Nkhani Yophunzira 14

Gulu Lankhondo Lochokera Kumpoto

Gulu Lankhondo Lochokera Kumpoto

“Pali mtundu umene walowa m’dziko langa.”—YOW. 1:6.

NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi M’bale Russell ndi anzake ankatsatira njira iti pophunzira Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani inali yothandiza?

ZAKA zoposa 100 zapitazo, M’bale C. T. Russell ndi anzake anapanga kagulu komwe kankasonkhana kuti kaphunzire Baibulo. Iwo ankafuna kupeza zoona zokhudza Yehova Mulungu, Yesu Khristu, zimene zimachitika munthu akamwalira komanso dipo. Njira imene ankatsatira pophunzira inali yosavuta. Munthu wina ankafunsa funso ndipo gululo linkafufuza mavesi onse onena za nkhani imeneyo. Kenako ankalemba zimene apeza. Yehova ankawadalitsa ndipo Akhristuwo anatulukira mfundo zambiri za m’Baibulo zomwe ndi zoona ndipo timaziona kuti ndi zofunika mpaka pano.

2. N’chiyani chingachititse kuti tisamvetse bwino tanthauzo la ulosi wina wa m’Baibulo?

2 Koma ophunzira Baibulowo anaona kuti kuphunzira zimene Baibulo limanena pa nkhani inayake kumakhala kosavuta kusiyana ndi kuzindikira tanthauzo lenileni la ulosi wa m’Baibulo. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chimodzi n’chakuti nthawi zambiri tanthauzo la ulosi wa m’Baibulo limaoneka pamene ulosiwu ukukwaniritsidwa kapena utakwaniritsidwa kale. Koma pali chifukwa china. Kuti timvetse bwino ulosi winawake, tiyenera kuganizira mbali zonse za ulosiwo. Tikangoganizira mbali imodzi mwina sitingamvetse bwino tanthauzo lake. Zikuoneka kuti umu ndi mmene zilili ndi ulosi wina wa m’buku la Yoweli. Tiyeni tikambirane ulosi umenewu kuti tione chifukwa chake tiyenera kusintha kafotokozedwe kake.

3-4. Kodi takhala tikufotokoza bwanji ulosi wa pa Yoweli 2:7-9?

3 Werengani Yoweli 2:7-9. Yoweli analosera kuti dzombe lidzasakaza dziko la Isiraeli. Ananena kuti dzombeli ndi la mano komanso nsagwada ngati za mikango ndipo lidzadya chomera chilichonse. (Yow. 1:4, 6) Kwa zaka zambiri, tinkafotokoza kuti ulosiwu unkanena za anthu a Yehova omwe amalalikira ngati dzombe lomwe silingaimitsidwe ndi chinthu chilichonse. Tinkaganiza kuti ntchito yolalikirayi imasakaza “dziko” kapena kuti anthu amene akulamuliridwa ndi atsogoleri achipembedzo. *

4 Tikangoganizira lemba la Yoweli 2:7-9, kafotokozedwe kameneka kangaoneke komveka. Koma tikaganizira mbali zonse za ulosi umenewu, tingaone kuti tiyenera kusintha kafotokozedwe kake. Tiyeni tsopano tikambirane zifukwa 4 zotichititsa kuti tisinthe.

ZIFUKWA 4 ZOTICHITITSA KUSINTHA

5-6. Kodi tingakhale ndi funso liti pambuyo poganizira (a) Yoweli 2:20? (b) Yoweli 2:25?

5 Choyamba, taganizirani zimene Yehova analonjeza zokhudza dzombeli. Iye anati: “Ndidzakuchotserani mdani wa kumpoto [dzombe] kuti akhale kutali ndi inu.” (Yow. 2:20) Ngati dzombeli likuimira a Mboni za Yehova omwe amamvera lamulo la Yesu loti tizilalikira ndi kuphunzitsa anthu, n’chifukwa chiyani Yehova akulonjeza zolichotsa? (Ezek. 33:7-9; Mat. 28:19, 20) Apa n’zodziwikiratu kuti Yehova sakuchotsa atumiki ake okhulupirika koma chinthu china kapena munthu wina amene amadana ndi anthu ake.

