Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

“Ife tilipo. Titumizeni”

“Ife tilipo. Titumizeni”

KODI inuyo mumafuna kuwonjezera utumiki wanu posamukira kumene kukufunika ofalitsa ambiri, mwina m’dziko lina? Ngati ndi choncho, nkhani ya M’bale ndi Mlongo Bergame ikuthandizani.

Jack ndi Marie-Line akhala akuchita limodzi utumiki wa nthawi zonse kuyambira mu 1988. Iwo savutika kuzolowera moyo watsopano ndipo akhala akuchita utumiki wosiyanasiyana ku Guadeloupe ndi ku French Guiana. Panopa malo amenewa amayang’aniridwa ndi nthambi ya ku France. Tiyeni tsopano tikambirane ndi Jack ndi Marie-Line mafunso angapo.

N’chifukwa chiyani munayamba utumiki wa nthawi zonse?

Marie-Line: Ndinakulira ku Guadeloupe. Ndipo ndili mwana, nthawi zambiri ndinkalalikira tsiku lonse ndi mayi anga omwe ankalalikirabe mwakhama. Ndimakonda kwambiri anthu. Choncho nditangomaliza sukulu mu 1985 ndinayamba upainiya.

Jack: Ndili mwana ndinkakhala ndi anthu amene ankachita utumiki wa nthawi zonse ndipo ankakonda kwambiri kulalikira. Ndikakhala pa holide ndinkakonda kuchita upainiya wothandiza. Nthawi zina, Loweruka ndi Lamlungu tinkakwera basi ndi apainiya ena kukalalikira m’magawo awo. Tinkalalikira tsiku lonse ndipo utumiki tinkamalizira kunyanja. Kunena zoona tinkasangalala kwambiri.

Titangokwatirana ndi Marie-Line mu 1988, ndinadziuza kuti, ‘Anthufetu tili ndi mipata yambiri ndiye tikhoza kuchita zambiri mu utumiki.’ Choncho ndinayamba kuchita upainiya limodzi ndi Marie-Line. Patangotha chaka chimodzi, tinapita kusukulu ya apainiya kenako anatiuza kuti tiyambe upainiya wapadera. Tinkasangalala kwambiri ndi utumiki wathu ku Guadeloupe kenako anatitumiza ku French Guiana.

Utumiki wanu wakhala ukusinthasintha kwambiri. Kodi n’chiyani chimakuthandizani kuti muzolowere moyo watsopano? 

Marie-Line: Abale ku Beteli ya ku French Guiana ankadziwa kuti timakonda lemba la Yesaya 6:8. Choncho akatiitana ankakonda kunena moseka kuti, “Mukukumbukira lemba limene mumalikonda lija?” Akatero tinkadziwiratu kuti utumiki ukusintha. Ndiye tinkangoyankha kuti, “Ife tilipo. Titumizeni.”

Timapewa kuyerekezera utumiki watsopano ndi wakale podziwa kuti zimenezi zikhoza kutilepheretsa kuyamikira zimene tili nazo. Timayesetsanso kudziwana bwino ndi abale ndi alongo kuti akhale anzathu.

Jack: M’mbuyomo, anzathu ena ankafuna kuti tisalole kuchoka n’cholinga choti tisasiyane nawo. Koma titachoka ku Guadeloupe, m’bale wina anatikumbutsa mawu a Yesu a pa Mateyu 13:38 akuti, “Munda ndiwo dziko.” Choncho utumiki wathu ukasintha n’kusamukira kwina tinkangokumbukira kuti tidakali m’munda umodzi. Ndipotu ofunika kwambiri ndi anthu m’gawo lililonse.

Tikafika kudera latsopano timaona kuti anthu akukhalako bwinobwino. Choncho timangoyesetsa kukhala ngati mmene eniakewo akukhalira. N’zoona kuti zakudya zimasiyana koma kudya ndi kudya basi ndipo kumwa ndi kumwa basi, bola osadwala nazo. Timayesetsa kuti tizilankhula zabwino zokhudza utumiki uliwonse.

Marie-Line: Timaphunzira zambiri kwa abale ndi alongo kulikonse kumene tasamukira. Chitsanzo ndi zimene zinachitika titasamukira ku French Guiana. Kunkagwa mvula yambiri ndiye ife tinaganiza kuti tidikire kaye kuti ikasiya tilowe mu utumiki. Ndiye mlongo wina anangondifunsa kuti: “Koma tipita?” Izi zinandidabwitsa kwambiri moti ndinamufunsa kuti, “Tiyenda bwanji?” Iye anati, “Mungotenga ambulera, tizipita panjinga.” Choncho ndinaphunzira kuyendetsa njinga uku nditafunda ambulera. Akanapanda kuchita zimenezi, ndiye kuti sindikanalalikira nyengo yamvula yonseyo.

Paja mwasintha utumiki maulendo 15. Kodi pali mfundo zina zimene mungatiuze zothandiza pa nkhani yosamuka?

