Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 23

“Dzina Lanu Liyeletsedwe”

“Dzina Lanu Liyeletsedwe”

“Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo mpaka kalekale.”—SAL. 135:13.

NYIMBO 10 Tamandani Yehova, Mulungu Wathu!

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Ni nkhani ziti zimene ife Mboni za Yehova timaona kuti n’zofunika kwambili?

PALI nkhani zofunika kwambili zimene zikutikhudza masiku ano. Yoyamba ni ya ulamulilo wa Yehova, ndipo ina ni ya kuyeletsedwa kwa dzina lake. Pokhala Mboni za Yehova, timakondwela kukambilana nkhani zofunika kwambili zimenezi. Koma sikuti nkhani zimenezi, ya ulamulilo wa Yehova komanso ya kuyeletsedwa kwa dzina lake, n’zosiyana ayi, n’zogwilizana kwambili.

2 Ife tonse tidziŵa kuti dzina la Mulungu lifunika kuyeletsedwa. Tidziŵanso kuti ulamulilo wake uyenela kudziŵika kuti ndiwo wabwino koposa. Nkhani zonsezi n’zofunika kwambili kwa ife.

3. Kodi dzina la Yehova limaphatikizapo ciani?

3 Dzina la Yehova limaphatikizapo ciliconse cokhudza Mulungu. Limaphatikizaponso kalamulidwe kake. Conco tikakamba kuti kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova n’kofunika kwambili, ndiye kuti tikutanthauzanso kuti ulamulilo wake uyenela kudziŵika kuti ndiwo wabwino koposa. Dzina la Yehova n’logwilizana kwambili na kalamulidwe kake monga Mfumu yamphamvuzonse.—Onani bokosi lakuti “ Mbali Zosiyana-siyana za Nkhani Yaikulu.”

4. Kodi lemba la Salimo 135:13 limakamba ciani ponena za dzina la Mulungu? Nanga tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?

4 Dzina lakuti Yehova n’lapadela kwambili. (Ŵelengani Salimo 135:13.) N’cifukwa ciani dzina la Mulungu limeneli n’lofunika kwambili? Kodi dzinali linadetsedwa bwanji paciyambi? Kodi Mulungu wakhala akucita ciani poyeletsa dzina lake? Nanga ife tingathandize bwanji kuyeletsa dzina limeneli? Tiyeni tikambilane mafunso amenewa.

KUFUNIKA KWA DZINA

5. Kodi ena angafunse funso lotani akamvela zakuti dzina la Mulungu lifunika kuyeletsedwa?

5 Yesu anati: “Dzina lanu liyeletsedwe.” (Mat. 6:9) Ici n’cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene iye anakamba kuti tiyenela kupemphelela. Koma kodi mawu amene Yesu anakamba akuti “dzina lanu liyeletsedwe” atanthauza ciani? Kuyeletsa cinthu kumatanthauza kucipangitsa kukhala cosadetsedwa kapena kuti caukhondo. Ena angafunse kuti, ‘Popeza kuti dzina la Mulungu n’loyela kale, n’cifukwa ciani lifunika kuyeletsedwa?’ Kuti tiyankhe funsoli, coyamba tiyenela kudziŵa kuti dzina n’ciani maka-maka.

6. N’ciani cimapangitsa dzina kukhala lofunika kwambili?

6 Dzina silitanthauza cabe mawu oitanila munthu kapena zilembo zongolembedwa pa pepala. Onani zimene Baibo imakamba. Imati: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi cuma coculuka.” (Miy. 22:1; Mlal. 7:1) Kodi n’cifukwa ciani dzina n’lofunika kwambili? Cifukwa cakuti limaphatikizapo mbili ya munthu, kutanthauza mmene anthu ena amamuonela mwini dzinalo. Conco cofunika kwambili si mmene dzina limalembedwela kapena mmene limachulidwila ayi, koma mmene anthu amaganizila akamvela dzinalo kapena akaliona.

7. Kodi anthu amadetsa bwanji dzina la Mulungu?

7 Anthu akamakamba mabodza ponena za Yehova, ndiye kuti akuipitsa mbili yake. Ndipo akaipitsa mbili yake, ndiye kutinso akudetsa dzina lake. Nthawi yoyamba pamene dzina la Mulungu linadetsedwa munali m’munda wa Edeni. Tsopano tiyeni tione zimene zinacitika panthawiyo na kukambilana zimene tingaphunzilepo.

