Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 9

Lolani Kuti Yehova Akutonthozeni

Lolani Kuti Yehova Akutonthozeni

“Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”​—SAL. 94:19.

NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. N’ciani cingacititse kuti tikhale na nkhawa? Nanga izi zingatipangitse kuganiza ciani?

KODI munavutikapo na nkhawa? * Mwina palipano muli na nkhawa cifukwa anthu ena anakukambilani kapena kukucitilani zinthu zimene zinakukhumudwitsani. Mwinanso muli na nkhawa cifukwa ca zimene inu eni munakamba kapena kucita. Mwacitsanzo, n’kutheka kuti munacita chimo, ndipo mukuda nkhawa kuti mwina Yehova sangakukhululukileni. Kuwonjezela apo, mungayambe kuganiza kuti nkhawa yaikulu imene muli nayo ni cizindikilo cakuti mulibe cikhulupililo komanso ndimwe munthu woipa. Koma kodi maganizo otelo ni a zoona?

2. N’zitsanzo ziti za m’Malemba zimene zionetsa kuti kukhala na nkhawa si cizindikilo cakuti tilibe cikhulupililo?

2 Onani zitsanzo zingapo izi za m’Malemba: Hana, amene anadzakhala mayi wa mneneli Samueli, anali munthu wa cikhulupililo cacikulu. Ngakhale n’conco, iye anavutika na nkhawa cifukwa wina wa m’banja mwawo mweni-mweni anali kumucitila nkhanza. (1 Sam. 1:7) Nayenso mtumwi Paulo anali na cikhulupililo colimba. Koma pa nthawi ina anavutika kwambili cifukwa ca “nkhawa imene [anali] nayo pa mipingo yonse.” (2 Akor. 11:28) Citsanzo cina ni ca Mfumu Davide. Iye anali na cikhulupililo colimba kwambili moti Yehova anamukonda ngako. (Mac. 13:22) Ngakhale zinali conco, Davide anacita macimo amene anamupangitsa kusautsika kwambili na nkhawa. (Sal. 38:4) Koma Yehova anatonthoza aliyense wa atumiki ake amenewa. Tiyeni manje tione zimene tingaphunzilepo pa zitsanzo zawo.

ZIMENE TIPHUNZILA KWA HANA MAYI WOKHULUPILIKA

3. Kodi zokamba za ena zingatipangitse bwanji kukhala na nkhawa?

3 Anthu ena akatilankhula mokhadzula kapena kucita nafe zinthu mopanda cikondi, tingakhale na nkhawa. Zimakhala zoŵaŵa kwambili ngati munthu amene wacita zimenezi ni mnzathu kapena wacibululu. Tingade nkhawa kuti ubwenzi wathu na munthuyo udzasokonezeka. Nthawi zina zingakhale kuti munthuyo wangokamba mawu mosaganiza bwino, koma mawuwo angatiŵaŵe kwambili monga kuti watilasa na lupanga. (Miy. 12:18) Nthawi zinanso, munthu angakambe mwadala mawu otikhumudwitsa. Izi n’zimene zinacitikila mlongo wina wacitsikana. Iye anati: “Zaka zingapo m’mbuyomo, munthu wina amene n’nali kumuona ngati mnzanga wabwino anayamba kufalitsa mabodza ponena za ine pa Intaneti. Cinaniŵaŵa maningi, ndipo n’nada nkhawa. Zinanivuta kumvetsetsa cifukwa cake anali kuniipitsila mbili mwanjila imeneyo.” Ngati mnzanu kapena wacibululu anakukhumudwitsani, mungaphunzile zambili pa citsanzo ca Hana.

4. Ni mavuto aakulu ati amene Hana anakumana nawo?

4 Hana anakumana na mavuto aakulu. Kwa zaka zambili, iye sanali kubeleka. (1 Sam. 1:2) Malinga na cikhalidwe ca Aisiraeli, mkazi wosabeleka anali kuonedwa ngati wotembeleledwa. Conco, Hana anali kucita manyazi kwambili na vuto lake la kusabeleka. (Gen. 30:1, 2) Kuonjezela apo, mwamuna wake anali na mkazi wina dzina lake Penina, amene anali kumubelekela ana. Penina anali kucitila nsanje Hana, cakuti “anali kum’sautsa kwambili n’colinga coti amukhumudwitse.” (1 Sam. 1:6) Poyamba, izi zinali kumuvutitsa maganizo kwambili Hana moti “anali kulila ndiponso sankadya.” Baibo imati “anali wokhumudwa kwabasi” mu mtima. (1 Sam. 1:7, 10) Kodi Hana anapeza kuti citonthozo?

5. Kodi pemphelo linamuthandiza bwanji Hana?

5 Hana anakhuthulila Yehova nkhawa zake m’pemphelo. Pambuyo popemphela, anafotokoza vuto lake kwa Mkulu wa Ansembe Eli. Kenako, Eli anamuuza kuti: “Pita mu mtendele, ndipo Mulungu wa Isiraeli akupatse zimene wam’pempha.” Kodi panakhala zotulukapo zotani? Hana “anacoka ndi kupita kukadya, ndipo sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:17, 18) Pemphelo linamuthandiza Hana kukhalanso na mtendele wa mumtima.

Mofanana na Hana, kodi tingacite ciani kuti tikhalebe na mtendele wa mumtima? (Onani ndime 6-10)

6. Pa nkhani ya pemphelo, kodi tingaphunzile ciani kwa Hana komanso pa mawu a pa Afilipi 4:6, 7?

6 Tingakhale na mtendele wa mumtima ngati tilimbikila kupemphela. Hana anakamba na Atate wake wakumwamba kwa nthawi yaitali. (1 Sam. 1:12) Na ife tingapatule nthawi yaitali yokamba na Yehova. Tingamuuze zimene zikuticititsa mantha, nkhawa zathu, na zofooka zathu. Komabe, mapemphelo athu safunika kucita kukhala okometsela mwapadela kapena monga mwandakatulo. Nthawi zina, tingafike ngakhale polila kwinaku tikumuuza Yehova mavuto athu m’pemphelo. Olo zikhale conco, Yehova salema nawo mapemphelo athu ngakhale pang’ono. Kuonjezela pa kupempha Yehova kuti atithandize pa mavuto athu, tifunikanso kukumbukila malangizo a pa Afilipi 4:6, 7. (Ŵelengani.) Pa lembali, Paulo anakamba kuti tiyenela kupeleka mapemphelo oyamikila. Pali zinthu zambili zimene ziyenela kutisonkhezela kuyamikila Yehova. Mwacitsanzo, tingamuyamikile cifukwa ca mphatso ya moyo, zinthu zokongola zimene anapanga, cikondi cake cokhulupilika, na ciyembekezo cokondweletsa cimene anatipatsa. N’ciani cina cimene tingaphunzile kwa Hana?

7. Kodi nthawi zonse Hana na mwamuna wake anali kucita ciani?

7 Ngakhale kuti Hana anali kukumana na mavuto, nthawi zonse iye na mwamuna wake anali kupita ku Silo kukalambila Yehova. (1 Sam. 1:1-5) Mwacitsanzo, Hana anali ku cihema pamene Mkulu wa Ansembe Eli anamulimbikitsa mwa kukamba mawu oonetsa kuti anali kukhulupilila kuti Yehova adzayankha pemphelo lake.—1 Sam. 1:9, 17.

8. Kodi misonkhano imatithandiza bwanji? Fotokozani.

8 Tingakhale na mtendele wa mumtima ngati tipitiliza kusonkhana. Pemphelo lotsegulila misonkhano, kaŵili-kaŵili limaphatikizapo kupempha mzimu wa Mulungu kuti utitsogolele. Mtendele ni limodzi mwa makhalidwe amene mzimuwo umabala. (Agal. 5:22) Ngati tipezeka ku misonkhano olo kuti tili na nkhawa, Yehova komanso abale na alongo athu angatilimbikitse na kutithandiza kupezanso mtendele wa mumtima. Pemphelo na misonkhano ndizo njila zofunika kwambili zimene Yehova amagwilitsila nchito potitonthoza. (Aheb. 10:24, 25) Tsopano tiyeni tione mfundo ina imene tingaphunzilepo pa citsanzo ca Hana.

9. Pa vuto la Hana, n’ciani cimene sicinasinthe? Nanga n’ciani cinam’thandiza kupilila?

9 Mavuto amene anali kucititsa Hana kukhala na nkhawa, anatenga nthawi kuti athe. Mwacitsanzo, iye atabwelako ku cihema kumene anapita kukalambila Mulungu, anapitiliza kukhala pa nyumba imodzi na Penina. Ndipo Baibo sionetsa kuti Penina anasintha khalidwe lake. Conco, n’zoonekelatu kuti Hana anapitiliza kutonzedwa na Penina. Koma iye anakwanitsa kukhalabe na mtendele wa mumtima. Kumbukilani kuti Baibo imakamba kuti Hana atasiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova, sanakhalenso na nkhawa. Anadalila Yehova kuti amutonthoze. Patapita nthawi, Yehova anayankha pemphelo lake ndipo anayamba kubeleka ana.—1 Sam. 1:19, 20; 2:21.

10. Tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Hana?

10 Tingakhalebe na mtendele wa mu mtima olo kuti vuto lathu likalipo. Nthawi zina, mavuto angapitilizebe ngakhale kuti timapemphela mocokela pansi pa mtima na kupezeka pa misonkhano nthawi zonse. Koma pa citsanzo ca Hana tiphunzilapo kuti ngati tidalila Yehova, iye sadzalephela kutonthoza mitima yathu yosautsika. Yehova sadzatiiŵala olo pang’ono, ndipo pa nthawi yake adzatidalitsa cifukwa ca kukhulupilika kwathu.—Aheb. 11:6.

ZIMENE TIPHUNZILA KWA MTUMWI PAULO

11. Ni zinthu ziti zimene zinapangitsa Paulo kukhala na nkhawa?

11 Panali zambili zimene zinapangitsa Paulo kukhala na nkhawa. Mwacitsanzo, cifukwa cokonda Akhristu anzake, mavuto amene abale na alongo anali kukumana nawo anali kumupangitsa kukhala na nkhawa kwambili. (2 Akor. 2:4; 11:28) Cina, pamene Paulo anali kucita utumiki wake monga mtumwi, nthawi zambili anthu otsutsa anali kumumenya na kum’ponya m’ndende. Panalinso mavuto ena amene anamupangitsa kukhala na nkhawa. Mwacitsanzo, nthawi zina anali ‘kusowa’ zinthu zofunikila mu umoyo. (Afil. 4:12) Kuwonjezela apo, popeza kuti combo cinamuswekelapo katatu panyanja, ayenela kuti anali kukhala na nkhawa kwambili akamayenda ulendo wa pamadzi. (2 Akor. 11:23-27) Kodi n’ciani cinamuthandiza Paulo pamene anali na nkhawa?

12. N’ciani cinathandiza kucepetsa nkhawa zimene Paulo anali nazo?

12 Paulo anali kudela nkhawa abale na alongo amene anali kukumana na mavuto, koma sanayese kuthetsa yekha mavuto awo. Anali munthu wodzicepetsa. Iye anapempha ena kuti azimuthandiza posamalila abale na alongo mu mpingo. Mwacitsanzo, anapatsa amuna okhulupilika monga Timoteyo na Tito maudindo ambili. Abalewa anali kumuthandiza kusamalila nchito zina, ndipo mosakayikila izi zinathandiza Paulo kucepetsa nkhawa imene anali nayo.—Afil. 2:19, 20; Tito 1:1, 4, 5.

Mofanana na mtumwi Paulo, kodi tingacite ciani kuti tisapanikizike na nkhawa? (Onani ndime 13-15)

13. Kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca Paulo?

13 Pemphani ena kuti akuthandizeni. Mofanana na Paulo, akulu ambili acikondi masiku ano amadela nkhawa abale na alongo amene akukumana na mavuto. Koma mkulu mmodzi sangakwanitse yekha kuthandiza ofalitsa onse mu mpingo. Conco, ngati mkulu ni wodzicepetsa, nchito zina amagaŵilako amuna ena oyenelela. Komanso amaphunzitsa abale acinyamata kuti azithandiza kusamalila nkhosa za Mulungu.—2 Tim. 2:2.

14. Kodi Paulo sanade nkhawa na ciani? Nanga tiphunzilapo ciani pa citsanzo cake?

14 Vomelezani kuti mufunikila cilimbikitso. Paulo anali wodzicepetsa. Conco, anazindikila kuti anafunikila cilimbikitso kucokela kwa mabwenzi ake. Iye sanade nkhawa kuti ena adzamuona kuti ni wofooka akavomeleza kuti Akhristu anzake anamulimbikitsa. Polembela kalata Filimoni, Paulo anati: “Cikondi cako m’bale candisangalatsa ndi kundilimbikitsa kwambili.” (Filim. 7) Paulo anachulanso anchito anzake ena angapo amene anamulimbikitsa kwambili pamene anali na nkhawa. (Akol. 4:7-11) Ngati tidzicepetsa na kuvomeleza kuti tifunika cilimbikitso, abale na alongo athu adzakondwela kutithandiza.

15. N’ciani cinalimbikitsa Paulo pa nthawi yovuta?

15 Dalilani Mawu a Mulungu. Paulo anali kudziŵa kuti Malemba angamulimbikitse. (Aroma 15:4) Anadziŵanso kuti Malemba adzam’patsa nzelu zomuthandiza kupilila mayeselo. (2 Tim. 3:15, 16) Pamene Paulo anaponyedwa m’ndende kaciŵili ku Roma, anazindikila kuti watsala pang’ono kuphedwa. Kodi iye anacita ciani pa nthawi yovuta imeneyo? Anapempha Timoteyo kuti abwele kwa iye mwamsanga, ndiponso kuti amubweletsele “mipukutu.” (2 Tim. 4:6, 7, 9, 13) Cifukwa ciani? Cifukwa mipukutu imeneyo iyenela kuti inali mbali ya Malemba Aciheberi amene Paulo anali kuseŵenzetsa pocita phunzilo laumwini. Ngati titengela citsanzo ca Paulo mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse, Yehova adzaseŵenzetsa Malembawo potitonthoza ngakhale titakumana na mavuto abwanji.

ZIMENE TIPHUNZILA KWA MFUMU DAVIDE

Mofanana na Mfumu Davide, n’ciani cingatithandize ngati tacita chimo lalikulu? (Onani ndime 16-19)

16. Ni mavuto otani amene Davide anakumana nawo cifukwa ca macimo amene anacita?

16 Davide anali kuvutika na cikumbumtima cifukwa ca macimo aakulu amene anacita. Anacita cigololo na Bati-seba, anakonza ciwembu cophetsa mwamuna wake, ndipo kwa kanthawi anayesa kubisa macimo ake. (2 Sam. 12:9) Poyamba, Davide ananyalanyaza cikumbumtima cake. Izi zinasokoneza ubwenzi wake na Yehova. Cina, zinapangitsa kuti akhale na nkhawa kwambili mpaka kufika podwala. (Sal. 32:3, 4) Kodi n’ciani cinathandiza Davide kulimbana na nkhawa imene anali nayo cifukwa ca macimo aakulu amene anacita? Nanga ife n’ciani cingatithandize ngati tacita chimo lalikulu?

17. Kodi lemba la Salimo 51:1-4 lionetsa bwanji kuti Davide analapadi kucokela pansi pa mtima?

17 Pemphani cikhululukilo. M’kupita kwa nthawi, Davide anapemphela kwa Yehova. Analapa mocokela pansi pamtima na kuulula macimo ake. (Ŵelengani Salimo 51:1-4.) Kucita izi kunamuthandiza kupezanso mtendele wa mumtima. (Sal. 32:1, 2, 4, 5) Ngati mwacita chimo lalikulu, simufunika kubisa. Mufunika kupemphela kwa Yehova na kumuuza zonse zimene munacita. Mukatelo, mudzapeza mtendele wa mumtima, ndipo cikumbumtima canu cidzaleka kukuvutitsani. Koma kuti mukonze ubwenzi wanu na Yehova, palinso zina zimene mufunika kucita kuonjezela pa kupemphela.

18. Kodi Davide anacita ciani atapatsidwa cilango?

18 Landilani cilango. Pamene Yehova anatumiza mneneli Natani kuti akavumbule chimo la Davide, iye sanapeleke zifukwa zodzikhululukila kapena kuyesa kupeputsa chimo lake. M’malomwake, mwamsanga anavomeleza kuti anacimwila mwamuna wa Bati-seba, komanso kuti koposa zonse anacimwila Yehova. Davide analandila cilango cocokela kwa Yehova, ndipo anakhululukidwa. (2 Sam. 12:10-14) Ngati tinacita chimo lalikulu, tifunika kuuza akulu amene Yehova anawaika monga abusa athu. (Yak. 5:14, 15) Tifunikanso kupewa kupeleka zifukwa zodzikhululukila. Ngati tivomeleza cilango mwamsanga na kuseŵenzetsa uphungu umene tapatsidwa, mwamsanganso tidzapeza cimwemwe na mtendele wa mumtima.

19. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani?

19 Yesetsani kupewa kubwelezanso chimo limene munacita. Mfumu Davide anadziŵa kuti anafunika thandizo la Yehova kuti apewe kubwelezanso macimo amene anacita. (Sal. 51:7, 10, 12) Yehova atamukhululukila, Davide anayesetsa kupewa kuganizilanso zinthu zoipa. Izi zinamuthandiza kupezanso mtendele wa mumtima.

20. Popeza Yehova amakhululuka macimo, kodi ife tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimenezi?

20 Popeza Yehova amakhululuka macimo, kodi ife tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimenezi? Tingatelo mwa kumupempha kuti atikhululukile, kulandila cilango cake, na kuyesetsa kupewa kubwelezanso chimo limene tinacita. Tikacita zimenezi tidzapeza mtendele wa mumtima. M’bale James amene anacita chimo lalikulu, anadzionela yekha kuti mfundo imeneyi ni ya zoona. Iye anati: Pamene n’naulula chimo langa kwa akulu, n’namvela monga anitula cikatundu colema. Ndipo n’nayambanso kukhala na mtendele wa mumtima.” Ndithudi, n’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”—Sal. 34:18.

21. Kodi tingacite ciani kuti Yehova atitonthoze?

21 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, mwacionekele tidzakumana na zambili zobweletsa nkhawa. Mukakhala na nkhawa, mwamsanga muzipemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni. Muziŵelenga Baibo mwakhama. Tengelani citsanzo ca Hana, Paulo, na Davide. Pemphani Atate wanu wakumwamba kuti akuthandizeni kuzindikila zimene zimakupatsani nkhawa. (Sal. 139:23) Muloleni kuti akuthandizeni pa mavuto anu, maka-maka aja amene simungakwanitse kulimbana nawo kapena kuwathetsa. Mukatelo, mudzafanana na wamasalimo amene anaimbila Yehova kuti: “Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”—Sal. 94:19.

NYIMBO 4 ‘Yehova ni M’busa Wanga’

^ ndime 5 Ife tonse nthawi zina timakhala na nkhawa cifukwa ca mavuto amene timakumana nawo. M’nkhani ino, tikambilana zitsanzo zitatu za atumiki a Yehova a m’nthawi yakale amene anavutikapo na nkhawa. Tikambilananso mmene Yehova anatonthozela aliyense wa iwo.

^ ndime 1 KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Nkhawa imatanthauza kucita mantha kapena kupanikizika maganizo cifukwa ca vuto linalake. Nkhawa ingabwele cifukwa ca mavuto azacuma, matenda, mavuto a m’banja, kapena mavuto ena. Tingakhalenso na nkhawa cifukwa coganizila macimo amene tinacita m’mbuyomu, kapena cifukwa coganiza kuti tidzakumana na mavuto ena ake kutsogolo.