Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 25

“Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”

“Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”

“Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.”​—EZEK. 34:11.

NYIMBO NA. 105 “Mulungu Ndiye Chikondi”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani Yehova akudziyerekezera ndi mayi woyamwitsa?

M’NTHAWI ya mneneri Yesaya, Yehova anafunsa kuti: “Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa?” Poyankha, Yehova anauza anthu ake kuti: “Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala, koma ine sindidzakuiwala.” (Yes. 49:15) Si nthawi zonse pamene Yehova amadziyerekezera ndi zimene mayi amachita ngati mmene anachitira panthawiyi. Iye anafotokoza zachikondi chimene chimakhalapo pakati pa mayi ndi mwana wake pofuna kusonyeza mmene amakondera atumiki ake. Azimayi ambiri angagwirizane ndi zimene mlongo wina dzina lake Jasmin ananena. Iye anati: “Mayi woyamwitsa amakondana kwambiri ndi mwana wake ndipo chikondi chimenechi sichitherapo.”

2. Kodi Yehova amamva bwanji mtumiki wake wina akasiya kumutumikira?

2 Yehova amadziwa ngati mtumiki wake wina wasiya kulalikira kapena kusonkhana. Ndiye taganizirani mmene zimam’pwetekera kuona kuti chaka chilichonse atumiki ake ambirimbiri akufooka * n’kusiya kumutumikira.

3. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene afooka achite chiyani?

3 Pakapita nthawi, abale ndi alongo ambiri omwe anafooka amayambiranso kutumikira Yehova ndipo timawalandira ndi manja awiri. Yehova amafunitsitsa kuti abwerere ndipo ifenso timalakalaka atabwerera. (1 Pet. 2:25) Koma kodi tingawathandize bwanji kuti abwererenso? Tisanayankhe funsoli, tiyeni tikambirane zifukwa zimene zimachititsa anthu ena kuti asiye kusonkhana komanso kulalikira.

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMASIYA KUTUMIKIRA YEHOVA?

4. Kodi ntchito imasokoneza bwanji anthu ena?

4 Anthu ena amatanganidwa kwambiri ndi ntchito yawo. M’bale wina wa ku Asia dzina lake Hung * ananena kuti: “Ndinkatanganidwa kwambiri ndi ntchito yanga. Ndinkadzinamiza kuti ndikapeza ndalama zambiri, ndizidzatumikira Yehova mosavuta. Choncho ndinayamba kugwira ntchito kwa maola ambiri. Ndinayamba kujomba kumisonkhano ndipo kenako ndinangosiyiratu kusonkhana. Zikuoneka kuti Satana amagwiritsa ntchito dzikoli pofuna kusokoneza anthu kuti pang’ono ndi pang’ono asiye kutumikira Mulungu.”

5. Kodi Mlongo Anne anakumana ndi mavuto otani, nanga zinamukhudza bwanji?

5 Abale ndi alongo ena amafooka chifukwa cha mavuto omwe amakumana nawo. Chitsanzo ndi mlongo wina wa ku Britain dzina lake Anne. Mlongoyu ali ndi ana 5 ndipo anafotokoza kuti: “Mwana wanga wachiwiri anabadwa wolumala. Patapita nthawi, mwana wanga wachitatu anachotsedwa mumpingo ndipo mwana wanga wa nambala 4 anadwala matenda a mu ubongo ndipo ankafunika kumusamalira mwapadera. Ndinasokonezeka maganizo kwambiri moti ndinasiya kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Kenako ndinangosiyiratu kutumikira Yehova.” Zimatikhudza kwambiri tikaganizira za anthu ngati Anne ndi ena omwe akukumana ndi mavuto ngati amenewa.