NTHAWI YOYAMBA PAMENE DZINA LA MULUNGU LINADETSEDWA

8. N’ciani cimene Adamu na Hava anali kudziŵa? Nanga pakubuka mafunso ati?

8 Adamu na Hava anali kulidziŵa dzina la Mulungu lakuti Yehova. Anali kudziŵanso zinthu zambili zofunika zokhudza Yehovayo. Mwacitsanzo, anali kudziŵa kuti iye ni Mlengi, amene anawapatsa moyo, malo okhala okongola, komanso banja labwino. (Gen. 1:26-28; 2:18) Koma kodi iwo anapitiliza kuganizila zinthu zimene Yehova anawacitila? Kodi anapitiliza kukulitsa ciyamikilo cawo na cikondi cawo pa Yehova? Mayankho pa mafunso amenewa anadziŵika pamene mdani wa Mulungu anawayesa.

9. Mogwilizana na Genesis 2:16, 17 na 3:1-5, kodi Yehova anawauza ciani anthu aŵili oyamba? Nanga Satana anapotoza bwanji coonadi?

9 Ŵelengani Genesis 2:16, 17 na 3:1-5. Kupitila mwa njoka, Satana anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Pa funso limeneli, panali mfundo yabodza imene inapangitsa Hava kuyamba kukayikila Mulungu. M’ceni-ceni, Mulungu anauza Adamu na Hava kuti angadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamo, kupatulako umodzi cabe. Mitengo imene iwo anauzidwa kuti azidya zipatso zake iyenela kuti inali yambili-mbili komanso yosiyana-siyana. (Gen. 2:9) Ndithudi, Yehova ni wowolowa manja kwambili. Komabe, panali mtengo umodzi umene Mulungu anauza Adamu na Hava kuti asadye zipatso zake. Conco funso limene Satana anafunsa linali lopotoza coonadi. Linapangitsa Adamu na Hava kuganiza kuti Mulungu ni womana. N’kutheka kuti mumtima mwake Hava anayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndiye kuti Mulungu akutimana zinazake zabwino?’

10. Kodi Satana anaipitsa bwanji dzina la Mulungu? Nanga zotulukapo zake zinali zotani?

10 Pamene Satana anafunsa Hava funso limenelo, Hava anali akali na mtima wofuna kumvela Yehova. Conco, iye poyankha Satana, anabwelezanso lamulo lomveka bwino limene Yehova anawapatsa. Hava anakambanso kuti Mulungu anawauza kuti asaukhudze n’komwe mtengowo. Iye anali kukumbukila zimene Mulungu anawauza zakuti ngati sadzamumvela adzafa. Koma Satana anati: “Kufa simudzafa ayi.” (Gen. 3:2-4) Apa Satana tsopano anayamba kukamba bodza mosapita m’mbali. Anaipitsa dzina la Mulungu mwa kuuza Hava kuti Yehova ni wabodza. Mwa ici, Satana anakhala Mdyelekezi, kapena kuti woneneza. Hava ananyengeka kothelatu. Anakhulupilila zimene Satana anamuuza. (1 Tim. 2:14) Iye anakhulupilila kwambili Satana kuposa Yehova. Izi zinacititsa kuti Hava apange cosankha colakwika kwambili. Anasankha kusamvela Yehova, moti anadya cipatso cimene Yehova anawauza kuti asadye. Pambuyo pake, anapatsako Adamu.—Gen. 3:6.

11. Kodi makolo athu oyamba anafunika kucita ciani?

11 Bwanji tiyelekezele kuti Hava anayankha Satana kuti: “Sinikudziŵa iwe, koma Atate wanga, Yehova, nimawadziŵa, komanso nimawakonda na kuwakhulupilila. Iwo ndiwo anapatsa ine na mwamuna wanga zonse zimene tili nazo. Nanga n’cifukwa ciani ukuwanena? Coka apa!” Hava akanakamba conco, sembe anaonetsa kuti anali wokhulupilika komanso kuti anali kuwakonda Atate wake. Ndipo kukamba zoona, Yehova akanakondwela kwambili kumva mwana wake wamkazi akukamba mawu ngati amenewa. (Miy. 27:11) Koma onse aŵili, Adamu na Hava, sanali kum’konda Yehova Atate wawo. Pa cifukwa cimeneci, analephela kuikila kumbuyo dzina la Yehova pamene Satana anali kum’kambila zoipa.

12. Kodi Satana anapangitsa bwanji Hava kuyamba kukayikila Mulungu? Nanga Adamu na Hava analephela kucita ciani?

12 Monga taonela, Satana ponyengelela Hava, anayamba mwa kum’pangitsa kukhala na maganizo okayikila. Iye anakamba mawu amene anacititsa Hava kuyamba kukayikila zakuti Yehova ni Tate wabwino. Ndiyeno, Adamu na Hava analephela kuikila kumbuyo dzina la Yehova pamene Satana anali kum’kambila mabodza. Izi zinapangitsa kuti agonjele Satana mosavuta na kupandukila Atate wawo. Masiku ano, Satana amacitanso zofanana na zimenezi. Amaipitsa dzina la Yehova mwa kukamba mabodza ponena za iye. Cifukwa cokhulupilila mabodza a Satana, anthu amakana ulamulilo wolungama wa Yehova.

