Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 24

“Ndipatseni Mtima Wosagawanika Kuti Ndiope Dzina Lanu”

“Ndipatseni Mtima Wosagawanika Kuti Ndiope Dzina Lanu”

“Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu. Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.”—SAL. 86:11, 12.

NYIMBO 7 Yehova Ndiye Mphamvu Zathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi kuopa Mulungu n’kutani? Nanga n’cifukwa ciani anthu okonda Yehova afunika kumuopa?

IFE Akhristu timamukonda Mulungu komanso timamuopa. Kwa ena, mfundo imeneyi ingaoneke monga yodzitsutsa. Komabe, pano sitikukamba za mantha amene timakhala nawo cifukwa coopa cinthu cinacake coopsa. M’nkhani ino, tikambilana za mantha enaake apadela—mantha oopa Mulungu. Kuopa Mulungu ni mantha amene anthu amakhala nawo cifukwa cakuti amamulemekeza kwambili. Iwo safuna kucita zinthu zokhumudwitsa Atate wawo wakumwamba cifukwa safuna kuwononga ubwenzi wawo na iye.—Sal. 111:10; Miy. 8:13.

2. Malinga na mawu a Mfumu Davide pa Salimo 86:11, kodi tikambilana zinthu ziŵili ziti?

2 Ŵelengani Salimo 86:11. Mukaganizila mawu amenewa, mungathe kuona kuti Mfumu yokhulupilika Davide anali kudziŵa kuti kuopa Mulungu n’kofunika kwambili. Tsopano tiyeni tikambilane mmene tingaseŵenzetsele mfundo imene Davide anakamba pa lembali. Coyamba, tiona zifukwa zina zimene tiyenela kuopela dzina la Mulungu. Caciŵili, tikambilana mmene tingaonetsele kuti timaopa dzina la Mulungu mu umoyo wathu wa tsiku na tsiku.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUOPA DZINA LA YEHOVA?

3. Ni cocitika citi cimene ciyenela kuti cinathandiza Mose kupitilizabe kuopa dzina la Mulungu?

3 Ganizilani mmene Mose anamvelela pamene anali m’phanga n’kuona ulemelelo wa Yehova ukudutsa. Buku la Insight on the Scriptures limakamba kuti zimene Mose anaona “zinali zocititsa mantha kwambili. Ndipo palibe munthu amene anali ataonapo masomphenya aconco Yesu Khristu asanabwele padziko lapansi.” Mose anamva mawu amene ayenela kuti anakambidwa na mngelo. Mawuwo anali akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo.” (Eks. 33:17-23; 34:5-7) Mosakayikila, Mose anali kukumbukila masomphenyawo akachula dzina la Yehova. Conco n’zosadabwitsa kuti pambuyo pake, iye anauza anthu a Mulungu Aisiraeli kuti ‘aziopa dzina laulemelelo ndi locititsa manthali.’—Deut. 28:58.

4. Kodi tiyenela kuganizila za makhalidwe ati a Yehova kuti tizimuopa kwambili?

4 Poganizila za dzina la Yehova, tingacitenso bwino kusinkha-sinkha za makhalidwe ake. Tiyenela kusinkha-sinkha za makhalidwe ake monga mphamvu, nzelu, cilungamo, na cikondi cake. Kuganizila makhalidwe amenewa na ena kungatithandize kuti tizimuopa kwambili Mulungu.—Sal. 77:11-15.

5-6. (a) Kodi dzina la Mulungu limatanthauza ciani? (b) Kulingana na Ekisodo 3:13, 14 komanso Yesaya 64:8, kodi Yehova amapangitsa zinthu kucitika m’njila ziti?

5 Kodi dzina la Mulungu limatanthauza ciani? Akatswili ambili amati dzina la Yehova limatanthauza kuti, “Amacititsa Kukhala.” Tanthauzo limeneli limatikumbutsa kuti palibe ciliconse cimene cingalepheletse Yehova kucita zimene afuna, komanso kuti angapangitse zinthu kucitika. Motani?

