka.’​SAL. 136:23.

NYIMBO 33 Tulila Yehova Nkhawa Zako

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi atumiki a Yehova ambili akukumana na mavuto abwanji? Nanga pangakhale zotulukapo zotani?

GANIZILANI zitsanzo zitatu izi: M’bale wacicepele akudwala matenda aakulu ofooketsa thupi. M’bale wa zaka zopitilila 50 amene ni wolimbikila nchito, amucotsa nchito. Iye akuyesetsa kufuna-funa nchito ina koma sakuipeza. Komanso, mlongo wokalamba wokhulupilika akulephela kucita zambili potumikila Yehova.

2 Ngati mukukumana na ena mwa mavuto amene tachula pamwambapa, ndiye kuti mwina mumadziona kuti ndinu wosafunika. Mavuto amenewo angakulandeni cimwemwe, na kukupangitsani kudziona kuti ndinu wosafunika, ndipo izi zingaononge ubwenzi wanu na ena.

3. Kodi Satana ndi anthu amene ali ku mbali yake amauona bwanji moyo?

3 Anthu m’dzikoli amaona moyo wa munthu monga mmene Satana amauonela. Satana nthawi zonse wakhala akucita zinthu mosawaganizila anthu. Amawaona ngati osafunika. Mwacitsanzo, ganizilani nkhanza imene iye anaonetsa mwa kuuza Hava kuti ngati sadzamvela Mulungu adzakhala na ufulu, pamene m’ceni-ceni anali kudziŵa bwino kuti akacita zimenezo adzafa. Komanso Satana ndiye wakhala akulamulila magulu andale, amalonda, na acipembedzo. Conco, n’zosadabwitsa kuti mofanana ndi Satana, anthu ambili amalonda, andale, na acipembedzo, saganizila anthu ena komanso salemekeza moyo.

4. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

4 Mosiyana na Satana, Yehova amafuna kuti tizidziona kuti ndife ofunika, ndipo amatithandiza tikakumana na mavuto amene angatipangitse kudziona ngati acabe-cabe. (Sal. 136:23; Aroma 12:3) M’nkhani ino, tidzakambilana mmene Yehova amatithandizila (1) pamene tikudwala, (2) pamene takumana na mavuto azacuma, komanso (3) ngati timaona kuti palibe ciliconse ca phindu cimene tingacite potumikila Yehova cifukwa ca ukalamba. Koma coyamba, tiyeni tikambilane cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti Yehova amaona aliyense wa ife kukhala wofunika.

YEHOVA AMATIONA KUTI NDIFE OFUNIKA

5. N’cifukwa ciani mumakhulupilila kuti anthu ni amtengo wapatali kwa Yehova?

5 Olo kuti tinapangidwa kucokela ku dothi, ndife amtengo wapatali kwa Yehova. (Gen. 2:7) Onani zina mwa zifukwa zimene zimatipangitsa kukhulupilila kuti Yehova amationa kukhala ofunika. Iye anatipanga m’njila yakuti tizitha kutengela makhalidwe ake. Pa cifukwa ici, ndife apamwamba kwambili kuposa colengedwa ciliconse ca pa dziko lapansi. (Gen. 1:27) Cinanso, anatipatsa udindo wosamalila dziko lapansi na vinyama.—Sal. 8:4-8.

6. N’ciani cina cimene cionetsa kuti Yehova amationa kuti ndife ofunika olo kuti ndife opanda ungwilo?

6 Ngakhale pamene Adamu anacimwa, Yehova anapitiliza kuona anthu kuti ni ofunika. Iye amatikonda kwambili cakuti anapeleka mwana wake wokondedwa, Yesu, kuti akhale dipo lotiwombola ku macimo. (1 Yoh. 4:9, 10) Cifukwa ca dipo limeneli, Yehova adzaukitsa anthu “olungama ndi osalungama omwe,” amene anafa cifukwa ca ucimo wa Adamu. (Mac. 24:15) Mawu a Mulungu amaonetsa kuti Yehova amationa kuti ndife amtengo wapatali olo tikuvutika na matenda, mavuto a zacuma, kapena ukalamba.—Mac. 10:34, 35.

