Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 5

Tipita Nanu Limodzi

Tipita Nanu Limodzi

Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’​—ZEK. 8:23.

NYIMBO 26 Munacitila Ine

ZIMENE TIKAMBILANE *

A nkhosa zina (“amuna 10”) amaona kuti ni mwayi wapadela kulambila Yehova pamodzi na odzozedwa (“Myuda”) (Onani ndime 1-2)

1. Kodi Yehova anakamba kuti n’ciani cidzacitika masiku ano?

YEHOVA anakambilatu kuti masiku ano, “amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zek. 8:23) Pa lembali, “Myuda” akuimila anthu amene Mulungu anawadzoza na mzimu woyela. Iwo amachedwanso “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) “Amuna 10” akuimila anthu amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi kwamuyaya. Iwo amadziŵa kuti odzozedwa ni anthu amene Yehova anawasankha mwapadela, ndipo amaona kuti ni mwayi kutumikila Mulungu pamodzi nawo.

2. Kodi “amuna 10” amapita bwanji limodzi na odzozedwa?

2 Popeza n’zosatheka kudziŵa maina a odzozedwa onse amene ali padziko lapansi, * zingatheke bwanji kuti a nkhosa zina ‘apite nawo limodzi’? Baibo imakamba kuti “amuna 10” “adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” Lembali lakamba kuti Myuda ngati kuti likunena za munthu mmodzi. Koma mawu akuti “nanu” ndi akuti “anthu inu,” aonetsa kuti likukamba za anthu ambili osati za munthu mmodzi. Izi zitanthauza kuti Myuda ameneyu si munthu mmodzi koma akuimila gulu lonse la odzozedwa. Akhristu a nkhosa zina amatumikila Yehova pamodzi na odzozedwa, koma saona odzozedwa monga atsogoleli awo. Amadziŵa kuti Yesu ndiye Mtsogoleli wathu.—Mat. 23:10.

3. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana mafunso ati?

3 Popeza Akhristu odzozedwa akalipo pano pa dziko lapansi, ena angafunse kuti: (1) Kodi odzozedwa ayenela kudziona bwanji? (2) Kodi Mkhristu wina mu mpingo akayamba kudya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso, tiyenela kucita naye zinthu motani? (3) Kodi tiyenela kuda nkhawa tikaona kuti ciŵelengelo ca amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso cikukwela? Nkhani ino idzayankha mafunso amenewa.

KODI ODZOZEDWA AYENELA KUDZIONA BWANJI?

4. Ni cenjezo liti lopezeka pa 1 Akorinto 11:27-29 limene odzozedwa ayenela kuliganizila mosamala? Nanga n’cifukwa ciani?

4 Odzozedwa ayenela kuganizila mosamala cenjezo limene lili pa 1 Akorinto 11:27-29. (Ŵelengani.) Kodi wodzozedwa angadye bwanji mkate na kumwa vinyo “mosayenelela” pa Cikumbutso? Angacite izi ngati wadya mkate na kumwa vinyo pamene zocita zake sizigwilizana na mfundo zolungama za Yehova. (Aheb. 6:4-6; 10:26-29) Odzozedwa amadziŵa kuti ayenela kukhalabe okhulupilika kuti akalandile “mphoto ya ciitano ca Mulungu copita kumwamba, codzela mwa Khristu Yesu.”—Afil. 3:13-16.

5. Kodi odzozedwa ayenela kudziona bwanji?

5 Mzimu woyela wa Yehova umathandiza atumiki ake kukhala odzicepetsa, osati odzikuza. (Aef. 4:1-3; Akol. 3:10, 12) Conco, odzozedwa sadziona kuti ni apamwamba kuposa anthu ena. Saganiza kuti cifukwa ni odzozedwa, Yehova amawapatsa mzimu woyela wambili kuposa a nkhosa zina. Ndipo sadziona kuti ndiwo amadziŵa kwambili coonadi ca m’Baibo kuposa anthu ena. Komanso sangauze munthu wina kuti nayenso wadzozedwa ndipo ayambe kudya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso. M’malomwake, amakhala odzicepetsa ndipo amadziŵa kuti Yehova yekha ndiye amaitana anthu kuti akapite kumwamba.