6 Yehova amapangitsa zinthu kucitika mwa kukhala ciliconse cimene afuna, kuti akwanilitse colinga cake. (Ŵelengani Ekisodo 3:13, 14.) Nthawi zambili, takhala tikulimbikitsidwa kuti tiziganizila mbali yocititsa cidwi imeneyi ya mmene Mulungu alili. Yehova angacititsenso atumiki ake opanda ungwilo kukhala ciliconse cimene iye afuna kuti am’tumikile na kukwanilitsa colinga cake. (Ŵelengani Yesaya 64:8.) Mwa njila zimenezi, Yehova amapangitsa cifunilo cake kucitika. Ndipo palibe cimene cingamulepheletse kukwanilitsa zolinga zake.—Yes. 46:10, 11.

7. Tingacite ciani kuti tizimulemekeza kwambili Atate wathu wakumwamba?

7 Tingacite ciani kuti tizimulemekeza kwambili Atate wathu wakumwamba? Tingatelo mwa kusinkha-sinkha pa zimene iye wacita komanso zimene watithandiza kucita. Mwacitsanzo, tikamasinkha-sinkha pa zinthu zodabwitsa za m’cilengedwe, timacita cidwi kwambili poona zimene Yehova wacita. (Sal. 8:3, 4) Ndipo ngati tiganizila pa zimene Yehova watithandiza kucita pokwanilitsa cifunilo cake, timayamba kumulemekeza kwambili. Ndithudi, dzina la Yehova n’lofunika kulilemekeza kwambili! Dzinali limaphatikizapo zonse zokhudza mmene Atate wathu alili, zonse zimene wacita, komanso zonse zimene adzacita kutsogolo.—Sal. 89:7, 8.

“NDIDZALENGEZA DZINA LA YEHOVA”

Zimene Mose anali kuphunzitsa zinali zotsitsimula. Iye pophunzitsa anali kukamba kwambili za dzina la Yehova Mulungu komanso makhalidwe ake (Onani ndime 8) *

8. Kodi lemba la Deuteronomo 32:2, 3 lionetsa kuti Yehova amafuna kuti anthu azicita nalo ciani dzina lake?

8 Aisiraeli atangotsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anam’phunzitsa nyimbo Mose. (Deut. 31:19) Nayenso Mose anafunika kuphunzitsako Aisiraeli nyimboyo. (Ŵelengani Deuteronomo 32:2, 3.) Tikaganizila mawu a mu vesi 2 na 3, tingathe kuona kuti Yehova safuna kuti dzina lake libisike kwa anthu. Safuna kuti anthu aziopa kulichula cifukwa coona kuti n’lopatulika kwambili. Iye amafuna kuti anthu onse na angelo alidziŵe dzina lake. Ndithudi, unali mwayi waukulu kwa Aisiraeli kumvela Mose akuwaphunzitsa za Yehova komanso za dzina lake laulemelelo. Zimene Mose anawaphunzitsa zinalimbitsa cikhulupililo cawo, ndiponso zinawatsitsimula monga mmene mvula yowaza imatsitsimulila zomela. Nanga ife tingacite ciani kuti kaphunzitsidwe kathu kazikhala kolimbikitsa komanso kotsitsimula?

