Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Yophunzira 5

Tipita Nanu Limodzi

Tipita Nanu Limodzi

“Tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”​—ZEK. 8:23.

NYIMBO NA. 26 Munachitira Ine Amene

ZIMENE TIPHUNZIRE *

A nkhosa zina (“amuna 10”) akuona kuti ndi mwayi waukulu kulambira Yehova limodzi ndi odzozedwa (“Myuda”) (Onani ndime 1-2)

1. Kodi Yehova ananeneratu zinthu ziti zokhudza nthawi yathuyi?

YEHOVA ananeneratu za nthawi yathu kuti: “Amuna 10 ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zek. 8:23) Palembali, “Myuda” akuimira anthu amene Mulungu wawadzoza ndi mzimu woyera. Iwo amatchedwanso “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) “Amuna 10” akuimira anthu amene akuyembekezera moyo wosatha padzikoli. Iwo amadziwa kuti Yehova akudalitsa odzozedwawa ndipo ndi mwayi kutumikira nawo limodzi.

2. Kodi “amuna 10” amapita bwanji limodzi ndi odzozedwa?

2 N’zoona kuti masiku ano sitingadziwe mayina a odzozedwa onse amene ali padzikoli. * Koma n’zotheka kuti amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli ‘apite nawo limodzi.’ Kodi tingapite nawo bwanji? Baibulo limanena kuti “amuna 10 . . . adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda n’kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” Lembali likutchula za Myuda mmodzi. Koma mawu oti “anthu inu” komanso “inu” akunena za anthu ambiri. Zimenezi zikutanthauza kuti mawu oti Myuda sakunena za munthu mmodzi koma gulu lonse la odzozedwa. Anthu amene si odzozedwa amatumikira Yehova limodzi ndi odzozedwa. Koma saona kuti odzozedwawo ndi atsogoleri awo chifukwa Mtsogoleri wawo ndi Yesu.​—Mat. 23:10.

3. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

3 Popeza odzozedwa ena adakali padzikoli, munthu angadzifunse kuti: (1) Kodi odzozedwa ayenera kudziona bwanji? (2) Kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu amene amadya zizindikiro pa Chikumbutso? (3) Nanga tizidandaula ngati odya zizindikiro akuwonjezereka? Munkhaniyi tipeza mayankho a mafunso amenewa.

KODI AKHRISTU ODZOZEDWA AYENERA KUDZIONA BWANJI?

4. Kodi odzozedwa ayenera kuganizira kwambiri chenjezo liti pa 1 Akorinto 11:27-29? Perekani chifukwa.

4 Odzozedwa ayenera kuganizira kwambiri chenjezo lopezeka pa 1 Akorinto 11:27-29. (Werengani.) Kodi Mkhristu wodzozedwa angadye bwanji zizindikiro “mosayenerera” pa Chikumbutso? Iye angachite zimenezi ngati atadya zizindikirozo koma asakutsatira mfundo za Yehova. (Aheb. 6:4-6; 10:26-29) Odzozedwa amadziwa kuti ayenera kukhalabe okhulupirika ngati akufuna kupeza “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.”​—Afil. 3:13-16.

5. Kodi Akhristu odzozedwa ayenera kudziona bwanji?

5 Mzimu woyera wa Yehova umathandiza atumiki ake kuti akhale odzichepetsa osati onyada. (Aef. 4:1-3; Akol. 3:10, 12) Choncho odzozedwa sadziona kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena. Iwo amadziwa kuti Yehova sapereka kwambiri mzimu woyera kwa odzozedwa kuposa atumiki ake ena. Saganiza kuti iwo amamvetsa bwino mfundo za m’Baibulo kuposa Akhristu ena. Sangauzenso munthu wina kuti nayenso wadzozedwa ndipo ayenera kuyamba kudya zindikiro pa Chikumbutso. M’malomwake, amazindikira kuti Yehova yekha ndi amene amasankha anthu kuti apite kumwamba.

6. Malinga ndi 1 Akorinto 4:7, 8, kodi Akhristu odzozedwa sayenera kuchita chiyani?

6 Odzozedwa amaona kuti ndi mwayi waukulu kusankhidwa kuti apite kumwamba, koma sayembekezera kuti anthu azichita nawo zinthu m’njira yapadera. (Afil. 2:2, 3) Iwo amadziwanso kuti Yehova atawadzoza sanadziwitse anthu ena. Choncho munthu wodzozedwa sadabwa ngati poyamba anthu ena sakukhulupirira kuti wadzozedwa. Iye amazindikira kuti Baibulo limatiuza kuti tisamafulumire kukhulupirira munthu amene wanena kuti Mulungu wamupatsa udindo wapadera. (Chiv. 2:2) Mkhristu wodzozedwa sangafune kudzionetsera, choncho sangauze anthu amene wakumana nawo koyamba kuti ndi wodzozedwa. Ndipo sangadzitame ngakhale pang’ono kuti wadzozedwa.​—Werengani 1 Akorinto 4:7, 8.

