Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 20

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndani Masiku Ano?

Kodi “Mfumu ya Kumpoto” Ndani Masiku Ano?

“Iyo idzafika kumapeto a moyo wake ndipo sipadzapezeka woithandiza.”​—DANIELI 11:45.

NYIMBO 95 Kuwala Kuwonjezeleka

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

LELOLINO kuposa kale lonse, tili na umboni woculuka wakuti tikukhala ku mapeto kwa masiku otsiliza a dzikoli. Posacedwa, Yehova na Yesu Khristu adzawononga maboma onse amene amatsutsa Ufumu wa Mulungu. Koma izi zisanacitike, mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela adzapitiliza kulimbana okha-okha komanso kulimbana ndi anthu a Mulungu.

2 M’nkhani ino, tikambilana ulosi wa pa Danieli 11:40 mpaka Danieli 12:1. Pokambilana, tiona kuti mfumu ya kumpoto ndani masiku ano. Tionanso cifukwa cake sitiyenela kuda nkhawa na mavuto amene tidzakumana nawo kutsogoloku.

MFUMU YATSOPANO YA KUMPOTO IONEKELA

3-4. Kodi mfumu ya kumpoto ndani masiku ano? Fotokozani.

3 Ulamulilo wa Soviet Union utatha mu 1991, anthu a Mulungu m’maiko amene anali kulamulidwa na bomalo analandila “thandizo locepa,” kutanthauza kuti anakhala na ufulu kwa kanthawi. (Dan. 11:34) Pa cifukwa cimeneci, iwo anayamba kulalikila mwaufulu, ndipo posapita nthawi anthu masauzande ambili m’maikowo anakhala Mboni. M’kupita kwa nthawi, Russia na maiko ogwilizana naye anakhala mfumu ya kumpoto. Monga tinakambila m’nkhani yapita, boma limakhala mfumu ya kumpoto kapena ya kum’mwela ngati: (1) zocita zake zimakhudza mwacindunji anthu a Mulungu, (2) limacita zinthu zoonetsa kuti limazonda Yehova ndi anthu ake, komanso (3) limalimbana na mfumu inzake yamphamvu.

4 N’cifukwa ciani takamba kuti Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto masiku ano? Onani zifukwa izi: (1) Zocita zawo zakhudza mwacindunji anthu a Mulungu. Analetsa nchito yolalikila, ndiponso azunza abale na alongo athu masauzande ambili amene amakhala m’maikowo. (2) Zimene acitazi zaonetsa kuti amazonda Yehova komanso anthu ake. (3) Maiko amenewa akhala akulimbana na mfumu ya kum’mwela, imene ni Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. Tsopano tiyeni tione zimene Russia na maiko ogwilizana naye acita, zoonetsa kuti iwo ni mfumu ya kumpoto.

MFUMU YA KUMPOTO NA MFUMU YA KUM’MWELA AKUPITILIZA KUKANKHANA

5. Kodi Danieli 11:40-43 inakambilatu zocitika za pa nthawi iti? Nanga inati n’ciani cidzacitika pa nthawiyo?

5 Ŵelengani Danieli 11:40-43. Mbali imeneyi ya ulosi wa Danieli ikamba za zocitika za m’nthawi ya mapeto. Mavesiwa akamba za kulimbana pakati pa mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela. Danieli anakambilatu kuti m’nthawi ya mapeto, mfumu ya kum’mwela idzayamba “kukankhana nayo” mfumu ya kumpoto.—Dan. 11:40.

6. Kodi pali umboni wotani woonetsa kuti mfumu ya kumpoto yakhala ikukankhana na mfumu ya kum’mwela?

6 Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akulimbilana ulamulilo wa dziko lonse. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha. Pambuyo pa nkhondoyo, Boma la Soviet Union linayamba kulamulila madela ambili ku Europe. Izi zinakakamiza mfumu ya kum’mwela kupanga mgwilizano wa zankhondo na maiko ena. Mgwilizano umenewo umachedwa NATO (North Atlantic Treaty Organization). Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akupikisana pofuna kupanga gulu lankhondo lamphamvu kwambili padziko lonse. Iwo amawononga ndalama zambili pocita zimenezi. Kuwonjezela apo, mfumu ya kumpoto inalimbana na mfumu ya kum’mwela mwa kuthandiza maiko kapena magulu odana na mfumu ya kum’mwelayo mu Africa, ku Asia, na ku Latin America. M’zaka zaposacedwa, Russia na maiko ogwilizana naye akhala amphamvu kwambili padzikoli. Iwo amalimbana na mfumu ya kum’mwela poseŵenzetsa makompyuta. Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela amaimbana milandu yakuti akuwonongelana mapulogilamu a pa kompyuta, pofuna kusokoneza cuma ca mfumu inzake kapena kugwetsa boma. Ndiponso monga mmene Danieli anakambila, mfumu ya kumpoto ikupitiliza kuzunza anthu a Mulungu.—Dan. 11:41.