6. Kodi kusatsatira malangizo apa Akolose 3:13, kungachititse bwanji munthu kuti asiye kutumikira Yehova?

6 Werengani Akolose 3:13. Atumiki a Yehova ena anakhumudwitsidwa ndi Akhristu anzawo. Mtumwi Paulo ankadziwa kuti nthawi zina tikhoza kukhala ndi chifukwa chomveka “chodandaulira” zochita za m’bale kapena mlongo wina. N’kutheka kuti m’bale kapena mlongo angatichitiredi zinthu zopanda chilungamo koma ngati sitingasamale tikhoza kupsa mtima kwambiri. Munthu akakhumudwa akhoza kusiya kutumikira Yehova. Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina wa ku South America, dzina lake Pablo. Munthu wina anamunamizira kuti wachita zinazake zoipa ndipo anachotsedwa paudindo. Kodi Pablo anatani? Iye anati: “Ndinakhumudwa kwambiri ndipo pang’ono ndi pang’ono ndinafooka.”

7. Kodi chingachitike n’chiyani munthu akamadziimbabe mlandu pa zimene anachita?

7 Enanso amafooka chifukwa choti nthawi ina anachita tchimo lalikulu ndiye amadziimbabe mlandu n’kumaona ngati Mulungu sangawakondenso. Ngakhale kuti analapa komanso anasonyezedwa chifundo, angamadzionebe kuti si oyenera kukhala atumiki a Mulungu. Umu ndi m’mene m’bale wina dzina lake Francisco ankamvera. Iye anati: “Ndinadzudzulidwa chifukwa ndinachita chiwerewere. Ngakhale kuti kumayambiriro ndinkapezekabe pamisonkhano, ndinkavutika maganizo n’kumadziona kuti sindingakhale mtumiki wa Yehova. Ndinkadziimba mlandu kwambiri ndipo ndinkakayikira ngati Yehova anandikhululukiradi. Kenako ndinasiya kusonkhana.” Kodi mumamva bwanji mukaganizira za abale ndi alongo amene amakumana ndi mavuto amene takambirana m’ndimezi? Kodi mumawamvera chisoni? Nanga Yehova amamva bwanji akaganizira za atumiki akewa?

YEHOVA AMAKONDA ATUMIKI AKE

Abusa a ku Isiraeli ankadera nkhawa kwambiri nkhosa imene yasochera (Onani ndime 8-9) *

8. Kodi Yehova amaiwala anthu amene anamutumikirapo? Fotokozani.

8 Yehova saiwala anthu amene anamutumikirapo koma anasiya. Komanso samaiwala zimene anachita pomutumikira. (Aheb. 6:10) Mneneri Yesaya anafotokoza fanizo labwino losonyeza mmene Yehova amasamalirira anthu ake. Iye analemba kuti: “Iye adzaweta gulu lake la nkhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” (Yes. 40:11) Kodi Yehova, yemwe ndi M’busa Wamkulu amamva bwanji mtumiki wake akasiya kumutumikira? Yesu anafotokoza mmene Yehova amamvera pamene anafunsa ophunzira ake kuti: “Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo? Akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwera kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasochera zija.”​—Mat. 18:12, 13.

9. Kodi abusa abwino ankasamalira bwanji nkhosa zawo? (Onani chithunzi chapachikuto.)

9 N’chifukwa chiyani tingayerekezere Yehova ndi m’busa? Chifukwa chakuti m’nthawi zakale, m’busa wabwino ankakonda kwambiri nkhosa zake. Mwachitsanzo, Davide analimbana ndi mkango komanso chimbalangondo pofuna kuteteza nkhosa zake. (1 Sam. 17:34, 35) M’busa wabwino sangalephere kudziwa ngati nkhosa yake yasowa, ngakhale itakhala imodzi yokha. (Yoh. 10:3, 14) M’busa wotereyu angasiye nkhosa zake 99 pamalo otetezeka kaya m’khola kapena kusiyira abusa anzake n’kupita kukafunafuna nkhosa yosowayo. Yesu anagwiritsa ntchito fanizoli pofuna kutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri. Iye anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”​—Mat. 18:14.

