Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 11

Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?

Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?

“Cofanana ndi cingalawaco cikupulumutsanso inuyo tsopano. Cimeneci ndico ubatizo.”​—1 PET. 3:21.

NYIMBO 28 Kukhala Bwenzi la Yehova

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi munthu afunika kucita ciani asanayambe kumanga nyumba?

GANIZILANI za munthu amene afuna kumanga nyumba. Iye amakhala kuti adziŵa mtundu wa nyumba imene afuna kumanga. Koma kodi amangopita ku shopu mwamsanga kukagula zinthu zomangila na kuyamba kumanga? Iyayi. Asanayambe kumanga, pali cina cake cofunika kwambili cimene amafunika kucita. Amafunika kuŵelengela ndalama zimene adzawononga pomanga nyumbayo. Cifukwa ciani? Cifukwa amafuna kudziŵa ngati ali na ndalama zokwanila zoti amangile nyumbayo mpaka kutsiliza. Ngati angaŵelengeletu mosamala ndalama zimene adzawononge, mwacionekele angakwanitse kumanga nyumbayo na kuitsiliza.

2. Malinga na Luka 14:27-30, n’ciani cimene muyenela kuganizila mosamala mukalibe kubatizika?

2 Kodi kukonda Yehova komanso kumuyamikila pa zimene wakucitilani kwakusonkhezelani kuganizila zobatizika? Ngati n’conco, ndiye kuti mofanana na munthu amene afuna kumanga nyumba, muyenela kudzipenda kuti muone ngati ndimwe wokonzeka kubatizika. N’cifukwa ciani takamba telo? Onani zimene Yesu anakamba pa Luka 14:27-30. (Ŵelengani.) Pamene Yesu anakamba mawu amenewa, anali kufotokoza tanthauzo la kukhala wophunzila wake. Kuti munthu akhale wotsatila wa Yesu, afunika “kuŵelengela” mtengo wake—kutanthauza kukhala wokonzeka kukumana na mavuto komanso kudzimana zinthu zina. (Luka 9:23-26; 12:51-53) Conco musanabatizike, muyenela kuganizila mosamala zovuta zimene mungakumane nazo, komanso zinthu zimene mudzafunika kudzimana mukadzakhala wophunzila wa Khristu. Mukatelo, mudzakhala wokonzeka kupitiliza kutumikila Mulungu mokhulupilika monga Mkhristu wobatizika.

3. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 Popeza kukhala wophunzila wa Khristu wobatizika kumafuna kupilila na kudzimana, kodi kubatizika kulidi na phindu? Inde, cifukwa kumatsegula mwayi wolandila madalitso ambili-mbili, lomba na kutsogolo. Tsopano, tiyeni tikambilane mafunso angapo ofunika kwambili okhudza ubatizo. Kukambilana zimenezi kudzakuthandizani kuona ngati ndimwe wokonzeka kubatizika.

ZIMENE MUFUNIKA KUDZIŴA ZA KUDZIPATULILA KOMANSO UBATIZO

4. (a) Kodi kudzipatulila kumatanthauza ciani? (b) Kodi ‘kudzikana mwekha’ kumene lemba la Mateyu 16:24 limakamba kumatanthauza ciani?

4 Kodi kudzipatulila kumatanthauza ciani? Mukalibe kubatizika, mufunika kudzipatulila. Kudzipatulila kumatanthauza kuuza Yehova m’pemphelo mocokela pansi pa mtima kuti mudzamutumikila kwa moyo wanu wonse. Mukadzipatulila kwa Mulungu, ‘mumadzikana mwekha.’ (Ŵelengani Mateyu 16:24.) Izi zitanthauza kuti tsopano ndimwe a Yehova. Umenewu ni mwayi waukulu kwambili. (Aroma 14:8) Pamene mukudzipatulila, mumamuuza kuti kuyambila lelo, cofunika kwambili kwa imwe ni kumutumikila osati kucita zofuna zanu. Kudzipatulila kwanu ni lumbilo kapena kuti lonjezo lapadela limene mumapanga kwa Mulungu. Yehova satikakamiza kupanga lumbilo limeneli. Koma tikapanga lumbiloli, iye amafuna kuti tilisunge.—Sal. 116:12, 14.