7. Kodi odzozedwa amapewa kuchita zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Akhristu odzozedwa sacheza okhaokha poganiza kuti ali m’gulu lapadera. Safufuza odzozedwa ena kuti akambirane za kudzozedwa kwawo kapena kupanga timagulu tophunzirira Baibulo. (Agal. 1:15-17) Ngati Akhristu odzozedwa atachita zimenezi akhoza kusokoneza mgwirizano mumpingo. Ndipo zimenezi zingakhale zosemphana ndi mzimu woyera umene umathandiza anthu a Mulungu kukhala mwamtendere komanso mogwirizana.​—Aroma 16:17, 18.

KODI TIYENERA KUCHITA BWANJI ZINTHU NDI ODZOZEDWA?

Tisamachite zinthu ndi odzozedwa kapena abale ena amene amatsogolera m’gulu ngati ndi anthu otchuka (Onani ndime 8) *

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala pochita zinthu ndi anthu amene amadya zizindikiro? (Onani mawu am’munsi.)

8 Kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi abale ndi alongo odzozedwa? Si bwino kugomera kwambiri munthu ngakhale atakhala wodzozedwa, kapena kuti m’bale wake wa Khristu. (Mat. 23:8-12) Baibulo limanena kuti tiyenera ‘kutsanzira chikhulupiriro’ cha akulu osati kuona munthu winawake ngati mtsogoleri wathu. (Aheb. 13:7) N’zoona kuti Baibulo limanena kuti anthu ena ndi oyenera kuwapatsa “ulemu waukulu.” Koma limanena kuti tizichita zimenezi chifukwa choti ‘amatsogolera bwino’ komanso “amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa,” osati chifukwa choti adzozedwa. (1 Tim. 5:17) Tikamachita chidwi kwambiri ndi odzozedwa kapena kuwatamanda zikhoza kuwachititsa manyazi. * Apo ayi, tikhoza kuwachititsa kuti ayambe kunyada. (Aroma 12:3) Ndiye palibe amene angafune kuchititsa abale a Yesu kuti alakwitse zinthu chonchi.​—Luka 17:2.

9. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Akhristu odzozedwa?

9 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza anthu amene adzozedwa ndi Yehova? Si bwino kuwafunsa kuti, ‘Kodi chinachitika n’chiyani pamene munkadzozedwa?’ Nkhani imeneyi ndi yawo ndipo ifeyo sikutikhudza. (1 Ates. 4:11; 2 Ates. 3:11) Tisamaganizenso kuti anthu ena a m’banja lawo ndi odzozedwanso. Nkhani yodzozedwayi imachokera kwa Mulungu osati m’banja. (1 Ates. 2:12) Tizipewanso kufunsa mafunso amene akhoza kukhumudwitsa anthu ena. Mwachitsanzo, si bwino kufunsa mkazi wa m’bale wodzozedwa kuti, ‘Kodi mumamva bwanji mukaganiza kuti mudzakhala ndi moyo wosatha padzikoli mwamuna wanu kulibe?’ Paja tonse sitikayikira kuti m’dziko latsopano Yehova ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’​—Sal. 145:16.

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti timadziteteza tikamapewa ‘kutamanda anthu ena’?

10 Timadzitetezanso tikamapewa kuona kuti odzozedwa ndi ofunika kwambiri kuposa anthu ena. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limasonyeza kuti mwina odzozedwa ena angasiye kukhala okhulupirika. (Mat. 25:10-12; 2 Pet. 2:20, 21) Choncho tikamapewa ‘kutamanda anthu ena’ zimatithandiza kuti tisamangowatsatira ngakhale atakhala kuti ndi odzozedwa, odziwika kwambiri kapena amene atumikira Yehova kwa nthawi yaitali. (Yuda 16) Ndiye ngati atakhala osakhulupirika kapena kuchoka mumpingo, sitingasiye kukhulupirira Yehova kapena kumutumikira.

KODI TIZIDANDAULA NGATI ANTHU ODYA ZIZINDIKIRO AKUWONJEZEREKA?

11. Kodi n’chiyani chakhala chikuchitika pa chiwerengero cha anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso?

11 Kwa zaka zambiri, chiwerengero cha anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso chinkachepa. Koma posachedwapa, chiwerengerochi chakhala chikuwonjezereka chaka chilichonse. Kodi tiyenera kudandaula ndi zimenezi? Ayi. Tiyeni tikambirane mfundo zina zimene tiyenera kuzikumbukira.

12. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudandaula ndi chiwerengero cha anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso?

12 “Yehova amadziwa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Mosiyana ndi Yehova, abale amene amawerenga anthu odya zizindikiro pa Chikumbutso sadziwa amene adzozedwadi. Choncho pa chiwerengerochi pamakhalanso anthu amene amangoganiza kuti ndi odzozedwa koma asanadzozedwe. Ndipo pali Akhristu ena amene poyamba ankadya zizindikiro koma anasiya. Ena akhoza kukhala ndi matenda a maganizo amene amawachititsa kuganiza kuti adzakalamulira ndi Khristu kumwamba. Kunena zoona, sitidziwa chiwerengero chenicheni cha odzozedwa amene ali padziko lapansili.