YEHOVA ADZAYELETSA DZINA LAKE

13. Malinga na Ezekieli 36:23, kodi mfundo yaikulu m’Baibo ni yotani?

13 Kodi Yehova sacitapo kanthu kuti ayeletse dzina lake limene linadetsedwa? Amacitapo kanthu, moti Baibo yonse imakamba zimene Yehova wakhala akucita pofuna kuyeletsa dzina lake limene linadetsedwa mu Edeni. (Gen. 3:15) Tingakambe kuti mfundo yaikulu m’Baibo ni yakuti: Yehova adzayeletsa dzina lake poseŵenzetsa Ufumu wake wolamulidwa na Mwana wake, ndipo adzabwezeletsa cilungamo na mtendele padziko lapansi. Zimene Baibo imakamba zimatithandiza kumvetsetsa mmene Yehova adzayeletsela dzina lake.—Ŵelengani Ezekieli 36:23.

14. Kodi zimene Yehova anacita pamene Satana ndi anthu anam’pandukila mu Edeni, zathandiza bwanji poyeletsa dzina lake?

14 Satana wakhala akucita zilizonse zimene angathe kuti alepheletse Yehova kukwanilitsa colinga cake. Koma walephela. Baibo imafotokoza zimene Yehova wakhala akucita, ndipo imaonetsa kuti palibe wolamulila wina wacikondi komanso wabwino monga Atate wathu, Yehova Mulungu. N’zoona kuti kupanduka kwa Satana na onse amene asankha kukhala kumbali yake kumamuŵaŵa kwambili Yehova. (Sal. 78:40) Ngakhale n’conco, pofuna kuthetsa nkhaniyi, iye wacita zinthu mwanzelu, moleza mtima, komanso mwacilungamo. Iye wacitanso zinthu zambili zoonetsa kuti ni wamphamvuzonse. Koposa zonse, cikondi cake cimaonekela m’zocita zake zonse. (1 Yoh. 4:8) Ndipo Yehova akupitilizabe kuyeletsa dzina lake.

Satana anauza Hava mabodza ponena za Yehova, ndipo kwa zaka zambili iye wapitilizabe kumukambila zoipa Mulungu (Onani ndime 9-10, 15) *

15. Kodi Satana amaipitsa bwanji dzina la Mulungu masiku ano? Nanga zotulukapo zake zakhala zotani?

15 Satana akupitilizabe kudetsa dzina la Mulungu masiku ano. Iye amapangitsa anthu kukayikila zakuti Mulungu ni wamphamvu, wacilungamo, wanzelu, komanso wacikondi. Mwacitsanzo, amacititsa anthu kukayikila zakuti Yehova ni Mlengi. Ndipo anthu amene amakhulupilila kuti Mulungu aliko, Satana amawapangitsa kuona kuti Mulunguyo ni woumitsa zinthu komanso wopanda cilungamo. Amawapangitsanso kuona kuti mfundo zake n’zovuta kuzitsatila. Kuposa pamenepa, Satana amaphunzitsa anthu kuti Yehova ni Mulungu wopanda cifundo komanso wankhanza, amene amashoka anthu ku moto wa helo. Anthu akakhulupilila mabodza amenewa, cimakhala cosavuta kwa iwo kukana ulamulilo wa Yehova. Satana sadzaleka kumunenela zoipa Yehova mpaka pamene adzawonongedwa. Ndipo na imwe adzayesetsa kukupatutsani kuti muleke kumvela Yehova. Kodi mudzalola kuti akugonjetseni?

UDINDO WANU POTHANDIZA KUTHETSA NKHANI YAIKULU

16. N’ciani cimene mungacite comwe Adamu na Hava analephela kucita?

16 Yehova anapatsa anthu opanda ungwilo mwayi wothandiza kuyeletsa dzina lake. Motelo, mungakwanitse kucita zimene Adamu na Hava analephela kucita. Olo kuti tikhala m’dziko lodzala ndi anthu amene amanyoza dzina la Yehova na kulidetsa, tili na mwayi woikila kumbuyo dzina lake mwa kuuza anthu kuti iye ni woyela, wolungama, wabwino, komanso wacikondi. (Yes. 29:23) Tilinso na mwayi wocilikiza ulamulilo wake. Tingatelo mwa kuthandiza anthu kuona kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wokha wabwino, umene udzapangitsa kuti m’cilengedwe conse mukhale mtendele na cimwemwe.—Sal. 37:9, 37; 146:5, 6, 10.

17. Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu kudziŵa dzina la Atate wake?

