Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBILI YATHU

“Ife Tilipo! Titumizeni”

“Ife Tilipo! Titumizeni”

KODI mufuna kuwonjezela utumiki wanu mwa kukatumikila ku gawo limene kuli ofalitsa ocepa, mwina ku dziko lina? Ngati n’telo, ndiye kuti mungapindule kwambili na mbili ya M’bale na Mlongo Bergame.

M’bale Jack na mkazi wake Marie-Line atumikila pamodzi mu utumiki wa nthawi zonse kuyambila mu 1988. Iwo amajaila mwamsanga umoyo watsopano, ndipo acitapo mautumiki osiyana-siyana ku Guadeloupe komanso French Guiana. Madela aŵiliwa tsopano amayang’anilidwa na nthambi ya France. Tiyeni tikambilaneko nawo mafunso angapo.

N’ciani cinakulimbikitsani kuyamba utumiki wa nthawi zonse?

Mlongo Marie-Line: Ine n’nakulila ku Guadeloupe. Nili wacicepele, nthawi zambili n’nali kulalikila tsiku lonse pamodzi na amayi, amene anali Mboni yokangalika. Popeza nimakonda anthu, nitangotsiliza sukulu, mu 1985 n’nayamba upainiya.

M’bale Jack: Pamene n’nali wacinyamata, nthawi zonse n’nali kukhala na atumiki a nthawi zonse okonda ulaliki. Tikavalila sukulu, n’nali kukonda kucitako upainiya wothandiza. Kumapeto kwa wiki, nthawi zina tinali kuyenda pa basi kupita kukalalikila pamodzi na apainiya m’gawo lawo. Tinali kulalikila tsiku lonse, ndipo tikatsiliza tinali kupita kukasangalala ku nyanja. Imeneyo inali nthawi yokondweletsa ngako!

Nitangokwatila Marie-Line mu 1988, mu mtima n’nati, ‘Popeza tilibe maudindo ambili, kodi n’kulekelanji kuwonjezela utumiki wathu?’ Conco, mofanana na mkazi wanga Marie-Line, nanenso n’nayamba upainiya. Patapita caka, tinaloŵa Sukulu ya Apainiya, ndipo pambuyo pake tinaikidwa kukhala apainiya apadela. Tinacita mautumiki osiyana-siyana okondweletsa ku Guadeloupe. Pambuyo pake, anatiitana kuti tikatumikile ku French Guiana.

Utumiki wanu wasintha kambili-mbili m’zaka zapitazi. N’ciani cakuthandizani kujaila umoyo watsopano pocita mautumiki amenewa?

Mlongo Marie-Line: Abale a pa Beteli ku French Guiana anali kudziŵa kuti lemba lathu la pamtima ni Yesaya 6:8. Conco, akatitumila foni, nthawi zambili poyamba anali kukamba nafe mwanthabwala, amvekele, “Kodi mukumbukila lemba lanu lapamtima?” Tikamva izi, tinali kudziŵa kuti utumiki wathu usintha posacedwa. Conco, tinali kuyankha kuti, “Ife tilipo! Titumizeni!”

Timapewa kuyelekezela utumiki wathu wakale na utumiki umene ticita lomba, cifukwa kucita izi kungapangitse kuti tisamasangalale na utumiki umene ticita. Timayesetsanso kudziŵana bwino na abale na alongo a ku malo atsopano kumene titumikilako.

M’bale Jack: Kumbuyoko, tikafuna kusamuka, anzathu ena anali kutiuza kuti tisasamuke cifukwa cofuna kuti tipitilize kukhala nawo. Koma pamene tinali kucoka ku Guadeloupe, m’bale wina anatikumbutsa mawu a Yesu a pa Mateyu 13:38, akuti “Munda ndiwo dziko.” Conco, utumiki wathu ukasintha, timayesetsa kukumbukila kuti mosasamala kanthu za kumene tili, tikutumikilabe m’munda wauzimu umodzi-modzi. Ndi iko komwe, cofunika kwambili ni anthu komanso gawo lolalikilamo.

