Nkhani Yophunzira 17

“Ndakutchani Mabwenzi”

“Ndakutchani Mabwenzi”

“Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”​—YOH. 15:15.

NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi n’chiyani chimafunika kuti anthu ayambe kugwirizana?

KUTI tiyambe kugwirizana ndi munthu wina, nthawi zambiri timafunika kupeza nthawi yocheza naye. Zili choncho chifukwa mumauzana maganizo komanso zimene zakuchitikirani pa moyo wanu. Koma si zophweka kuti Yesu akhale mnzathu wapamtima. Kodi chimene chimachititsa kuti zikhale zovuta n’chiyani?

2. Kodi vuto loyamba lomwe timakumana nalo ndi liti?

2 Vuto loyamba ndi lakuti ifeyo sitinakumanepo ndi Yesu. Akhristu ena mu nthawi ya atumwi analinso ndi vuto lomweli. Koma mtumwi Petulo anawauza kuti: “Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye.” (1 Pet. 1:8) Choncho ndi zotheka kukhala anzake a Yesu ngakhale kuti sitinakumanepo naye.

3. Kodi vuto lachiwiri ndi liti?

3 Vuto lachiwiri ndi loti sitingalankhule ndi Yesu. Tikamapemphera timalankhula ndi Yehova. N’zoona kuti timapemphera m’dzina la Yesu, koma sitilankhula ndi Yesuyo. Ndipo Yesu safuna kuti tizipemphera kwa iye. Zili choncho chifukwa chakuti pemphero ndi mbali ya kulambira kwathu, ndipo Yehova yekha ndi amene tiyenera kumulambira. (Mat. 4:10) Komabe tikhoza kusonyeza kuti timakonda Yesu.

4. Kodi vuto lachitatu ndi liti, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

4 Vuto lachitatu ndi loti Yesu amakhala kumwamba. Choncho sitingakhale naye limodzi. Komabe tikhoza kudziwa zambiri zokhudza Yesu ngakhale kuti sitingakhale naye. Munkhaniyi tikambirana zinthu 4 zimene tingachite kuti tikhale anzake a Yesu. Koma choyamba, tiyeni tikambirane chifukwa chake tiyenera kukhala anzake.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHALA ANZAKE A YESU?

5. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala anzake a Yesu? (Onani bokosi lakuti “ Kukhala Anzake a Yesu Kungatithandize Kukhalanso Anzake a Yehova” komanso lakuti “ Tiziona Yesu Moyenera.”)

5 Tiyenera kukhala anzake a Yesu kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Izi zili choncho pa zifukwa ziwiri. Choyamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Atateyo amakukondani, chifukwa munandikonda ine.” (Yoh. 16:27) Iye ananenanso kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yoh. 14:6) Kuyesetsa kukhala mnzake wa Yehova popanda kukhala mnzake wa Yesu kuli ngati kuyesetsa kulowa m’nyumba popanda kudzera pakhomo. Yesu anagwiritsa ntchito chitsanzo chimenechi pamene ananena kuti iye ndi “khomo la nkhosa.” (Yoh. 10:7) Chachiwiri, Yesu ankatsanzira ndendende makhalidwe a Atate ake. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Choncho njira yofunika yotithandiza kudziwa Yehova ndi kuphunzira za Yesu. Tikamaphunzira za Yesu timayamba kumukonda kwambiri. Ndipo tikayamba kukonda kwambiri Yesu tidzayambanso kukonda Atate ake.

6. Kodi chifukwa china chotichititsa kukhala anzake a Yesu n’chiyani? Fotokozani.

6 Tiyenera kukhala anzake a Yesu kuti mapemphero athu aziyankhidwa. Kungonena mawu akuti “m’dzina la Yesu” m’mapemphero athu si kokwanira. Koma tiyenera kudziwa mmene Yehova amagwiritsira ntchito Yesu poyankha mapemphero athu. Yesu anauza atumwi kuti: “Chilichonse chimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzachichita.” (Yoh. 14:13) N’zoona kuti Yehova ndi amene amamvetsera komanso kuyankha mapemphero athu koma wapatsa Yesu udindo wochita zimene Yehovayo wasankha. (Mat. 28:18) Choncho Mulungu asanayankhe mapemphero athu amaona kaye ngati timatsatira malangizo a Yesu. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani. Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.” (Mat. 6:14, 15) Choncho tiyenera kukomera mtima anthu ena ngati mmene Yehova ndi Yesu amachitira ndi ifeyo.