Marie-Line: Kunena zoona, kusamuka n’kovuta. Koma chimene chimangofunika n’kupeza malo abwino oti uzifikirako ukaweruka mu utumiki.

Jack: Ndimakonda kupentanso m’nyumba imene talowa. Nthawi zina abale akunthambi akadziwa kuti sitichedwa kumene atitumizako ankandiuza kuti, “Jack, usavutike ndi kupenta nyumba.”

Marie-Line ali ndi luso lolongedza katundu. Amaika katundu m’makatoni n’kuwalemba kuti “kubafa,” “kuchipinda,” “kukhitchini” ndi kwina. Choncho tikafika kunyumba yatsopano sitivutika kuika zinthu pamalo oyenera. Amalembanso pepala pabokosi lililonse losonyeza zimene zili mkati, choncho sitivutika kupeza zimene tikufuna.

Marie-Line: Taphunzira kuchita zinthu mwadongosolo choncho sizivuta kuti tikangofika tiziyamba msanga utumiki wathu.

Kodi mumagawa bwanji nthawi kuti ‘muzikwaniritsa mbali zonse za utumiki wanu’?​—2 Tim. 4:5.

Marie-Line: Lolemba, timapuma n’kumakonzekera misonkhano. Kuyambira Lachiwiri, timalowa mu utumiki.

Jack: N’zoona kuti anatiuza maola amene tiyenera kukwanitsa koma sitiganizira kwambiri zimenezo. Timaona kuti chofunika kwambiri ndi kulalikirako. Timayesetsa kulankhula ndi anthu tikangonyamuka pakhomo mpaka pamene tafikanso pakhomo.

Marie-Line: Tikapita kwinakwake kukasangalala ndimatenga timapepala. Anthu ena amatha kubwera kudzapempha mabuku ngakhale kuti sitinawauze zoti ndife a Mboni za Yehova. Choncho timayesetsa kuvala bwino komanso kuchita zinthu mwaulemu chifukwa anthu amaona zonsezi.

Jack: Timayesetsanso kuchitira umboni posonyeza khalidwe labwino. Mwachitsanzo, timatola zinyalala n’kukazitaya komanso timasesa. Anthu akaona zimenezi amatha kutipempha kuti, “Mungatigawireko Baibulo?”

Mwakhala mukulalikira m’madera ambiri akumidzi. Pali zina zimene simuiwala m’madera ngati amenewa?

Jack: Ku Guiana, timalalikira m’madera ena ovuta kufikako. Nthawi zambiri, pa mlungu timayenda makilomita 600 m’misewu yovuta kwambiri. Sitiiwala zimene zinachitika titapita ku St. Élie munkhalango ya Amazon. Tinagwiritsira ntchito galimoto yoyenda m’misewu yovuta kwambiri komanso boti la injini ndipo zinatitengera maola angapo kuti tikafikeko. Anthu ambiri amene tinkawapeza anali ogwira ntchito m’migodi ya golide. Ena ankatipatsa timiyala tagolide poyamikira mabuku amene tinkawapatsa. Madzulo tinaonetsa anthu mavidiyo a gulu ndipo kunafika anthu ambiri.

Marie-Line: Posachedwapa, Jack anapemphedwa kuti akakambe nkhani ya Chikumbutso ku Camopi. Kuti tikafike, tinayenda maola ambiri pa boti la injini mumtsinje wa Oyapock. Zinali zosangalatsa kwambiri.

Jack: Tinkaopa tikafika pamene madzi anali ochepa koma akuthamanga kwambiri. Zinkasangalatsa kuona madziwo akuthamanga koma woyendetsa botiyo ankafunika kukhala waluso kuti tidutse bwinobwino. Tinasangalala kwambiri ndi ulendowu. Kuderali kunali abale ndi alongo 6 okha koma anthu 50 anafika pa Chikumbutso ndipo ena anali a Chiamerindiyani.

Marie-Line: Achinyamata nawonso akhoza kusangalala ndi madalitso ngati amenewa akasankha kutumikira Yehova. Pamafunika kudalira Yehova kuti munthu achite utumiki wosiyanasiyana. Yehova wakhala akutithandiza nthawi zambiri ndipo zimenezi zimachititsa kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba.

Mwaphunzira zilankhulo zingapo. Kodi munabadwa ndi luso lophunzira zilankhulo?

Jack: Ayi ndithu. Tinafunika kuphunzira zilankhulozi kuti tizikwanitsa kulalikira komanso kuthandiza anthu mumpingo umene tili. Mwachitsanzo, ndinapemphedwa kuti ndizichititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda mu Chisiranantongo * ndisanapatsidwe n’komwe mbali ya kuwerenga Baibulo. Nditafunsa m’bale wina ngati ndinkalankhula zomveka. Iye anati: “Pena sitimakumvetsetsani, koma zinali bwino kwambiri.” Ndinaphunzira zambiri kwa ana chifukwa ndikalakwitsa mawu enaake sankachita manyazi kundiuza, koma akuluakulu sankandiuza ndikalakwitsa.

