Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 27

Musamadziganizire Kuposa Mmene Muyenera Kudziganizira

Musamadziganizire Kuposa Mmene Muyenera Kudziganizira

“Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.”​—AROMA 12:3.

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mogwirizana ndi Afilipi 2:3, kodi kudzichepetsa kumathandiza bwanji kuti tizigwirizana ndi anthu ena?

TIMAMVERA Yehova modzichepetsa chifukwa timadziwa kuti iyeyo amadziwa zimene zingatithandize. (Aef. 4:22-24) Kudzichepetsa kumatithandiza kuona kuti kuchita chifuniro cha Yehova n’kofunika kwambiri kuposa zofuna zathu. Kumatithandizanso kuona kuti anthu ena amatiposa m’njira inayake. Zimenezi zingathandize kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso Akhristu anzathu.​—Werengani Afilipi 2:3.

2. Kodi zimene mtumwi Paulo ananena zimasonyeza chiyani, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Ngati sitingasamale tikhoza kusokonezedwa ndi anthu a m’dziko la Satanali, omwe ndi onyada komanso odzikonda. * Zikuoneka kuti Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi anatengera makhalidwe oipawa. Tikutero chifukwa mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu a ku Roma n’kuwauza kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.” (Aroma 12:3) Pamenepa Paulo anasonyeza kuti anthufe timafunikabe kudziganizira. Koma tiyenera kukhala odzichepetsa kuti tizidziona moyenera. Munkhaniyi tikambirana mmene kudzichepetsa kungatithandizire kupewa mtima wonyada m’mbali zitatu izi: (1) m’banja mwathu, (2) tikapatsidwa utumiki winawake komanso (3) pa nkhani ya zithunzi, mavidiyo ndi nkhani zomwe timaika pa intaneti.

MUZIKHALA ODZICHEPETSA M’BANJA MWANU

3. N’chifukwa chiyani anthu angasemphane maganizo m’banja, nanga ena amachita chiyani pofuna kuthetsa mavuto awo?

3 Yehova amafuna kuti mwamuna ndi mkazi azisangalala m’banja. Koma popeza siife angwiro, nthawi zina tingasemphane maganizo. Ndipotu Paulo analemba kuti anthu amene ali m’banja adzakumana ndi mavuto ena. (1 Akor. 7:28) Ena amangokhalira kukangana ndi mkazi kapena mwamuna wawo ndipo amaona kuti mwina sanasankhe bwino. Ndiye akalola kusokonezedwa ndi maganizo a m’dziko la Satanali, amaona kuti ndi bwino angothetsa banja. Iwo amangoganiza za iwo okha ndipo amaona kuti kuthetsa banja lawo kungawathandize kuti akhale osangalala.

4. Kodi tiyenera kupewa chiyani?

4 Tikakhala ndi mavuto m’banja tiyenera kupewa kuganiza kuti njira yabwino ndi kungolithetsa. Timadziwa kuti Baibulo limavomereza kuti banja likhoza kutha pokhapokha ngati wina wachita chigololo. (Mat. 5:32) Ndiye tikakumana ndi mavuto ngati mmene Paulo analembera, mtima wonyada usamatichititse kuyamba kuganiza kuti: ‘Kodi banja limeneli likundithandiza? Kodi ndikukondedwadi ngati mmene ndinkafunira? Kapena mwina ndingamasangalale nditakwatirana ndi munthu wina?’ Tikamaganiza chonchi, ndiye kuti tikungoganizira zofuna zathu osati za mnzathuyo. Nzeru zadzikoli zimalimbikitsa kuti munthu azingochita zimene mtima wake ukufuna komanso zomwe akuona kuti zichititsa kuti iyeyo azisangalala. Amalolera kuchita zimenezi ngakhale zitachititsa kuti banja lake lithe. Pamene nzeru zochokera kwa Mulungu zimalimbikitsa kuti: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afil. 2:4) Yehova amafuna kuti anthu okwatirana asasiyane. (Mat. 19:6) Ndiponso amafuna kuti muziganizira choyamba zofuna zake osati zanu zokha.