6. Malinga na 1 Akorinto 4:7, 8, kodi odzozedwa ayenela kukhala na khalidwe lotani?

6 N’zoona kuti odzozedwa amaona kuti ni mwayi wamtengo wapatali kuitanidwa kupita kumwamba, koma sayembekezela kuti anthu azicita nawo zinthu mwapadela. (Afil. 2:2, 3) Iwo amadziŵa kuti pamene Yehova anawadzoza sanadziŵitse munthu aliyense. Conco, wodzozedwa sayenela kudabwa ngati anthu sakhulupilila mwamsanga kuti iye wadzozedwa. Amadziŵa kuti Baibo imatilangiza kuti sitiyenela kukhulupilila mwamsanga ngati munthu wakamba kuti Mulungu anam’patsa udindo winawake wapadela. (Chiv. 2:2) Popeza kuti odzozedwa sadzifunila ulemu, iwo sauza munthu aliyense amene akumana naye koyamba kuti ni odzozedwa. Komanso, sadzitama pakati pa ena cifukwa cakuti anadzozedwa.—Ŵelengani 1 Akorinto 4:7, 8.

7. Kodi Akhristu odzozedwa amapewa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

7 Akhristu odzozedwa saona kuti afunika kumaceza na odzozedwa anzawo okha-okha, monga kuti ali m’kabungwe kena-kake kapadela. Iwo safufuza odzozedwa anzawo kuti azikambilana nkhani zokhudza odzozedwa, ndipo sakumana m’tumagulu kuti aziphunzila Baibo. (Agal. 1:15-17) Ngati odzozedwa angacite zimenezi, mpingo sungakhale wogwilizana. Ndipo kucita izi kungakhale ngati kulimbana na mzimu woyela, umene umathandiza anthu a Mulungu kukhala mwamtendele na mogwilizana.—Aroma 16:17, 18.

KODI ODZOZEDWA TIYENELA KUCITA NAWO ZINTHU MOTANI?

Odzozedwa kapena abale ena amene amatsogolela m’gulu sitiyenela kucita nawo zinthu monga anthu ochuka a m’dzikoli (Onani ndime 8) *

8. N’cifukwa ciani tiyenela kusamala na mmene timacitila zinthu na Akhristu amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso? (Onaninso mawu a munsi.)

8 Kodi odzozedwa tiyenela kucita nawo zinthu motani? Si bwino kutamanda kapena kulemekeza munthu mopambanitsa, ngakhale atakhala m’bale wodzozedwa wa Khristu. (Mat. 23:8-12) Ponena za akulu mu mpingo, Baibo imatilangiza kuti tiyenela ‘kutsanzila cikhulupililo cawo.’ Koma siitilangiza kuti tiyenela kuona munthu wina aliyense monga mtsogoleli wathu. (Aheb. 13:7) N’zoona kuti Baibo imakamba kuti akulu afunika ‘kupatsidwa ulemu waukulu.’ Koma imakamba zimenezo osati cifukwa cakuti ni odzozedwa, koma cifukwa cakuti ‘amatsogolela bwino’ ndiponso “amacita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” (1 Tim. 5:17) Sitiyenela kulemekeza odzozedwa mopambanitsa cifukwa kucita zimenezi kungawacititse manyazi. * Ndipo vuto lalikulu n’lakuti tingapangitse kuti ayambe kudzikweza. (Aroma 12:3) Tonsefe sitifuna kupangitsa aliyense wa abale odzozedwa a Khristu kucita colakwa cacikulu ngati cimeneci.—Luka 17:2.

9. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza Akhristu odzozedwa?