Tikafika m’dela latsopano, timaona kuti ena akukhala bwino-bwino mosangalala. Conco, timayesetsa kukhala mmene iwo akukhalila. Cakudya cawo cingakhale cosiyana na cimene tinajaila. Komabe, timadya zimene iwo amadya komanso timamwa zimene iwo amamwa. Pa nthawi imodzi-modziyo, timakhala osamala kuti titeteze thanzi lathu. Timayesetsa kukamba zabwino za utumiki uliwonse umene tapatsidwa.

Mlongo Marie-Line: Timaphunzilanso zambili kwa abale na alongo a ku malo kumene tikutumikilako. Nikumbukila zimene zinacitika tsiku lina titangofika ku French Guiana. Kunali kugwa mvula yamphamvu, ndipo tinaganiza kuti tifunika kuyembekezela mpaka ikate kuti tiyende mu ulaliki. Koma mlongo wina ananiuza kuti, “Tiyeni tiyambepo.” Ine n’nadabwa, ndipo n’namufunsa kuti, “Tiyenda bwanji?” Iye anati, “Tengani ambulela yanu, ndipo tiyenda pa njinga zathu.” Umu ni mmene n’naphunzilila kuyendetsa njinga nitagwila ambulela ku dzanja lina. Nikanapanda kuphunzila zimenezi, sembe sin’nakwanitse kulalikila m’nyengo yamvula imeneyo!

Mwakukapo maulendo pafupi-fupi 15. Kodi pali malangizo aliwonse othandiza okhudza kusamuka amene mungafune kuuzako ena?

Mlongo Marie-Line: Kukuka kungakhale kovuta. Komabe, ngati wakuka, zimakhala bwino kupeza nyumba yoyenelela yokhalamo, imene ungamapumulilemo ukacoka mu ulaliki.

M’bale Jack: Nikakukila m’nyumba yatsopano, nthawi zambili nimaipentanso mkati. Nthawi zina, abale a ku nthambi podziŵa kuti sitidzakhalitsa kumene takukila, anali kuniuza kuti, “M’bale Jack, ulendo uno musavutike na kupenta nyumbayi.”

Mkazi wanga ni katswili wodziŵa kupakila katundu. Amaika katundu yense m’mabokosi na kulembapo mawu akuti, “zam’bafa,” “zam’cipinda,” “zam’khichini,” na mawu ena ngati amenewa. Conco, tikafika ku nyumba yathu yatsopano, sizikhala zovuta kuika mabokosiwo pa malo ake oyenelela. Iye amalembanso m’ndandanda wa zimene zili m’bokosi iliyonse n’colinga cakuti tisavutike kupeza zimene tifuna.

Mlongo Marie-Line: Popeza taphunzila kukhala adongosolo, tikasamuka sitivutika kuyambilanso kucita zinthu mmene tinali kucitila poyamba.

Kodi mumagaŵa bwanji nthawi kuti ‘mukwanilitse mbali zonse za utumiki wanu?’—2 Tim. 4:5.

Mlongo Marie-Line: Pa Mande paliponse, timapumula na kukonzekela misonkhano. Ndipo kuyambila pa Ciŵili mpaka kumapeto kwa wiki, timayenda mu ulaliki.

M’bale Jack: Olo kuti tili na maola ofunika kukwanilitsa pa mwezi, sitisumika maganizo athu pa zimenezi. Ulaliki ndiye cinthu cofunika kwambili pa umoyo wathu. Tikangocoka pa nyumba, timayesetsa kulalikila uthenga wabwino kwa aliyense amene takumana naye. Pobwelela, timacitanso cimodzi-modzi.

Mlongo Marie-Line: Mwacitsanzo, tikapita kukasangalala kwinakwake, nthawi zonse nimatengako mathilakiti. Anthu ena amabwela pali ife na kutipempha zofalitsa, olo kuti sitinawauze kuti ndife Mboni za Yehova. Conco, timasamala mavalidwe athu na khalidwe lathu, cifukwa anthu amaona zimenezi.

M’bale Jack: Timacitilanso umboni mwa kucita zinthu mokoma mtima na maneba athu. Mwacitsanzo, nimawathandiza mwa kutola mapepala na kukawataya m’bini. Maneba athu amacita cidwi na zimenezi, ndipo nthawi zina amafunsa kuti, “Nifunako Baibo, kodi mungakhaleko nayo?”