7. Kodi ndi ndani amene amathandizidwa ndi nsembe ya dipo ya Yesu?

7 Anzake apamtima a Yesu ndi okhawo amene amathandizidwa ndi nsembe yake ya dipo. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Yesu ananena kuti adzapereka “moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Anthu okhulupirika amene anakhala moyo Yesu asanabwere padzikoli adzafunika kuphunzira za iye komanso kumukonda. N’zoona kuti anthu monga Abulahamu, Sara, Mose ndi Rahabi adzaukitsidwa. Koma kuti adzapeze moyo wosatha, adzayenera kudziwa za Yesu komanso kukhala anzake.​—Yoh. 17:3; Mac. 24:15; Aheb. 11:8-12, 24-26, 31.

8-9. Malinga ndi Yohane 15:4, 5, kodi kukhala anzake a Yesu kumatithandiza bwanji, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi ndi zofunika?

8 Timasangalala kugwira ntchito ndi Yesu polalikira komanso kuphunzitsa anthu uthenga wabwino wa Ufumu. Yesu ali padzikoli anali mphunzitsi. Atabwerera kumwamba, iye anakhala mutu wa mpingo ndipo akupitiriza kutsogolera pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Yesu amaona komanso kuyamikira zimene mumachita poyesetsa kuthandiza anthu kuti amudziwe iyeyo ndiponso Atate wake. Sitingakwanitse kugwira bwino ntchito imeneyi popanda kuthandizidwa ndi Yehova komanso Yesu.​—Werengani Yohane 15:4, 5.

9 Mawu a Mulungu amaphunzitsa momveka bwino kuti tiyenera kukonda Yesu kuti tizisangalatsa Yehova. Choncho tiyeni tikambirane zinthu 4 zimene tingachite kuti tikhale anzake a Yesu.

KODI TINGATANI KUTI TIKHALE ANZAKE A YESU?

Tikhoza kukhala anzake a Yesu (1) tikamayesetsa kumudziwa bwino, (2) tikamatsanzira maganizo ndi zochita zake, (3) tikamathandiza abale ake komanso (4) tikamachita zinthu mogwirizana ndi mpingo (Onani ndime 10-14) *

10. Tchulani chinthu choyamba chimene tingachite kuti tikhale anzake a Yesu.

10 (1) Tiyenera kumudziwa bwino Yesu. Tingaphunzire za moyo wa Yesu powerenga mabuku a m’Baibulo a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane. Tikamaganizira nkhani za m’mabukuwa timaona kuti Yesu ankachitira chifundo anthu ndipo izi zimachititsa kuti tizimukonda komanso kumulemekeza. Mwachitsanzo, ngakhale kuti iye anali Ambuye wa ophunzira ake, sankachita nawo zinthu ngati akapolo ake. Koma ankawafotokozera maganizo ake ndi zimene zinali mumtima mwake. (Yoh. 15:15) Yesu akaona otsatira ake akuvutika zinkamupweteka kwambiri ndipo ankalira nawo. (Yoh. 11:32-36) Ngakhale anthu amene ankadana naye anavomereza kuti iye ankagwirizana ndi anthu amene ankamvetsera uthenga wake. (Mat. 11:19) Tikamatsanzira zimene Yesu ankachitira ophunzira ake, timayamba kugwirizana ndi anzathu, timakhala osangalala komanso timayamba kukonda kwambiri Khristu.

11. Kodi chinthu chachiwiri chimene tingachite kuti tikhale anzake a Yesu n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

11 (2) Tizitsanzira maganizo ndi zochita za Yesu. Tikadziwa bwino maganizo a Yesu n’kumamutsanzira timayamba kugwirizana naye kwambiri. (1 Akor. 2:16) Koma kodi tingatsanzire bwanji Yesu? Tiyeni tingokambirana njira imodzi. Yesu ankaganizira kwambiri zothandiza anthu ena osati kudzisangalatsa yekha. (Mat. 20:28; Aroma 15:1-3) Maganizo amenewa anamuthandiza kuti azichita zinthu modzipereka komanso azikhululukira anthu ena. Iye sankakhumudwa msanga anthu akalankhula zinthu zolakwika zokhudza iyeyo. (Yoh. 1:46, 47) Komanso sankasungira anthu zifukwa. (1 Tim. 1:12-14) Yesu ananena kuti: “Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, “Kodi ineyo ndimatsanzira Yesu pochita zonse zimene ndingathe kuti ndizikhala mwamtendere ndi abale ndi alongo?”