9. Kodi tingathandize bwanji kuyeletsa dzina la Yehova?

9 Polalikila ku nyumba na nyumba kapena pocita ulaliki wapoyela, tiyenela kuonetsa anthu dzina la Mulungu lakuti Yehova poseŵenzetsa Baibo. Ndiponso tingawagaŵile mabuku, mavidiyo, na zinthu zina za pa webusaiti yathu zimene n’zolemekeza Yehova. Tikakhala kunchito, kusukulu, kapena paulendo, tingapeze mpata wouzako ena za Mulungu wathu wacikondi kuti amudziŵe. Tikamauzako ena za colinga ca Yehova kwa anthu komanso dziko lapansi, timawathandiza kuzindikila kuti iye amatikonda kwambili. Timathandizanso kuyeletsa dzina la Mulungu mwa kuuzako ena coonadi ponena za Atate wathu wacikondi. Tikatelo, timawathandiza kuti aleke kukhulupilila mabodza amene anthu ena anawaphunzitsa ponena za Yehova. Coonadi ca m’Baibo cimene timaphunzitsa anthu cimawatsitsimula kwambili.—Yes. 65:13, 14.

10. Pophunzitsa anthu Baibo, n’cifukwa ciani sitiyenela kungowaphunzitsa malamulo na mfundo za Mulungu?

10 Potsogoza maphunzilo a Baibo, tizikhala na colinga cowathandiza kudziŵa dzina la Mulungu lakuti Yehova na kuliseŵenzetsa. Kuwonjezela apo, tiziwathandiza kum’dziŵa bwino Yehova. Koma kodi zimenezi zingatheke ngati ophunzila timangowaphunzitsa cabe malamulo a Mulungu na mfundo zake? Wophunzila Baibo wakhama angaphunzile malamulo a Mulungu na kuwadziŵa bwino, mpaka kuyamba kuwalemekeza kwambili. Koma kodi izi zingamusonkhezele kukonda Yehova na kuyamba kumumvela? Kumbukilani Hava. Iye anali kulidziŵa bwino lamulo la Mulungu. Koma sanam’konde na mtima wonse Mulungu amene anapeleka lamulolo. Adamu nayenso sanali kum’konda Mulungu. (Gen. 3:1-6) Conco, pophunzitsa anthu Baibo, tisamangowaphunzitsa cabe malamulo a Mulungu.

11. Pophunzitsa anthu za malamulo a Mulungu na mfundo zake, tingawathandize bwanji kuyamba kukonda Mulungu amene anapeleka malamulowo?

11 Malamulo a Yehova ni abwino kwambili. (Sal. 119:97, 111, 112) Koma ophunzila Baibo athu sangaone kuti malamulowo ni abwino ngati sanafike pomvetsetsa mfundo yakuti Yehova anaika malamulowo cifukwa cotikonda. Conco tingacite bwino kufunsa ophunzila athu kuti: “Muganiza kuti n’cifukwa ciani Mulungu amauza atumiki ake kuti azicita izi komanso kuti azipewa izi? Kodi zimenezi zionetsa kuti iye ni wotani?” Ngati tiphunzitsa ophunzila Baibo kuti aziganizila za Yehova, ndiponso kuti ayambe kukonda dzina lake laulemelelo, tidzawafika pamtima. Iwo adzayamba kukonda malamulo ake komanso Mulungu amene anapeleka malamulowo. (Sal. 119:68) Adzakhala na cikhulupililo colimba cimene cidzawathandiza kupilila mayeselo okhala ngati moto amene adzakumana nawo kutsogolo.—1 Akor. 3:12-15.

“IFE TIDZAYENDA M’DZINA LA YEHOVA”

Panthawi ina, Davide analola mtima wake kugaŵanika (Onani ndime 12)