Mwalalikilako kambili m’magawo akutali. Kodi pali zilizonse zosaiŵalika zimene zinacitika pa maulendo anu okalalikila m’madela akutali?

M’bale Jack: Ku Guiana, magawo ena ni ovuta kufikako. Nthawi zambili, timayenda mtunda wa makilomita 600 pa wiki, m’misewu yoipa. Ulendo wathu wopita ku mudzi wa St. Élie, ku nkhalango ya Amazon, unali wosaiŵalika. Kuti tikafike kumeneko, tinayenda kwa maawazi angapo pa motoka komanso pa boti ya ingini. Anthu ambili okhala kumeneko amagwila nchito yokumba miyala ya golide. Poyamikila zofalitsa zathu, ena a iwo anatipatsa tumiyala twa golide monga copeleka. M’madzulo, tinatambitsa imodzi mwa mavidiyo athu. Ndipo anthu ambili anapezekapo.

Mlongo Marie-Line: Zaka zingapo zapitazo, mwamuna wanga anapemphedwa kuti akakambe nkhani ya Cikumbutso ku Camopi. Kuti tikafike kumeneko, tinayenda kwa maawazi anayi pa boti mu mtsinje wa Oyapock. Unali ulendo wokondweletsa maningi.

M’bale Jack: Pamene madzi mu mtsinje wa Oyapock anali ocepa, malo osondomoka pamene madzi amathamanga kwambili anali owopsa kupitapo. Kukamba zoona, zinali zocititsa cidwi kwambili mukamayandikila pa madzi othamanga amenewo. Woyendetsa boti anali kufunika kucita zinthu mosamala kwambili akafika pa malo amenewo. Koma unali ulendo wabwino kwambili. Ngakhale kuti ku Camopi kunali Mboni 6 cabe, anthu pafupi-fupi 50 anapezeka pa Cikumbutsoco, kuphatikizapo eni nthaka a ku America.

Mlongo Marie-Line: Acicepele amene afuna kucita zambili potumikila Yehova angakumane na zinthu zolimbikitsa ngati zimenezi. Pa zocitika ngati zimenezi, cofunika ni kudalila Yehova. Ndipo ukatelo, cikhulupililo cako cimalimba. Nthawi zambili, ife timaona thandizo la Yehova pa umoyo wathu.

Mwaphunzila vitundu vambili. Kodi ndiye kuti imwe sizikuvutani kuphunzila citundu?

M’bale Jack: Iyayi, nanenso zimanivuta. N’naphunzila vitundu vimenevi cifukwa ca kusoŵa kumene kunalipo mu mpingo. N’nayamba kutsogoza phunzilo la Nsanja ya Mlonda m’Cisranantongo * nikalibe kupatsidwako nkhani yoŵelenga Baibo. Pambuyo pake, n’nafunsa m’bale wina kuti aniuze ngati anthu anali kumva zimene n’nali kukamba. Iye anakamba kuti, “Pena sitinali kumva zimene munali kukamba, koma mwatsogoza bwino kwambili.” Ana ananithandiza ngako. Nikalakwitsa kukamba, anali kuniuza. Koma akulu-akulu anali kungokhala cete. N’naphunzila zambili kwa ana.

Mlongo Marie-Line: M’gawo lina, n’nali na maphunzilo a Baibo a Cifulenchi, Cipwitikizi, na Cisranantongo. Mlongo wina ananiuza kuti ningacite bwino kuyambila kutsogoza maphunzilo a citundu cimene cinali kunivuta, ca Cipwitikizi, na kutsilizila maphunzilo a citundu cimene n’nali kucidziŵa bwino. Posapita nthawi, n’nadzionela nekha ubwino wotsatila malangizo amenewo.

Tsiku lina, n’natsogoza phunzilo mu Cisranantongo, ndipo phunzilo laciŵili linali la Cipwitikizi. N’tayamba kutsogoza phunzilo laciŵili, mlongo amene n’nali naye anati, “Mlongo Marie-Line, niona ngati pali vuto linalake.” Atakamba izi, n’nazindikila kuti nikukamba Cisranantongo kwa mayi wocokela ku Brazil, m’malo mokamba naye mu Cipwitikizi.