12. Kodi chinthu chachitatu chimene tingachite kuti tikhale anzake a Yesu n’chiyani, nanga tingachite bwanji zimenezi?

12 (3) Tizithandiza abale a Khristu. Yesu amaona kuti zimene timachita pothandiza abale ake odzozedwa, tikuchitira iyeyo. (Mat. 25:34-40) Njira yofunika kwambiri imene tingathandizire odzozedwa ndi kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu yomwe Yesu analamula otsatira ake kuti aziigwira. (Mat. 28:19, 20; Mac. 10:42) Abale a Khristu angakwanitse kugwira ntchito yolalikira padziko lonse pokhapokha ngati akuthandizidwa ndi a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Ngati ndinu a nkhosa zina, nthawi iliyonse imene mumagwira ntchitoyi mumasonyeza kuti mumakonda odzozedwa komanso Yesu.

13. Kodi tingatsatire bwanji malangizo a Yesu a pa Luka 16:9?

13 Timagwirizananso ndi Yehova ndi Yesu tikamapereka ndalama zathu kuti zithandize pa ntchito imene akutsogolera. (Werengani Luka 16:9.) Tingapereke ndalama zothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Ndalama zimenezi zimathandiza polalikira m’madera akutali, pomanga ndi kukonza malo olambirira komanso pothandiza anthu amene akumana ndi ngozi zadzidzidzi. Tikhozanso kupereka ndalama zothandiza pa mpingo wathu ndiponso kuthandiza abale athu amene akuvutika. (Miy. 19:17) Tikamachita zonsezi timakhala kuti tikuthandiza abale a Khristu.

14. Mogwirizana ndi Aefeso 4:15, 16, kodi chinthu cha nambala 4 chimene tiyenera kuchita kuti tikhale anzake a Yesu n’chiyani?

14 (4) Muzichita zinthu mogwirizana ndi mpingo wa Chikhristu. Popeza Yesu ndi mutu wa mpingo, timakhalanso anzake tikamachita zinthu mogwirizana ndi anthu amene wawasankha kuti azitiyang’anira. (Werengani Aefeso 4:15, 16.) Mwachitsanzo, masiku ano gulu lakonza zoti Nyumba za Ufumu zizigwiritsidwa ntchito mokwanira. Kuti zimenezi zitheke, mipingo ina inaphatikizidwa ndipo magawo a mipingoyo anasinthidwa. Zimenezi zathandiza kuti ndalama zimene abale amapereka zizigwiritsidwa ntchito bwino. Koma zachititsanso kuti zinthu zisinthe pa moyo wa abale ndi alongo ena. Mwachitsanzo, ena anakhala mumpingo wina kwa nthawi yaitali ndipo ankagwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo mumpingowo. Koma panopa apemphedwa kuti azitumikira mumpingo wina. Yesu ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona Akhristu okhulupirikawa akutsatira bwinobwino malangizowa.

TINGAKHALE ANZAKE A YESU MPAKA KALEKALE

15. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kukhala anzake apamtima a Yesu m’tsogolomu?

15 Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera akuyembekezera kudzakhala ndi Yesu kwamuyaya komanso kulamulira naye mu Ufumu wa Mulungu. Iwo adzatha kumuona, kulankhula naye komanso kuchita naye zinthu zina. (Yoh. 14:2, 3) Yesu adzasonyezanso chikondi kwa anthu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli. Ngakhale kuti anthuwo sadzamuona, adzayamba kukhala anzake apamtima kwambiri akamadzasangalala ndi moyo umene Yehova ndi Yesuyo adzawapatse.​—Yes. 9:6, 7.

16. Kodi timapeza madalitso ati chifukwa chokhala anzake a Yesu?

16 Timapeza madalitso ambiri tikamayesetsa kukhala anzake a Yesu. Mwachitsanzo, panopa iye amatisonyeza chikondi ndiponso kutithandiza. Komanso tili ndi mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. Ndipo koposa zonse, kukhala anzake a Yesu kumatithandiza kupeza mwayi wamtengo wapatali wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate ake, Yehova. Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala anzake a Yesu.

NYIMBO NA. 17 “Ndikufuna”

^ ndime 5 Atumwi anakhala zaka zingapo akucheza komanso kugwira ntchito ndi Yesu, ndipo anakhala anzake apamtima. Yesu amafuna kuti ifenso tikhale anzake, koma si zapafupi tikayerekezera ndi mmene zinalili ndi atumwi. Munkhaniyi tikambirana zinthu zimene zingachititse kuti zikhale zovuta kukhala anzake a Yesu koma tionanso zimene tingachite kuti zimenezi zitheke.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: ((1) Pa kulambira kwa pabanja, tingaphunzire za moyo ndi utumiki wa Yesu. (2) Mumpingo, tiziyesetsa kukhala mwamtendere ndi abale athu. (3) Tingathandize abale ake a Khristu pochita zonse zomwe tingathe mu utumiki. (4) Mipingo ikaphatikizidwa, tizichita zinthu mogwirizana ndi zimene akulu asankha.