Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 9

Muzilola Kuti Yehova Azikutonthozani

Muzilola Kuti Yehova Azikutonthozani

“Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”​—SAL. 94:19.

NYIMBO NA. 44 Pemphero la Munthu Wovutika

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatidetse nkhawa, nanga nkhawazo zingatikhudze bwanji?

KODI munavutikapo ndi nkhawa? * Mwina munadapo nkhawa chifukwa chokhumudwa ndi zimene anthu ena ananena kapena kuchita. Apo ayi, mungamade nkhawa ndi zimene inuyo munanena kapena kuchita. Mwachitsanzo, mwina munalakwitsapo zinazake ndipo mumaona kuti Yehova sangakukhululukireni. Mwinanso mumaganiza kuti popeza mumada nkhawa kwambiri, ndiye kuti mulibe chikhulupiriro chokwanira ndipo si inu munthu wabwino. Koma kodi zimenezi ndi zoona?

2. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti kuda nkhawa sikutanthauza kuti tilibe chikhulupiriro?

2 Tiyeni tikambirane zitsanzo za anthu ena otchulidwa m’Baibulo. Chitsanzo choyamba ndi Hana, yemwe anadzakhala mayi ake a mneneri Samueli. Iye anali ndi chikhulupiriro cholimba koma ankada nkhawa kwambiri chifukwa chakuti munthu wina wa m’banja lake ankamuchitira nkhanza. (1 Sam. 1:7) Nayenso mtumwi Paulo anali ndi chikhulupiriro cholimba koma ankavutika ndi ‘nkhawa imene ankakhala nayo pa mipingo yonse.’ (2 Akor. 11:28) Chitsanzo china ndi Mfumu Davide yemwe anali ndi chikhulupiriro champhamvu ndipo Yehova ankamukonda kwambiri. (Mac. 13:22) Koma Davide analakwitsa zinthu zina zimene zinachititsa kuti azida nkhawa kwambiri. (Sal. 38:4) Yehova anatonthoza atumiki ake onsewa ndipo anawathandiza kuti apezenso mtendere. Tsopano tiyeni tikambirane zimene tikuphunzira kwa atumiki amenewa.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA HANA

3. N’chifukwa chiyani tingamade nkhawa ndi zolankhula za ena?

3 Tingayambe kuda nkhawa munthu wina akatilankhula zinthu zopweteka kapena kutichitira zinthu mopanda chikondi. Ndipo zimakhala zopweteka kwambiri ngati munthuyo ndi mnzathu wapamtima kapena wachibale. Tikhoza kumada nkhawa kuti mwina sitidzagwirizananso ndi munthuyo. Nthawi zina munthu angatilankhule mosaganiza bwino ndipo zingakhale zopweteka ngati talasidwa ndi lupanga. (Miy. 12:18) Pomwe ena angatilankhule mwadala mawu opweteka kwambiri. Zimenezi zinachitikirapo mlongo wina. Iye anati: “Zaka zochepa zapitazo, mnzanga wina wapamtima anayamba kufalitsa pa intaneti mabodza okhudza ineyo. Zinandipweteka ndipo ndinayamba kuda nkhawa. Sindinkamvetsa chimene chinamuchititsa kuchita zimenezi.” Ngati munakhumudwitsidwapo ndi mnzanu wapamtima kapena wachibale, kodi mungaphunzire chiyani kwa Hana?

4. Kodi Hana anakumana ndi mavuto otani?

4 Hana anakumana ndi mavuto aakulu. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri anali wosabereka. (1 Sam. 1:2) Aisiraeli ambiri ankakhulupirira kuti ngati munthu ndi wosabereka ndiye kuti Mulungu sakumudalitsa. Choncho Hana ankachita manyazi kwambiri. (Gen. 30:1, 2) Kuwonjezera pamenepa, mwamuna wake anali ndi mkazi wina dzina lake Penina ndipo anabereka naye ana. Penina ankachitira nsanje Hana ndipo ‘ankamusautsa kwambiri n’cholinga choti amukhumudwitse.’ (1 Sam. 1:6) Poyamba, Hana ankakhumudwa kwambiri ndi zimenezi moti ‘ankalira ndiponso sankadya.’ (1 Sam. 1:7, 10) Kodi Hana anathandizidwa bwanji?

5. Kodi kupemphera kunathandiza bwanji Hana?

5 Hana anapemphera kwa Yehova n’kumuuza mmene ankamvera mumtima mwake. Atapemphera, anafotokozera nkhaniyi Eli, yemwe anali mkulu wa ansembe. Ndiyeno Eli anamuuza kuti: “Pita mu mtendere, ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wam’pempha.” Ndiye chinachitika n’chiyani? Hana “anachoka ndi kupita kukadya, ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:17, 18) Kupemphera kunamuthandiza kupezanso mtendere wamumtima.

