Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 13

Muzikondana Kwambili

Muzikondana Kwambili

“Kondanani kwambili kucokela mumtima.”​—1 PET. 1:22.

NYIMBO 109 Tizikondana ndi Mtima Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE *

Pamene Yesu anali na atumwi ake madzulo akuti maŵa adzaphedwa, anagogomeza za kufunika kwa cikondi (Onani ndime 1-2)

1. Ni lamulo lomveka bwino liti limene Yesu anapatsa ophunzila ake? (Onani cithunzi ca pa cikuto.)

MADZULO akuti maŵa adzaphedwa, Yesu anapatsa ophunzila ake lamulo lomveka bwino. Anati: “Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana.” Kenako anakamba kuti: “Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.”—Yoh. 13:34, 35.

2. N’cifukwa ciani kuonetsa cikondi pakati pathu n’kofunika?

2 Yesu anakamba kuti anthu adzatha kuwazindikila mosavuta ophunzila ake oona ngati iwo amaonetsa cikondi cofanana na cimene iye anaonetsa. Cikondi n’cimene cinadziŵikitsa Akhristu oona m’nthawi ya atumwi. Ndipo n’cimenenso cimadziŵikitsa Akhristu oona masiku ano. Ndiye cifukwa cake tifunika kuyesetsa kukonda Akhristu anzathu ngakhale pamene zili zovuta kutelo.

3. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 Cifukwa copanda ungwilo, nthawi zina zimativuta kukondana kwambili na abale na alongo athu. Ngakhale n’telo, tifunika kuyesetsa kutengela citsanzo ca Khristu. M’nkhani ino, tikambilana mmene cikondi cimatithandizila kukhala anthu obweletsa mtendele, opanda tsankho, komanso oceleza. Ndipo pamene tiphunzila nkhaniyi, mungacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Niphunzilapo ciani pa zitsanzo za abale na alongo amene amaonetsabe cikondi kwa ena ngakhale kuti pali zovuta zina?’

KHALANI OBWELETSA MTENDELE

4. Malinga na Mateyu 5:23, 24, n’cifukwa ciani tifunika kukhazikitsa mtendele ngati m’bale wathu ali nafe cifukwa?

4 Yesu anatiphunzitsa za kufunika kokhazikitsa mtendele na m’bale kapena mlongo wathu amene ali nafe cifukwa. (Ŵelengani Mateyu 5:23, 24) Iye anagogomeza kuti tifunika kukhala pa ubale wabwino na Akhristu anzathu kuti tikondweletse Mulungu. Yehova amakondwela ngati ticita zonse zotheka kuti tikhale pa mtendele na abale athu. Iye sangavomeleze kulambila kwathu ngati tisungila ena cakukhosi na kukana kukhazikitsa mtendele.—1 Yoh. 4:20.

5. N’cifukwa ciani zinali zovuta kuti m’bale Mark akhazikitse mtendele?

5 Nthawi zina, cingakhale covuta kukhazikitsa mtendele. Cifukwa ciani? Onani zimene zinacitikila m’bale Mark. * Iye anakhumudwa pamene m’bale wina anamunena na kuyamba kumudyela miseche mu mpingo. Kodi iye anacitapo ciani? Mark anati: “N’nalephela kuugwila mtima ndipo n’nakwiya.” Koma pambuyo pake, anadzimvela cisoni cifukwa ca zimene anacita, moti anapita kukapepesa kwa m’bale winayo n’colinga cobwezeletsa mtendele. Koma m’baleyo anakana kum’khululukila. Ataona kuti wakana, Mark mu mtima anati: ‘Nivutikilenji kukambilana na munthu amene safuna kuti tikhazikitse mtendele?’ Komabe, woyang’anila dela anam’limbikitsa kuti asafooke. Kodi iye anacita ciani?

6. (a) Kodi Mark anayesetsa bwanji kukhazikitsa mtendele? (b) Kodi iye anatsatila bwanji malangizo a pa Akolose 3:13, 14?

6 M’bale Mark atadzifufuza, anazindikila kuti sanali wodzicepetsa komanso kuti anali kudziona wolungama. Iye anaona kuti anafunika kusintha khalidwe lake. (Akol. 3: 8, 9, 12) Modzicepetsa, anapitanso kwa m’bale uja kukamupepesa kaciŵili pa zimene anamucitila. Mark analembelanso m’baleyo makalata acipepeso na kumupempha kuti ayambenso kugwilizana. Cinanso, anapatsa m’baleyo mphatso zina zocepa zimene anaona kuti angazikonde. Koma n’zacisoni kuti m’baleyo anapitilizabe kum’sungila cakukhosi. Ngakhale n’telo, Mark anapitiliza kumvela lamulo la Yesu lakuti tiyenela kukonda abale athu na kuwakhululukila. (Ŵelengani Akolose 3:13, 14.) Nthawi zina, tingayesetse kukambilana na m’bale wathu kuti tikhazikitse mtendele, koma osaphula kanthu. Olo zikhale conco, ngati timakonda anthu mmene Yesu anali kucitila, tidzapitiliza kum’khululukila komanso kupemphela kuti tidzakhalenso naye pamtendele.—Mat. 18:21, 22; Agal. 6:9.

