Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 15

Kodi Anthu Am’gawo Lanu Mumawaona Bwanji?

Kodi Anthu Am’gawo Lanu Mumawaona Bwanji?

“Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.”​—YOH. 4:35.

NYIMBO NA. 64 Tizigwira Ntchito Yokolola Mosangalala

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Yesu ananena mawu a pa Yohane 4:35, 36?

TSIKU lina Yesu ankadutsa m’munda womwe uyenera kuti unali ndi balere wongomera kumene. (Yoh. 4:3-6) Kunali kutatsala miyezi pafupifupi 4 kuti adzakololedwe. Koma Yesu ananena mawu amene mwina anadabwitsa anthu. Iye anati: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Werengani Yohane 4:35, 36.) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani?

2 Zikuoneka kuti Yesu ankanena za ntchito yosonkhanitsa anthu ngati mbewu. Taganizirani zimene zinali zitangochitika kumene. Ayuda sankagwirizana ndi Asamariya koma Yesu analalikira kwa mayi wachisamariya ndipo anamvetsera bwino. Yesu akulankhula zokhudza kukololazi, gulu la Asamariya omwe anamva za Yesu kuchokera kwa mayi uja linali likubwera kuti lidzaphunzire zambiri. (Yoh. 4:9, 39-42) Buku lina lofotokoza za Baibulo linanena kuti: “Anthuwo ankafunitsitsa kumvetsera . . . Zimenezi zikusonyeza kuti anali ngati mbewu zofunika kukolola.”

Kodi tizichita chiyani tikaona kuti m’minda yathu ndi ‘moyera ndipo m’mofunika kukolola’? (Onani ndime 3)

3. Kodi kuona anthu mmene Yesu ankawaonera kungakuthandizeni bwanji pa ntchito yolalikira?

3 Kodi inuyo mumaona bwanji anthu amene mumawalalikira? Kodi mumawaona kuti ali ngati mbewu zofunika kukolola? Ngati mumawaona choncho, zikhoza kukuthandizani m’njira zitatu. Choyamba, mudzalalikira mwakhama kwambiri. Paja nthawi yokolola imakhala yochepa ndipo munthu amafunika kugwira ntchito mwakhama. Chachiwiri, mudzasangalala mukaona anthu akumvetsera uthenga wabwino. Baibulo limanena kuti: ‘Anthu amasangalala pa nthawi yokolola.’ (Yes. 9:3) Ndipo chachitatu, mudzaona kuti munthu aliyense akhoza kukhala wophunzira. Choncho mudzasintha uthenga wanu kuti ugwirizane ndi zimene munthuyo amakonda.

4. Kodi munkhaniyi tikambirana mfundo ziti zokhudza Paulo?

4 N’kutheka kuti otsatira a Yesu ankaona kuti Asamariya ndi okanika koma si mmene Yesu ankawaonera. Iye ankaona kuti akhoza kukhala ophunzira ake. Nafenso tiyenera kuona kuti anthu am’gawo lathu akhoza kukhala ophunzira a Khristu. Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Paulo? Munkhaniyi tikambirana kuti iye (1) ankadziwa zimene anthu amene ankawalalikirawo amakhulupirira, (2) ankadziwa zimene anthu amakonda ndiponso (3) ankawaona kuti akhoza kukhala ophunzira a Yesu.

KODI AMAKHULUPIRIRA ZOTANI?

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Paulo ankamasuka kukambirana ndi anthu musunagoge?

5 Paulo ankakonda kulalikira m’masunagoge a Chiyuda. Mwachitsanzo, musunagoge wa ku Tesalonika, “kwa masabata atatu anakambirana nawo [Ayuda] mfundo za m’Malemba.” (Mac. 17:1, 2) Paulo ayenera kuti ankamasuka kukambirana ndi anthu musunagoge chifukwa anakulira m’chipembedzo cha Chiyuda. (Mac. 26:4, 5) Iye ankamvetsa bwino Ayuda choncho ankatha kuwalalikira mopanda mantha.​—Afil. 3:4, 5.

6. Kodi anthu amumsika wa ku Atene anali osiyana bwanji ndi amene Paulo ankawalalikira musunagoge?

6 Paulo atathamangitsidwa ndi adani ku Tesalonika komanso ku Bereya, anafika ku Atene. Kumeneko anapitanso musunagoge ndipo ‘anayamba kukambirana ndi Ayuda komanso anthu ena opembedza Mulungu.’ (Mac. 17:17) Koma mumsika anapeza anthu osiyana kwambiri ndi Ayuda. Pa anthu amene ankawalalikira kumeneko panali akatswiri a nzeru za anthu komanso anthu amitundu ina omwe ankaona kuti uthenga wa Paulo unali ‘chiphunzitso chatsopano.’ Iwo anamuuza kuti: “Zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo m’makutu mwathu.”​—Mac. 17:18-20.

7. Malinga ndi Machitidwe 17:22, 23, kodi Paulo anasintha bwanji uthenga wake?

7 Werengani Machitidwe 17:22, 23. Paulo sanalalikire anthu amitundu ina ku Atene ngati mmene analalikirira Ayuda musunagoge. Iye ayenera kuti anadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu a ku Atenewa amakhulupirira zotani?’ Ankayang’ana kwambiri zinthu zamumzindawu kuti adziwe za miyambo yawo yachipembedzo. Kenako Paulo ankayesetsa kupeza mfundo za m’chipembedzo chawo zomwe zinkafanana ndi mfundo zoona za m’Malemba. Pofotokoza za Paulo, katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Popeza anali Mkhristu wa Chiyuda, ankadziwa kuti Agiriki ambiri sankalambira Mulungu ‘woona,’ yemwe Ayuda ndiponso Akhristu ankamulambira. Koma iye anayesetsa kusonyeza kuti Mulungu amene ankamulalikira kwa anthuwo sanali wachilendo kwa anthu a ku Atene.” Izi zikusonyeza kuti Paulo ankasintha uthenga wake kuti ugwirizane ndi anthu amene ankawalalikira. Iye anauza anthu a ku Atene kuti uthenga wake umachokera kwa “Mulungu Wosadziwika” yemwe iwo ankayesa kumulambira. Ngakhale kuti anthuwa sankadziwa Malemba, Paulo ankayesetsabe kuwalalikira. Iye ankawaona kuti ali ngati mbewu zofunika kukolola ndipo anasintha njira yolalikirira uthenga wabwino.

Tizitsanzira mtumwi Paulo pokhala tcheru, posintha uthenga wathu komanso poona kuti anthu akhoza kukhala ophunzira a Khristu (Onani ndime 8, 12, 18) *

8. (a) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kudziwa zimene anthu am’gawo lanu amakhulupirira? (b) Kodi mungayankhe bwanji ngati munthu wanena kuti ali ndi chipembedzo chake?

8 Mofanana ndi Paulo, tizikhala tcheru. Tiziyesetsa kuona zinthu zimene zingatithandize kudziwa zomwe anthu am’gawo lathu amakhulupirira. Mwachitsanzo, kodi munthu wakongoletsa bwanji nyumba yake? Kodi dzina lake, zovala zake kapena mawu amene amagwiritsa ntchito zikusonyeza kuti ali m’chipembedzo chinachake? Koma nthawi zina munthu angachite kukuuzani yekha kuti ali ndi chipembedzo chake. Mpainiya wina wapadera dzina lake Flutura ananena zimene amachita akauzidwa zimenezi. Iye amanena kuti: “Sindinabwere kuti ndikukakamizeni kukhulupirira zimene ndimakhulupirira koma kuti tikambirane nkhani iyi . . . ”

9. Kodi mungakambirane nkhani ngati ziti ndi munthu wachipembedzo?

9 Kodi ndi nkhani ngati ziti zimene mungakambirane ndi anthu achipembedzo? Muziyesetsa kukambirana nawo zinthu zimene angagwirizane nazo. Mwachitsanzo, mwina amalambira Mulungu mmodzi, amavomereza kuti Yesu ndi Mpulumutsi wathu kapena mwina amakhulupirira kuti tikukhala m’dziko loipa lomwe liwonongedwe posachedwapa. Mukadziwa zimene munthu amakhulupirira, muzimulalikira mogwirizana ndi zimene angasangalale nazo.

10. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

10 Muzikumbukira kuti anthu ena sakhulupirira mfundo zonse zimene chipembedzo chawo chimaphunzitsa. Choncho ngakhale mutadziwa chipembedzo cha munthu, yesetsani kudziwa zimene iyeyo amakhulupirira. Mpainiya wina wapadera wa ku Australia dzina lake David ananena kuti: “Anthu ambiri amaphatikiza nzeru za anthu ndi zikhulupiriro za chipembedzo chawo.” Mlongo wina wa ku Albania dzina lake Donalta anati: “Anthu ena amene timakumana nawo amanena kuti ali m’chipembedzo chinachake koma kenako amanena kuti sakhulupirira kuti kuli Mulungu.” Mmishonale wina wa ku Argentina ananena kuti anthu ena akhoza kunena kuti amakhulupirira za Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera. Koma mwina nawonso sakhulupirira kuti onsewa ali mwa Mulungu mmodzi. Iye anati: “Ndikazindikira zimenezi sindivutika kupeza nkhani zimene angagwirizane nazo.” Choncho tiyenera kuyesetsa kudziwa zimene anthu amakhulupirira. Kenako tikhoza kukhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana” ngati mmene Paulo ankachitira.​—1 Akor. 9:19-23.

KODI AMAKONDA ZOTANI?

11. Malinga ndi Machitidwe 14:14-17, kodi Paulo anasintha bwanji uthenga wake kuti ugwirizane ndi anthu a ku Lusitara?

11 Werengani Machitidwe 14:14-17. Paulo ankasintha uthenga wake kuti ugwirizane ndi zimene anthu amakonda. Mwachitsanzo, atafika ku Lusitara anapeza anthu amene sankadziwa kwenikweni za Malemba. Choncho iye anakambirana nawo nkhani zimene iwo ankazidziwa. Anakambirana nawo za zokolola komanso zinthu zina zosangalatsa. Iye ankagwiritsa ntchito mawu komanso zitsanzo zimene anthuwo akanamvetsa mosavuta.

12. Kodi tingazindikire bwanji zimene anthu amakonda, nanga tingasinthe bwanji uthenga wathu kuti ugwirizane ndi zimenezo?

12 Muziyesetsa kuzindikira zimene anthu amakonda m’gawo lanu n’kusintha uthenga wanu kuti ugwirizane ndi zimenezo. Kodi mungadziwe bwanji zimene munthu amakonda? Chofunika ndi kukhala tcheru. Kodi munthuyo akulima, kuwerenga buku, kukonza galimoto kapena kuchita zinthu zina? Ndiyeno ngati n’zotheka muziyamba n’kukambirana zimene akuchitazo. (Yoh. 4:7) Mukhoza kudziwanso zambiri pongoona zimene munthu wavala. Mwina zingasonyeze dziko limene akuchokera, ntchito yake kapena timu ya masewera imene amaikonda. M’bale wina dzina lake Gustavo anati: “Ndinayamba kukambirana ndi mnyamata wina wazaka 19 amene anavala tisheti yokhala ndi chithunzi cha woimba wina wotchuka. Nditamufunsa za tishetiyo anafotokoza chifukwa chake amakonda woimbayo. Izi zinachititsa kuti tiyambe kuphunzira Baibulo ndipo panopa ndi m’bale.”

13. Kodi tingathandize bwanji munthu kuti afune kuphunzira Baibulo?

13 Mukamapempha munthu kuti muziphunzira naye Baibulo muzimuthandiza kuona kuti kuphunzirako ndi kosangalatsa ndipo kudzamuthandiza. (Yoh. 4:13-15) Chitsanzo ndi mlongo wina dzina lake Poppy. Tsiku lina anauzidwa kuti alowe m’nyumba ya mayi wina amene anasonyeza chidwi. Poppy ataona satifiketi ya mayiyo pakhoma yosonyeza kuti ndi pulofesa, ananena kuti ifenso timaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito Baibulo komanso misonkhano yathu. Mayiyo anavomera kuphunzira, tsiku lotsatira anapezeka pamisonkhano ndipo kenako anadzapezeka pamsonkhano wadera. Patangotha chaka chimodzi anabatizidwa. Ndiye dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amene ndikukachitako ulendo wobwereza amakonda zinthu ziti? Kodi ndingawafotokozere zophunzira Baibulo m’njira imene angakopeke nayo?’

14. Kodi mungatani kuti muziphunzitsa Baibulo mogwirizana ndi munthu aliyense?

14 Mukayamba kuphunzira ndi munthu, muzipeza nthawi yokonzekera phunziro lililonse n’kumaganizira moyo wa wophunzirayo komanso zimene amakonda. Muziganizira malemba amene mungawerenge, mavidiyo amene mungaonetse komanso zitsanzo zimene mungagwiritse ntchito pofotokoza mfundo za m’Baibulo. Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndi mfundo ziti zimene zingamusangalatse komanso kumufika pamtima?’ (Miy. 16:23) Ku Albania, mpainiya wina dzina lake Flora ankaphunzira ndi mayi wina yemwe ananena mwamphamvu kuti, “Sindingakhulupirire zoti akufa adzauka.” Flora sanamukakamize kuti akhulupirire. Iye anati: “Ndinaona kuti mayiyo ayenera kudziwa kaye Mulungu amene walonjeza kuti adzaukitsa akufa.” Ndiyeno pa phunziro lililonse, Flora ankatsindika za chikondi, nzeru komanso mphamvu za Yehova. Kenako mayiyo anayamba kukhulupirira zoti akufa adzauka ndipo panopa ndi wa Mboni za Yehova wakhama kwambiri.

MUZIONA KUTI AKHOZA KUKHALA OPHUNZIRA

15. Malinga ndi Machitidwe 17:16-18, kodi ndi makhalidwe ati a ku Girisi amene Paulo sanasangalale nawo, nanga n’chifukwa chiyani sanagwe ulesi pothandiza anthu a ku Atene?

15 Werengani Machitidwe 17:16-18. Paulo sanagwe ulesi pothandiza anthu a ku Atene ngakhale kuti mumzindawu munali mafano ambiri, chiwerewere, nzeru za anthu komanso anthuwo ankamunyoza. Paja Paulo anakhala Mkhristu ngakhale kuti poyamba anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) Yesu anaona kuti Paulo akhoza kukhala wophunzira wake. Ndiyeno Paulo anatsanzira Yesu n’kumaona kuti anthu a ku Atene akhoza kukhala ophunzira. Ndipotu ena mwa anthuwo anakhaladi ophunzira.​—Mac. 9:13-15; 17:34.

16-17. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu osiyanasiyana akhoza kukhala ophunzira a Khristu? Perekani chitsanzo.

16 M’nthawi ya atumwi, anthu osiyanasiyana anakhala ophunzira a Yesu. Polembera Akhristu amumzinda wa Korinto ku Girisi, Paulo ananena kuti anthu ena amumpingowo poyamba ankachita zinthu zoipa kwambiri. Kenako ananena kuti: “Ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera.” (1 Akor. 6:9-11) Mukanakhala inuyo, kodi mukanaona kuti anthu oterewa angasinthe n’kukhala ophunzira?

17 Masiku anonso, anthu ambiri amasintha n’kukhala ophunzira a Yesu. Mwachitsanzo, mpainiya wina wapadera ku Australia dzina lake Yukina anaona kuti anthu osiyanasiyana amatha kusintha akaphunzira uthenga wa m’Baibulo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtsikana wina amene anamupeza ku ofesi inayake yemwe anali atadzilembalemba pathupi komanso anavala zovala zazikulu kwambiri. Yukina anati: “Poyamba ndinkamukayikira koma kenako ndinayamba kumulankhula. Ndinazindikira kuti mtsikanayo ankakonda kwambiri Baibulo moti zinthu zina zimene analemba pathupi lake anali mavesi a m’buku la Salimo.” Mtsikanayo anayamba kuphunzira ndiponso kupezeka pamisonkhano. *

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruza anthu?

18 Kodi Yesu anaona kuti minda inali yofunika kukolola chifukwa chakuti ankayembekezera kuti anthu ambiri adzamutsatira? Ayi. Malemba anali ataneneratu kuti anthu ochepa ndi amene adzamukhulupirira. (Yoh. 12:37, 38) Ndipo Yesu anali ndi luso lodziwa zamumtima wa munthu. (Mat. 9:4) Ngakhale zinali choncho, ankalalikira kwa anthu onse koma ankathandiza kwambiri anthu ochepa omwe akanatha kumukhulupirira. Choncho popeza ifeyo sitingadziwe zamumtima wa munthu, tiyenera kupewa kuweruza anthu. M’malomwake, tiyenera kuona kuti munthu aliyense akhoza kukhala wophunzira. Mmishonale wina wa ku Burkina Faso dzina lake Marc ananena kuti: “Anthu amene ndimaona kuti akhoza kukhala ophunzira a Khristu amasiya kuphunzira. Koma amene ndimaganiza kuti sangapite patali ndi amene amachita bwino kwambiri. Choncho ndaona kuti ndi bwino kungolola kuti mzimu wa Yehova uzititsogolera.”

19. Kodi tiyenera kuona bwanji anthu am’gawo lathu?

19 Poyamba, tingaone kuti m’gawo lathu mulibe anthu ambiri amene ali ngati mbewu zofunika kukolola. Koma kumbukirani zimene Yesu anauza ophunzira ake. Iye ananena kuti m’minda ndi moyera, kapena kuti ndi mofunika kukolola. Anthu amatha kusintha n’kukhala ophunzira a Khristu. Yehova amaona kuti anthuwo ali ngati “zinthu zamtengo wapatali.” (Hag. 2:7) Ngati timaona anthu mmene Yehova ndi Yesu amawaonera, tidzayesetsa kudziwa za moyo wawo komanso zimene amakonda. Sitidzawaona ngati anthu achilendo koma ngati anthu amene akhoza kudzakhala abale ndi alongo athu.

NYIMBO NA. 57 Tizilalikira kwa Anthu a Mitundu Yonse

^ ndime 5 Kodi mmene timaonera anthu am’gawo lathu zimakhudza bwanji mmene timalalikirira komanso kuphunzitsa? Munkhaniyi tiona mmene Yesu ndi Paulo ankaonera anthu. Tikambirananso zimene tingachite kuti tiziwatsanzira poganizira zimene anthu amakhulupirira, zimene amakonda komanso powaona kuti akhoza kukhala ophunzira a Khristu.

^ ndime 17 Munkhani za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu” muli zitsanzo zambiri za anthu amene anasintha. Nkhani zimenezi zinkapezeka mu Nsanja ya Olonda mpaka mu 2017. Koma panopa zimapezeka pa jw.org®. Pitani pamene alemba kuti ZOKHUDZA IFEYO > ZOCHITIKA PA MOYO WA A MBONI ZA YEHOVA.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI Tsamba 10-11: Banja likulalikira kunyumba ndi nyumba ndipo laona (1) nyumba yosamaliridwa bwino, yokhala ndi maluwa; (2) nyumba ya banja limene lili ndi ana aang’ono; (3) nyumba yauve kunja ndi mkati momwe komanso (4) nyumba ya anthu achipembedzo. Kodi ndi nyumba iti imene mungapeze munthu yemwe angadzakhale wophunzira?