12. Kodi pa nthawi ina Davide analephela bwanji kukhala na mtima wosagaŵanika? Nanga panakhala zotulukapo zotani?

12 Pa Salimo 86:11 pali mawu ofunika kwambili akuti “ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” Mfumu Davide ndiye anauzilidwa kulemba mawu amenewa. Mu umoyo wake, iye anadzionela yekha kuti n’capafupi munthu kukhala na mtima wogaŵanika. Mwacitsanzo, nthawi ina pamene anali pa mtenje wa nyumba yake, anaona mkazi wa munthu wina akusamba. Kodi panthawiyo, Davide anakhalabe na mtima wamphumphu kapena kuti wosagaŵanika? Iyai. Iye anali kulidziŵa lamulo la Yehova lakuti, “Usalakelake mkazi wa mnzako.” (Eks. 20:17) Olo zinali conco, cioneka kuti anapitiliza kuyang’ana mkaziyo moti mtima wake unagaŵanika. Iye anali kulaka-laka mkazi uja Bati-seba, ndipo pa nthawi imodzi-modziyo anali kufuna kukondweletsa Yehova. Ngakhale kuti kwa nthawi yaitali Davide anali kukonda Yehova na kumuopa, panthawiyi anagonja ku cilako-lako cadyela, ndipo anacita zinthu zoipa kwambili. Iye anabweletsa citonzo pa dzina la Yehova. Komanso, anabweletsa mavuto aakulu kwa anthu osalakwa, kuphatikizapo a m’banja lake.—2 Sam. 11:1-5, 14-17; 12:7-12.

13. Tidziŵa bwanji kuti mtima wa Davide unakhalanso wathunthu?

13 Yehova anathandiza Davide kuzindikila kuti chimo limene anacita linali lalikulu, ndipo iye analapa moti anakhalanso pa ubale wabwino na Yehova. (2 Sam. 12:13; Sal. 51:2-4, 17) Davide anali kukumbukila mavuto amene anakumana nawo cifukwa colola mtima wake kukhala wogaŵanika. Kodi Yehova anam’thandiza Davide kukhalanso na mtima wosagaŵanika, kapena kuti wathunthu? Inde anamuthandiza. Tikutelo cifukwa patapita nthawi, Yehova anakamba kuti Davide anatumikila “Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.”—1 Maf. 11:4; 15:3.

14. Kodi tiyenela kudzifunsa funso liti? Cifukwa ciani?

14 Citsanzo ca Davide n’colimbikitsa komanso n’coticenjeza. Kugwela kwake m’chimo lalikulu ni cenjezo kwa atumiki a Mulungu masiku ano. Kaya tangoyamba kumene kutumikila Yehova kapena takhala tikum’tumikila kwa nthawi yaitali, tonse tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimayesetsa kukana mayeselo a Satana amene anganipangitse kukhala na mtima wogaŵanika?’

Satana adzayesetsa kutipangitsa kukhala na mtima wogaŵanika. Koma tisamulole! (Onani ndime 15-16) *

15. Kodi kuopa Mulungu kumatiteteza bwanji tikaona zithunzi zoutsa cilakolako ca kugonana?

15 Mwacitsanzo, mukaona cithunzi coutsa cilakolako ca kugonana pa TV kapena pa intaneti, kodi mumacita ciani? Cingakhale cosavuta munthu kuyamba kuganiza kuti cithunzico kapena filimuyo si yoipa kweni-kweni cifukwa sionetselatu zamalisece. Koma filimuyo kapena cithunzico cingakhale cida cimene Satana angaseŵenzetse pofuna kucititsa mtima wathu kukhala wogaŵanika. (2 Akor. 2:11) Cithunzico tingaciyelekezele na nkhwangwa imene munthu amaseŵenzetsa pofuna kupandula cinkhuni cacikulu. Akayamba kucitema, sicipanduka nthawi yomweyo. Koma akacitema mobweleza-bweleza, m’pamene cimapanduka. Mofananamo, munthu akaona zithunzi zoutsa cilakolako ca kugonana, mavuto ake sangaonekele nthawi yomweyo. Koma zimene waonazo zingamupangitse kukhala na mtima wogaŵanika, ndipo pamapeto pake angacite chimo. Conco, musalole kuti maganizo alionse oipa aloŵe mumtima mwanu! Pitilizani kukhala na mtima wathunthu kuti muziopa dzina la Yehova.

