Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 4

‘Mzimu Umacitila Umboni Limodzi Ndi Mzimu Wathu’

‘Mzimu Umacitila Umboni Limodzi Ndi Mzimu Wathu’

“Pakuti mzimuwo umacitila umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.”​—AROMA 8:16.

NYIMBO 25 Cuma Capadela

ZIMENE TIKAMBILANE *

Pa Pentekosite, Yehova anatsanulila mzimu wake woyela mwa njila yapadela pa gulu la Akhristu pafupi-fupi 120 (Onani ndime 1-2)

1-2. N’ciani capadela cimene cinacitika pa Pentekosite mu 33 C.E.?

YELEKEZELANI kuti mukuona zimene zinacitika ku Yerusalemu pa Sondo m’mawa pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Gulu la ophunzila a Yesu pafupi-fupi 120 lasonkhana m’cipinda cam’mwamba m’nyumba inayake. (Mac. 1:13-15; 2:1) Apa n’kuti papita masiku ocepa kucokela pamene Yesu anawalamula kuti asacoke mu Yerusalemu kuti alandile mphatso inayake yapadela. (Mac. 1:4, 5) Kodi n’ciani cinacitika pambuyo pake?

2 “Mwadzidzidzi kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu.” Mkokomowo unadzaza m’nyumba monse. Kenako, “malawi amoto ooneka ngati malilime” anaonekela pa mitu ya ophunzilawo. Ndipo onse amene anasonkhana “anadzazidwa ndi mzimu woyela.” (Mac. 2:2-4) Mwa njila yapadela imeneyi, Yehova anatsanulila mzimu woyela pa ophunzilawo. (Mac. 1:8) Iwo anali oyamba kudzozedwa na mzimu woyela * na kupatsidwa ciyembekezo cokalamulila na Yesu kumwamba.

N’CIANI CIMACITIKA MUNTHU AKADZOZEDWA?

3. N’cifukwa ciani Akhristu amene anasonkhana pa Pentekosite sanakayikile kuti anadzozedwa na mzimu woyela?

3 Mukanakhalapo pa nthawi imene ophunzila a Yesu anasonkhana m’cipinda cam’mwamba pa Pentekosite, simukanaiŵala zimene zinacitika pa tsikulo. Cina cake cooneka ngati lawi la moto cinabwela na kukhala pa mutu wa aliyense wa iwo, ndipo anayamba kulankhula m’malilime. (Mac. 2:5-12) Iwo sanakaikile olo pang’ono kuti adzozedwa na mzimu woyela. Koma kodi onse amene amadzozedwa na mzimu woyela amalandila mzimuwo m’njila yapadela komanso pa nthawi imodzi? Iyai. Tidziŵa bwanji zimenezi?

4. Kodi Akhristu onse amene anadzozedwa m’nthawi ya atumwi analandila mzimu woyela pa nthawi yofanana? Fotokozani.

4 Tiyeni coyamba tikambilane za nthawi imene munthu amadzozedwa. Sikuti gulu lija la Akhristu pafupi-fupi 120 ndiwo okha amene anadzozedwa na mzimu woyela pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Pa nthawi ina tsiku lomwelo, Akhristu enanso pafupi-fupi 3,000 analandila mzimu woyela umene Yesu analonjeza. Iwo anadzozedwa atabatizika. (Mac. 2:37, 38, 41) Koma m’zaka zotsatila, si Akhristu onse amene anadzozedwa pa nthawi ya ubatizo wawo. Mwacitsanzo, Asamariya anadzozedwa patapita nthawi kucokela pamene anabatizidwa. (Mac. 8:14-17) Ndipo kudzozedwa kwa Koneliyo na a m’banja lake kunali kwapadela kwambili. Iwo anadzozedwa akalibe kubatizika n’komwe.—Mac. 10:44-48.