7. Kodi ife atumiki a Mulungu tili na zifukwa zina ziti zokhulupilila kuti Yehova amationa kuti ndife ofunika?

7 Palinso zifukwa zina zimene zimatipangitsa kukhulupilila kuti Yehova amaona kuti ndife ofunika. Yehova watikokela kwa iye ndipo amakondwela poona kuti tinalabadila uthenga wabwino. (Yoh. 6:44) Pamene tinayamba kumuyandikila Yehova, iyenso anayamba kutiyandikila. (Yak. 4:8) Cinanso, amayesetsa kutiphunzitsa. Izi zionetsa kuti amationa kuti ndife amtengo wapatali. Yehova amatidziŵa bwino ndipo amadziŵanso kuti tingawongolele mbali zimene siticita bwino. Kuwonjezela apo, tikalakwa amatipatsa cilango cifukwa amatikonda. (Miy. 3:11, 12) Ndithudi, uwu ni umboni wamphamvu wakuti Yehova amationa kuti ndife ofunika!

8. Kodi mawu a pa Salimo 18:27-29 angakhudze bwanji mmene timaonela mavuto athu?

8 Ganizilani za Mfumu Davide. Anthu ena anali kumuona monga munthu wacabe-cabe. Koma iye anali kudziŵa kuti Yehova anali kum’konda na kumuthandiza. Kudziŵa izi kunamuthandiza kupilila pamene ena anali kumunyoza. (2 Sam. 16:5-7) Tikakumana na mavuto kapena tikayamba kuvutika maganizo, Yehova angatithandize kuona zinthu moyenela. Angatithandizenso kupilila mavuto alionse amene tingakumane nawo. (Ŵelengani Salimo 18:27-29.) Cifukwa ca thandizo la Yehova, palibe cimene cingatilepheletse kum’tumikila mwacimwemwe. (Aroma 8:31) Tsopano tiyeni tikambilane mavuto atatu amene tikakumana nawo, timafunika kukumbukila kwambili kuti Yehova amatikonda na kutiona kukhala ofunika.

PAMENE TIKUDWALA

Kuŵelenga mawu ouzilidwa a Yehova kudzatithandiza kucepetsa nkhawa imene timakhala nayo ngati tikudwala (Onani ndime 9-12)

9. Kodi matenda angacititse kuti tiyambe kudziona motani?

9 Matenda angatipangitse kukhala na nkhawa kwambili mpaka kufika podziona ngati osafunika. Nthawi zambili timadzimvela cisoni tikadwala kapena ngati timangodalila thandizo la ena cifukwa ca vuto limene tili nalo. Ngakhale ena asadziŵe kuti tikudwala, tingadzimvele ndithu cisoni cifukwa coona kuti tikulephela kucita zinthu zimene tinali kucita kale. Pa nthawi yovuta imeneyo, Yehova amatilimbikitsa. Motani?

10. Malinga na Miyambo 12:25, n’ciani cingatilimbikitse pamene tikudwala?

10 Tikadwala, “mawu abwino” angatilimbikitse. (Ŵelengani Miyambo 12:25.) M’Baibo, Yehova anaikamo mawu olimbikitsa amene amatikumbutsa kuti iye amationa kuti ndife ofunika olo pamene tikudwala. (Sal. 31:19; 41:3) Ngati tiŵelenga mawu ouzilidwa amenewo, ngakhale mavesi amodzi-modzi mobweleza-bweleza, Yehova adzatithandiza kulimbana na nkhawa zimene tingakhale nazo pamene tikudwala.

11. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji m’bale Jorge?

11 Ganizilani citsanzo ca m’bale Jorge. Ali wacinyamata, anadwala matenda ofooketsa amene anakula m’kanthawi kocepa ndipo anali kumupangitsa kudziona ngati wopanda pake. Iye anati: “Sin’nali kuyembekezela kuti ningadwale matenda otele amene amacititsa kuti nizingodzimvela cisoni, komanso kuti anthu azingoyang’ana pa ine. Pamene matendawo anali kukulila-kulila, n’nayamba kudela nkhawa za mmene umoyo wanga udzakhalila. N’nadzimvela cisoni kwambili, ndipo n’nacondelela Yehova m’pemphelo kuti anithandize.” Kodi anamuthandiza bwanji? M’bale Jorge anati: “Popeza zinali kunivuta kuika maganizo pa zimene n’nali kuŵelenga, n’nayamba kuŵelenga mavesi ocepa cabe m’buku la Masalimo, amene amaonetsa cikondi cimene Yehova ali naco pa atumiki ake. N’nali kuŵelenga mavesiwo mobweleza-bweleza tsiku lililonse, ndipo ananilimbikitsa na kunitonthoza. M’kupita kwa nthawi, anthu anaona kuti nayamba kuoneka wacimwemwe. Iwo anafika poniuza kuti amalimbikitsidwa na mzimu wacimwemwe umene nimaonetsa. N’nazindikila kuti Yehova wayankha mapemphelo anga. Iye ananithandiza kucepetsa maganizo odzimvela cisoni. N’nayamba kuganizila kwambili pa zimene Mawu ake amakamba, zoonetsa kuti amaona kuti ndife ofunika olo tikudwala.”