6 Chifukwa chachiwiri chikupezeka pa Yoweli 2:25. Palembali, Yehova ananena kuti: “Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonse zimene dzombe ndi ana a dzombe oyenda pansi opanda mapiko, mphemvu ndi mbozi zinadya. Limeneli ndi gulu langa lankhondo lamphamvu limene ndinatumiza pakati panu.” Apa Yehova akulonjeza kuti ‘adzabwezera’ zinthu zimene zinawonongedwa ndi dzombe. Ngati dzombe likuimira anthu amene amalalikira, zikanatanthauza kuti uthenga wawo umawononga zinthu. Koma uthenga wawo wopulumutsa moyo ungathandize anthu oipa kuti alape. (Ezek. 33:8, 19) Zimenezi zingawabweretsere madalitso ambiri.

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu akuti “zimenezi zikadzachitika” opezeka pa Yoweli 2:28, 29?

7 Werengani Yoweli 2:28, 29. Chifukwa chachitatu chikukhudza mmene zinthu zikuchitikira mu ulosiwu. Onani kuti Yehova ananena kuti: “Zimenezi zikadzachitika ndidzatsanulira mzimu wanga,” kutanthauza kuti dzombelo likadzamaliza kuwonongako. Ndiye ngati dzombeli likuimira anthu olalikira za Ufumu wa Mulungu, n’chifukwa chiyani Yehova akuwatsanulira mzimu wake pambuyo poti amaliza ntchito yawo yolalikira? Zoona zake n’zakuti anthu a Yehova sakanakwanitsa kulalikira kwa zaka zambirimbiri akanapanda kuthandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti akhala akutsutsidwa komanso nthawi zina ntchito yawo imaletsedwa.

M’bale J. F. Rutherford komanso abale ena odzozedwa omwe ankatsogolera gulu lathu ankalengeza molimba mtima uthenga wachiweruzo cha Mulungu kwa anthu oipa am’dzikoli (Onani ndime 8)

8. Kodi dzombe lotchulidwa pa Chivumbulutso 9:1-11 likuimira ndani? (Onani chithunzi chapachikuto.)

8 Werengani Chivumbulutso 9:1-11. Tiyeni tsopano tikambirane chifukwa cha nambala 4. Poyamba, tinkaona kuti ulosi wa dzombe m’buku la Yoweli ukuimira ntchito yolalikira chifukwa cha ulosi wina wonena za dzombe m’buku la Chivumbulutso. Dzombe la m’buku la Chivumbulutso lili ndi nkhope za anthu ndipo pamitu pawo pali “zisoti zagolide zooneka ngati zachifumu.” (Chiv. 9:7) Ndipo likuzunza adani a Mulungu kapena kuti anthu “amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo.” Likuchita zimenezi kwa miyezi 5 yomwe ikuimira nthawi imene dzombe lenileni limakhala moyo. (Chiv. 9:4, 5) Apa zikuonekeratu kuti ulosiwu ukunena za atumiki a Yehova odzozedwa. Iwo amalalikira molimba mtima uthenga wakuti Mulungu adzaweruza dziko loipali ndipo izi zimachititsa kuti anthu m’dzikoli asamasangalale nawo.

9. Kodi dzombe limene Yoweli anaona likusiyana bwanji ndi limene Yohane anafotokoza?

9 N’zoona kuti ulosi wam’buku la Chivumbulutso umafanana ndi wam’buku la Yoweli pa zinthu zina koma maulosiwa ndi osiyana kwambiri. Mwachitsanzo, mu ulosi wa Yoweli, dzombe lake limasakaza zomera. (Yow. 1:4, 6, 7) Koma m’masomphenya a Yohane, dzombelo “linauzidwa kuti lisawononge zomera za padziko lapansi.” (Chiv. 9:4) Dzombe limene Yoweli anaona linachokera kumpoto. (Yow. 2:20) Pomwe limene Yohane anaona linachokera kuphompho. (Chiv. 9:2, 3) Dzombe la mu ulosi wa Yoweli linachotsedwa. Pomwe la m’buku la Chivumbulutso linaloledwa kuti limalize ntchito yake ndipo palibe zimene zikusonyeza kuti Yehova sanasangalale nalo.​—Onani bokosi lakuti “ Maulosi Onena za Dzombe​—Kodi Akusiyana Bwanji?

10. Perekani chitsanzo cha m’Malemba chosonyeza kuti dzombe limene Yoweli anaona likhoza kukhala losiyana ndi limene Yohane anaona.