Marie-Line: M’gawo lina ndinali ndi maphunziro a Baibulo mu Chifulenchi, Chipwitikizi ndi Chisiranantongo. Mlongo wina anandiuza kuti ndiziyamba kuchititsa maphunziro a zilankhulo zomwe zinkandivuta kwambiri n’kumalizira ndi a zilankhulo zomwe ndinkazidziwa bwino. Ndinaona kuti zinalidi zothandiza.

Tsiku lina ndinachititsa maphunziro a Baibulo awiri, loyamba mu Chisiranantongo, linalo mu Chipwitikizi. Nditayamba kuchititsa lachiwirilo mlongo yemwe ndinayenda naye anati, “Marie-Line, ndikuona kuti sizikuyenda.” Kenako ndinazindikira kuti ndikulankhula Chisiranantongo kwa mzimayi wa ku Brazil m’malo molankhula Chipwitikizi.

Abale ndi alongo amene mwatumikira nawo limodzi amakukondani kwambiri. N’chiyani chimakuthandizani kuti muzigwirizana ndi abale?

Jack: Lemba la Miyambo 11:25 limati: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto.” Timapeza nthawi yocheza ndi abale komanso kuwachitira zinthu zina. Mwachitsanzo, nthawi zina pokonza Nyumba ya Ufumu, abale ena amandiuza kuti: “Ntchito imeneyi ndi ya ofalitsa.” Koma ndimayankha kuti: “Nanenso ndi wofalitsa. Ndiye ngati pali ntchito yoti tigwire, ndigwira nawo basi.” Ngakhale kuti nthawi zina timafunika nthawi yokhala patokha, sitilola kuti zimenezi zitilepheretse kuchitira ena zabwino.

Marie-Line: Timayesetsa kuchita chidwi ndi abale komanso alongo athu. Zimenezi zimatithandiza kudziwa zomwe akufunikira, kaya ndi kuyang’anira ana awo pakhomo kapena kukatenga anawo kusukulu. Ndiyeno timasintha zomwe tinakonza kuti tichite panthawiyo kuti tikwanitse kuwathandiza. Kukhala okonzeka kuthandiza ena n’kumene kumathandiza kuti tizikondana nawo kwambiri.

Kodi mwapeza madalitso otani potumikira kumene kukufunika ofalitsa ambiri?

Jack: Tapeza madalitso ambiri chifukwa chokhala mu utumiki wa nthawi zonse. Nthawi zambiri timakhala ndi mwayi woona zinthu zosangalatsa zam’chilengedwe cha Yehova. N’zoona kuti sipalephera kukhala zovuta zina, koma tili ndi mtendere wamumtima chifukwa timadziwa kuti kulikonse komwe tingapite anthu a Mulungu akatithandiza.

Ndili wachinyamata, ndinamangidwapo ku French Guiana chifukwa chopewa zandale. Sindinkayembekezera kuti tsiku lina ndingadzabwererekonso ndili mmishonale n’kuloledwa kukalalikira kundende. Ndimaona kuti Yehova wandidalitsa kwambiri.

Marie-Line: Ndimasangalala kwambiri ndikamathandiza ena. Ndife osangalala chifukwa tikutumikira Yehova. Utumikiwu wathandizanso kuti banja lathu likhale lolimba. Nthawi zambiri Jack akandifunsa ngati tingaitane banja lina kwathu kuti tidzalilimbikitse, ndimayankha kuti: “Nanenso ndimaganiza zomwezo.” Nthawi zambiri zimangokhala ngati tikuganiza zofanana.

Jack: Posachedwapa anandipeza ndi matenda a khansa. Pali mfundo ina imene ndinauza Marie-Line ngakhale kuti sinamusangalatse. Ndinamuuza kuti: “Ngati ndingafe mawa, ndiye kuti ndidzafa ndisanakalambe koma ndili wosangalala. Ndikutero chifukwa chakuti moyo wanga ndaugwiritsira ntchito potumikira Yehova ndipo zimenezi ndi zinthu zofunika kwambiri.”​—Gen. 25:8.

Marie-Line: Yehova watipatsa mwayi wa utumiki womwe sitinkayembekezera ndipo tachita zinthu zimene sitinkaganiza kuti tingazikwanitse. Pa moyo wathu takumana ndi zinthu zosangalatsa zambiri. Tidzapita kulikonse kumene gulu la Yehova lidzatitumize chifukwa tikudziwa kuti Yehovayo adzatithandiza nthawi zonse.

^ ndime 32 Chisiranantongo chinayamba ndi anthu omwe anali akapolo, ndiye mawu ake anatengedwa ku Chingelezi, Chidatchi, Chipwitikizi, ndi zilankhulo zina za ku Africa.