16. Tikayesedwa kuti ticite zoipa, ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa?

16 Kuwonjezela pa zithunzi zoipa, Satana amaseŵenzetsanso zinthu zina zambili potiyesa kuti ticite zoipa. Kodi timacita ciani tikayesedwa? N’capafupi kukhala na maganizo odzikhululukila. Mwacitsanzo, tingaganize kuti: ‘Nikacita izi sanganicotse mumpingo. Conco zilibe vuto kweni-kweni.’ Maganizo otelo ni olakwika kwambili. Telo tingacite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi n’kutheka kuti Satana akuseŵenzetsa mayeselo amenewa pofuna kugaŵanitsa mtima wanga? Ngati nagonja ku zilako-lako zoipa, kodi sinidzabweletsa citonzo pa dzina la Yehova? Kodi kucita izi kudzanipangitsa kuyandikila kwambili Mulungu, kapena kudzanipangitsa kutalikilana naye?’ Mungacite bwino kumasinkha-sinkha pa mafunso ngati amenewa. Ndipo pemphani nzelu kwa Mulungu kuti muthe kuyankha mafunso amenewa moona mtima. (Yak. 1:5) Kucita izi kudzakutetezani kwambili. Mudzakwanitsa kukana mayeselo molimba mtima, monga mmene Yesu anacitila pamene anati: “Coka Satana!”—Mat. 4:10.

17. N’cifukwa ciani kukhala na mtima wogaŵanika si kwabwino? Fotokozani citsanzo.

17 Kukhala na mtima wogaŵanika si kwabwino. Tiyelekezele kuti m’timu inayake ya bola muli anthu osagwilizana. Ena afuna kuti anthu azingotamanda iwo basi, enanso safuna kutsatila malamulo pochaya bola, ndiponso ena salemekeza kochi. Mosakayikila, timu yaconco singawine mpikisano. Koma timu imene ni yogwilizana nthawi zambili imawina. Mtima wathu tingauyelekezele na timu yowina imeneyo, malinga ngati zoganiza zathu, mmene timamvelela, komanso zolaka-laka zathu, zonse zikhala zogwilizana na mfundo za Yehova. Musaiŵale kuti Satana amafuna kugaŵanitsa mtima wanu. Amafuna kuti muzilakalaka kucita zinthu zimene mudziŵa kuti Mulungu amaletsa. Koma kuti mupitilize kutumikila Yehova, mufunika kukhala na mtima wosagaŵanika kapena kuti wathunthu. (Mat. 22:36-38) Musalole kuti Satana apangitse mtima wanu kukhala wogaŵanika.

18. Mogwilizana na Mika 4:5, kodi mudzayesetsa kucita ciani?

18 Monga Davide, tiyeni nafenso tizipemphela kwa Yehova kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” Citani zonse zotheka kuti muzicita zinthu mogwilizana na pemphelo limeneli pa umoyo wanu. Tsiku lililonse popanga zosankha, kaya zazing’ono kapena zazikulu, muziyesetsa kuonetsa kuti mumaopa kwambili dzina loyela la Yehova. Mukatelo, monga Mboni ya Yehova, mudzathandiza kuyeletsa dzina la Yehova. (Miy. 27:11) Ndipo tonsefe tidzatha kukamba monga mmene mneneli Mika anakambila kuti: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5.

NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde

^ ndime 5 M’nkhani ino, tikambilana mbali ya pemphelo la Mfumu Davide yopezeka pa Salimo 86:11, 12. Kodi kuopa dzina la Yehova kutanthauza ciani? N’zinthu ziti zimene zimatisonkhezela kuopa dzina lalikulu limeneli? Nanga kuopa Mulungu kungatiteteze bwanji tikayesedwa kuti ticite zoipa?

^ ndime 53 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mose anaphunzitsa Aisiraeli nyimbo yolemekeza Yehova.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Hava anagonja ku cilakolako coipa. Mosiyana na iye, ise timapewa kuona zithunzi kapena kuŵelenga mameseji yoipa amene angatipangitse kukhala na zilakolako zoipa zimene zingabweletse citonzo pa dzina la Mulungu.