9 Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza odzozedwa a Yehova? Sitiyenela kuwafunsa mmene anadzozedwela cifukwa iyi ni nkhani yaumwini, imene sitifunika kudziŵa. (1 Ates. 4:11; 2 Ates. 3:11) Sitiyenela kuganiza kuti mwamuna kapena mkazi wa wodzozedwa, makolo ake, kapena abululu ake naonso ni odzozedwa. Munthu salandila ciyembekezo cimeneci monga colowa ca banja lake, koma amacita kuitanidwa na Mulungu. (1 Ates. 2:12) Tiyenelanso kupewa kufunsa mafunso amene angakhumudwitse ena. Mwacitsanzo, sitiyenela kufunsa mkazi wa wodzozedwa kuti; ‘Kodi mumamvela bwanji mukaganizila zokhala m’dziko latsopano kwamuyaya popanda amuna anu?’ Tisakayikile olo pang’ono kuti m’dziko latsopano, Yehova ‘adzakhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.’—Sal. 145:16.

10. Kodi timadziteteza bwanji ngati tipewa ‘kutamanda anthu ena’?

10 Ngati tipewa kuona odzozedwa kukhala apamwamba kuposa ena, timadziteteza. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cakuti Baibo imakamba kuti odzozedwa ena angakhale osakhulupilika m’kupita kwa nthawi. (Mat. 25:10-12; 2 Pet. 2:20, 21) Conco, ngati tipewa ‘kutamanda anthu ena,’ sitidzatsatila munthu aliyense, ngakhale atakhala wodzozedwa, m’bale wodziŵika, kapena amene watumikila Yehova kwa nthawi yaitali. (Yuda 16) Ndipo munthuyo atasintha n’kukhala wosakhulupilika kapena atacotsedwa mu mpingo, sitidzataya cikhulupililo cathu mwa Yehova kapena kuleka kum’tumikila.

KODI TIYENELA KUDA NKHAWA NA KUCULUKA KWA CIŴELENGELO CAWO?

11. N’ciani cakhala cikucitika na ciŵelengelo ca Akhristu amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso?

11 Kwa zaka zambili, ciŵelengelo ca amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso cinali kutsika. Koma m’zaka zaposacedwa, ciŵelengeloci cakhala cikukwela caka ciliconse. Kodi izi ziyenela kutidetsa nkhawa? Iyai. Tiyeni tikambilane mfundo zina zofunika kukumbukila pa nkhaniyi.

12. N’cifukwa ciani sitiyenela kuda nkhawa na ciŵelengelo ca amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso?

12 “Yehova amadziŵa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Mosiyana na Yehova, abale amene amaŵelenga anthu odya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso sadziŵa kuti odzozedwa eni-eni ni ati. Motelo, ciŵelengelo cimeneco cimaphatikizapo anthu amene si odzozedwa eni-eni. Mwacitsanzo, anthu ena anali kudya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso, koma patapita nthawi analeka. Ena ali na matenda a maganizo kapena nkhawa yaikulu imene imapangitsa kuti ayambe kukhulupilila kuti adzalamulila na Khristu kumwamba. Conco, sitidziŵa ciŵelengelo ceni-ceni ca odzozedwa amene akali padziko lapansi.

13. Kodi Baibo imachula ciŵelengelo ca odzozedwa amene adzakhala pa dziko lapansi pa nthawi imene cisautso cacikulu cidzayamba?

13 M’madela ambili pa dziko lapansi, mudzakhala odzozedwa pamene Yesu adzabwela kudzawatenga kuti apite kumwamba. (Mat. 24:31) N’zoona kuti Baibo imakamba kuti m’masiku otsiliza, pa dziko lapansi padzakhala odzozedwa ocepa. (Chiv. 12:17) Koma sikamba kuti ni angati amene adzakhalapo cisautso cacikulu cikadzayamba.

Kodi Mkhristu wina mu mpingo akayamba kudya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso, tiyenela kumuona bwanji? (Onani ndime 14)