MFUMU YA KUMPOTO ILOŴA “M’DZIKO LOKONGOLA”

7. Kodi “dziko lokongola” n’ciani?

7 Lemba la Danieli 11:41 limakamba kuti mfumu ya kumpoto idzaloŵa “m’Dziko Lokongola.” Kodi dziko limeneli n’ciani? Kale, dziko la Isiraeli n’limene linali kuonedwa kuti ni “dziko lokongola kwambili kuposa maiko onse.” (Ezek. 20:6) Dziko limenelo linali kuonedwa lokongola kwambili cifukwa cakuti n’kumene anthu anali kulambila Yehova. Koma kucokela pa Pentekosite wa mu 33 C.E., “dziko lokongola” si dela leni-leni padzikoli. Takamba telo cifukwa tsopano anthu a Yehova ali kulikonse padziko lapansi. Conco, masiku ano, “dziko lokongola” ni paradaiso wauzimu wa anthu a Yehova. Paradaiso ameneyu aphatikizapo zimene anthu a Yehova amacita pom’lambila, monga kusonkhana pamodzi na kulalikila.

8. Kodi mfumu ya kumpoto inaloŵa bwanji “m’Dziko Lokongola”?

8 M’masiku otsiliza ano, mfumu ya kumpoto yaloŵa mobweleza-bweleza “m’Dziko Lokongola.” Mwacitsanzo, pamene boma la Nazi ku Germany linali mfumu ya kumpoto, linaloŵa “m’Dziko Lokongola” mwa kuzunza na kupha anthu a Mulungu. Izi zinacitika kwambili pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Pambuyo pa nkhondoyo, boma la Soviet Union n’limene linakhala mfumu ya kumpoto. Bomali nalonso linaloŵa “m’Dziko Lokongola” mwa kuzunza anthu a Mulungu na kuwathamangitsila ku Siberia, dela lakutali kwambili na kwawo.

9. Kodi Russia na maiko ogwilizana naye aloŵa bwanji “m’Dziko Lokongola” m’zaka zaposacedwapa?

9 M’zaka zaposacedwa, nalonso boma la Russia na maiko ogwilizana nalo aloŵa “m’Dziko Lokongola.” Motani? Mu 2017, mfumu ya kumpoto yatsopano imeneyi inaletsa nchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo, ndiponso inaponya m’ndende ena mwa abale na alongo athu. Bomali linaletsanso mabuku athu, kuphatikizapo Baibulo la Dziko Latsopano. Kuwonjezela apo, linalanda ofesi yathu ya nthambi ya m’dzikolo, Nyumba zina za Ufumu, na Mabwalo ena a Misonkhano. Izi zitacitika, mu 2018 Bungwe Lolamulila linaona kuti Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto. Koma ngakhale anthu a Yehova azunzidwe bwanji na boma, iwo salimbana nalo kapena kuyesa kusintha ulamulilo. M’malomwake, amatsatila malangizo a m’Baibo akuti tiyenela kupemphelela “anthu onse apamwamba,” maka-maka ngati akupanga zosankha zimene zingakhudze ufulu wa kulambila.—1 Tim. 2:1, 2.

KODI MFUMU YA KUMPOTO IDZAGONJETSA MFUMU YA KUM’MWELA?

10. Kodi mfumu ya kumpoto idzagonjetsa mfumu ya kum’mwela? Fotokozani.

10 Ulosi wa pa Danieli 11:40-45 umakamba kwambili za mfumu ya kumpoto. Kodi izi zitanthauza kuti mfumuyi idzagonjetsa mfumu ya kum’mwela? Iyai. Mfumu ya kum’mwela idzakhala ikali ‘yamoyo’ pamene Yehova na Yesu azidzawononga maboma onse a anthu pa Aramagedo. (Chiv. 19:20) Tidziŵa bwanji zimenezi? Onani zimene maulosi a m’buku la Danieli komanso a m’buku la Chivumbulutso amakamba.