5. Malinga na 2 Akorinto 1:21, 22, n’ciani cimacitika munthu akadzozedwa na mzimu woyela?

5 Tsopano tiyeni tikambilane cimene cimacitika munthu akadzozedwa na mzimu woyela. Akhristu ena akadzozedwa, poyamba cimawavuta kuvomeleza kuti Yehova wawasankha kuti akapite kumwamba. Iwo angayambe kudzifunsa kuti; ‘N’cifukwa ciani Mulungu wasankha ine?’ Koma ena sakhala na maganizo amenewa. Mulimonsemo, mtumwi Paulo anafotokoza zimene zimacitika kwa munthu aliyense amene wadzozedwa. Iye anati: “Kudzelanso mwa iye, mutakhulupilila munaikidwa cidindo * ca mzimu woyela wolonjezedwawo, umene ndi cikole ca colowa cathu cam’tsogolo.” (Aef. 1:13, 14) Cotelo, pogwilitsila nchito mzimu woyela, Yehova amathandiza Akhristu amenewa kudziŵa kuti anasankhidwa kuti akapite kumwamba. Ndipo iwo sakayikila zimenezi olo pang’ono. Mwa njila imeneyi, mzimu woyela umakhala ‘cikole ca colowa cawo cam’tsogolo,’ kapena kuti citsimikizo cakuti adzakhala kumwamba kwamuyaya osati pano padziko lapansi.—Ŵelengani 2 Akorinto 1:21, 22.

6. Kodi Mkhristu aliyense wodzozedwa afunika kucita ciani kuti akalandile mphoto yake yakumwamba?

6 Ngati Mkhristu wadzozedwa, kodi ndiye kuti basi adzapita kumwamba? Iyai. Iye amakhala wotsimikiza na mtima wonse kuti wasankhidwa kuti akapite kumwamba. Koma afunika kukumbukila malangizo awa: “Abale, citani ciliconse cotheka kuti mukhalebe okhulupilika, n’colinga coti mupitilizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha, pakuti mukapitiliza kucita zinthu zimenezi simudzalephela ngakhale pang’ono.” (2 Pet. 1:10) Conco, ngakhale kuti Mkhristu anaitanidwa kapena kuti kusankhidwa kuti akapite kumwamba, iye adzalandila mphoto yake kokha ngati akhalabe wokhulupilika kwa Mulungu.—Afil. 3:12-14; Aheb. 3:1; Chiv. 2:10.

KODI MUNTHU AMADZIŴA BWANJI KUTI WADZOZEDWA?

7. Kodi odzozedwa amadziŵa bwanji kuti asankhidwa kuti adzapita kumwamba?

7 Kodi munthu amadziŵa bwanji kuti wasankhidwa kuti akapite kumwamba? Yankho lili m’mawu amene Paulo analembela Akhristu a ku Roma, amene ‘anaitanidwa kukhala oyela.’ Iye anati: “Simunalandile mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandila mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: ‘Abba, Atate!’ Pakuti mzimuwo umacitila umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu.” (Aroma 1:7; 8:15, 16) Motelo, pogwilitsila nchito mzimu woyela, Mulungu amathandiza munthu amene wadzozedwa kudziŵa popanda kukayikila kulikonse kuti wasankhidwa kuti akapite kumwamba.—1 Ates. 2:12.

8. Kodi lemba la 1 Yohane 2:20, 27 lionetsa bwanji kuti Akhristu odzozedwa safunikila kuuzidwa na munthu wina kuti atsimikizile kuti ni odzozedwa?

8 Yehova amathandiza Akhristu odzozedwa kutsimikiza na mtima wonse kuti anasankhidwa kuti adzapite kumwamba. (Ŵelengani 1 Yohane 2:20, 27.) N’zoona kuti mofanana na ife tonse, Akhristu odzozedwa amafunika kuphunzitsidwa na Yehova kupitila mu mpingo. Koma iwo safunika kuuzidwa na munthu wina kuti atsimikizile kuti ni odzozedwa. Yehova kudzela mwa mzimu wake woyela, umene ni wamphamvu kuposa cina ciliconse m’cilengedwe, amathandiza Akhristuwo kukhulupilila na mtima wonse kuti anadzozedwadi.