5. Kodi kudzipatulila kumasiyana bwanji na ubatizo?

5 Kodi kudzipatulila kumagwilizana bwanji na ubatizo? Munthu amasankha yekha kudzipatulila, ndipo amacita zimenezi popanda ena kudziŵa. Kudzipatulila ni nkhani ya pakati pa imwe na Yehova basi. Koma ubatizo umacitikila pamaso pa anthu, kaŵili-kaŵili pa msonkhano wadela kapena wacigawo. Mukabatizika, mumaonetsa kwa anthu kuti munadzipatulila kale kwa Yehova. * Conco, ubatizo wanu umadziŵitsa ena kuti mumakonda Yehova Mulungu wathu na mtima wanu wonse, moyo, maganizo, komanso mphamvu zanu zonse, ndiponso kuti mwasankha kumutumikila kwa moyo wanu wonse.—Maliko 12:30.

6-7. Malinga na 1 Petulo 3:18-22, kodi n’zifukwa ziŵili ziti zimene zimapangitsa ubatizo kukhala wofunika kwambili?

6 Kodi kubatizika n’kofunikadi? Onani zimene Baibo imakamba pa 1 Petulo 3:18-22. (Ŵelengani.) Cingalawa cinali umboni woonetsa kuti Nowa anali na cikhulupililo mwa Mulungu. Mofananamo, ubatizo wanu ni umboni woonetsa kuti munadzipatulila kwa Yehova. Koma kodi kubatizika n’kofunikadi? Inde, n’kofunika. Petulo anafotokoza cifukwa cake n’kofunika. Coyamba, iye anakamba kuti ubatizo ‘umakupulumutsani.’ Ubatizo ungatipulumutse ngati ticita zinthu zoonetsa kuti tili na cikhulupililo mwa Yesu, timakhulupilila kuti anatifela, ndipo anaukitsidwa na kupita kumwamba, komanso kuti “ali kudzanja lamanja la Mulungu.”

7 Caciŵili, ubatizo umatithandiza kukhala na “cikumbumtima cabwino.” Tikadzipatulila kwa Mulungu na kubatizika, timakhala naye pa ubale wapadela. Iye amatikhululukila macimo athu cifukwa tinalapa mocokela pansi pa mtima ndipo timakhulupilila dipo la Yesu. Izi zimatithandiza kukhala na cikumbumtima cabwino pamaso pa Mulungu.

8. Kodi n’ciani ciyenela kukusonkhezelani kubatizika?

8 Kodi n’ciani ciyenela kukusonkhezelani kubatizika? Cifukwa cophunzila Baibo mosamala, mwadziŵa zambili za Yehova. Mwadziŵa makhalidwe ake komanso mmene amacitila zinthu. Zimene munaphunzilazo zinakufikani pa mtima na kukusonkhezelani kum’konda kwambili Yehova. Mwacionekele, kukonda Yehova kumeneku ndiye cifukwa cacikulu cimene cakusonkhezelani kufuna kubatizika.

9. Kodi zimene Mateyu 28:19, 20 imakamba zakuti munthu ayenela kubatizika m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela zimatanthauza ciani?

9 Cina cimene cakusonkhezelani kufuna kubatizika n’cakuti munaphunzila coonadi ca m’Baibo, ndipo mumakhulupillila zimene munaphunzilazo. Ganizilani zimene Yesu anakamba popeleka lamulo lakuti tizipanga ophunzila. (Ŵelengani Mateyu 28:19, 20.) Iye anakamba kuti ofuna kubatizika ayenela kubatizika “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyela.” Kodi anatanthauza ciani pamenepa? Anatanthauza kuti mufunika kukhulupilila na mtima wonse mfundo zonse za coonadi zimene munaphunzila m’Baibo ponena za Yehova, Mwana wake Yesu, na mzimu woyela. Mfundo za coonadi zimenezi n’zamphamvu ngako, ndipo zingakukhudzeni mtima kwambili. (Aheb. 4:12) Tsopano tiyeni tikambilane zina mwa mfundo zimenezi.