12. Kodi Yehova amatithandiza bwanji pamene tikudwala?

12 Ngati mukudwala, dziŵani kuti Yehova amaona mavuto amene mukupitamo. Conco, m’pempheni kuti akuthandizeni kuona mavutowo m’njila yoyenela. Ndiyeno, ŵelengani Baibo kuti mupeze mawu abwino amene Yehova anaikamo kuti atilimbikitse. Ŵelengani mosamala mavesi amene amaonetsa kuti Yehova amakonda kwambili atumiki ake. Mukacita zimenezi, mudzaona kuti Yehova amakomela mtima atumiki ake onse amene amam’tumikila mokhulupilika.—Sal. 84:11.

TIKAKUMANA NA MAVUTO AZACUMA

Kukumbukila lonjezo la Yehova lakuti adzatisamalila, kudzatilimbikitsa ngati tisakila nchito koma sitikuipeza (Onani ndime 13-15)

13. Kodi mutu wa banja angamvele bwanji ngati amucotsa nchito?

13 Mutu wa banja aliyense amafuna kupeza zofunikila za banja lake. Koma tiyelekeze kuti m’bale amucotsa nchito olo kuti sanalakwitse ciliconse. Iye akuyesetsa kusakila nchito ina, koma sakuipeza. Cifukwa ca vuto limeneli, m’baleyo angayambe kudziona wacabe-cabe. Kodi kukumbukila malonjezo a Yehova kungamulimbikitse bwanji?

14. N’cifukwa ciani Yehova amasunga malonjezo ake?

14 Yehova amasunga malonjezo ake nthawi zonse. (Yos. 21:45; 23:14) Pali zifukwa zingapo zimene amacitila zimenezi. Cifukwa coyamba n’cakuti zimakhudza dzina lake kapena kuti mbili yake. Yehova analonjeza kuti adzasamalila atumiki ake okhulupilika, ndipo amaona kuti ali na udindo wokwanilitsa lonjezo limeneli. (Sal. 31:1-3) Cifukwa cina n’cakuti Yehova amadziŵa kuti pokhala anthu a m’banja lake, tingataye mtima ngati iye sakutisamalila. Iye analonjezanso kuti adzatisamalila mwakuthupi na mwauzimu, ndipo palibe cimene cingamulepheletse kukwanilitsa lonjezo limeneli.—Mat. 6:30-33; 24:45.

15. (a) Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi anakumana na vuto lotani? (b) Nanga Salimo 37:18, 19 imatitsimikizila za ciani?

15 Kukumbukila cifukwa cake Yehova amasunga malonjezo ake, kudzatithandiza kuti tisakhale na nkhawa kwambili tikakumana na mavuto a zacuma. Ganizilani zimene zinacitikila Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Pamene mpingo wa ku Yerusalemu unakumana na cizunzo cacikulu, Akhristu ‘onse anabalalika kupatulapo atumwi okha.’ (Mac. 8:1) Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Iwo anayamba kukumana na mavuto a zacuma cifukwa n’zodziŵikilatu kuti pamene anathaŵa, anasiya nyumba zawo, nchito, na mabizinesi awo. Koma Yehova sanawasiye, ndiponso Akhristuwo anapitiliza kukhala acimwemwe. (Mac. 8:4; Aheb. 13:5, 6; Yak. 1:2, 3) Yehova anawathandiza Akhristu okhulupilika amenewo ndipo nafenso adzatithandiza.—Ŵelengani Salimo 37:18, 19.