‘AMABADWANSO’

9. Malinga na Aefeso 1:18, ni kusintha kotani kumene kumacitika kwa munthu amene wadzozedwa?

9 Atumiki ambili a Mulungu masiku ano amalephela kumvetsetsa zimene zimacitika munthu akadzozedwa na Mulungu. Zimenezi n’zosadabwitsa cifukwa iwo si odzozedwa. Mulungu analenga anthu kuti akhale pa dziko lapansi kwamuyaya, osati kumwamba. (Gen. 1:28; Sal. 37:29) Koma Yehova amasankha anthu ena kuti akakhale kumwamba. Conco, Mulungu akadzoza munthu, amacititsa kuti ciyembekezo cake na maganizo ake zisinthe nthawi yomweyo, moti amayamba kuyembekezela kukakhala na moyo kumwamba.—Ŵelengani Aefeso 1:18.

10. Kodi “kubadwanso” kumatanthauza ciani? (Onani mawu amunsi.)

10 Akhristu akadzozedwa na mzimu woyela, ‘amabadwanso.’ * Yesu anaonetsa kuti Mkhristu ‘akabadwanso’ kapena kuti ‘akabadwa mwa mzimu,’ n’zosatheka kufotokoza momveka bwino mmene amamvelela kwa munthu amene sanadzozedwe.—Yoh. 3:3-8.

11. Kodi maganizo a Mkhristu amasintha bwanji akadzozedwa?

11 Kodi Akhristu akadzozedwa, maganizo awo amasintha bwanji? Akhristu asanadzozedwe na Yehova, amakhala na ciyembekezo codzakhala na moyo wamuyaya pano pa dziko lapansi. Amayembekezela mwacidwi nthawi imene Yehova adzathetsa zoipa zonse na kupanga dzikoli kukhala paradaiso. Mwinanso amayelekezela m’maganizo mwawo kuti akulandila m’bululu wawo kapena bwenzi lawo amene anamwalila. Koma akadzozedwa, maganizo awo amasintha. N’cifukwa n’ciani amasintha? Sikuti amasintha cifukwa coganiza kuti kukhala na moyo wamuyaya pa dziko sikwabwino. Sasintha cifukwa ca nkhawa kapena cifukwa cakuti anakumana na mavuto ena aakulu. Komanso sasintha mwadzidzidzi cifukwa coganiza kuti moyo wosatha pano padziko lapansi sudzakhala wokondweletsa. M’malomwake, Yehova ni amene amawasankha kuti akakhale kumwamba. Akawasankha, amacititsa kuti maganizo na ciyembekezo cawo zisinthe. Iye amacita zimenezi pogwilitsila nchito mzimu wake woyela.

12. Malinga na 1 Petulo 1:3, 4, kodi Akhristu odzozedwa amamvela bwanji akaganizila za ciyembekezo cawo?

12 Mkhristu amene wadzozedwa, nthawi zina akhoza kumaona kuti ni wosayenelela kulandila mwayi wapadela umenewu. Koma sakayikila ngakhale pang’ono kuti Yehova wamusankha. Amakhala wacimwemwe komanso woyamikila ngako akaganizila za ciyembekezo cake cokakhala na moyo kumwamba.—Ŵelengani 1 Petulo 1:3, 4.

