Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 14

Kuukila kwa Mdani Wocokela Kumpoto!

Kuukila kwa Mdani Wocokela Kumpoto!

Pali mtundu umene walowa m’dziko langa.”​—YOWELI 1:6.

NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi M’bale Russell na anzake anali kutsatila njila yotani pophunzila Baibo? Nanga n’cifukwa ciani inali yothandiza?

ZAKA zoposa 100 zapitazo, M’bale C. T. Russell na kagulu kocepa ka ophunzila Baibo anzake, anayamba kukumana pamodzi. Colinga cawo cinali kuphunzila kuti adziŵe zeni-zeni zimene Baibo imaphunzitsa ponena za Yehova Mulungu, Yesu Khristu, dipo, komanso mkhalidwe wa anthu akufa. Njila imene anali kutsatila pophunzila inali yosavuta. Wina anali kufunsa funso. Ndiyeno, onse pamodzi anali kuŵelenga mosamala lemba lililonse la m’Baibo logwilizana na nkhani imene wafunsayo. Pamapeto pake, anali kulemba mfundo zimene apeza. Mwa dalitso la Yehova, abale akhama amenewa anakwanitsa kumvetsetsa mfundo zoculuka komanso zofunika kwambili za coonadi ca m’Baibo, zimene n’zofunikabe kwa ife masiku ano.

2. N’ciani cingapangitse kuti kamvedwe kathu ka ulosi wa m’Baibo kakhale kolakwika?

2 Koma posapita nthawi, ophunzila Baibo anazindikila kuti kumvetsetsa maulosi a m’Baibo n’kovuta kusiyana na kumvetsetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa cimodzi n’cakuti maulosi a m’Baibo nthawi zambili timawamvetsetsa bwino pamene akukwanilitsidwa, kapena pambuyo pakuti akwanilitsidwa. Koma palinso cifukwa cina. Kuti timvetsetse bwino ulosi, nthawi zambili timafunika kupenda mosamala mbali zonse za ulosiwo. Ngati tipenda cabe mbali imodzi, kamvedwe kathu ka ulosiwo kangakhale kolakwika. Cioneka kuti izi n’zimene zinacitika popenda ulosi winawake wa m’buku la Yoweli. Tiyeni lomba tipendenso mosamala ulosi umenewo na kukambilana cifukwa cake tiyenela kusintha kamvedwe kathu.

3-4. Kodi takhala tikukhulupilila zotani zokhudza ulosi wa pa Yoweli 2:7-9?

3 Ŵelengani Yoweli 2:7-9. Yoweli anakambilatu kuti mlili wa dzombe udzawononga dziko la Isiraeli. Anakamba kuti dzombe lanjala, lokhala na mano komanso nsagwada monga za mikango, lidzadya comela ciliconse m’dzikolo! (Yow. 1:4, 6) Kwa zaka zambili, takhala tikukhulupilila kuti ulosiwu ni wophiphilitsila, ndipo umakamba za atumiki a Yehova amene akupitiliza kugwila nchito yolalikila monga gulu la dzombe limene palibe angaliletse. Tinali kukhulupilila kuti nchitoyi imasautsa ‘dziko,’ kapena kuti anthu amene amatsogoleledwa na atsogoleli a zipembedzo. *

4 Tikaŵelenga cabe Yoweli 2:7-9, tingaone monga kamvedwe kathu kali bwino-bwino. Koma tikaŵelenga mosamala mbali zonse za ulosiwu, tiona kuti m’poyenela kusintha kamvedwe kathu. Tiyeni lomba tikambilane zifukwa zinayi zimene tiyenela kusinthila.

ZIFUKWA ZINAYI ZOSINTHILA KAMVEDWE KATHU

5-6. Ni funso liti limene tingafunse pamene tiŵelenga mosamala lemba la: (a) Yoweli 2:20? (b) Yoweli 2:25?