Anthu amene mumawatumikila amakukondani kwambili. Kodi n’ciani cakuthandizani kupanga ubwenzi wolimba na abale na alongo?

M’bale Jack: Miyambo 11:25 imati: “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandila mphoto.” Conco, ife timayesetsa kupatula nthawi yoceza na ena komanso kuwathandiza. Ponena za kugwila nchito yokonza zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu, abale ena amaniuza kuti: “Alekeleni ofalitsa agwile nchitoyi.” Koma ine nimayankha kuti: “Cabwino, koma inenso ndine wofalitsa. Ndipo pakakhala nchito, nanenso nimafuna kugwilako.” Komanso, n’zoona kuti tonsefe timafuna kukhalako patekha nthawi zina. Koma ife sitilola zimenezi kutilepheletsa kucitila ena zabwino.

Mlongo Marie-Line: Timayesetsa kuwaonetsa cidwi abale na alongo. Mwa kucita izi, timatha kudziŵa ngati pali winawake amene afuna munthu wom’thandiza kuyang’anila ana kapena kukawatenga ku sukulu. Tikadziŵa zimenezi, timaona mmene tingasinthile mapulogilamu athu kuti tiwathandize. Timakhala okonzeka kuwathandiza pamene afunika thandizo. Mwakutelo, tapanga ubwenzi wolimba na ena.

Kodi mwapeza madalitso otani cifukwa cotumikila ku malo amene kuli ofalitsa ocepa?

M’bale Jack: Tapeza madalitso ambili cifukwa cotumikila mu utumiki wa nthawi zonse. Nthawi zambili, timaona komanso kusangalala na zinthu zosiyana-siyana zimene Yehova analenga. Olo kuti takhala tikukumana na zovuta zina, tili na mtendele wa m’maganizo cifukwa timadziŵa kuti kulikonse kumene tingapite kuli anthu a Mulungu amene angatithandize.

Pamene n’nali mnyamata, n’naponyedwa m’ndende ku French Guiana cifukwa cokana kuloŵa usilikali. Sin’nali kuyembekezela kuti nthawi ina nidzabwelelanso ku French Guiana monga mmishonale, komanso kupatsidwa mwayi wolalikila anthu m’ndende za kumeneko. Ndithudi! Yehova amadalitsa mowoloŵa manja.

Mlongo Marie-Line: Cimene cimanikondweletsa kwambili ni kudzipeleka kuthandiza ena. Ndife okondwa kutumikila Yehova. Kutumikila Yehova kwatithandizanso kukhala ogwilizana kwambili monga banja. Nthawi zina, mwamuna wanga amanipempha kuti: ‘Bwanji tiitaneko banja lakuti-lakuti kuti tidzadyele nawo limodzi na kuwalimbikitsako?’ Nthawi zambili, nimayankha kuti, ‘Inenso n’zimene n’nali kuganiza!’ Kaŵili-kaŵili umu ni mmene zimakhalila.

M’bale Jack: Posacedwapa, ananipeza na khansa ya pulositeti. Mkazi wanga safuna kumva zakuti mwina posacedwa ningafe. Koma n’namuuza kuti: “Wokondeka, n’zoona kuti ngati ningafe maŵa, siningamwalile nili ‘wokalamba,’ koma ningamwalile nili wokhutila, podziŵa kuti naseŵenzetsa moyo wanga potumikila Yehova, cimene ni cinthu cofunika kwambili.”—Gen. 25:8.

Mlongo Marie-Line: Yehova anatitsegulila mwayi wa mautumiki amene sitinali kuyembekezela, komanso watilola kucita zinthu zimene sitinali kuyembekezela kuti tingakwanitse kucita. Tapezadi madalitso ambili pa umoyo wathu. Podalila Mulungu na mtima wonse, ndife okonzeka kutumikila kulikonse kumene gulu lake lingatipemphe kukatumikila.

^ ndime 32 Cisranantongo ni citundu cophatikiza Cizungu, Cidachi, Cipwitikizi, na vitundu vina va ku Africa. Anayambitsa citundu cimeneci ni akapolo.