Pa Aramagedo, Ufumu wa Mulungu umene umayelekezedwa na mwala, udzaphwanya maboma a anthu, amene akuimilidwa na cifanizilo cacikulu. (Onani ndime 11)

11. Kodi lemba la Danieli 2:43-45 limaonetsa ciani? (Onani cithunzi pacikuto.)

11 Ŵelengani Danieli 2:43-45. Mneneli Danieli anafotokoza za maboma osiyana-siyana a anthu amene zocita zawo zinakhudza mwacindunji anthu a Mulungu. Maboma amenewa anawayelekezela na mbali zosiyana-siyana za cifanizilo cacikulu. Boma lotsiliza pa maboma amenewo likuyelekezedwa na mapazi a cifaniziloco, amene ni acitsulo cosakanizika na dongo. Mapaziwo aimila Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. Ulosi umenewu uonetsa kuti ulamulilowu udzakhalabe ukulamulila pamene Ufumu wa Mulungu udzaphwanya na kuwononga maboma onse a anthu.

12. Kodi mutu wa 7 wa cilombo uimila ciani? Nanga n’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi n’kofunika?

12 Nayenso mtumwi Yohane anakamba za maboma amphamvu padziko lonse amene zocita zawo zinakhudza anthu a Yehova. Mu ulosi wa Yohane, maboma amenewa anawayelekezela na cilombo ca mitu 7. Mutu wa 7 wa cilombo cimeneci uimila Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. Kudziŵa mfundo imeneyi n’kofunika cifukwa Baibo imaonetsa kuti cilomboci sicidzakhalanso na mutu wina. Mutu wa 7 umenewu udzakhalabe ukulamulila pamene Khristu na magulu ake ankhondo akumwamba adzawononga mutuwo pamodzi na cilombo. *Chiv. 13:1, 2; 17:13, 14.

KODI MFUMU YA KUMPOTO IDZACITA CIANI POSACEDWA?

13-14. Kodi “Gogi wa kudziko la Magogi” ndani? Nanga zioneka kuti n’ciani cidzamusonkhezela kuukila anthu a Mulungu?

13 Ulosi wina m’buku la Ezekieli umatithandiza kudziŵa zimene zingadzacitike pamene mafumu aŵili amenewa, ya kumpoto na ya kum’mwela, ali pafupi kuwonongedwa. Cioneka kuti maulosi a pa Ezekieli 38:10-23; Danieli 2:43-45; Danieli 11:44 mpaka caputa 12:1; komanso Chivumbulutso 16:13-16, 21 amafotokoza zocitika zimodzi-modzi. Ngati zilidi conco, ndiye kuti zinthu zotsatilazi n’zimene zidzacitika kutsogolo.

14 Pa nthawi inayake mkati mwa cisautso cacikulu, “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzapanga mgwilizano wa mitundu. (Chiv. 16:13, 14; 19:19) M’Baibo, mgwilizano umenewo umachedwa “Gogi wa kudziko la Magogi.” (Ezek. 38:2) Mgwilizano wa mitundu umenewu udzaukila anthu a Mulungu komaliza kuti uwafafanize kothelatu. Kodi n’ciani cidzakwiyitsa Gogi kuti acite zimenezi? M’masomphenya aulosi okhudza nthawiyi, mtumwi Yohane anaona matalala akulu-akulu kwambili akugwela adani a Mulungu. Zioneka kuti matalala amenewa akuimila uthenga woŵaŵa waciweluzo, umene anthu a Yehova azikalengeza. N’kutheka kuti uthenga umenewu ndiwo udzakwiyitsa Gogi wa Magogi kuti aukile anthu a Mulungu n’colinga cakuti awafafaniziletu padziko lapansi.—Chiv. 16:21.

15-16. (a) Kodi zioneka kuti lemba la Danieli 11:44, 45 limakamba za ciani? (b) N’ciani cidzacitikila mfumu ya kumpoto na mitundu ina yonse imene idzakhala Gogi wa Magogi?

15 Ŵelengani Danieli 11:44, 45. Cioneka kuti lemba limeneli nalonso limakamba za uthenga woŵaŵa waciweluzo komanso za kuukilidwa komaliza kwa anthu a Mulungu. Pa lembali, Danieli anakamba kuti “kotulukila dzuwa ndi kumpoto kudzacokela mauthenga” amene adzasokoneza mfumu ya kumpoto. Ndipo iyo idzapita na “ukali waukulu” kuti ‘ikawononge ambili.’ Zioneka kuti “ambili” amene achulidwa pa lembali ni anthu a Yehova. * Conco, Danieli ayenela kuti anali kukamba za adani amene adzaukila anthu a Mulungu komaliza, n’colinga cakuti awawononge kothelatu.