10 Kusiyana kwa maulosiwa kukusonyeza kuti matanthauzo ake ndi osiyananso. Kodi pamenepa tikutanthauza kuti dzombe lofotokozedwa ndi Yoweli ndi losiyana ndi limene likupezeka m’buku la Chivumbulutso? Inde. M’Baibulo chinthu chimodzi chikhoza kuimira zinthu zosiyana. Mwachitsanzo, pa Chivumbulutso 5:5 Yesu amatchulidwa kuti “Mkango wa fuko la Yuda” pomwe pa 1 Petulo 5:8 pamanena kuti Mdyerekezi ndi “mkango wobangula.” Mfundo zimene takambiranazi zikusonyeza kuti payenera kukhala kafotokozedwe katsopano ka ulosi wa Yoweli. Ndiye kodi tingaufotokoze bwanji?

KODI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?

11. Kodi lemba la Yoweli 1:6 ndi 2:1, 8, 11 limatithandiza bwanji kudziwa amene dzombe likuimira?

11 Tikaganizira kwambiri mbali zonse za ulosi wa Yoweli, tingaone kuti iye ankalosera za gulu lankhondo. (Yow. 1:6; 2:1, 8, 11) Yehova ananena kuti adzagwiritsa ntchito ‘gulu lake lankhondo lamphamvu’ (asilikali a ku Babulo) kuti alange Aisiraeli osamvera. (Yow. 2:25) M’pomveka kuti asilikaliwa akutchedwa “mdani wa kumpoto” chifukwa choti Ababulo analowa mu Isiraeli kuchokera kumpoto. (Yow. 2:20) Ndipo gulu lankhondolo likuyerekezeredwa ndi dzombe. Pofotokoza za asilikaliwa, Yoweli ananena kuti: “Amayendabe ngati mwamuna wamphamvu amene akuyenda panjira yake. . . . Iwo amathamangira m’mizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda. Amakwera nyumba ndipo amalowa m’nyumbamo kudzera pawindo ngati mbala.” (Yow. 2:8, 9) Tangoganizirani mmene zinalili. Asilikali anali paliponse ndipo panalibe malo obisala. Panalibe munthu amene akanatha kuthawa lupanga la Ababulo.

12. Kodi ulosi wa Yoweli wonena za dzombe unakwaniritsidwa bwanji?

12 Ababulo (kapena kuti Akasidi) analowa ngati dzombe mumzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E. Baibulo limanena kuti: “Mfumu ya Akasidi yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga . . . sinachitire chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena nkhalamba yotheratu. Mulungu anapereka zonse m’manja mwake. Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona ndi kugwetsa mpanda wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino, mpaka zonse zinawonongedwa.” (2 Mbiri 36:17, 19) Ababulo atamaliza kuwononga, anthu akanatha kungonena kuti: “Dziko ili ndi bwinja, lopanda munthu wokhalamo kapena nyama yoweta. Linaperekedwa m’manja mwa Akasidi.”​—Yer. 32:43.

13. Fotokozani tanthauzo la Yeremiya 16:16, 18.

13 Patapita zaka 200 kuchokera pamene Yoweli analemba ulosi wake, Yehova anagwiritsa ntchito Yeremiya kuti alosere zinthu zina zokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Iye ananena kuti Aisiraeli amene ankachita zoipa adzafufuzidwa kwambiri mpaka kugwidwa. Ulosiwu umati: “‘Inetu ndikuitana asodzi ambiri,’ watero Yehova, ‘ndipo adzawawedza. Kenako ndidzaitana anthu ambiri osaka nyama, ndipo adzawasaka m’phiri lililonse, pachitunda chilichonse, ndi m’mapanga a m’matanthwe. . . . Ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse ndi machimo awo onse.’”​—Yer. 16:16, 18.