Nthawi zina, tingafunike kuyesa njila zosiyana-siyana kuti tikhazikitse mtendele (Onani ndime 7-8) *

7. (a) Kodi Yesu anatilangiza kuti tiyenela kucita ciani? (b) Kodi mlongo Lara anakumana na vuto lanji?

7 Yesu anatilangiza kuti tiyenela kupitiliza kucitila ena zinthu zimene timafuna kuti nawonso aziticitila. Anakambanso kuti sitiyenela kukonda cabe anthu okhawo amene amatikonda. (Luka 6:31-33) Koma bwanji ngati Mkhristu winawake mu mpingo amangokudutsani osakupatsani moni? Ngakhale kuti izi sizicitika kaŵili-kaŵili, n’zimene zinacitikila mlongo Lara. Iye anati: “Mlongo wina anali kungonidutsa osanipatsa moni, ndipo sin’nali kudziŵa cifukwa cake. Izi zinayamba kunivutitsa maganizo kwambili, moti sin’nali kusangalalanso nikaganizila zopita ku misonkhano.” Poyamba, mlongo Lara mu mtima anati: ‘Sin’namulakwile ciliconse, ndipo enanso mu mpingo amakamba kuti iye ali na vuto.’

8. Kodi mlongo Lara anacita ciani kuti akhazikitse mtendele? Nanga tiphunzilapo ciani pa citsanzo cake?

8 Mlongo Lara anacitapo kanthu kuti akhazikitse mtendele. Anapemphela kwa Yehova, ndipo anaganiza zopita kukakambilana na mlongoyo. Iwo anakambilana za vutolo, kukumbatilana, na kukhazikitsa mtendele. Zonse zinaoneka monga zakhala bwino. Lara anati: “Koma patapita nthawi, mlongoyo anayambanso kuninyalanyaza monga poyamba. Izi zinanilefula kwambili.” Panthawiyi, Lara anafika poganiza kuti sangakhalenso wacimwemwe ngati mlongoyo sangasinthe khalidwe lake. Koma m’kupita kwa nthawi, anazindikila kuti cothandiza kwambili cimene ayenela kucita ni kupitiliza kumuonetsa cikondi mlongoyo na ‘kumukhululukila ndi mtima wonse.’ (Aef. 4:32–5:2) Lara anakumbukila kuti cikondi ceni-ceni cacikhristu “sicisunga zifukwa. Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.” (1 Akor. 13:5, 7) Conco, analeka kudela nkhawa za vutolo. Ndipo m’kupita kwa nthawi, mlongo winayo anayamba kuonetsa mzimu waubwenzi. Mukayesetsa kukhazikitsa mtendele na abale na alongo anu komanso kupitiliza kuwaonetsa cikondi, mosakayikila “Mulungu wacikondi ndi wamtendele adzakhala nanu.”—2 Akor. 13:11.

KHALANI OPANDA TSANKHO

9. Malinga na Machitidwe 10:34, 35, n’cifukwa ciani tiyenela kukhala opanda tsankho?

9 Yehova alibe tsankho. (Ŵelengani Machitidwe 10:34, 35.) Conco, tikakhala opanda tsankho, timaonetsa kuti ndife ana ake. Timaonetsanso kuti timamvela lamulo lakuti tizikonda anzathu monga mmene timadzikondela tekha. Komanso, timathandiza kuti m’banja lathu lauzimu mukhalebe mtendele.—Aroma 12:9, 10; Yak. 2:8, 9.

10-11. Kodi mlongo Ruth anakwanitsa bwanji kuthetsa maganizo a tsankho?

10 Kukhala opanda tsankho kungakhale kovuta kwa Akhristu ena. Mwacitsanzo, ganizilani za mlongo wina dzina lake Ruth. Pamene anali wacicepele, munthu wina wocokela ku dziko lina anacitila banja lawo zinthu zoipa kwambili. Kodi iye anamvela bwanji? Mlongo Ruth anati: “N’nayamba kuzonda ciliconse ca ku dziko limenelo. N’nali kuona kuti anthu onse ocokela ku dzikolo, ngakhale abale na alongo, ali na makhalidwe oipa.” Kodi mlongoyu anacita ciani kuti athetse maganizo ake olakwika?