16 Mfumu ya kumpoto na maboma ena padzikoli akadzaukila anthu a Mulungu, adzaputa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuzonse, ndipo izi zidzayambitsa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Panthawiyo, mfumu ya kumpoto pamodzi na mitundu ina yonse imene idzakhala Gogi wa Magogi, idzawonongedwa kothelatu, ndipo “sipadzapezeka woithandiza.”—Dan. 11:45.

Pa nkhondo ya Aramagedo, Yesu Khristu na magulu ake ankhondo a kumwamba adzawononga dziko loipa la Satana na kupulumutsa anthu a Mulungu (Onani ndime 17)

17. Kodi “Mikayeli, kalonga wamkulu” wochulidwa pa Danieli 12:1 ndani? Kodi acita ciani palipano, nanga adzacita ciani kutsogolo?

17 Vesi yoyamba m’caputa 12 ca buku la Danieli, imafotokoza mmene mfumu ya kumpoto na maboma ogwilizana nayo adzawonongedwela. Imafotokozanso mmene Yehova adzatipulumutsila. (Ŵelengani Danieli 12:1.) Kodi vesiyi imatanthauza ciani? Mikayeli ni dzina lina la Mfumu yathu, Khristu Yesu. Kuyambila mu 1914 pamene Ufumu unakhazikitsidwa kumwamba, Khristu ‘anaimilila kuti azithandiza’ anthu a Mulungu. Koma posacedwapa, iye “adzaimilila,” kutanthauza kuti adzawononga adani ake pankhondo ya Aramagedo. Nkhondo imeneyo ndiyo idzakhala cocitika cothela pa “nthawi ya masautso” aakulu kwambili amene Danieli anakamba kuti sanacitikepo. Mu ulosi wa Yohane wolembedwa m’buku la Chivumbulutso, nthawi yovuta imeneyo yomwe idzathela pa Aramagedo, imachedwa “cisautso cacikulu.”—Chiv. 6:2; 7:14.

KODI DZINA LANU ‘LIDZALEMBEDWA M’BUKU’?

18. N’cifukwa ciani sitiyenela kukhala na nkhawa tikaganizila zimene zidzacitika kutsogolo?

18 Onse aŵili, Danieli na Yohane anakamba kuti Yehova na Yesu adzapulumutsa atumiki awo pa “cisautso cacikulu.” Conco, sitiyenela kukhala na nkhawa tikaganizila zimene zidzacitika kutsogolo. Danieli anakamba kuti anthu amene maina awo ‘adzalembedwa m’buku’ ndiwo adzapulumuka. (Dan. 12:1) Tingacite ciani kuti maina athu alembedwe m’buku limenelo? Tifunika kucita zinthu zoonetsa kuti tili na cikhulupililo mwa Yesu, “Mwanawankhosa wa Mulungu.” (Yoh. 1:29) Tifunikanso kudzipatulila kwa Mulungu na kubatizika. (1 Pet. 3:21) Kuwonjezela apo, tifunika kucilikiza Ufumu wa Mulungu mwa kucita zonse zimene tingathe pophunzitsa ena za Yehova.

19. Kodi tiyenela kucita ciani panthawi ino? Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kucita zimenezo?

19 Ino ndiyo nthawi yofunika kuphunzila kudalila kwambili Yehova na gulu la atumiki ake okhulupilika. Ino ndiyo nthawi yofunika kucilikiza Ufumu wa Mulungu. Tikatelo, tidzapulumuka pamene Ufumu wa Mulungu udzawononga mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela.

NYIMBO 149 Nyimbo ya Cipambano

^ ndime 5 Kodi “mfumu ya kumpoto” ndani masiku ano? Nanga idzawonongedwa bwanji? Kudziŵa mayankho pa mafunso amenewa kungalimbitse cikhulupililo cathu, komanso kungatithandize kukonzekela mayeselo amene tidzakumana nawo posacedwa.

^ ndime 12 Kuti mumve mafotokozedwe atsatane-tsatane a Danieli 2:36-45 na Chivumbulutso 13:1, 2, onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012, peji 7-11,12,13-17,18-19.