13. Kodi Akhristu odzozedwa amamvela bwanji akaganizila za moyo wawo pano pa dziko lapansi?

13 Kodi zimenezi zitanthauza kuti odzozedwa amalaka-laka kufa? Mtumwi Paulo anayankha funso limeneli. Iye anayelekezela thupi laumunthu la odzozedwa na msasa. Kenako anati: “Ndipotu, ife amene tili mumsasa uno tikubuula cifukwa colemedwa. Kwenikweni si cifukwa cofuna kuuvula, koma kuti tivale nyumba inayo, kuti cokhoza kufaci cilowedwe m’malo ndi moyo.” (2 Akor. 5:4) Conco, sikuti Akhristu odzozedwa anatopa nawo moyo wa pa dziko lapansi. Iwo safuna kufa mwamsanga. Amakondwela kukhala na moyo, ndipo amafuna kutumikila Yehova tsiku lililonse pamodzi na banja lawo ndiponso mabwenzi awo. Koma pa ciliconse cimene akucita, nthawi zonse amakumbukila za ciyembekezo cawo caulemelelo.—1 Akor. 15:53; 2 Pet. 1:4; 1 Yoh. 3:2, 3; Chiv. 20:6.

KODI YEHOVA ANAKUDZOZANI?

14. Ni zinthu ziti zimene si umboni wakuti munthu anadzozedwa na mzimu woyela?

14 Mwina nthawi zina mumaganiza kuti Yehova anakudzozani na mzimu woyela kuti mukapite kumwamba. Ngati n’conco, yankhani mafunso ofunika awa: Kodi muli na mtima wofunitsitsa kucita cifunilo ca Yehova? Kodi mumaona kuti ndinu wacangu kwambili pa nchito yolalikila? Kodi mumakonda kuphunzila Baibo mwakhama, kuphatikizapo “zinthu zozama za Mulungu”? (1 Akor. 2:10) Kodi muona kuti Yehova wakudalitsani pa nchito yolalikila? Kodi mumakonda kwambili anthu ena ndipo mumafunitsitsa kuwathandiza kutumikila Yehova? Kodi mwaona umboni wosonyeza kuti Yehova wakuthandizani m’njila zosiyana-siyana pa umoyo wanu? Ngati mwayankha na mtima wonse kuti inde pa mafunso amenewa, kodi ndiye kuti munasankhidwa kuti mudzapita kumwamba? Iyai, si conco. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti atumiki onse a Mulungu akhoza kumvela mwanjila imeneyi, kaya ni odzozedwa kapena ayi. Ndipo pogwilitsila nchito mzimu woyela, Yehova angapeleke mphamvu yofanana kwa mtumiki wake aliyense, mosasamala kanthu za ciyembekezo cimene ali naco. Ndiponso ngati sindinu wotsimikiza kuti mudzapita kumwamba, ndiye kuti simunadzozedwe. Akhristu amene anadzozedwa sakayikila ngakhale pang’ono kuti anadzozedwa. Iwo amadziŵa ndithu.

Yehova anaseŵenzetsa mzimu wake woyela popatsa mphamvu Abulahamu, Sara, Davide, na Yohane M’batizi kuti acite zinthu zazikulu. Koma sanawadzoze na mzimuwo kuti adzapite kumwamba (Onani ndime 15-16) *

15. Tidziŵa bwanji kuti ena amene analandila mzimu wa Mulungu sanapite kumwamba?

15 M’Baibo muli zitsanzo zambili za atumiki a Mulungu okhulupilika amene analandilapo mzimu woyela, koma analibe ciyembekezo cokakhala kumwamba. Mwacitsanzo, Davide anali kutsogoleledwa na mzimu woyela. (1 Sam. 16:13) Mzimu woyela unamuthandiza kumvetsa zinthu zozama zokhudza Yehova, ndiponso unamutsogolela polemba Mawu a Mulungu. (Maliko 12:36) Ngakhale zinali conco, mtumwi Petulo anakamba kuti Davide “sanakwele kumwamba.” (Mac. 2:34) Citsanzo cina ni Yohane M’batizi. Iye ‘anadzazidwa na mzimu woyela.’ (Luka 1:13-16) Yesu anakamba kuti Yohane anali wamkulu kuposa anthu onse. Koma pambuyo pake anakambanso kuti Yohane sadzakhala m’gulu la olamulila mu ufumu wakumwamba. (Mat. 11:10, 11) Yehova anaseŵenzetsa mzimu wake popatsa atumiki ake amenewa mphamvu yocita zinthu zazikulu. Koma sanawadzoze na mzimuwo kuti adzapite kumwamba. Kodi izi zitanthauza kuti anthu amenewa sanali okhulupilika kwambili poyelekezela na Akhristu amene anasankhidwa kukalamulila kumwamba? Iyai. Zimangotanthauza kuti Yehova adzawaukitsa m’Paradaiso pano padziko lapansi.—Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15.