Mofanana ndi Hana, kodi tingatani kuti tikhale ndi mtendere wamumtima? (Onani ndime 6-10)

6. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Hana komanso palemba la Afilipi 4:6, 7 pa nkhani yopemphera?

6 Kupemphera mosalekeza kungatithandize kupezanso mtendere wamumtima. Hana anapemphera kwa nthawi yaitali kwa Atate wake wakumwamba. (1 Sam. 1:12) Ifenso tingamapemphere kwa nthawi yaitali n’kumafotokozera Yehova nkhawa zathu, zimene zikutichititsa mantha komanso zimene talakwitsa. Sikuti tiyenera kugwiritsa ntchito mawu apamwamba kapena kutchula chilichonse mosalakwitsa. Nthawi zina tingafike polira tikamafotokozera Yehova nkhawa zathu. Ngakhale zili choncho, Yehova sangatope kutimvetsera tikamapemphera. Kuwonjezera pa kufotokozera Yehova mavuto athu, tizikumbukiranso malangizo a pa Afilipi 4:6, 7. (Werengani.) Paulo anatiuza kuti tiyenera kuyamikira Yehova m’mapemphero athu. Kunena zoona, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuyamikira Yehova. Mwachitsanzo, tikhoza kumuthokoza chifukwa anatipatsa moyo, analenga zinthu zokongola, amatisonyeza chikondi chokhulupirika komanso anatipatsa chiyembekezo chabwino. Kodi tingaphunzirenso chiyani kwa Hana?

7. Kodi Hana ndi mwamuna wake ankakonda kuchita chiyani?

7 Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, Hana ankakonda kupita limodzi ndi mwamuna wake ku Silo kukalambira Yehova. (1 Sam. 1:1-5) Hana ali kuchihema, Eli anamulimbikitsa pomuuza kuti Mulungu amupatse zimene wamupempha.​—1 Sam. 1:9, 17.

8. Kodi misonkhano ingatithandize bwanji? Fotokozani.

8 Kupitiriza kupezeka pamisonkhano kungatithandize kuti tizipeza mtendere wamumtima. Nthawi zambiri, m’bale amene amapereka pemphero loyamba pamisonkhano amapempha kuti mzimu wa Yehova ukhale nafe. Ndipo mtendere ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimuwo umatulutsa. (Agal. 5:22) Tikamapezeka pamisonkhano ngakhale kuti tikuda nkhawa, timalola kuti Yehova ndiponso abale ndi alongo athu azitilimbikitsa komanso kutithandiza kuti tipeze mtendere wamumtima. Pemphero komanso misonkhano ndi zinthu ziwiri zofunika kwambiri zimene Yehova amagwiritsa ntchito potitonthoza. (Aheb. 10:24, 25) Tiyeni tikambiranenso zinthu zina zimene tikuphunzira kwa Hana.

9. Kodi n’chiyani sichinasinthe pa moyo wa Hana, nanga chinasintha n’chiyani?

9 Mavuto a Hana sanatheretu nthawi yomweyo. Iye atabwerera kwawo kuchokera ku Silo, ankakhalabe m’nyumba imodzi ndi Penina. Ndipo Baibulo silisonyeza kuti Penina anasiya kumunyoza. Choncho tinganene kuti Hana anafunika kupirirabe mawu opweteka a mkazi mnzake. Koma sanapitirize kukhumudwa ndipo anali ndi mtendere wamumtima. Kumbukirani kuti Hana atafotokozera Yehova mavuto ake sanakhalenso ndi nkhawa. Iye analola kuti Yehova amutonthoze komanso kumuthandiza kupeza mtendere wamumtima. Patapita nthawi, Yehova anadalitsa Hana pomupatsa ana.​—1 Sam. 1:19, 20; 2:21.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Hana?

10 Tikhoza kupeza mtendere wamumtima ngakhale kuti mavuto athu sanathe. Mavuto ena angapitirire ngakhale titapemphera mochokera pansi pa mtima komanso kupitiriza kupezeka pamisonkhano. Koma chitsanzo cha Hana chikusonyeza kuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kutitonthoza. Yehova sangatiiwale ndipo adzatidalitsa tikapitirizabe kumukhulupirira.​—Aheb. 11:6.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA MTUMWI PAULO

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinkadetsa nkhawa Paulo?