10-11. Ni mfundo za coonadi ziti ponena za Atate zimene munaphunzila na kuzikhulupilila?

10 Ganizilani mfundo za coonadi zimene munaphunzila ponena za Atate. Munaphunzila kuti dzina lake ni “Yehova,” ni “Wam’mwambamwamba” pa “dziko lonse lapansi,” komanso kuti iye yekha ndiye “Mulungu woona.” (Sal. 83:18; Yes. 37:16) Yehova ndiye Mlengi wathu, ndipo “cipulumutso cimacokela kwa [iye].” (Sal. 3:8; 36:9) Iye anakonza zotipulumutsa ku ucimo na imfa, ndipo anatipatsa ciyembekezo cokakhala na moyo wamuyaya. (Yoh. 17:3) Kudzipatulila kwanu na kubatizika kudzaonetsa kuti tsopano ndimwe Mboni ya Yehova. (Yes. 43:10-12) Mudzakhala m’banja la padziko lonse la anthu olambila Mulungu, amene amanyadila kuchedwa na dzina lake komanso kulidziŵikitsa kwa ena.—Sal. 86:12.

11 Ni mwayi waukulu kumvetsetsa zimene Baibo imaphunzitsa ponena za Atate wathu. Kukhulupilila mfundo zimenezi za coonadi ca mtengo wapatali, kudzakusonkhezelani kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika.

12-13. Ni mfundo za coonadi ziti zimene munaphunzila na kuzikhulupilila ponena za Mwana wa Mulungu?

12 Kodi munamvela bwanji mutaphunzila coonadi ponena za Mwana wa Mulungu? Munaphunzila kuti Yesu ni waciŵili wofunika kwambili m’cilengedwe conse. Iye ni Wotiwombola. Analolela kupeleka moyo wake kaamba ka ife. Tikamacita zinthu zoonetsa kuti timakhulupilila dipo, macimo athu amakhululukidwa, timakhala pa ubale na Mulungu, komanso tidzapeza moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Yesu ni Mkulu wathu wa Ansembe. Amafuna kutithandiza kuti tipindule na dipo, ndiponso kuti tikhale pa ubale wolimba na Mulungu. (Aheb. 4:15; 7:24, 25) Yesu ni Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, ndipo ni amene Yehova adzamuseŵenzetsa poyeletsa dzina lake, kuthetsa zoipa zonse, na kubweletsa madalitso osatha m’Paradaiso akubwelayo. (Mat. 6:9, 10; Chiv. 11:15) Kuwonjezela apo, Yesu ni citsanzo cimene tiyenela kutengela. (1 Pet. 2:21) Iye anatipatsa citsanzo cabwino mwa kukhala wodzipeleka pocita cifunilo ca Mulungu.—Yoh. 4: 34.

13 Mukakhulupilila zimene Baibo imaphunzitsa ponena za Yesu, mumayamba kum’konda Mwana wokondedwa ameneyu wa Mulungu. Cikondi cimeneco cimapangitsa kuti muzifuna kucita cifunilo ca Mulungu, monga mmene Yesu anacitila. Ndipo izi zidzakusonkhezelani kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika.

14-15. Ni mfundo za coonadi ziti zimene munaphunzila na kuzikhulupilila ponena za mzimu woyela?

14 Kodi munamvela bwanji mutaphunzila coonadi ponena za mzimu woyela? Munaphunzila kuti mzimu woyela si mulungu, koma ni mphamvu yogwila nchito ya Mulungu. Yehova anaseŵenzetsa mzimu woyela pouzila anthu kulemba Baibo. Cinanso, mzimuwu umatithandiza kumvetsetsa zimene timaŵelenga m’Baibo na kuzigwilitsila nchito. (Yoh. 14:26; 2 Pet. 1:21) Poseŵenzetsa mzimu wake, Yehova amatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7) Mzimu woyela umatithandiza polalikila uthenga wabwino, polimbana na mayeselo, komanso popilila mavuto na zinthu zina zolefula. Umatithandizanso kukhala na makhalidwe abwino amene “mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22) Mulungu amapeleka mowolowa manja mzimu wake woyela kwa anthu amene amamudalila na kumupempha mocokela pansi pa mtima.—Luka 11:13.