13. Kodi Baibulo limatchula chiwerengero cha odzozedwa amene adzakhale padzikoli chisautso chachikulu chikamadzayamba?

13 Padzakhala odzozedwa m’mayiko ambiri Yesu akamadzabwera kudzawatenga. (Mat. 24:31) Baibulo limasonyeza kuti m’masiku otsiriza, padzatsala odzozedwa ena ochepa padzikoli. (Chiv. 12:17) Koma silimatchula chiwerengero cha odzozedwa amene adzakhale adakali padzikoli chisautso chachikulu chikamadzayamba.

Kodi tiyenera kuchita chiyani munthu wina akadya zizindikiro pa Chikumbutso? (Onani ndime 14)

14. Malinga ndi Aroma 9:11, 16, kodi tiyenera kumvetsa mfundo iti pa nkhani ya kusankhidwa kwa odzozedwa?

14 Yehova amasankha nthawi imene akufuna kudzoza anthu. (Aroma 8:28-30) Yehova anayamba kusankha odzozedwa Yesu ataukitsidwa. Zikuoneka kuti nthawi ya atumwi, Akhristu onse anali odzozedwa. Pa zaka zambiri zotsatira, anthu ambiri amene ankati ndi Akhristu sanalidi otsatira enieni a Khristu. Ngakhale zinali choncho, pa nthawiyo Yehova ankadzozabe anthu ochepa amene anali Akhristu oona. Iwo anali ngati tirigu amene Yesu ananena kuti adzakulira limodzi ndi namsongole. (Mat. 13:24-30) M’masiku otsirizawa, Yehova wapitiriza kusankha anthu kuti akhale m’gulu la 144,000. * Choncho ngati Mulungu atasankha kudzoza ena mapeto atatsala pang’ono kufika, sitiyenera kukayikira nzeru zake. (Werengani Aroma 9:11, 16.) * Si bwino kuchita zinthu ngati antchito amene Yesu anawatchula m’fanizo lake lina. Iwo anadandaula ndi zimene mbuye wawo anachitira anthu amene anayamba kugwira ntchito pa ola lomaliza.​—Mat. 20:8-15.

15. Kodi odzozedwa onse ali m’gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wotchulidwa pa Mateyu 24:45-47? Fotokozani.

15 Si onse amene akuyembekezera kupita kumwamba omwe ali m’gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Werengani Mateyu 24:45-47.) Mofanana ndi nthawi ya atumwi, masiku ano Yehova ndi Yesu akugwiritsa ntchito abale ochepa kuti azidyetsa, kapena kuti kuphunzitsa, anthu ambiri. M’nthawi ya atumwi, Akhristu odzozedwa ochepa okha ndi amene anagwiritsidwa ntchito kulemba Malemba Achigiriki. Masiku anonso, Akhristu odzozedwa ochepa okha ndi amene ali ndi udindo wopatsa anthu a Mulungu “chakudya pa nthawi yoyenera.”

16. Kodi mwaphunzira chiyani munkhaniyi?

16 Kodi taphunzira chiyani munkhaniyi? Taphunzira kuti Yehova anasankha kuti anthu ake ambiri adzakhale ndi moyo wosatha padzikoli ndipo ochepa adzakalamulire ndi Yesu kumwamba. Yehova amadalitsa atumiki ake onse, kaya ali m’gulu la “Myuda” kapena la “amuna 10.” Ndipo amafuna kuti onse azimvera malamulo ake komanso kukhalabe okhulupirika. Onse amafunikanso kukhala odzichepetsa, kutumikira Yehova limodzi komanso kukhala ogwirizana. Ayeneranso kuyesetsa kuti mumpingo muzikhalabe mtendere. Pamene mapeto akuyandikira, tiyeni tonse tizitumikira Yehova komanso kutsatira Khristu monga “gulu limodzi.”​—Yoh. 10:16.

^ ndime 5 Chaka chino, mwambo wokumbukira imfa ya Khristu udzachitika Lachiwiri pa April 7. Kodi tiyenera kuwaona bwanji anthu amene adzadye zizindikiro? Kodi tiyenera kudandaula ngati odya zizindikiro akuwonjezereka? Munkhaniyi tipeza mayankho a mafunso amenewa ndipo mfundo zake zikugwirizana ndi za mu Nsanja ya Olonda ya January 2016.

^ ndime 2 Malinga ndi Salimo 87:5, 6, m’tsogolomu Mulungu akhoza kudzaulula mayina a anthu onse amene akulamulira ndi Yesu kumwamba.​—Aroma 8:19.

^ ndime 8 Onani bokosi lakuti “Chikondi ‘Sichichita Zosayenera’” mu Nsanja ya Olonda ya January 2016.

^ ndime 14 Ngakhale kuti lemba la Machitidwe 2:33 limasonyeza kuti mzimu woyera umaperekedwa kudzera mwa Yesu, Yehova ndi amene amasankha munthu aliyense.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri, onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2007.

NYIMBO NA. 34 Kuyenda ndi Mtima Wosagawanika

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kungakhale kupanda ulemu kwambiri ngati abale ataunjikira m’bale woimira likulu ndi mkazi wake n’cholinga choti awajambule pa msonkhano.