11 Iye anazindikila kuti anafunika kuyesetsa kuthetsa maganizo a tsankho amenewo. Anayamba kuŵelenga zocitika na malipoti okhudza dzikolo mu Buku Lapachaka. Anati: “N’nacita zonse zotheka kuti niyambe kuganizila zabwino zokhudza anthu a ku dzikolo. Ndiyeno, n’nayamba kuona kuti abale na alongo a kumeneko ni okangalika potumikila Yehova. N’nazindikila kuti nawonso ali mbali ya gulu la padziko lonse la abale.” Patapita nthawi, mlongoyu anazindikila kuti anafunika kuwaonetsa cikondi anthu ocokela ku dzikolo. Iye anati: “Nikakumana na abale na alongo a ku dzikolo, n’nali kuyesetsa kukhala waubwenzi. N’nali kuceza nawo na kuyesetsa kuwadziŵa bwino.” Kodi panakhala zotulukapo zotani? Mlongo Ruth anati: “M’kupita kwa nthawi, maganizo a tsankho anathelatu.”

Ngati ‘timakonda kwambili gulu lonse la abale,’ tidzapewa kucita tsankho (Onani ndime 12-13) *

12. Kodi mlongo Sarah anali na vuto lotani?

12 Anthu ena angakhale na tsankho, koma osazindikila kuti ali nalo. Mwacitsanzo, mlongo wina dzina lake Sarah anali kuganiza kuti alibe tsankho, cifukwa sanali kuweluza anthu potengela cikhalidwe cawo, udindo umene ali nawo m’gulu, kapena potengela kuti ni olemela kapena osauka. Koma iye anati: “N’nayamba kuzindikila kuti m’ceni-ceni n’nali na tsankho.” Motani? Sarah anakulila m’banja la anthu ophunzila kwambili, ndipo anali kukondanso kugwilizana na Akhristu ophunzila kwambili. Pa nthawi ina, iye anafika ngakhale pouza mnzake kuti: “Ine nimakonda kugwilizana na Akhristu ophunzila kwambili. Nimapewa kugwilizana na Akhristu osaphunzila kweni-kweni.” N’zoonekelatu kuti mlongoyu anafunika kusintha khalidwe lake. Kodi anasintha bwanji?

13. Kodi tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene mlongo Sarah anasinthila khalidwe lake?

13 Woyang’anila dela wina anathandiza mlongoyu kuti aonenso bwino khalidwe lake. Sarah anati: “Ananiyamikila cifukwa cotumikila Yehova mokhulupilika, komanso cifukwa ca ndemanga zolimbikitsa zimene nimapeleka, na cidziŵitso ca m’Malemba cimene nili naco. Ndiyeno anafotokoza kuti pamene cidziŵitso cathu cikukula, timafunikanso kukulitsa makhalidwe abwino monga kudzicepetsa na cifundo.” Sarah anaseŵenzetsa malangizo amene woyang’anila dela anamupatsa. Iye anati: “N’nazindikila kuti cofunika kwambili ni kukhala wokoma mtima komanso wacikondi.” Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Iye anayamba kuona abale na alongo moyenela. Mlongo Sarah anati: “N’nayesetsa kuganizila makhalidwe abwino amene amacititsa kuti Yehova aziwaona kukhala amtengo wapatali.” Nanga ife tiphunzilapo ciani? Tiyenela kupewelatu kudziona apamwamba kuposa ena cifukwa ca maphunzilo amene tinacita. Ngati ‘timakonda kwambili gulu lonse la abale,’ tidzapewa khalidwe la tsankho.—1 Pet. 2:17.

KHALANI OCELEZA

14. Malinga na Aheberi 13:16, kodi Yehova amamvela bwanji ngati tikhala oceleza?

14 Yehova amakondwela ngati ndife oceleza. (Ŵelengani Aheberi 13:16.) Iye amaona kuti kuceleza ni mbali ya kulambila kwathu, maka-maka tikathandiza osoŵa. (Yak. 1:27; 2:14-17) Ndiye cifukwa cake Malemba amatilimbikitsa ‘kukhala oceleza.’ (Aroma 12:13) Tikamaceleza ena, timaonetsa kuti timawakondadi, timasamala za iwo, ndipo timafunadi kukhala mabwenzi awo. Yehova amakondwela ngati tipatula nthawi yoceza na ena, kapena kuwapatsako zakudya kapenanso zakumwa. (1 Pet. 4:8-10) Komabe, pangakhale zopinga zina zimene zingapangitse kuti cikhale covuta kwa ife kukhala oceleza.

““Kale, sin’nali kukonda kuceleza ena. Koma tsopano n’nasintha, ndipo napeza cimwemwe coculuka” (Onani ndime 16) *

15-16. (a) N’cifukwa ciani ena amaona kuti sangakwanitse kuceleza ena? (b) N’ciani cinathandiza mlongo Edit kuthetsa vuto lake loopa kuceleza ena?

15 Nthawi zina, tingayope kuceleza ena cifukwa ca mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, mmene tinakulila, kapena cifukwa ca zizoloŵezi zimene tinali nazo kale. Ganizilani citsanzo ca mlongo wina wamasiye, dzina lake Edit. Akalibe kukhala Mboni, sanali kukonda kuceza na ena. Iye anali kuona kuti anthu ena ndiwo anali oyenelela kuceleza ena.

16 Atakhala Mboni, mlongo Edit anasintha maganizo ake. Anacitapo kanthu kuti akhale woceleza. Iye anati: “Pamene tinali kumanga Nyumba yathu ya Ufumu yatsopano, mkulu wina ananiuza kuti kubwela m’bale na mkazi wake amene adzatithandiza pa nchito yomangayo. Ndipo ananipempha ngati ningawapatseko malo ogona kwa mawiki aŵili. Ataniuza zimenezo, n’nakumbukila mmene Yehova anadalitsila mkazi wamasiye wa ku Zarefati.” (1 Maf. 17:12-16) Mlongo Edit anadzipeleka kulandila banja limeneli. Kodi anapeza madalitso aliwonse? Inde. Iye anati: “N’nakondwela kwambili cifukwa iwo anakhala kunyumba kwathu osati cabe kwa mawiki aŵili, koma kwa miyezi iŵili. Pa nthawiyo, tinapanga ubwenzi wolimba.” Dalitso lina n’lakuti wapeza mabwenzi apamtima mu mpingo. Mlongoyu lomba ni mpainiya, ndipo amakondwela kuitanila kunyumba kwake abale na alongo amene amalalikila nawo kuti akadye nawo zakudya zopepuka. Iye anati: “Kupatsa kumanibweletsela cimwemwe. Ndipo kukamba zoona, madalitso amene nimalandila cifukwa ca kupatsa kumeneku ni oculuka koposa.”—Aheb. 13:1, 2.

17. Kodi m’bale Luke na mkazi wake anazindikila ciani?

17 N’kutheka kuti tili na mtima woceleza, koma pangakhale mbali zina zofunika kuwongolela. Mwacitsanzo, m’bale Luke na mkazi wake amakonda kuceleza ena. Poyamba, anali kukonda kuitanila kunyumba kwawo makolo awo, acibululu, mabwenzi awo, komanso woyang’anila dela na mkazi wake. Komabe, m’bale Luke anati: “Tinazindikila kuti tinali kungoitanila anthu okhawo amene tinali kugwilizana nawo kwambili.” Kodi iye na mkazi wake anathetsa bwanji vuto limeneli?

18. Kodi m’bale Luke na mkazi wake anathetsa bwanji vuto limene anali nalo pa nkhani yoceleza?

18 M’bale Luke na mkazi wake anasintha maganizo awo pambuyo poganizila mawu a Yesu akuti: “Mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandila mphoto yotani?” (Mat. 5:45-47) Iwo anazindikila kuti anafunika kutengela citsanzo ca Yehova, amene ni woolowa manja kwa onse. Conco, anakonza zakuti ayambe kuitanila abale na alongo amene sanawaitanilepo. Iye anati: “Tonse lomba timasangalala kwambili pa maceza amenewa. Timalimbikitsidwa mwakuuzimu.”

19. Kodi tingaonetse bwanji kuti ndifedi ophunzila a Yesu? Nanga imwe mwatsimikiza mtima kucita ciani?

19 M’nkhani ino, takambilana mmene kukondana kwambili kungatithandizile kukhala anthu obweletsa mtendele, opanda tsankho, komanso oceleza. Tisalole ciliconse kutilepheletsa kukonda abale na alongo athu kucokela mu mtima. Tikatelo, tidzakhala acimwemwe, ndiponso tidzaonetsa kuti ndifedi ophunzila a Yesu.—Yoh. 13:17, 35.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

^ ndime 5 Yesu anakamba kuti cikondi n’cimene cimadziŵikitsa Akhristu oona. Kukonda abale na alongo athu kumatisonkhezela kukhala anthu obweletsa mtendele, opanda tsankho, komanso oceleza. Kucita izi nthawi zina kungakhale kovuta. M’nkhani ino, tikambilana malangizo amene angatithandize kuti tipitilize kukondana kwambili kucokela mu mtima.

^ ndime 5 Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akuyesa kukambilana na mlongo mnzake kuti akhazikitse mtendele, koma poyamba sizikuphula kanthu. Olo n’telo, iye akupitilizabe kuyesa-yesa. Ndipo pamapeto pake wakwanitsa kukhazikitsa mtendele.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacikulile akuona kuti ena mu mpingo amunyalanyaza.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo amene poyamba anali kuyopa kuceleza ena wasintha maganizo ake, ndipo wapeza cimwemwe cifukwa coceleza.