16. Ni ciyembekezo cotani cimene atumiki ambili a Mulungu ali naco?

16 Atumiki ambili a Mulungu masiku ano alibe ciyembekezo copita kumwamba. Mofanana na Abulahamu, Sara, Davide, Yohane M’batizi, ndi anthu ena akale, iwo ali na ciyembekezo codzakhala na moyo pano pa dziko lapansi, pamene Boma la Mulungu lidzalamulila dzikoli.—Aheb. 11:10.

17. Tidzakambilana mafunso ati m’nkhani yotsatila?

17 Popeza Akhristu odzozedwa akalipo pa dziko lapansi, tingakhale na mafunso osiyana-siyana. (Chiv. 12:17) Mwacitsanzo, kodi Akhristu odzozedwa ayenela kudziona bwanji? Kodi Mkhristu wina mu mpingo mwanu akayamba kudya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso, muyenela kumuona bwanji? Nanga muyenela kumvela bwanji mukaona kuti ciŵelengelo ca amene amadya pa Cikumbutso cikukwela? Kodi muyenela kuda nkhawa? Tidzayankha mafunso amenewa m’nkhani yotsatila.

^ ndime 5 Kungoyambila pa Pentekosite wa mu 33 C.E, Yehova wakhala akupatsa Akhristu ena ciyembekezo capadela cokalamulila na Mwana wake kumwamba. Koma kodi iwo amadziŵa bwanji kuti asankhidwa kukalamulila na Yesu kumwamba? Nanga n’ciani cimacitika munthu akadzozedwa? Nkhani ino ni yozikidwa pa nkhani ya mu Nsanja ya Mlonda ya January 2016, ndipo idzayankha mafunso ocititsa cidwi amenewa.

^ ndime 2 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Kudzozedwa na mzimu woyela: Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake woyela kusankha anthu amene adzalamulila na Yesu kumwamba. Poseŵenzetsa mzimu wake, iye amapatsa anthuwo lonjezo la zinthu zakutsogolo kapena kuti ‘cikole ca colowa cawo cam’tsogolo.’ (Aef. 1:13, 14) Ndiye cifukwa cake Akhristu amenewa angakambe kuti mzimu woyela ‘umawacitila umboni,’ kapena kuti kuwatsimikizila kuti adzalandila mphoto yakumwamba.—Aroma 8:16.

^ ndime 5 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Cidindo. Kuika cidindo cotsiliza pa Mkhristu wodzozedwa kumacitika akatsala pang’ono kumwalila ali wokhulupilika, kapena kudzacitika cisautso cacikulu citatsala pang’ono kuyamba.—Aef. 4:30; Chiv. 7:2-4; onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda ya April 2016.

^ ndime 10 Kuti mudziŵe zambili za tanthauzo la kubadwanso, onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 2009, peji 3; 5; 6; 7; 8; 9-12.

NYIMBO 27 Ana a Mulungu Adzaonekela

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Kaya tinaikidwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cathu, kapena tili na mwayi wolalikila na kuphunzitsa coonadi mwaufulu, timayembekezela mwacidwi kudzakhala na moyo pano dziko lapansi, pamene Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila.