Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwala umene analembapo dzina la Belisazara (kukula kwake ndi komweku)

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi zimene asayansi apeza zikutsimikizira bwanji kuti Belisazara anali mfumu ku Babulo?

KWA zaka zambiri, anthu otsutsa Baibulo akhala akunena kuti Mfumu Belisazara, yemwe anatchulidwa m’buku la Danieli, sanakhaleko. (Dan. 5:1) Ankanena zimenezi chifukwa choti asayansi anali asanapeze umboni uliwonse woti analiko. Koma zimenezi zinasintha m’chaka cha 1854. N’chifukwa chiyani tikutero?

M’chaka chimenechi, kazembe wina wa ku Britain dzina lake J. G. Taylor anakachita kafukufuku m’malo amene kunali mzinda wa Uri kum’mwera kwa dziko la Iraq. Iye anapeza miyala yolembedwa ndi zilembo zakalekale. Mwala uliwonse unali wa masentimita 10 m’litali. Pamwala wina panalembedwa pemphero lopempha kuti Mfumu Nabonidasi wa ku Babulo ndi mwana wake wamkulu dzina lake Belisazara akhale ndi moyo wautali. Ngakhale otsutsa Baibulo anavomereza kuti mwalawu ukupereka umboni wakuti Belisazara analikodi.

Koma Baibulo limanena kuti Belisazara analinso mfumu. Anthu ena ankatsutsanso zimenezi. Mwachitsanzo, wasayansi wina wa ku England dzina lake William Talbot, yemwe anakhalapo m’zaka za m’ma 1800, analemba kuti anthu ena amanena kuti “Belisazara ankalamulira limodzi ndi bambo ake Nabonidasi. Koma palibe umboni uliwonse wa zimenezi.”

Koma anthu anasiya kutsutsa zimenezi pamene miyala ina inapezeka yomwe imasonyeza kuti Mfumu Nabonidasi ankachoka kulikulu la dzikolo kwa zaka zingapo. Kodi n’chiyani chinkachitika iye akachoka? Buku la Encyclopaedia Britannica limati: “Nabonidasi akachoka, ankasiyira mwana wake Belisazara ufumu komanso kuti azitsogolera asilikali.” Choncho tinganene kuti Belisazara ankakhalanso mfumu ku Babulo pa nthawi imeneyo. N’chifukwa chake katswiri wina wa zinthu zakale komanso zilankhulo dzina lake Alan Millard ananena kuti zimene “buku la Danieli limanena kuti Belisazara anali ‘mfumu’” ndi zolondola.

Koma atumiki a Mulungu amaona kuti umboni waukulu woti buku la Danieli ndi lodalirika komanso louziridwa ndi Mulungu umapezeka m’Baibulo lomwelo.​—2 Tim. 3:16.