15 N’zokhazika mtima pansi ndiponso n’zolimbikitsa kudziŵa kuti olambila Yehova amadalila mzimu woyela kuti uwathandize potumikila Mulungu. Kukhulupilila mfundo za coonadi zimene munaphunzila ponena za mzimu woyela, kudzakusonkhezelani kudzipatulila kwa Mulungu na kubatizika.

16. Pofika pano, kodi takambilana ciani?

16 Cosankha canu cofuna kudzipatulila kwa Mulungu komanso kubatizika n’cofunika kwambili. Koma monga taphunzilila m’nkhani ino, mufunika kuŵelengela” mtengo wake—kutanthauza kukhala wokonzeka kukumana na mavuto komanso kudzimana zinthu zina. Kukamba zoona, madalitso amene mudzapeza ni oculuka kwambili kuposa mavuto amene mungakumane nawo. Ubatizo ungakupulumutseni ndiponso ungakuthandizeni kukhala na cikumbumtima cabwino pamaso pa Mulungu. Kukonda Yehova Mulungu ndiye cifukwa cacikulu cimene cakusonkhezelani kufuna kubatizika. Mufunikanso kukhulupilila na mtima wonse mfundo zonse za coonadi zimene munaphunzila m’Baibo ponena za Yehova, Mwana wake Yesu, na mzimu woyela. Malinga na zimene takambilana m’nkhani ino, kodi muona kuti ndimwe wokonzeka kubatizika?

ZIMENE MUFUNIKA KUCITA MUKALIBE KUBATIZIKA

17. Ni zinthu ziti zimene munthu afunika kucita akalibe kubatizika?

17 Ngati muona kuti ndimwe wokonzeka kubatizika, ndiye kuti mwacionekele munacita kale zambili zokuthandizani kukhala pa ubale wabwino na Yehova. * Cifukwa cophunzila Baibo nthawi zonse, mwadziŵa zambili za Yehova na Yesu. Apa tsopano muli na cikhulupililo. (Aheb. 11:6) Mumakhulupilila na mtima wonse malonjezo a Yehova opezeka m’Baibo. Komanso simukayikila kuti kukhulupilila nsembe ya Yesu kungakupulumutseni ku ucimo na imfa. Kuwonjezela apo, munalapa macimo anu, kutanthauza kuti munamvela cisoni kwambili na zoipa zimene munali kucita, ndipo munapempha Yehova kuti akukhululukileni. Cinanso, munatembenuka, kutanthauza kuti munaipidwa na makhalidwe anu oipa akale, ndipo munayamba kukhala na umoyo wokondweletsa Mulungu. (Mac. 3:19) Lomba ndimwe wofunitsitsa kuuzako ena zimene mumakhulupilila. Munayenelela kukhala wofalitsa wosabatizika ndipo munayamba kulalikila na mpingo. (Mat. 24:14) Yehova amakunyadilani poona kuti munacita zinthu zofunika kwambili zimenezi kuti mubatizike. Zimene munacita zimam’kondweletsa kwambili.—Miy. 27:11.

18. N’ciani cina cimene mufunika kucita mukalibe kubatizika?

18 Mukalibe kubatizika, pali zinthu zina zingapo zimene mufunika kucita. Monga taphunzilila kuciyambi, mufunika kudzipatulila kwa Mulungu. Pamwekha, pemphelani kwa Yehova mocokela pansi pa mtima na kumulonjeza kuti tsopano muzicita cifunilo cake pa umoyo wanu. (1 Pet. 4:2) Ndiyeno dziŵitsani mgwilizanitsi wa bungwe la akulu kuti mufuna kubatizika. Iye adzapempha akulu kuti aonane namwe. Koma simuyenela kuyopa kuonana nawo. Kumbukilani kuti akulu okoma mtima amenewa amakudziŵani kale ndiponso amakukondani. Iwo adzakambilana namwe ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo zimene munaphunzila. Colinga cawo ni kuona ngati mumamvetsetsa ziphunzitso zimenezo. Amafunanso kuona ngati mudziŵa bwino kufunika kodzipatulila na kubatizika. Iwo akaona kuti ndimwe woyenelela, adzakudziŵitsani kuti mungabatizike pa msonkhano wadela kapena wacigawo wotsatila.