11 Panali zinthu zambiri zimene Paulo ankada nazo nkhawa. Mwachitsanzo, popeza ankakonda kwambiri abale ndi alongo, mavuto awo ankamudetsa nkhawa. (2 Akor. 2:4; 11:28) Anthu amene ankamutsutsa pa ntchito yake yolalikira nthawi zina ankamumenya komanso kumutsekera m’ndende. Paulo ankakumananso ndi mavuto amene ankamudetsa nkhawa monga ‘kusowa’ zinthu zina zofunika pa moyo. (Afil. 4:12) Komanso popeza chombo chinamuswekerapo katatu, n’zosachita kufunsa kuti ankakhala ndi nkhawa akamayenda panyanja. (2 Akor. 11:23-27) Kodi n’chiyani chinkathandiza Paulo akakhala ndi nkhawa?

12. N’chiyani chinathandiza kuti Paulo asamade nkhawa kwambiri?

12 Paulo ankada nkhawa ndi mavuto amene abale ndi alongo ake ankakumana nawo, koma sankalimbana ndi mavuto onsewo payekha. Iye ankadziwa kuti sangakwanitse kuchita zimenezi. Choncho anakonza zoti abale ena azithandiza posamalira mipingo. Mwachitsanzo, iye anapatsa abale okhulupirika monga Timoteyo ndi Tito maudindo ena mumpingo. N’zodziwikiratu kuti ntchito imene abalewa ankagwira inathandiza kuti Paulo asamade nkhawa kwambiri.​—Afil. 2:19, 20; Tito 1:1, 4, 5.

Malinga ndi chitsanzo cha Paulo, kodi tingapewe bwanji kuda nkhawa kwambiri? (Onani ndime 13-15)

13. Kodi akulu angatsanzire bwanji Paulo?

13 Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Mofanana ndi Paulo, akulu ambiri achikondi masiku ano amadera nkhawa abale ndi alongo amene akukumana ndi mavuto. Koma mkulu mmodzi sangakwanitse kuthandiza onse. Choncho mkulu wodziwa malire ake amalola abale ena oyenerera kuti azigwira naye ntchito yosamalira mpingo. Amaphunzitsanso abale achinyamata kuti azimuthandiza posamalira nkhosa za Mulungu.​—2 Tim. 2:2.

14. Kodi Paulo sankadera nkhawa za chiyani, nanga tingaphunzire chiyani kwa iye?

14 Muzizindikira kuti mumafunikira kulimbikitsidwa. Paulo anali wodzichepetsa choncho ankapempha komanso kulola kuti anzake azimulimbikitsa. N’zoonekeratu kuti sankadera nkhawa zoti ena azimuona ngati wofooka chifukwa cholola kuti anthu ena amulimbikitse. Iye analembera Filimoni kuti: “Chikondi chako m’bale chandisangalatsa ndi kundilimbikitsa kwambiri.” (Filim. 7) Paulo anatchulanso antchito anzake ena ambiri amene anamulimbikitsa pa nthawi ya mavuto. (Akol. 4:7-11) Tikavomereza modzichepetsa kuti tikufunika kulimbikitsidwa, abale ndi alongo athu adzatithandiza mosangalala.

15. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo atakumana ndi mavuto odetsa nkhawa?

15 Muzidalira Mawu a Mulungu. Paulo ankadziwa kuti Malemba angamulimbikitse. (Aroma 15:4) Ankadziwanso kuti angamupatse nzeru zomuthandiza akakumana ndi mavuto. (2 Tim. 3:15, 16) Atamangidwa kachiwiri ku Roma, Paulo ankaona kuti imfa yake yayandikira. Ndiye kodi anatani? Iye anapempha Timoteyo kuti abwere msanga komanso amubweretsere “mipukutu.” (2 Tim. 4:6, 7, 9, 13) Paulo anachita zimenezi chifukwa mipukutuyo iyenera kuti inali mbali za Malemba Achiheberi zimene akanagwiritsa ntchito pophunzira payekha. Tikamatsanzira Paulo pophunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, Yehova adzagwiritsa ntchito Malemba potitonthoza, ngakhale mavuto athu atakhala aakulu.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA MFUMU DAVIDE

Mofanana ndi Davide, kodi n’chiyani chingatithandize ngati tachita tchimo lalikulu? (Onani ndime 16-19)

16. Kodi Davide anadzibweretsera mavuto ati?

16 Davide anachita zinthu zimene zinkamuchititsa kudziimba mlandu kwambiri. Iye anachita chigololo ndi Batiseba, kukonza zoti mwamuna wake aphedwe komanso anabisa machimo akewo kwa nthawi ndithu. (2 Sam. 12:9) Poyamba, Davide ankanyalanyaza chikumbumtima chake. Zimenezi zinasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova, kumuvutitsa maganizo komanso kumudwalitsa. (Sal. 32:3, 4) Kodi n’chiyani chinathandiza Davide kuti asamade nkhawa kwambiri ndi mavuto amene anadzibweretserawa? Nanga n’chiyani chingatithandize tikachita tchimo lalikulu?

17. Kodi lemba la Salimo 51:1-4 limasonyeza bwanji kuti Davide analapa mochokera pansi pa mtima?

17 Tipemphe Yehova kuti atikhululukire. Patapita nthawi, Davide anapemphera kwa Yehova n’kufotokoza zimene analakwitsa komanso analapa mochokera pansi pa mtima. (Werengani Salimo 51:1-4.) Zimenezi zinamuthandiza kuti asakhalenso ndi nkhawa. (Sal. 32:1, 2, 4, 5) Ngati mwachita tchimo lalikulu, musamabise zimene mwachitazo. Koma muzipemphera kwa Yehova n’kumuuza momasuka zimene mwalakwitsa. Izi zingakuthandizeni kuti musiye kudziimba mlandu komanso kuda nkhawa. Koma kuti mukonze ubwenzi wanu ndi Yehova, kungopemphera si kokwanira.

18. Kodi Davide anatani atapatsidwa chilango?

18 Muvomereze chilango chimene mwapatsidwa. Yehova atatumiza mneneri Natani kuti akauze Davide za tchimo lake, Davideyo sanapereke zifukwa zodzikhululukira kapena kupeputsa tchimolo. M’malomwake, nthawi yomweyo anavomereza kuti anachimwira mwamuna wa Batiseba koma kuposa zonse anachimwira Yehova. Davide anavomereza chilango chimene Yehova anamupatsa ndipo Yehova anamukhululukira. (2 Sam. 12:10-14) Ngati tachita tchimo lalikulu, tiyenera kulankhula ndi abale amene Yehova wawasankha kuti azitiyang’anira. (Yak. 5:14, 15) Tiyeneranso kupewa mtima wofuna kupereka zifukwa zodzikhululukira. Tikavomereza msanga chilango chimene tapatsidwa, tikhoza kupezanso mtendere mofulumira n’kumakhalanso osangalala.

19. Kodi tiyenera kuyesetsa kuti tisachite chiyani?

19 Muziyesetsa kuti musabwereze machimowo. Mfumu Davide ankadziwa kuti ankafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti asabwerezenso machimo ake. (Sal. 51:7, 10, 12) Iye atakhululukidwa ndi Yehova, ankayesetsa kupewa maganizo oipa. Zimenezi zinamuthandiza kuti apezenso mtendere wamumtima.

20. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chifundo cha Yehova?

20 Timasonyeza kuti timayamikira chifundo cha Yehova tikamapemphera kuti atikhululukire, kuvomereza chilango chimene tapatsidwa komanso tikamayesetsa kuti tisabwereze machimo athu. Tikamachita zimenezi tidzapezanso mtendere wamumtima. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale James yemwe anachita tchimo lalikulu. Iye anati: “Nditaulula tchimo langa kwa akulu, ndinamva ngati ndatula chikatundu cholemera. Ndinayamba kupezanso mtendere wamumtima.” N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—Sal. 34:18.

21. Kodi tingalole bwanji kuti Yehova azitithandiza?

21 Pamene mapeto akuyandikira, nkhawa zathu zikhoza kumawonjezereka. Mukamada nkhawa muyenera kupempha Yehova mwamsanga kuti akuthandizeni. Muyeneranso kuphunzira Baibulo mwakhama. Muzitengera chitsanzo cha Hana, Paulo ndi Davide. Muzipemphanso Atate wanu wakumwamba kuti akuthandizeni kudziwa zimene zikukuchititsani kuda nkhawa. (Sal. 139:23) Muzimulola kuti asenze mavuto anu, makamaka ngati palibe zimene mungachite kuti muwathetse. Mukatero, mukhoza kufanana ndi wolemba masalimo amene anaimbira Yehova kuti: “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”​—Sal. 94:19.

NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”

^ ndime 5 Nthawi zina, tonsefe timakhala ndi nkhawa chifukwa cha mavuto amene timakumana nawo. Munkhaniyi tikambirana za atumiki atatu a Yehova otchulidwa m’Baibulo amene anavutikapo ndi nkhawa. Tikambirananso mmene Yehova anawatonthozera n’kuwathandiza kuti apeze mtendere.

^ ndime 1 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kuda nkhawa kumatanthauza kuchita mantha kapena kudandaula za zinthu zinazake. Tikhoza kuda nkhawa chifukwa cha mavuto azachuma, matenda, mavuto a m’banja kapena mavuto ena. Tingamadenso nkhawa chifukwa cha zolakwa zimene tinachita m’mbuyo kapena mavuto amene tikuganiza kuti tingadzakumane nawo m’tsogolo.