Abusa a ku Isiraeli ankadera nkhawa kwambiri nkhosa imene yasochera (Onani ndime 9)

YEHOVA AMAFUNAFUNA NKHOSA ZAKE

10. Mogwirizana ndi Ezekieli 34:11-16, kodi Yehova analonjeza kuti adzachita chiyani ndi nkhosa zake zosochera?

10 Yehova amatikonda tonsefe kuphatikizapo anthu amene asiya kumutumikira. Kudzera mwa mneneri Ezekieli, Mulungu analonjeza kuti adzafunafuna nkhosa zake zosochera n’kuzithandiza kuti zikhalenso naye pa ubwenzi wabwino. Ndipo iye anafotokoza zimene adzachite pofuna kupulumutsa atumiki akewo. Zimene anafotokozazo ndi zomwenso m’busa wachiisiraeli ankachita ngati nkhosa yake yasowa. (Werengani Ezekieli 34:11-16.) Choyamba, m’busa ankasakasaka nkhosayo, zimene zinkafunika nthawi yambiri komanso khama. Ndiye akaipeza, amaibweretsa kugulu la nkhosa zake. Kuwonjezera apo, ngati nkhosayo yavulala kapena ili ndi njala, m’busayo ankaithandiza pomanga mabala ake, kuinyamula komanso kuidyetsa. Akulu, omwe ndi abusa a “gulu la nkhosa za Mulungu” ayeneranso kuchita zofanana ndi zimenezi akamathandiza anthu amene asiya kusonkhana. (1 Pet. 5:2, 3) Akulu amafufuza anthu amenewa, kuwathandiza kuti abwerere mumpingo komanso kuwasonyeza chikondi powathandiza kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova. *

11. Kodi m’busa wabwino ankadziwa chiyani?

11 M’busa wabwino ankadziwa kuti nkhosa ikhoza kusochera. Choncho nkhosa ikasiyana ndi zinzake, sankaichitira nkhanza. Tiyeni tione chitsanzo chimene Yehova anasonyeza pothandiza atumiki ake ena omwe kwa kanthawi anasiya kuchita zimene iye anawauza.

12. Kodi Yehova anathandiza bwanji Yona?

12 Nthawi ina mneneri Yona sanamvere zimene Yehova anamuuza kuti apite ku Nineve. Ngakhale zinali choncho, Yehova sanamusiye. Monga m’busa wabwino, anamuthandiza kuti apezenso mphamvu zimene ankafunikira kuti akwaniritse utumiki wake. (Yona 2:7; 3:1, 2) Kenako iye anagwiritsa ntchito chomera cha mtundu wamphonda pofuna kuthandiza Yona kumvetsa kuti moyo wa munthu aliyense ndi wofunika kwambiri. (Yona 4:10, 11) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani? Akulu sayenera kutaya mtima msanga akamathandiza anthu amene afooka. M’malomwake ayenera kumvetsa chimene chinachititsa kuti anthuwo afooke. Ndiyeno munthuyo akabwerera kwa Yehova, akulu amapitiriza kumusonyeza chikondi komanso kuti amamuganizira.

13. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Yehova anachita ndi wolemba Salimo 73?

13 Munthu amene analemba Salimo 73, nthawi ina anakhumudwa poona kuti anthu oipa ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino. Iye anayamba kukayikira ngati kutumikira Mulungu kunali ndi phindu lililonse. (Sal. 73:12, 13, 16) Ndiye kodi Yehova anachita chiyani? Iye sanamuone ngati munthu woipa. M’malomwake Mulungu anachititsa kuti mawu a wolemba masalimoyu alembedwe m’Baibulo. Kenako, wolemba masalimoyu anazindikira kuti palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. (Sal. 73:23, 24, 26, 28) Ndiye kodi tikuphunzirapo chiyani? Akulu asamafulumire kuweruza anthu amene ayamba kukayikira ngati kutumikira Yehova kuli kwa phindu. M’malo mowaona ngati anthu oipa, akulu ayenera kumvetsa chimene chikuchititsa anthuwo kulankhula kapena kuchita zinthu mwa njira imeneyo. Kenako ndi pamene angapeze mfundo za m’Malemba zimene angagwiritsire ntchito powalimbikitsa.