5. Mogwirizana ndi Aefeso 5:33, kodi anthu okwatirana ayenera kuchita chiyani?

5 Anthu okwatirana ayenera kumalemekezana. (Werengani Aefeso 5:33.) Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala opatsa m’malo momangoyembekezera kulandira. (Mac. 20:35) Kodi ndi khalidwe liti limene lingathandize kuti anthu okwatirana azikondana komanso kulemekezana? Khalidwe lake ndi kudzichepetsa. Amuna ndi akazi omwe ndi odzichepetsa samangochita zopindulitsa iwo okha basi koma ‘zopindulitsanso ena.’​—1 Akor. 10:24.

Anthu okwatirana akakhala odzichepetsa salimbana koma amathandizana (Onani ndime 6)

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Steven ndi Stephanie ananena?

6 Kudzichepetsa kwathandiza mabanja ambiri a Chikhristu kuti azikhala osangalala. Mwachitsanzo, mwamuna wina dzina lake Steven anati: “Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuchitira zinthu limodzi, makamaka pakakhala mavuto. M’malo moganizira kuti ‘n’chiyani chingandithandize?’ muziganizira kuti ‘n’chiyani chingatithandize?’” Mkazi wake Stephanie, ananenanso zofanana ndi zimenezi. Iye anati: “Palibe amene amafuna kukhala ndi munthu amene amangokhalira kukangana naye. Ndiye tikasemphana maganizo, timayesetsa kupeza chimene chayambitsa vutolo. Tikatero timapemphera, kufufuza mfundo zimene zingatithandize komanso kukambirana zimene tingachite. Timalimbana ndi vutolo osati kulimbana tokhatokha.” Anthu okwatirana amakhala osangalala ngati aliyense sadziona kuti ndi wofunika kuposa mnzake.

MUZITUMIKIRA YEHOVA “MODZICHEPETSA NTHAWI ZONSE”

7. Kodi m’bale ayenera kuchita chiyani akapatsidwa udindo winawake?

7 Timaona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira Yehova m’njira iliyonse imene tingathe. (Sal. 27:4; 84:10) Ngati m’bale ali ndi mtima wofuna kuchita zambiri potumikira Yehova, ndiye kuti akuchita bwino. Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) Koma m’bale akapatsidwa udindo winawake, sayenera kuyamba kudziganizira kwambiri kuposa mmene ayenera kudziganizira. (Luka 17:7-10) Ayenera kukhala ndi cholinga chotumikira ena modzichepetsa.​—2 Akor. 12:15.

8. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Diotirefe, Uziya ndi Abisalomu anachita?

8 Baibulo limanena za anthu amene ankadziganizira kwambiri kuposa mmene ankayenera kudziganizira. Mmodzi mwa anthuwa ndi Diotirefe, yemwe sanasonyeze mtima wodzichepetsa koma ankakonda kukhala “woyamba” mumpingo. (3 Yoh. 9) Wina ndi Uziya, yemwe chifukwa cha kunyada anagwira ntchito imene sankayenera kugwira. (2 Mbiri 26:16-21) Winanso ndi Abisalomu, yemwe ankanamizira kuti amakonda anthu pofuna kuwakopa kuti amuthandize kukhala mfumu. (2 Sam. 15:2-6) Zitsanzo za m’Baibulozi zikusonyeza kuti Yehova sasangalala ndi anthu amene amadzifunira ulemerero. (Miy. 25:27) M’kupita kwa nthawi anthu onyada komanso amene amafuna kuti anthu ena aziwalemekeza, amapeza mavuto.​—Miy. 16:18.

9. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani?

9 Yesu anali wosiyana kwambiri ndi anthu onyadawa. Baibulo limati: “Ngakhale kuti iye anali ndi maonekedwe a Mulungu, kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.” (Afil. 2:6) Yesu ndi wachiwiri kwa Yehova, komatu sadziganizira kwambiri kuposa mmene ayenera kudziganizira. Iye anauza ophunzira ake kuti: “Aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.” (Luka 9:48) Timasangalala kwambiri kutumikira limodzi ndi apainiya, atumiki othandiza, akulu komanso oyang’anira madera omwe ndi odzichepetsa ngati Yesu. Atumiki a Yehova amene ndi odzichepetsa amasonyeza chikondi. Zimenezi zimathandiza kuti azidziwika kuti ndi atumiki a Mulungu.​—Yoh. 13:35.

10. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukuona kuti mumpingo muli mavuto enaake ndipo mukuganiza kuti akulu sakuwasamalira bwino?

