Nkhani Yophunzira 16

Tizimvetsera Anthu, Kuwadziwa Komanso Kuwachitira Chifundo

Tizimvetsera Anthu, Kuwadziwa Komanso Kuwachitira Chifundo

“Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”​—YOH. 7:24.

NYIMBO NA. 101 Tizigwira Ntchito Mogwirizana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Baibulo limanena mfundo yolimbikitsa iti yokhudza Yehova?

KODI mungakonde kuti munthu akuweruzeni potengera khungu lanu, nkhope yanu kapena thupi lanu? N’zosachita kufunsa kuti simungakonde zimenezi. Choncho n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova satiweruza potengera zimene anthu amaona. Mwachitsanzo, pamene Samueli ankayang’ana ana a Jese sankaona zimene Yehova ankaona. Yehova anauza Samueli kuti mwana wina wa Jese adzakhala mfumu ya Aisiraeli. Koma kodi anali mwana uti? Samueli ataona mwana wamkulu wa Jese dzina lake Eliyabu ananena kuti: “Mosakayikira wodzozedwa wake waonekera pamaso pa Yehova.” Eliyabu ankaoneka wolemekezeka ngati mfumu. “Koma Yehova anauza Samueli kuti: ‘Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake, pakuti ine ndamukana ameneyu.’” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova ananenanso kuti: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”​—1 Sam. 16:1, 6, 7.

2. Malinga ndi Yohane 7:24, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruza munthu potengera maonekedwe ake? Perekani chitsanzo.

2 Anthufe timakonda kuweruza anthu ena potengera maonekedwe awo. (Werengani Yohane 7:24.) Koma zimene timaona ndi maso athu sizingatithandize kudziwa zambiri zokhudza munthu. Mwachitsanzo, ngakhale dokotala wanzeru kwambiri sangadziwe zambiri akangoona wodwala. Iye ayenera kumvetsera mwatcheru zimene munthuyo angafotokoze zokhudza matenda amene anadwalapo kale, mmene maganizo ake alili komanso mmene akumvera m’thupi. Mwina dokotalayo akhoza kupempha kuti munthuyo akajambulidwe kuti aone mkati mwa thupi lake. Kupanda kutero, akhoza kumupatsa mankhwala olakwika. N’chimodzimodzinso ndi ifeyo. Sitingadziwe bwino abale ndi alongo athu pongoona mmene amaonekera. Tiyenera kuyesetsa kudziwa mmene alili. N’zoona kuti sitingaone zamumtima mwa munthu choncho sitingadziwe anthu mmene Yehova amawadziwira. Koma n’zotheka kuchita zonse zimene tingathe pomutsanzira. Kodi tingamutsanzire bwanji?

3. Kodi nkhani za m’Baibulo zimene tikambirane zitithandiza bwanji kutsanzira Yehova?

3 Kodi Yehova amachita bwanji zinthu ndi atumiki ake? Iye amawamvetsera, amaganizira mmene moyo wawo ulili komanso amawachitira chifundo. Tikambirana mmene Yehova anachitira zimenezi ndi Yona, Eliya, Hagara ndi Loti. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizitsanzira Yehova pochita zinthu ndi abale ndi alongo athu.

TIZIMVETSERA MWATCHERU

4. N’chifukwa chiyani tingakhale ndi maganizo olakwika okhudza Yona?

4 Popeza sitikudziwa zonse zokhudza Yona, tikhoza kuganiza kuti anali wosadalirika kapenanso wosakhulupirika. Iye analamulidwa ndi Yehova kuti akalalikire uthenga wachiweruzo ku Nineve. Koma m’malo momvera, ‘anathawa Yehova’ n’kukwera chombo chopita kutali ndi Nineve.’ (Yona 1:1-3) Mukanakhala inuyo, kodi mukanamupatsa Yona mwayi wina woti achite zimene munamuuzazo? Mwina ayi. Koma Yehova anaona kuti ndi woyenera kumupatsa mwayi wina.​—Yona 3:1, 2.

5. Kodi inuyo mukuphunzira chiyani za Yona pa mawu ake a pa Yona 2:1, 2, 9?

5 Yona anasonyeza mmene analili mu pemphero lina limene anapereka. (Werengani Yona 2:1, 2, 9.) N’zosakayikitsa kuti anapereka mapemphero ambirimbiri, koma pemphero limeneli limatithandiza kuti tisamangomuona kuti ndi munthu amene anathawa ntchito. Mawu am’pempheroli amasonyeza kuti anali wodzichepetsa, woyamikira komanso wofunitsitsa kumvera Yehova. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yehova sanangoona zomwe Yona analakwitsa, koma anayankha pemphero lake n’kupitiriza kumugwiritsa ntchito monga mneneri.

Kudziwa nkhani yonse kungatithandize kukhala achifundo (Onani ndime 6) *

6. N’chifukwa chiyani kumvetsera mwatcheru n’kofunika?

6 Kuti tizimvetsera anthu mwatcheru, tiyenera kukhala odzichepetsa komanso oleza mtima. Pali zifukwa zitatu zochitira zimenezi. Choyamba, zidzatithandiza kuti tisamaweruze anthu molakwika. Chachiwiri, tidzadziwa mmene m’bale kapena mlongo wathu akumvera komanso zolinga zake. Ndipo zimenezi zingatithandize kuti timumvetse n’kumuchitira chifundo. Chachitatu, tikhoza kumuthandiza kuti amvetse mmene akumvera mumtima mwake. Nthawi zina munthu amamvetsa mmene akumvera mumtima mwake pokhapokha atafotokoza maganizo ake kwa munthu wina. (Miy. 20:5) Mkulu wina wa ku Asia anati: “Nthawi ina ndinapupuluma, n’kulankhula ndisanamvetsere. Ndinauza mlongo wina kuti ayenera kuyesetsa kuti ndemanga zake zizikhala zogwira mtima. Kenako ndinazindikira kuti amavutika kuwerenga moti si zapafupi kuti ayankhe.” Zimenezi zikusonyeza kuti akulu amafunika kuti ‘azimvetsetsa’ nkhani yonse asanapereke malangizo.​—Miy. 18:13.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachita ndi Eliya?

7 Abale ndi alongo athu ena amavutika kufotokoza maganizo awo chifukwa cha chikhalidwe chawo, mmene anakulira kapena mmene alili panopa. Kodi tingawathandize bwanji kuti azimasuka n’kumatifotozera mmene akumvera? Tizikumbukira zimene Yehova anachita ndi Eliya pamene ankathawa Yezebeli. Panadutsa masiku ambiri Eliya asanafotokozere Yehova zonse zamumtima mwake. Yehova anamvetsera mwatcheru. Kenako analimbikitsa Eliya n’kumupatsa ntchito ina yofunika. (1 Maf. 19:1-18) Zingatengenso nthawi kuti abale ndi alongo athu azimasuka nafe, koma akamatifotokozera maganizo awo m’pamene tingayambe kuwamvetsa. Tikamatsanzira Yehova pokhala oleza mtima, anthu akhoza kuyamba kumasuka nafe. Ndiyeno akayamba kutifotokozera maganizo awo, tizimvetsera mwatcheru.

MUZIYESETSA KUDZIWA BWINO ABALE NDI ALONGO

8. Malinga ndi Genesis 16:7-13, kodi Yehova anathandiza bwanji Hagara?

8 Hagara, yemwe anali wantchito wa Sarai, anachita zinthu mopusa ataloledwa kuti akhale mkazi wa Abulamu. Iye atakhala woyembekezera anayamba kunyoza Sarai chifukwa choti analibe mwana. Zinthu zinafika poipa kwambiri moti Sarai anayamba kumuzunza ndipo anathawa. (Gen. 16:4-6) Popeza si ife angwiro, tikhoza kuganiza kuti Hagara anali wamwano ndipo m’pake kuti ankamuzunza. Koma umu si mmene Yehova ankamuonera. Iye anatumiza mngelo amene anathandiza Hagara kuti asinthe maganizo ake ndipo kenako anamudalitsa. Hagara anazindikira kuti Yehova ankaona zonse zimene zinkamuchitikira. Iye anafika ponena kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.” Ananenanso kuti Mulungu amamuona iyeyo.​—Werengani Genesis 16:7-13.

9. Kodi Mulungu ankaganizira zinthu ziti zokhudza Hagara?

9 Kodi ndi zinthu ziti zokhudza Hagara zimene Yehova ankadziwa? Iye ankadziwa mmene anakulira komanso zimene anakumana nazo pa moyo wake. (Miy. 15:3) Hagara anali wa ku Iguputo koma ankakhala m’banja la Chiheberi. Kodi mwina ankadziona kuti ndi mlendo? Nanga ankasowa achibale ake n’kumalakalaka atabwerera kwawo? Iye analinso m’banja la mitala. Paja kwa nthawi ndithu atumiki a Yehova ena ankakhala ndi akazi angapo ngakhale kuti si zimene Yehova ankafuna poyambirira. (Mat. 19:4-6) M’pake kuti zinkachititsa anthu kuyamba nsanje komanso kudana. Yehova sanasangalale ndi chipongwe cha Hagara koma ayenera kuti ankaganiziranso mmene zinthu zinalili pa moyo wake.

Yesetsani kudziwa bwino abale ndi alongo (Onani ndime 10-12) *

10. Kodi tingatani kuti tiwadziwe bwino abale ndi alongo athu?

10 Nafenso tiyenera kutsanzira Yehova poyesetsa kuwamvetsa anzathu. Tiziyesetsa kuti tiwadziwe bwino abale ndi alongo athu. Tizicheza nawo misonkhano isanayambe komanso ikatha, tiziyenda nawo mu utumiki ndipo ngati n’kotheka, tiziwaitanira chakudya. Mukatero mwina mudzadabwa kuona kuti mlongo amene amaoneka ngati wosachezeka ali ndi vuto la manyazi, m’bale amene amaoneka ngati wokonda ndalama ali ndi mtima wochereza kapena banja limene limachedwa kumisonkhano limatsutsidwa. (Yobu 6:29) N’zoona kuti tiyenera kupewa ‘kulowerera nkhani za eni.’ (1 Tim. 5:13) Koma ndi bwino kudziwa zinthu zina zokhudza abale ndi alongo athu komanso zimene akumana nazo pa moyo wawo.

11. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kudziwa bwino abale ndi alongo?

11 Akulu makamaka ndi amene ayenera kudziwa zimene abale ndi alongo akumana nazo pa moyo wawo. Chitsanzo ndi m’bale Artur, yemwe anali woyang’anira dera. Iye limodzi ndi mkulu wina anapita kukaona mlongo wina amene ankaoneka wamanyazi komanso womangika. Artur anati: “Tinamva kuti mwamuna wake anamwalira atangokwatirana kumene. Koma ngakhale zinali choncho, iye analera bwino ana ake awiri m’choonadi. Pamene tinkacheza naye anali ndi vuto la maso komanso matenda amaganizo. Koma ankakonda Yehova komanso kumukhulupirira kwambiri. Tinazindikira kuti pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire kwa mlongoyu.” (Afil. 2:3) Apatu tingati woyang’anira derayu ankatsanzira Yehova. Yehova amadziwa nkhosa zake komanso mavuto amene zikukumana nawo. (Eks. 3:7) Akulu amene amadziwa bwino abale ndi alongo sangavutike kuwathandiza.

12. Kodi kudziwa bwino mlongo wina mumpingo kunathandiza bwanji Yip Yee?

12 Mukamudziwa bwino Mkhristu amene sakusangalatsani mukhoza kuyamba kumuchitira chifundo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Yip Yee, yemwe amakhala ku Asia. Iye anati: “Mlongo wina mumpingo wathu amakonda kulankhula mokweza kwambiri. Ndinkaganiza kuti ndi wopanda ulemu. Koma nditayenda naye mu utumiki ndinamva kuti ankathandiza makolo ake kugulitsa nsomba mumsika. Choncho ankafunika kulankhula mokweza poitanira malondawo.” Yip Yee ananenanso kuti: “Ndinazindikira kuti ndiyenera kudziwa zimene anthu akumana nazo pa moyo wawo kuti ndiziwamvetsa bwino.” Pamafunika khama kuti tiwadziwe bwino abale ndi alongo athu. Koma tikamatsatira malangizo a m’Baibulo akuti tifutukule mitima yathu timatsanzira Yehova amene amakonda anthu “kaya akhale a mtundu wotani.”​—1 Tim. 2:3, 4; 2 Akor. 6:11-13.

MUZICHITIRA CHIFUNDO ANTHU

13. Malinga ndi Genesis 19:15, 16, kodi angelo anachita chiyani pamene Loti ankazengereza kuchoka? Perekani chifukwa.

13 Pa nthawi ina yovuta kwambiri, Loti ankazengereza kutsatira malangizo a Yehova. Angelo awiri anafika n’kumuuza kuti iye ndi banja lake achoke mu Sodomu. N’chifukwa chiyani anamuuza zimenezi? Iwo anati: “Malo ano tiwawononga.” (Gen. 19:12, 13) Tsiku lotsatira, Loti ndi banja lake anali asanachokebe. Choncho angelo anamuchenjezanso koma Loti ‘ankazengerezabe.’ Mwina tingaone kuti Loti anali wamphwayi kapenanso wosamvera. Koma Yehova sanasiye kumuthandiza. Baibulo limati: “Mwa chifundo cha Yehova pa iye, anagwira dzanja iyeyo, mkazi wake, ndi ana ake aakazi awiriwo, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.”​—Werengani Genesis 19:15, 16.

14. Kodi mwina n’chifukwa chiyani Yehova anachitira chifundo Loti?

14 N’kutheka kuti panali zifukwa zambiri zochititsa Yehova kuti achitire chifundo Loti. Mwina Loti ankazengereza kuchoka chifukwa choopa anthu okhala kunja kwa mzindawo. Koma panali zinthu zinanso zoopsa. Loti ayenera kuti ankadziwa za mafumu amene anagwera m’maenje aphula omwe anali m’chigwa chapafupi ndi mzindawo. (Gen. 14:8-12) N’zosachita kufunsa kuti Loti ankadera nkhawa mkazi wake komanso ana ake. Kuwonjezera pamenepa, Loti anali wachuma choncho n’kutheka kuti anali ndi nyumba yapamwamba ku Sodomu. (Gen. 13:5, 6) N’zoona kuti zimenezi sizinali zifukwa zomveka zoti Loti alephere kumvera Yehova mwamsanga. Koma Yehova sanaganizire kwambiri zimene Loti analakwitsa ndipo ankamuonabe kuti ndi “munthu wolungama.”​—2 Pet. 2:7, 8.

Tikamamvetsera anthu, tikhoza kudziwa mmene tingawasonyezere chifundo (Onani ndime 15-16) *

15. M’malo moweruza munthu, kodi tiyenera kuchita chiyani?

15 M’malo moweruza msanga zolinga za munthu, tiyenera kuyesetsa kumumvetsa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Europe dzina lake Veronica. Iye anati: “Mlongo wina ankakhala wosasangalala nthawi zonse ndipo sankakonda kucheza ndi anthu ena. Nthawi zina ndinkaopa kumulankhula. Koma ndinaganiza kuti, ‘Ndikanakhala ineyo ndikanafuna munthu woti ndizicheza naye.’ Choncho ndinasankha zomufunsa mmene akumvera. Ndipo anayamba kundiuza zamumtima mwake. Panopa ndimamumvetsa.”

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha Yehova kuti azitithandiza kukhala achifundo?

16 Yehova yekha ndi amene amatimvetsa bwino. (Miy. 15:11) Choncho tizimupempha kuti azitithandiza kuona anthu ena mmene iye amawaonera komanso kudziwa mmene tingawachitire chifundo. Kupemphera kunathandiza mlongo wina dzina lake Anzhela kuti azichitira chifundo anthu ena. Mlongo wina wamumpingo wawo anayamba kuvuta kwambiri. Anzhela ananena kuti: “Zikanakhala zosavuta kuti ndingosiya kulankhula naye n’kumamupewa. Koma kenako ndinapempha Yehova kuti andithandize kumumvetsa mlongoyo.” Kodi Yehova anayankha pemphero lake? Anzhela anati: “Ndinayenda mu utumiki ndi mlongoyo ndipo titaweruka tinacheza kwa nthawi yaitali. Ndinamumvetsera mwachifundo pamene ankandiuza mmene akumvera. Panopa ndimamukonda kwambiri ndipo ndikufunitsitsa kumuthandiza.”

17. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

17 Sitingasankhe kuti abale ndi alongo awa tiziwachitira chifundo, awa ayi. Chifukwa onse amakumana ndi mavuto ngati mmene zinalili ndi Yona, Eliya, Hagara ndi Loti. Ndi zoona kuti nthawi zina angadzibweretsere okha mavutowo. Koma kunena zoona, ifenso tinachitapo zimenezi nthawi ina. Choncho m’pomveka kuti Yehova amafuna kuti tizichitirana chifundo. (1 Pet. 3:8) Tikamamvera Yehova, timathandiza kuti banja lathu lapadziko lonse likhale logwirizana. Choncho tiyeni tonse tiziyesetsa kumvetsera mwatcheru, kuwadziwa bwino anthu komanso kuwachitira chifundo.

NYIMBO NA. 87 Bwerani Mudzasangalale

^ ndime 5 Anthufe si angwiro ndipo timafulumira kuweruza anthu ena komanso zolinga zawo. Koma Yehova “amaona mmene mtima ulili.” (1 Sam. 16:7) Munkhaniyi tikambirana zimene Yehova anachita pothandiza Yona, Eliya, Hagara komanso Loti. Zimenezi zitithandiza kuti tizimutsanzira pochita zinthu ndi abale ndi alongo athu.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: M’bale wachikulire sakusangalala ataona m’bale wina wachinyamata akufika mochedwa pamisonkhano koma kenako akuzindikira kuti wachedwa chifukwa cha ngozi ya galimoto.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Poyamba woyang’anira kagulu ka utumiki ankaganiza kuti mlongo wina sakonda kucheza ndi ena koma kenako anamva kuti mlongoyo ndi wamanyazi ndipo amavutika kumasuka ndi anthu amene sawadziwa bwino.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo atayamba kudziwa bwino mlongo wina anazindikira kuti mlongoyo si wovuta ngati mmene ankaganizira atangokumana naye ku Nyumba ya Ufumu.