14. N’chifukwa chiyani Eliya ankafunika kuthandizidwa, nanga Yehova anamuthandiza bwanji?

14 Mneneri Eliya anathawa, Mfumukazi Yezebeli atamuopseza kuti amupha. (1 Maf. 19:1-3) Iye anaganiza kuti iye yekha ndi amene anali mneneri wa Yehova ndipo anaganiza kuti zonse zomwe anachita zinali zopanda phindu. Eliya anapanikizika kwambiri moti analakalaka atangofa. (1 Maf. 19:4, 10) Yehova sanamudzudzule koma anamutsimikizira kuti sanali yekha. Anamulimbikitsa kuti azimudalira chifukwa anali adakali ndi ntchito yambiri yoti agwire. Yehova anamvetsera Eliya moleza mtima komanso anamupatsa utumiki wina. (1 Maf. 19:11-16, 18) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tonsefe, makamaka akulu, tiyenera kuchita zinthu mokoma mtima ndi Akhristu anzathu. Munthu akamafotokoza kuti wakhumudwa ndi zinazake kapena akamakayikira ngati Mulungu angamukhululukiredi, akulu ayenera kumumvetsera moleza mtima. Komanso ayenera kumutsimikizira kuti Yehova amamukonda.

KODI NKHOSA ZA YEHOVA ZOMWE ZINASOCHERA TIZIZIONA BWANJI?

15. Mogwirizana ndi Yohane 6:39, kodi Yesu ankaona bwanji nkhosa za Atate wake?

15 Kodi Yehova amafuna kuti nkhosa zake zomwe zinasochera tiziziona bwanji? Tingaphunzire pa zomwe Yesu anachita. Yesu ankadziwa kuti nkhosa zonse za Yehova ndi zamtengo wapatali. Choncho ankachita zonse zomwe akanatha kuti athandize “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli” kuti zibwerere kwa Yehova. (Mat. 15:24; Luka 19:9, 10) Komanso chifukwa chakuti Yesu anali m’busa wabwino, ankachita zonse zomwe akanatha kuti nkhosa iliyonse ya Yehova isatayike.​—Werengani Yohane 6:39.

16-17. Kodi akulu ayenera kuona bwanji ntchito yothandiza anthu omwe asochera? (Onani bokosi lakuti “Mmene Nkhosa Yosochera Imamvera.”)

16 Mtumwi Paulo analimbikitsa akulu a mpingo wa ku Efeso kuti azitsanzira Yesu. Anawauza kuti: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.’” (Mac. 20:17, 35) Lembali likusonyeza kuti masiku anonso akulu ali ndi udindo wofunika kwambiri wosamalira nkhosa za Mulungu. Mkulu wina ku Spain ananena kuti: “Ndimaona kuti Yehova amadera nkhawa nkhosa zake zosochera ndipo zimenezi zimandilimbikitsa kuti inenso ndichite zonse zomwe ndingathe kuti ndithandize nkhosazi. Ndimadziwa kuti umenewu ndi udindo umene Yehova anandipatsa.”

17 Anthu onse omwe anasiya kutumikira Yehova omwe atchulidwa munkhaniyi, anathandizidwa ndipo anabwereranso kwa Yehova. Palinso ambiri omwe anasochera ndipo akufuna kubwerera. Nkhani yotsatira idzafotokoza zomwe tingachite powathandiza kuti abwererenso kwa Yehova.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

^ ndime 5 Kodi n’chifukwa chiyani anthu ena omwe akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, amafooka kapenanso kusiya kumutumikira? Kodi Mulungu amawaona bwanji anthuwa? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa. Itithandizanso kuona mmene Yehova anathandizira anthu ena akale omwe nthawi ina sanachite zimene anawauza.

^ ndime 2 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Wofalitsa amaonedwa kuti ndi wofooka ngati sanapereke malipoti ake autumiki kwa miyezi 6 kapena kuposerapo. Komabe anthu amenewa timawaonabe kuti ndi abale ndi alongo athu ndipo timawakonda kwambiri.

^ ndime 4 Mayina ena asinthidwa.

^ ndime 10 Nkhani yotsatira idzafotokoza mmene akulu angachitire zimenezi.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Abusa a ku Isiraeli ankadera nkhawa nkhosa yomwe yasochera. Ankaifufuza ndi kuithandiza kuti ibwererenso ku nkhosa zinzake. Abusa auzimu masiku ano amachitanso chimodzimodzi.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Mlongo wina wofooka ali m’basi ndipo akudikirira kuti inyamuke. Kenako akuona banja lina lomwe likulalikira mosangalala m’malo opezeka anthu ambiri.