14. Malinga na Aroma 9:11, 16, n’ciani cimene tiyenela kudziŵa pa nkhani yosankha odzozedwa?

14 Yehova ndiye amasankha nthawi yodzoza anthu. (Aroma 8:28-30) Yehova anayamba kusankha odzozedwa Yesu ataukitsidwa. Cioneka kuti m’nthawi ya atumwi, Akhristu onse oona anali odzozedwa. Zaka zambili pambuyo pake, anthu ambili amene anali kukamba kuti ni Akhristu sanali Akhristu oona. Ngakhale n’conco, Yehova anali kudzoza Akhristu oona ocepa amene analipo. Iwo anali ngati tiligu amene Yesu anakamba kuti adzamela pakati pa namsongole. (Mat. 13:24-30) M’masiku otsiliza ano, Yehova akusankhabe anthu amene adzakhala m’gulu la a 144,000. * Cotelo, ngati Mulungu akusankha anthu ena mapeto atatsala pang’ono kufika, sitiyenela kuona ngati akulakwitsa. (Ŵelengani Aroma 9:11, 16.) * Tiyenela kusamala kuti tisacite zinthu monga anchito amene Yesu anakamba m’fanizo lake. Iwo anadandaula cifukwa ca malipilo amene mbuye wawo anapatsa anchito ena amene anayamba kugwila nchito mu ola lotsiliza.—Mat. 20:8-15.

15. Kodi Akhristu onse odzozedwa ali mbali ya “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” wochulidwa pa Mateyu 24:45-47? Fotokozani.

15 Si odzozedwa onse amene ni mbali ya “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Ŵelengani Mateyu 24:45-47.) Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, masiku ano Yehova na Yesu akudyetsa anthu ambili kapena kuti kuwaphunzitsa pogwilitsila nchito anthu ocepa. M’nthawi ya atumwi, Mulungu anagwilitsila nchito Akhristu odzozedwa ocepa kuti alembe Malemba Acigiriki Acikhristu. Masiku anonso, ni Akhristu odzozedwa ocepa cabe amene ali na udindo wopatsa anthu a Mulungu “cakudya pa nthawi yoyenela.”

16. Kodi mwaphunzila ciani m’nkhani ino?

16 N’ciani cimene taphunzila m’nkhani ino? Yehova anakonza zopatsa atumiki ake ambili mwayi wokhala na moyo wosatha pano pa dziko lapansi, koma ena ocepa adzawapatsa mwayi wopita kumwamba kuti akalamulile pamodzi na Yesu. Yehova adzapatsa atumiki ake onse mphoto, amene akuimilidwa na “Myuda” ndiponso amene akuimilidwa na “amuna 10.” Iye amafuna kuti tonse tizimvela malamulo ake na kukhalabe okhulupilika. Tonse tifunika kukhalabe odzicepetsa. Tonse tifunika kum’tumikila pamodzi mogwilizana. Ndipo tonse tiyenela kuyesetsa kulimbikitsa mtendele mu mpingo. Pamene mapeto akuyandikila, tiyeni tonse tipitilize kutumikila Yehova na kutsatila Khristu monga gulu limodzi la nkhosa.—Yoh. 10:16.

^ ndime 5 Caka cino, Cikumbutso ca imfa ya Khristu cidzacitika pa Ciŵili, pa April 7. Kodi Akhristu amene adzadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso, tiyenela kuwaona bwanji? Kodi tiyenela kuda nkhawa tikaona kuti ciŵelengelo ca amene amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso cikukwela? Nkhani ino iyankha mafunso amenewa, ndipo yazikidwa pa nkhani imene inatuluka mu Nsanja ya Mlonda ya January 2016.

^ ndime 2 Malinga na lemba la Salimo 87:5, 6, n’kutheka kuti kutsogolo Mulungu adzatidziŵitsa maina a anthu onse amene adzakhala akulamulila na Yesu kumwamba.—Aroma 8:19.

^ ndime 8 Onani bokosi yakuti Cikondi “Sicicita Zosayenela” mu Nsanja ya Mlonda ya January 2016, peji 26.

^ ndime 14 Olo kuti lemba la Machitidwe 2:33 limaonetsa kuti munthu amalandila mzimu woyela kudzela mwa Yesu, Yehova ndiye amaitana munthuyo.

^ ndime 14 Kuti mudziŵe zambili pa nkhaniyi, ŵelengani nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2007.

NYIMBO 34 N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Yelekezelani kuti kwabwela m’bale woimila likulu la pa dziko lonse na mkazi wake, ndipo abale amuunjilila kuti amujambule. Kodi si kupanda ulemu kumeneku?