UTHENGA WABWINO

14. Kodi ulosi wa pa Yoweli 2:28, 29 unakwaniritsidwa liti?

14 Yoweli analoseranso uthenga wabwino wakuti m’dzikolo mudzakhalanso zomera zambiri. (Yow. 2:23-26) Iye anasonyezanso kuti pa nthawi ina m’tsogolo, chakudya chauzimu chambiri chidzayamba kupezeka. Yehova anati: “Ndidzatsanulira mzimu wanga pa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera. . . . Masiku amenewo ndidzatsanuliranso mzimu wanga pa antchito anu aamuna ndi aakazi.” (Yow. 2:28, 29) Koma Yehova sanatsanule mzimu wake Aisiraeli atangobwerera kumene m’dziko lawo kuchokera ku Babulo. Zimenezi zinachitika patapita zaka zambiri pa Pentekosite mu 33 C.E. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

15. Malinga ndi Machitidwe 2:16, 17, kodi Petulo anasintha mawu ati a pa Yoweli 2:28, nanga zimenezi zikusonyeza chiyani?

15 Petulo anauziridwa ndi Mulungu kuti asonyeze kuti ulosi wa pa Yoweli 2:28, 29 unakwaniritsidwa pa Pentekosite. Pa tsikulo m’ma 9 koloko m’mawa, mzimu woyera unatsanuliridwa pa anthu moti anayamba kulankhula “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:11) Koma Mulungu anauzira Petulo kuti asinthe pang’ono mawu a mu ulosi wa Yoweli. Kodi mwaona mawu amene anawasintha? (Werengani Machitidwe 2:16, 17.) M’malo moyamba ndi mawu akuti “zimenezi zikadzachitika,” anayamba ndi mawu akuti: “Ndipo m’masiku otsiriza” Mulungu adzatsanulira mzimu wake “pa anthu osiyanasiyana.” Ponena kuti “m’masiku otsiriza,” ankatanthauza kuti Yerusalemu ndi kachisi wake atatsala pang’ono kuwonongedwa. Izi zikusonyeza kuti panapita nthawi yaitali ulosi wa Yoweli usanakwaniritsidwe.

16. Kodi mzimu woyera unathandiza bwanji pa ntchito yolalikira nthawi ya atumwi, nanga wathandiza bwanji masiku ano?

16 Mzimu woyera utaperekedwa mu 33 C.E. m’pamene ntchito yolalikira inayamba kufalikira kwambiri. Pa nthawi imene Paulo ankalembera kalata Akhristu a ku Kolose cha m’ma 61 C.E., ananena kuti uthenga wabwino “unali utalalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Mawu oti “m’chilengedwe chonse” palembali akutanthauza madera onse amene ankadziwika pa nthawiyo. Mzimu wa Yehova wathandizanso kuti pofika pano uthenga wabwino ukhale utalalikidwa “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Mac. 13:47; onani bokosi lakuti “ Ndidzatsanulira Mzimu Wanga.”

N’CHIYANI CHASINTHA?

17. Kodi kafotokozedwe kathu ka ulosi wa Yoweli wonena za dzombe kasintha bwanji?

17 Kodi n’chiyani chasintha? Tsopano tamvetsa bwino ulosi wa pa Yoweli 2:7-9. Mwachidule tinganene kuti mavesi amenewa akunena zimene asilikali a Ababulo anachita poukira Yerusalemu mu 607 B.C.E., osati za ntchito yathu yolalikira.

18. Kodi n’chiyani sichinasinthe chokhudza anthu a Yehova?

18 Kodi n’chiyani chimene sichinasinthe? Anthu a Yehova akupitiriza kulalikira uthenga wabwino kulikonse ndipo amagwiritsa ntchito njira iliyonse imene angathe kuti achite zimenezi. (Mat. 24:14) Palibe lamulo lililonse la boma limene lingalepheretse ntchito imeneyi. Yehova akudalitsa kwambiri ntchitoyi ndipo tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu molimba mtima kuposa kale lonse. Timadalira Yehova modzichepetsa podziwa kuti pa nthawi yoyenera iye adzatithandiza kudziwa ‘choonadi chonse.’​—Yoh. 16:13.

NYIMBO NA. 97 Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala ndi Moyo

^ ndime 5 Kwa zaka zambiri, takhala tikukhulupirira kuti ulosi wa m’chaputala 1 ndi 2 cha buku la Yoweli umalosera za ntchito yathu yolalikira yamasiku ano. Koma pali zifukwa 4 zomveka zochititsa kuti tisinthe kafotokozedwe ka ulosi umenewu. Kodi zifukwa zake ndi ziti?

^ ndime 3 Mwachitsanzo, onani nkhani yakuti “Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2009, ndime 14-16.