ZIMENE MUDZAFUNIKA KUCITA PAMBUYO POBATIZIKA

19-20. Kodi mudzafunika kucita ciani pambuyo pobatizika? Nanga mungacite bwanji zimenezi?

19 Kodi mudzafunika kucita ciani pambuyo pobatizika? * Kumbukilani kuti kudzipatulila ni lumbilo, ndipo Yehova amafuna kuti musunge lumbilo lanu. Conco, mukabatizika muyenela kucita zinthu mogwilizana na kudzipatulila kwanu. Kodi mungacite bwanji zimenezi?

20 Pitilizani kugwilizana na mpingo. Monga Mkhristu wobatizika, tsopano muli ‘m’gulu la abale.’ (1 Pet. 2:17) Abale na alongo mu mpingo ni banja lanu lauzimu. Ngati mupezeka pa misonkhano nthawi zonse, mudzalimbitsa ubale wanu na iwo. Muziŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse na kuwasinkhasinkha. (Sal. 1:1, 2) Pambuyo poŵelenga Baibo, muzipatula nthawi yoganizila mozama zimene mwaŵelengazo. Mukatelo, zimene mwaŵelengazo zidzakufikani pa mtima. Cina, ‘muzipemphela kosalekeza.’ (Mat. 26:41) Mapemphelo anu ocokela pansi pa mtima adzakuthandizani kuyandikila kwambili Yehova. Cinanso, “pitilizani kufunafuna ufumu coyamba.” (Mat. 6:33) Mungacite zimenezi mwa kuika patsogolo nchito yolalikila mu umoyo wanu. Ngati mulalikila nthawi zonse, mudzakhalabe na cikhulupililo colimba, ndiponso mungathandize ena kuyamba kuyenda pa njila yotsogolela ku moyo wosatha.—1 Tim. 4:16.

21. Kodi ubatizo udzakupatsani mwayi wotani?

21 Kudzipatulila kwa Yehova komanso kubatizika ni cosankha cofunika kwambili cimene mungapange mu umoyo wanu. N’zoona kuti kukhala wodzipatulila na wobatizika kumafuna kudzimana zinthu zina na kupilila zovuta zosiyana-siyana. Olo n’telo, kucita zimenezi kumabweletsa madalitso. Mavuto alionse amene mungakumane nawo m’dzikoli ni “akanthawi ndipo ndi opepuka.” (2 Akor. 4:17) Koma ubatizo udzakupatsani mwayi wokhala na umoyo wabwino pali pano, ndipo kutsogolo mudzapeza “moyo weniweniwo.” (1 Tim. 6:19) Conco, ganizilani mosamala na kuipemphela nkhaniyi kuti muone ngati ndimwedi wokonzeka kubatizika.

NYIMBO 50 Pemphelo Langa Lodzipeleka kwa Mulungu

^ ndime 5 Kodi muganiza zobatizika? Ngati n’conco, nkhani ino yakonzedwela maka-maka imwe. Ubatizo ni cosankha cacikulu. Telo m’nkhani ino, tikambilana mafunso angapo ofunika kwambili ponena za ubatizo. Mayankho anu pa mafunso amenewo adzakuthandizani kuona ngati ndimwe wokonzeka kubatizika.

^ ndime 17 Onani nkhani 18 m’buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse.

^ ndime 19 Ngati mukalibe kutsiliza kuphunzila buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse komanso lakuti Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu, muyenela kupitiliza kuphunzila na mphunzitsi wanu mpaka mukatsilize mabuku onse aŵiliwa.