5 Coyamba, onani zimene Yehova analonjeza ponena za mlili wa dzombe. Iye anati: “Ndidzakucotselani mdani wa kumpoto [dzombe] kuti akhale kutali ndi inu.” (Yow. 2:20) Ngati dzombe liimila Mboni za Yehova zimene zimagwila nchito yolalikila na kupanga ophunzila pomvela lamulo la Yesu, n’cifukwa ciani Yehova analonjeza kuti adzalicotsa? (Ezek. 33:7-9; Mat. 28:19, 20) Izi zionetselatu kuti dzombe limene Yehova akulicotsa siliimila atumiki ake okhulupilika. Koma liimila cinacake kapena winawake amene amazunza anthu ake.

6 Cifukwa caciŵili cili m’mawu a pa Yoweli 2:25. Pa vesiyi, Yehova anati: “Ndidzakubwezelani mbewu za zaka zonse zimene dzombe ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko, mphemvu ndi mbozi zinadya. Limeneli ndi gulu langa lankhondo lamphamvu limene ndinatumiza pakati panu.” Onani kuti Yehova analonjeza kuti ‘adzabwezela’ zinthu zimene dzombe linawononga. Ngati dzombe liimila atumiki olengeza Ufumu, kodi izi sizingatanthauze kuti uthenga umene amalengeza ni wowononga? Koma zoona zake n’zakuti uthengawo ni wopulumutsa moyo, ndipo umasonkhezela anthu ena oipa kuti alape. (Ezek. 33:8, 19) Ndithudi, kusintha kumeneku ni dalitso kwa iwo.

7. Kodi mawu a pa Yoweli 2:28, 29 akuti, “zimenezi zikadzacitika,” atithandiza kumvetsetsa mfundo iti?

7 Ŵelengani Yoweli 2:28, 29. Cifukwa cacitatu cikhudza mmene zocitika za mu ulosiwu zinacitikila. Onani kuti Yehova anati: “Zimenezi zikadzacitika,” kutanthauza kuti dzombelo likadzatsiliza nchito yake, “ndidzatsanulila mzimu wanga pa camoyo ciliconse.” Izi zionetsa kuti dzombe siliimila alengezi a Ufumu, cifukwa ngati liimila alengezi a Ufumu, Yehova angatsanulile bwanji mzimu wake pa iwo pambuyo pakuti atsiliza kugwila nchito yawo yolalikila? Zoona zake n’zakuti popanda thandizo la mzimu woyela wamphamvu wa Mulungu, iwo sakanakwanitsa kugwila nchitoyi kwa zaka zambili, cifukwa pakhala zitsutso na ziletso zambili.

M’bale J. F. Rutherford na atumiki ena odzozedwa amene anakhala patsogolo polengeza molimba mtima uthenga waciweluzo wa Mulungu kwa anthu a m’dziko loipali (Onani ndime 8)

8. Kodi dzombe lochulidwa pa Chivumbulutso 9:1-11 likuimila ndani? (Onani cithunzi ca pa cikuto.)

8 Ŵelengani Chivumbulutso 9:1-11. Tsopano tiyeni tikambilane cifukwa cacinayi. Tinali kukhulupilila kuti mlili wa dzombe wa m’buku la Yoweli umaimila nchito yathu yolalikila, cifukwa ulosiwu umafananako na ulosi wa dzombe wa m’buku la Chivumbulutso. Ulosi wa m’buku la Chivumbulutso umakamba za gulu la dzombe lokhala na nkhope za anthu, ndiponso “zisoti zagolide zooneka ngati zacifumu” pamitu pawo. (Chiv. 9:7) Dzombelo likuzunza “anthu okhawo [adani a Mulungu] amene alibe cidindo ca Mulungu pamphumi pawo” kwa miyezi 5. Nthawi imeneyi ikufanana ndi nthawi imene dzombe limakhala na moyo. (Chiv. 9:4, 5) N’zonekelatu kuti ulosi umenewu ukamba za atumiki odzozedwa a Yehova. Iwo amalengeza uthenga waciweluzo wa Mulungu molimba mtima kwa anthu a m’dziko loipali, ndipo zotulukapo zake n’zakuti anthuwo amazunzika kwambili na uthengawo.