NGATI SITIKWANITSA KUCITA ZAMBILI CIFUKWA CA UKALAMBA

Kucita zimene tingathe olo ndife  okalamba, kudzatithandiza kukumbukila kuti Yehova amationa kuti ndife ofunika, komanso kuti amayamikila zimene timacita pom’tumikila mokhulupilika (Onani ndime 16-18)

16. N’ciani cingatipangitse kuona kuti Yehova sauŵelengela utumiki wathu?

16 Pamene tikukalamba, tingayambe kuona kuti zimene timacita potumikila Yehova n’zocepa kwambili. Nayenso Mfumu Davide ayenela kuti anali kumvela conco m’nthawi ya ukalamba wake. (Sal. 71:9) Kodi Yehova angatithandize bwanji ngati timamvela conco?

17. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca mlongo Jheri?

17 Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Jheri. Iye anaitanidwa kuti akacite nawo maphunzilo okhudza kukonza zoonongeka pa nyumba zolambilila. Maphunzilowo anacitikila pa Nyumba ya Ufumu. Koma mlongoyu sanafune kupitako. Cifukwa ciani? Iye anati: “Ndine wokalamba, wamasiye, komanso nilibe luso lililonse limene lingathandize pa nchitoyi. Nilibe nchito kwa Yehova.” Usiku wakuti mawa maphunzilo ayamba, mlongoyu anakhuthulila Yehova nkhawa zake m’pemphelo. Tsiku lotsatila, iye anapita ku Nyumba ya Ufumu, koma anali kudzionabe ngati wosayenela kucitako maphunzilowo. Maphunzilowo ali mkati, mkambi wina anagogomeza mfundo yakuti luso lofunika kwambili limene tili nalo ni kudzipeleka kuphunzitsidwa na Yehova. Mlongo Jheri anakamba kuti: “Mu mtima n’nati, ‘Luso limeneli nili nalo.’ N’nalila n’tazindikila kuti Yehova wayankha pemphelo langa. Iye ananithandiza kuona kuti pali cina cake ca mtengo wapatali cimene ningacite pomutumikila, komanso kuti ni wokonzeka kuniphunzitsa.” Mlongoyu anapitiliza kuti: “Pamene n’nayamba maphunzilowo, n’nali wamantha, wolefulidwa, komanso n’nali kudziona wosafunika. Koma n’natsiliza maphunzilowo nili wolimbikitsidwa, wolimba mtima, komanso n’nali kudziona kuti ndine wofunika.”

18. Kodi Baibo imaonetsa bwanji kuti Yehova amaonabe kuti utumiki wathu ni wofunika olo pamene takalamba?

18 Ngati ndimwe wokalamba, dziŵani kuti Yehova akali na nchito imene afuna kuti mucite. (Sal. 92:12-15) Nthawi zina tingaone kuti mphamvu na maluso athu n’zocepa, kapenanso kuti zimene timacita n’zosafunika kweni-kweni. Koma Yesu anatiphunzitsa kuti Yehova amayamikila zilizonse zimene timacita pom’tumikila. (Luka 21:2-4) Conco, muzicita zimene mungakwanitse. Mwacitsanzo, muziuzako ena za Yehova, muzipemphelela abale na alongo anu, komanso muzilimbikitsa ena kuti akhalabe okhulupilika. Yehova amakuonani kuti ndimwe wa nchito mnzake, osati cifukwa ca zimene mumakwanitsa kucita, koma cifukwa cakuti mumamumvela na mtima wonse.—1 Akor. 3:5-9.

19. Kodi Aroma 8:38, 39 imatitsimikizila za ciani?

19 Timayamikila kwambili kulambila Yehova, Mulungu amene amaona atumiki ake kukhala amtengo wapatali. Iye anatilenga na mtima wofuna kucita cifunilo cake, ndipo kulambila koona n’kumene kumatithandiza kukhala na umoyo waphindu. (Chiv. 4:11) Olo kuti anthu m’dzikoli amationa monga acabe-cabe, Yehova amaona kuti ndife ofunika. (Aheb. 11:16, 38) Tikakhala na nkhawa cifukwa ca matenda, mavuto a zacuma, kapena ukalamba, tifunika kukumbukila kuti palibe cimene cingatilekanitse na cikondi ca Atate wathu wakumwamba.—Ŵelengani Aroma 8:38, 39.

^ ndime 5 Kodi munakumanapo na mavuto amene anakupangitsani kudziona kuti ndinu wacabe-cabe? Nkhani ino, idzatithandiza kukumbukila kuti Yehova amatikonda kwambili na kutiona kukhala ofunika. Tidzakambilana mfundo zimene zingatithandize kuti tizidziona kukhala ofunika mosasamala kanthu za mavuto amene tikukumana nawo.

NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa