Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 6

Atate Wathu Yehova, Amatikonda Kwambili

Atate Wathu Yehova, Amatikonda Kwambili

Inu muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba.’” ​—MAT. 6:9.

NYIMBO 135 Yehova Alangiza Mwacikondi Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzelu”

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi munthu anali kufunika kucita ciani kuti akambe na mfumu ya Perisiya?

YELEKEZELANI kuti munali na moyo zaka 2,500 zapitazo, ndipo munali kukhala ku Perisiya. Mufuna kukamba na mfumu ya dzikolo pa nkhani inayake. Conco, mwanyamuka kupita ku mzinda wa Susani, kumene kukhala mfumuyo. Koma mucita kudziŵilatu kuti musanakambe na mfumuyo, mufunika kupempha cilolezo coyamba. Apo ayi, mukhoza kuphedwa!—Esitere 4:11.

2. Kodi Yehova amafuna kuti tizimangika pokamba naye?

2 Tiyamikila kwambili kuti Yehova sali monga mfumu ya Perisiya imeneyo. Olo kuti ni wamphamvu komanso wapamwamba kwambili kuposa wolamulila aliyense waumunthu, tingakambe naye nthawi iliyonse imene tafuna. Ndipo amafuna kuti tizikhala womasuka kukamba naye. Mwacitsanzo, ngakhale kuti ali na maina audindo apamwamba kwambili, monga akuti Mlengi Wamkulu, Wamphamvuzonse, ndiponso Ambuye Wamkulu Koposa, iye amafunanso kuti pokamba naye tizimuchula na dzina loonetsa cibale lakuti “Atate.” (Mat. 6:9) N’zokondweletsa kwambili kudziŵa kuti Yehova amafuna kuti tizimuona kuti ni Tate wathu.

3. N’cifukwa ciani timachula Yehova kuti “Atate” wathu? Nanga m’nkhani ino tikambilana ciani?

3 M’poyenela kuchula Yehova kuti “Atate” cifukwa ndiye anatilenga. (Sal. 36:9) Popeza kuti iye ni Atate wathu, tifunika kumamumvela. Ngati ticita zimenezi, tidzalandila madalitso osaneneka. (Aheb. 12:9) Madalitso amenewo aphatikizapo mwayi wodzakhala na moyo wamuyaya, kaya kumwamba kapena pano pa dziko lapansi. Ngakhale pali pano timalandila madalitso cifukwa comumvela. M’nkhani ino, tikambilana mmene Yehova amatisamalila pali pano monga Tate wathu, ndiponso cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti m’tsogolo sadzatisiya olo pang’ono. Koma coyamba, tiyeni tikambilane cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti Atate wathu wakumwamba Yehova amatikonda kwambili ndipo amafuna kutithandiza.

YEHOVA NI TATE WACIKONDI AMENE AMATISAMALILA

Yehova amafuna kuti tikhale bwenzi lake, monga mmene tate wacikondi amakhalila bwenzi la ana ake (Onani ndime 4)

4. N’cifukwa ciani anthu ena zimawavuta kuona Yehova monga Tate wawo?

4 Kodi zimakuvutani kuona Mulungu monga Tate wanu? Ena amadziona kuti ni osanunkha kanthu pamaso pa Yehova. Amakayikila zakuti Mulungu Wamphamvuzonse amawaona kuti ni ofunika. Komabe, Atate wathu wacikondiyo safuna kuti tizimuona mwanjila imeneyi. Iye anatipatsa moyo ndipo amafuna kuti tikhale naye pa ubale. Pambuyo pofotokoza mfundo imeneyi, mtumwi Paulo anauza anthu a ku Atene amene anali kumumvetsela kuti Yehova “sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:24-29) Yehova amafuna kuti tizikamba naye momasuka monga mmene mwana amakambila na kholo lake lacikondi.

5. Tiphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila mlongo amene wafotokozedwa m’ndimeyi?

5 Ena zimawavuta kuona Yehova monga Tate wawo cifukwa cakuti atate wawo wowabala sanali kuwaonetsa cikondi komanso sanali kucita nawo zinthu mokoma mtima. Ganizilani zimene mlongo wina anakamba. Iye anati: “Atate ŵanga anali kunicitila nkhanza kwambili. Conco n’tayamba kuphunzila Baibo, cinali covuta kuti niyambe kuona Yehova monga Atate anga akumwamba. Koma n’tamudziŵa bwino Yehova, vuto limeneli linasila.” Kodi na imwe mumamvela conco? Ngati n’telo, musataye mtima. Na imwe mungayambe kuona Yehova kuti ni Tate wabwino kwambili kuposa tate aliyense.

6. Malinga na Mateyu 11:27, n’ciani cimene Yehova anacita pofuna kutithandiza kuti tizimuona kuti ni Tate wathu wacikondi?

6 Cimodzi cimene Yehova anacita pofuna kutithandiza kuti tizimuona kuti ni Tate wathu wacikondi, ni kuonetsetsa kuti zimene Yesu anakamba na kucita zilembedwe m’Baibo. (Ŵelengani Mateyu 11:27.) Yesu anatengela kwambili makhalidwe a Atate wake moti anafika pokamba kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Nthawi zambili, Yesu anali kuchula Yehova kuti Atate. Mwacitsanzo, m’mabuku a Uthenga Wabwino mokha, amene alipo anayi, Yesu anali kuseŵenzetsa kaŵili-kaŵili dzina lakuti “Atate” pokamba za Yehova. N’cifukwa ciani Yesu anali kugwilitsila nchito kwambili dzina laudindo lakuti “Atate” pokamba za Yehova? Cifukwa cimodzi n’cakuti anali kufuna kuthandiza anthu kuti azikhulupilila kuti Yehova ni Tate wacikondi.—Yoh. 17:25, 26.

7. Tiphunzila ciani za Yehova tikaganizila mmene anali kucitila zinthu na Mwana wake?

7 Tsopano tiyeni tione zimene tingaphunzile ponena za Yehova mwa kukambilana mmene iye anali kucitila zinthu na Mwana wake Yesu. Nthawi zonse, Yehova anali kumvetsela mapemphelo a Yesu. Sanali kungomvetsela cabe mapemphelo ake, koma analinso kumuyankha. (Yoh. 11:41, 42) Pa mavuto alionse amene Yesu anali kukumana nawo, anali kuona kuti Atate wake anali kumuthandiza na kumukonda.—Luka 22:42, 43.

8. Kodi Yehova anali kumusamalila bwanji Yesu?

8 Yesu anali kudziŵa kuti Yehova ndiye anamupatsa moyo, komanso kuti ndiye anali kumupatsa zofunikila kuti akhalebe na moyo. Ndiye cifukwa cake anati: “Ine ndili ndi moyo cifukwa ca Atate.” (Yoh. 6:57) Yesu anali kudalila kwambili Yehova Atate wake, ndipo iye anali kupatsa Yesu zofunikila kuti apitilize kukhala na moyo. Cofunika kuposa zonse n’cakuti Yehova anali kum’samalila Yesu mwauzimu.—Mat. 4:4.

9. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kwa Yesu kuti ni Tate wacikondi?

9 Pokhala Tate wacikondi, Yehova anali kuonetsetsa kuti Yesu akudziŵa kuti Iye adzamuthandiza. (Mat. 26:53; Yoh. 8:16) Ngakhale kuti Yehova sanali kuchinjiliza Yesu ku mavuto onse, anali kumuthandiza kupilila mavutowo. Yesu anali kudziŵa kuti vuto lililonse limene angakumane nalo lidzakhala lakanthawi cabe. (Aheb. 12:2) Yehova anaonetsa kuti anali kum’konda Yesu mwa kumvetsela mapemphelo ake, kum’samalila, kumuphunzitsa, na kumuthandiza. (Yoh. 5:20; 8:28) Atate wathu wakumwamba amatisamalila monga mmene anali kusamalila Yesu. Tiyeni tione mmene amacitila zimenezi.

KODI ATATE WATHU WACIKONDI AMATISAMALILA BWANJI?

Tate wacikondi (1) amamvetsela kwa ana ake, (2) amawapatsa zofunikila pa umoyo, (3) amawaphunzitsa, ndiponso (4) amawateteza. Umu ni mmenenso Atate wathu wakumwamba amatisamalila (Onani ndime 10-15) *

10. Malinga na Salimo 66:19, 20, kodi Yehova amaonetsa bwanji kuti amatikonda?

10 Yehova amamvetsela mapemphelo athu. (Ŵelengani Salimo 66:19, 20.) Iye satiikila malile pa kuculuka kwa mapemphelo amene tingapeleke, utali wake, kapena zinthu zimene tingapemphe. Ndipo amatilimbikitsa kupemphela kaŵili-kaŵili. (1 Ates. 5:17) Tingapemphele kwa Mulungu wathu nthawi iliyonse, kulikonse kumene tingakhale. Iye sakhala wotangwanika kwambili moti n’kulephela kumvetsela mapemphelo athu. Ni womasuka nthawi zonse kumvetsela mwachelu tikamakamba naye. Tikazindikila kuti Yehova amayankha mapemphelo athu, timayamba kumukonda kwambili. Wamasalimo anati: “Mtima wanga ndi wodzaza ndi cikondi [pa Mulungu], cifukwa Yehova amamva mawu anga.”—Sal. 116:1.

11. Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphelo athu?

11 Kuwonjezela pa kumvetsela mapemphelo athu, Atate wathu amayankha mapemphelowo. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.” (1 Yoh. 5:14, 15) Nthawi zina, Yehova sayankha mapemphelo athu m’njila imene tinali kuyembekezela. Iye amadziŵa zimene zili zabwino kwambili kwa ife. Conco, nthawi zina yankho lake lingakhale ayi. Ndipo nthawi zinanso amafuna kuti tiyembekezele.—2 Akor. 12:7-9.

12-13. Kodi Atate wathu wakumwamba amatisamalila bwanji?

12 Yehova amatisamalila. Yehova amafuna kuti tate aliyense azisamalila banja lake, ndipo n’zimene iyenso amacita. (1 Tim. 5:8) Amatisamalila mwakuthupi monga ana ake. Safuna kuti tizidela nkhawa za cakudya, zovala, kapena pogona. (Mat. 6:32, 33; 7:11) Ndipo pokhala Tate wacikondi, iye wakonzanso zakuti adzatipatse zofunikila zonse zakutsogolo.

13 Cofunika kwambili n’cakuti Yehova amatisamalila mwauzimu. Kupitila m’Mawu ake, Yehova watiphunzitsa coonadi ponena za iye, colinga cake, colinga ca moyo, na zimene zidzacitika kutsogolo. Iye anaonetsa kuti amatikonda aliyense payekha mwa kutiphunzitsa coonadi. Anaseŵenzetsa makolo athu kapena ofalitsa ena potithandiza kuti timudziŵe bwino. Ndipo akupitiliza kutithandiza mokoma mtima kupitila mwa akulu acikondi komanso abale na alongo ena ofikapo mwauzimu. Kuwonjezela apo, Yehova amatilangiza kupitila m’misonkhano yampingo. Pa misonkhano imeneyi, timaphunzitsidwa pamodzi na abale na alongo athu auzimu. Izi ni zina mwa njila zimene Yehova amaonetsela cikondi kwa ife tonse monga Tate wathu.—Sal. 32:8.

14. N’cifukwa ciani Yehova amatilanga? Nanga amacita bwanji zimenezi?

14 Yehova amatiphunzitsa. Mosiyana na Yesu, ife ndife opanda ungwilo. Conco, monga njila ina yotiphunzitsila, Atate wathu wacikondi Yehova, amatipatsa cilango pakakhala pofunikila. Mawu ake amatikumbutsa kuti: “Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.” (Aheb. 12:6, 7) Yehova amatilanga m’njila zambili. Mwacitsanzo, zimene timaŵelenga m’Mawu ake kapena kumvetsela pa misonkhano zingatithandize kuwongolela mbali zimene siticita bwino. Nthawi zina, tingalandile malangizo ofunikila kupitila mwa akulu. Koma mulimonse mmene Yehova angapelekele cilango cake, nthawi zonse amacita izi cifukwa cotikonda.—Yer. 30:11.

15. Kodi Yehova amatiteteza bwanji?

15 Yehova amatithandiza tikakumana na mavuto. Tate amathandiza ana ake pamene akuvutika. Nawonso Atate wathu wakumwamba amatithandiza tikakumana na mavuto. Amatiteteza mwauzimu poseŵenzetsa mzimu wake woyela. (Luka 11:13) Kuwonjezela apo, Yehova amatithandiza tikalefuka. Mwacitsanzo, anatipatsa ciyembekezo cabwino kwambili. Ciyembekezo cimeneci cimatithandiza kupilila mavuto. Tangoganizani! Olo tikumane na mavuto otani, timadziŵa kuti Atate wathu wacikondi adzathetselatu zopweteka zonse zobwela cifukwa ca mavutowo. Mavuto aliwonse amene tikukumana nawo ni akanthawi cabe, koma madalitso amene Yehova adzatipatsa ni amuyaya.—2 Akor. 4:16-18.

ATATE WATHU SADZATISIYA OLO PANG’ONO

16. N’ciani cinacitika pamene Adamu anacimwila Atate wake wacikondi?

16 Timaona umboni wakuti Yehova amatikonda tikaganizila mmene anacitila zinthu pamene Adamu anaphwanya lamulo lake mu Edeni. Adamu atacimwa, anataya mwayi wake komanso wa mbadwa zake wokhala m’banja la Yehova la anthu acimwemwe. (Aroma 5:12; 7:14) Koma Yehova anacitapo kanthu kuti athandize mbadwa za Adamu.

17. Adamu atacimwa, kodi Yehova anacita ciani nthawi yomweyo?

17 Yehova anamupatsa cilango Adamu. Koma analonjeza kuti adzathandiza mbadwa zake. Adamu atangocimwa, Yehova nthawi yomweyo analonjeza kuti anthu omvela adzakhalanso mbali ya banja lake. (Gen. 3:15; Aroma 8:20, 21) Kuti izi zitheke, iye anapeleka Mwana wake wokondedwa, Yesu, monga nsembe ya dipo. Pamene anapeleka Mwana wake kaamba ka ife, Yehova anaonetsa cikondi cacikulu cimene ali naco pa ife.—Yoh. 3:16.

Ngati tinapatuka pa njila ya coonadi koma tsopano tinalapa, Atate wathu wacikondi Yehova ni wokonzeka kutilandila tikabwelela kwa iye (Onani ndime 18)

18. Tidziŵa bwanji kuti Yehova amafuna kuti tibwelele kwa iye olo kuti tinapatuka pa njila ya coonadi?

18 Olo kuti ndife opanda ungwilo, Yehova amafuna kuti tiloŵe m’banja lake. Sationa ngati ana ovuta. Nthawi zina tingamucimwile kapena tingapatuke pa njila ya coonadi, koma Yehova amaleza nafe mtima. Pofuna kuonetsa cikondi cimene Yehova ali naco monga Tate wathu, Yesu anakamba fanizo la mwana woloŵelela. (Luka 15:11-32) Tate wa m’fanizo limeneli sanataye ciyembekezo cakuti mwana wake adzabwelela. Mwanayo atabwelela ku nyumba, atate wake anamulandila na manja aŵili. Ngati munapatuka pa njila ya coonadi koma tsopano munalapa, dziŵani kuti Atate wathu wacikondi ni wokonzeka kukulandilani mukabwelela kwa iye.

19. Kodi Yehova adzakonza bwanji zinthu zimene zawonongeka cifukwa ca kupanduka kwa Adamu?

19 Atate wathu adzakonza zonse zimene zawonongeka cifukwa ca kupanduka kwa Adamu. Adamu atapanduka, Yehova anaganiza zotenga anthu 144,000 kuti akatumikile monga mafumu na ansembe kumwamba pamodzi na Mwana wake. Yesu na olamulila anzake amenewo adzathandiza anthu omvela kukhala angwilo m’dziko latsopano. Akadzakhalabe okhulupilika pa ciyeso cotsiliza, Mulungu adzawapatsa moyo wosatha. Pa nthawiyo, Yehova adzakondwela kwambili kuona kuti dziko lonse ladzala ndi ana ake angwilo, aamuna ndi aakazi. Ndithudi! Idzakhala nthawi yokondweletsa kwambili!

20. Kodi Yehova waonetsa m’njila ziti kuti amatikonda kwambili? Nanga m’nkhani yotsatila tidzakambilana ciani?

20 Yehova waonetsa kuti amatikonda kwambili. Iye ni Tate wabwino koposa. Amamva mapemphelo athu ndiponso amatisamalila, ponse paŵili mwakuthupi komanso mwauzimu. Kuwonjezela apo, amatiphunzitsa na kutithandiza. Ndipo m’tsogolo adzatipatsa madalitso osaneneka. N’zokondweletsa cotani nanga kudziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda na kutisamalila! Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene ife ana ake tingaonetsele kuti timayamikila cikondi cake.

NYIMBO 108 Cikondi Cokhulupilika ca Mulungu

^ ndime 5 Nthawi zambili, Yehova timamuona kuti ni Mlengi wathu komanso Wolamulila wa cilengedwe conse. Koma tiyenelanso kumuona monga Tate wathu wacikondi, ndipo pali zifukwa zomveka zotipangitsa kumuona mwa njila imeneyi. M’nkhani ino, tikambilana zifukwa zimenezo. Tikambilananso cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti Yehova sadzatisiya olo pang’ono.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Zithunzi zinayi zoonetsa tate na mwana wake: tate amvetsela mwachelu pamene mwana wake akamba naye, tate apatsa cakudya mwana wake, tate aphunzitsa mwana wake, komanso tate atonthoza mwana wake. Cithunzi ca dzanja la Yehova cimene cili kuseli kwa zithunzizo citikumbutsa kuti umu ni mmenenso Yehova amatisamalila.