17 Ngati tiikila kumbuyo dzina la Yehova, ndiye kuti tikutengela citsanzo ca Yesu Khristu. (Yoh. 17:26) Yesu anathandiza anthu kudziŵa dzina la Atate wake mwa kulichula, ndiponso mwa kuphunzitsa anthu coonadi ponena za Yehova. Mwacitsanzo, anatsutsa Afarisi amene anali kupangitsa anthu kuona kuti Yehova ni wankhanza, woumitsa zinthu, wosaganizila ena, komanso wopanda cifundo. Yesu anathandiza anthu kudziŵa kuti Atate wake ni wololela, woleza mtima, wokhululuka, komanso wacikondi. Cinanso, Yesu anali kucita zinthu motengela kwambili Atate wake. Mwa njila imeneyi, anathandiza anthu kum’dziŵa bwino Yehova.—Yoh. 14:9.

18. Tingacite ciani kuti tithandize kuyeletsa dzina la Yehova?

18 Mofanana na Yesu, nafenso tingauzeko ena zimene timadziŵa ponena za Yehova. Tingawaphunzitse kuti iye ni Mulungu wacikondi komanso wokoma mtima kwambili. Tikatelo, timathandiza anthu kuona kuti zinthu zoipa zimene ena amakamba ponena za Yehova n’zabodza. Komanso ndiye kuti tikuyeletsa dzina la Yehova, cifukwa timathandiza anthu kuliona kuti ni loyela. Tingayeletsenso dzina la Yehova mwa kutengela citsanzo cake. Zimenezi n’zotheka olo kuti ndise opanda ungwilo. (Aef. 5:1, 2) Ngati mwa zokamba na zocita zathu timathandiza anthu kum’dziŵa bwino Yehova, ndiye kuti tikuthandiza kuyeletsa dzina lake. Kuwonjezela apo, timayeletsa dzina limeneli mwa kuthandiza anthu kudziŵa coonadi ponena za Mulungu. * Timayeletsanso dzinali mwa kukhalabe okhulupilika ngakhale kuti ndife opanda ungwilo.—Yobu 27:5.

Tiyenela kuthandiza ophunzila Baibo athu kudziŵa kuti Yehova ni wokoma mtima komanso wacikondi (Onani ndime 18-19) *

19. Malinga na Yesaya 63:7, kodi colinga cathu cacikulu pophunzitsa anthu ciyenela kukhala ciani?

19 Palinso cina cimene tingacite pothandiza kuyeletsa dzina la Yehova. Pamene tiphunzitsa ena coonadi ca m’Baibo, timagogomezela kwambili za ulamulilo wa Mulungu. Timakamba kuti iye ndiye woyenela kulamulila cilengedwe conse, ndipo mfundo imeneyi ni yosatsutsika. Kuphunzitsa anthu malamulo a Mulungu n’kofunika kwambili. Koma colinga cathu cacikulu powaphunzitsa ni kuwathandiza kuti ayambe kukonda Yehova, Atate wathu, ndiponso kuti akhale okhulupilika kwa iye. Cotelo, pamene tikuphunzitsa anthu za Yehova, tifunika kugogomezela pa makhalidwe ake abwino kuti am’dziŵe kuti ni Mulungu wotani kweni-kweni. (Ŵelengani Yesaya 63:7.) Tikamaphunzitsa mwa njila imeneyi, timathandiza anthu kuyamba kum’konda Yehova. Zikatelo, amayamba kumumvela cifukwa cofuna kukhala okhulupilika kwa iye.

20. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Kodi tingacite ciani kuti makhalidwe athu na kaphunzitsidwe kathu zithandize kuyeletsa dzina la Yehova, komanso kuti zithandize anthu ena kuyamba kum’konda? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.

NYIMBO 2 Dzina Lanu Ndimwe Yehova

^ ndime 5 Kodi ni nkhani yofunika kwambili iti imene ikhudza anthu onse na angelo? N’cifukwa ciani nkhani imeneyo ni yofunika kwambili? Nanga ise tingacite ciani pothandiza kuthetsa nkhani imeneyo? Kudziŵa mayankho pa mafunso amenewa ndi ena okhudzana na nkhaniyo kungatithandize kulimbitsa ubale wathu na Yehova.

^ ndime 18 Nkhani ya kuyeletsa dzina la Yehova inafotokozedwa pa msonkhano wapacaka wa mu 2017.—Mvetselani pulogilamu ya JW Broadcasting ya January 2018 pa jw.org®. Pitani pa LAIBULALE > JW BROADCASTING®.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mdyelekezi ananeneza Mulungu. Anauza Hava kuti Mulungu ni wabodza. Kwa zaka zambili, Satana wakhala akufalitsa mabodza, monga lakuti Mulungu ni wankhanza. Komanso kupitila m’ciphunzitso ca cisanduliko, Satana amaphunzitsa anthu kuti Mulungu sindiye analenga anthu.

^ ndime 64 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene m’bale akutsogoza phunzilo la Baibo, akugogomezela pa makhalidwe a Mulungu.