9. Kodi dzombe limene Yoweli anaona m’masomphenya lisiyana bwanji na dzombe limene Yohane anaona?

9 Ngakhale kuti mbali zina za ulosi wa m’buku la Chivumbulutso zikufanana ndi za ulosi wa m’buku la Yoweli, pali mbali zina zosiyana kwambili. Mwacitsanzo, ganizilani izi: Mu ulosi wa Yoweli, dzombe linawononga zomela. (Yow. 1:4, 6, 7) Koma m’masomphenya a Yohane m’buku la Chivumbulutso, dzombe “linauzidwa kuti lisawononge zomela za padziko lapansi.” (Chiv. 9:4) Cinanso, dzombe limene Yoweli anaona linacokela kumpoto. (Yow. 2:20) Koma limene Yohane anaona linatuluka m’phompho. (Chiv. 9:2, 3) Kuwonjezela apo, dzombe lochulidwa m’buku la Yoweli linacotsedwa kapena kuti kuthamangitsidwa. Koma lochulidwa m’buku la Chivumbulutso silinathamangitsidwe. M’malomwake, linaloledwa kutsiliza nchito imene linapatsidwa. Ndipo palibe ciliconse cimene cionetsa kuti Yehova sanakondwele nalo dzombelo.—Onani bokosi yakuti “ Maulosi a Dzombe—Ofananako Koma Osiyana.”

10. Fotokozani citsanzo ca m’Malemba coonetsa kuti nthawi zina cinthu cimodzi cophiphilitsila cimakhala na matanthauzo osiyana malinga na nkhani yake.

10 Monga taonela, pali mbali zina zosiyana kwambili pakati pa maulosi aŵiliwa. Izi zionetsa kuti maulosiwa ali na matanthauzo osiyana. Kodi apa titanthauza kuti dzombe lochulidwa m’buku la Yoweli n’losiyana na dzombe la m’buku la Chivumbulutso? Inde. M’Baibo, nthawi zina cinthu cimodzi cophiphilitsila cimakhala na matanthauzo osiyana malinga na nkhani yake. Mwacitsanzo, pa Chivumbulutso 5:5, Yesu akuchulidwa kuti ni “mkango wa fuko la Yuda,” koma pa 1 Petulo 5:8, Mdyelekezi akuchulidwa kuti ni “mkango wobangula.” Pa zifukwa zinayi zimene takambilana, komanso mafunso amene akubuka, tiyenela kusintha kamvedwe kathu ka ulosi wa Yoweli. Kodi ulosiwu utanthauza ciani?

KODI ULOSIWU UTANTHAUZA CIANI?

11. Kodi malemba awa, Yoweli 1:6 komanso 2:1, 8, 11, amatithandiza bwanji kudziŵa cimene dzombe limaimila?

11 Tikaŵelenga mosamala mavesi ena mu ulosi wa Yoweli, tipeza kuti mneneliyu anali kulosela za kuukila kwa gulu la asilikali. (Yow. 1:6; 2:1, 8, 11) Yehova anakamba kuti adzaseŵenzetsa ‘gulu lake lankhondo lamphamvu’ (asilikali a Babulo) popeleka cilango kwa Aisiraeli osamvela. (Yow. 2:25) M’pake kuti gulu limeneli la asilikali oukila likuchedwa “mdani wa kumpoto,” cifukwa asilikali a Babulo anali kudzaukila Aisiraeli kucokela kumpoto. (Yow. 2:20) Gulu la asilikali limeneli likuyelekezeledwa na gulu la dzombe locita zinthu mwadongosolo. Pokamba za asilikaliwo, Yoweli anati: “[Msilikali aliyense] wamphamvu . . . akuyenda panjila yake. . . . Iwo amathamangila m’mizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda. Amakwela nyumba ndipo amalowa m’nyumbamo kudzela pawindo ngati mbala.” (Yow. 2:8, 9) Yelekezelani kuti mukuona mmene zinthu zinalili pa nthawiyo! Asilikali ali pali ponse. Palibe pamene munthu angabisale. Palibe amene angapulumuke ku lupanga la asilikali a Babulo.

12. Kodi ulosi wa Yoweli wokamba za dzombe unakwanilitsidwa bwanji?

12 Monga dzombe, Ababulo (kapena kuti Akasidi) anaukila mzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E. Baibo imati: “Mfumu ya Akasidi yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga . . . , sinacitile cisoni mnyamata kapena namwali, wacikulile kapena nkhalamba yothelatu. Mulungu anapeleka zonse m’manja mwake. Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona ndi kugwetsa mpanda wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambili za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino, mpaka zonse zinawonongedwa.” (2 Mbiri 36:17, 19) Asilikali a Babulo atatsiliza kuwononga dzikolo, anthu oona anali kungokamba kuti: “Dziko ili ndi bwinja, lopanda munthu wokhalamo kapena nyama yoweta. Linapelekedwa m’manja mwa Akasidi.”—Yer. 32:43.

13. Fotokozani zimene Yeremiya 16:16, 18 imatanthauza.

13 Patapita zaka 200 kucokela pamene ulosi wa Yoweli unapelekedwa, Yehova anaseŵenzetsa Yeremiya kulosela zinazake zokhudza kuukila kumeneku. Anakamba kuti asilikali oukila adzasakila Aisiraeli ocita zoipa kulikonse kumene ali, ndipo onse adzawagwila. “‘Inetu ndikuitana asodzi ambili,’ watelo Yehova, ‘ndipo adzawawedza. Kenako ndidzaitana anthu ambili osaka nyama, ndipo adzawasaka m’phili lililonse, pacitunda ciliconse, ndi m’mapanga a m’matanthwe. . . . Ndidzawabwezela zolakwa zawo zonse ndi macimo awo onse.’” Aisiraeli osalapa analibiletu poti n’kuthaŵila—kaya ni m’nyanja kapena m’nkhalango, kulikonse asilikali a Babulo akanawapeza.—Yer. 16:16, 18.

KUBWEZELETSA ZINTHU

14. Kodi ulosi wa pa Yoweli 2:28, 29 unakwanilitsidwa liti?

14 Pambuyo pake, Yoweli analengeza uthenga wabwino wobwezeletsa zinthu. Anakamba kuti m’dziko la Isiraeli mudzakhalanso zakudya zambili. (Yow. 2:23-26) Anakambanso kuti panthawi ina m’tsogolo, mudzakhala cakudya cauzimu coculuka. Yehova anati: “Ndidzatsanulila mzimu wanga pa camoyo ciliconse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenela . . . Ndidzatsanulilanso mzimu wanga pa anchito anu aamuna ndi aakazi.” (Yow. 2:28, 29) Mulungu sanatsanulile mzimu wake pa Aisiraeli atangobwelela ku dziko lawo kucoka ku Babulo. Koma izi zinacitika pa Pentekosite wa mu 33 C.E., apo n’kuti papita zaka zambili. Kodi tidziŵa bwanji zimenezi?

15. Malinga na Machitidwe 2:16, 17, ni mawu ati opezeka pa Yoweli 2:28 amene Petulo anawasinthako? Nanga zimenezi zionetsa ciani?

15 Mouzilidwa na Mulungu, mtumwi Petulo anakamba kuti zinthu zapadela zimene zinacitika pa tsikulo la Pentekosite zinakwanilitsa ulosi wa pa Yoweli 2:28, 29. Pa tsikulo, ca m’ma 9 awazi, mzimu woyela unatsanulidwa mozizwitsa pa anthu amene anasonkhana, moti anayamba kulankhula “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:11) Mouzilidwa, Petulo anasinthako mawu ena pogwila mawu a ulosi wa Yoweli. Kodi mwawaona mawu amene anawasinthako? (Ŵelengani Machitidwe 2:16, 17.) M’malo moyamba na mawu akuti “zimenezi zikadzacitika,” Petulo anati: “Ndipo m’masiku otsiliza,” mzimu wa Mulungu udzatsanulidwa “pa anthu osiyanasiyana.” Pa lembali, Petulo anali kukamba za masiku otsiliza, Yerusalemu na kacisi wake atatsala pang’ono kuwonongedwa. Izi zionetsa kuti panapita nthawi yaitali kuti ulosi umenewu wa Yoweli ukwanilitsidwe.

16. M’nthawi ya atumwi, kodi mzimu wa Mulungu unathandiza bwanji pa nchito yolalikila? Nanga masiku ano umathandiza bwanji?

16 Mulungu atatsanulila mzimu wake pa Akhristu a m’nthawi ya atumwi, nchito yolalikila inapita patsogolo kwambili moti m’kupita kwa nthawi uthenga wabwino unalengezedwa padziko lonse. Panthawi imene mtumwi Paulo anali kulembela kalata Akhristu a ku Kolose ca m’ma 61 C.E., anafotokoza kuti uthenga wabwino unafalikila kwambili cakuti unali utalalikidwa “m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Pamene Paulo anakamba kuti “m’cilengedwe conse,” anatanthauza madela amene iye na Akhristu ena anatha kufikako polalikila. Mothandizidwa na mphamvu ya mzimu woyela wa Yehova, nchito yolalikila yakula kwambili masiku ano—yafika “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi”!—Mac. 13:47; onani bokosi yakuti “ Ndidzatsanulila Mzimu Wanga” pa Atumiki Anga.

KODI N’CIANI CASINTHA?

17. Kodi kamvedwe kathu ka ulosi wa Yoweli wa dzombe kasintha motani?

17 Kodi n’ciani casintha? Tsopano tili na kamvedwe kolondola ka ulosi wa pa Yoweli 2:7-9. Kunena mwacidule, mavesi amenewa sakamba za nchito yathu yolalikila imene timaigwila mwakhama. Koma afotokoza zimene gulu la asilikali a Babulo linacita poukila mzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E.

18. N’ciani cimene sicinasinthe cokhudza atumiki a Yehova?

18 Kodi n’ciani cimene sicinasinthe? Atumiki a Yehova akupitiliza kulalikila uthenga wabwino kulikonse, ndipo akucita zimenezi poseŵenzetsa njila zosiyana-siyana za ulaliki. (Mat. 24:14) Palibe ciletso ciliconse ca boma cimene cingatilepheletse kugwilia nchito yolalikila imene tinapatsidwa. Ndipo mothandizidwa na Yehova, tikugwila nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu mokangalika ndiponso molimba mtima kuposa kale lonse! Komanso, modzicepetsa timadalilabe Yehova kuti azitithandiza kumvetsetsa maulosi a m’Baibo. Ndipo sitikayika konse kuti panthawi yake yoyenela, iye adzatithandiza kumvetsetsa ‘coonadi conse’!—Yoh. 16:13.

NYIMBO 97 Moyo Umadalila Mau a Mulungu

^ ndime 5 Kwa zaka zambili, takhala tikukhulupilila kuti ulosi wa m’macaputa 1 na 2 a buku la Yoweli, umakamba za nchito yolalikila imene tikugwila masiku ano. Koma pali zifukwa zinayi zomveka bwino zimene zionetsa kuti tifunika kusintha kamvedwe kathu ka ulosi wa m’macaputa amenewa a buku la Yoweli. Kodi zifukwa zimenezo n’ziti?

^ ndime 3 Mwacitsanzo, onani nkhani yakuti, “Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova,” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2009, ndime 14-16.