10 Tiyerekeze kuti mukuona kuti mumpingo muli mavuto enaake ndipo akulu sakuwasamalira bwino. Kodi mungatani? M’malo momangodandaula, mungasonyeze kuti ndinu odzichepetsa mukamachita zinthu mogwirizana ndi amene akutitsogolera. (Aheb. 13:17) Kuti muthe kuchita zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Kodi mavuto amene ndikuwaganizirawa ndi aakulu kwambiri moti akufunikadi kukonzedwa? Kodi ino ndi nthawi yoyenera kukonza zimenezi? Kodi ndi udindo wanga kukonza zimenezi? Kodi cholinga changa ndi kufuna kulimbikitsa mtendere mumpingo kapena ndikungofuna kutchuka?’

Kuwonjezera pa kukhala ndi luso, abale amene ali ndi udindo ayenera kukhala odzichepetsa (Onani ndime 11) *

11. Mogwirizana ndi Aefeso 4:2, 3, kodi pamakhala zotsatira zotani tikamatumikira Yehova modzichepetsa?

11 Yehova amaona kuti kukhala wodzichepetsa ndi kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi luso linalake. Amaonanso kuti kuchita zinthu mogwirizana ndi kofunika kwambiri kuposa kuchita zinthu mwaluso. Choncho muziyesetsa kutumikira Yehova modzichepetsa. Mukamachita zimenezi mudzathandiza kuti anthu mumpingo azigwirizana. (Werengani Aefeso 4:2, 3.) Muzigwira mwakhama ntchito yolalikira. Muzifufuza njira zimene mungatumikirire ena powachitira zinthu mokoma mtima. Muzichereza anthu onse kuphatikizapo amene alibe udindo mumpingo. (Mat. 6:1-4; Luka 14:12-14) Mukamachita zinthu limodzi ndi abale ndi alongo mumpingo, adzaona luso limene muli nalo komanso adzadziwa kuti ndinu wodzichepetsa.

MUZISONYEZA KUDZICHEPETSA MUKAMAGWIRITSA NTCHITO INTANETI

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo limatilimbikitsa kuti tikhale ndi anzathu?

12 Yehova amafuna kuti tizisangalala ndi achibale komanso anzathu. (Sal. 133:1) Yesu anali ndi anzake abwino. (Yoh. 15:15) Baibulo limafotokoza ubwino wokhala ndi anzathu apamtima. (Miy. 17:17; 18:24) Ndipo limatiuzanso kuti sibwino kudzipatula. (Miy. 18:1) Anthu ambiri amaona kuti kucheza ndi anthu pa intaneti kumawathandiza kupeza anzawo ambiri komanso kuti asamadzimve kuti ali okhaokha. Komabe tiyenera kusamala tikamacheza ndi anthu pogwiritsa ntchito njira imeneyi.

13. N’chifukwa chiyani anthu ena amene amagwiritsa ntchito intaneti amadziona kuti ali okhaokha komanso amayamba kuvutika maganizo?

13 Opanga kafukufuku ena anapeza kuti anthu omwe amathera nthawi yaitali akuona zimene ena alemba kapena kuika pa intaneti, akhoza kumadziona kuti ali okhaokha komanso kuyamba kuvutika maganizo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi chingakhale chakuti anthu amakonda kuika zithunzi pa intaneti za zinthu zabwino zimene achita kapena zomwe zawachitikira pa moyo wawo. Zithunzizi zingakhale zawo kapena za anzawo komanso zamalo okongola amene anapitako. Munthu amene amaona zithunzizo akhoza kumaona kuti moyo wake ndi wosasangalatsa poyerekezera ndi wa anzakewo. Mlongo wina wazaka 19 anati: “Nditaona mmene ena ankasangalalira kumapeto kwa mlungu, ndinayamba kuganiza kuti sindisangalala ndi moyo chifukwa ndimangokhala kunyumba.”

14. Kodi malangizo a pa 1 Petulo 3:8, angatithandize bwanji kuti tizigwiritsa ntchito intaneti mwanzeru?

14 N’zoona kuti intaneti ndi yothandiza. Mwachitsanzo, tingaigwiritse ntchito polankhulana ndi achibale komanso anzathu. Koma kodi mumaona kuti zinthu zina zomwe anthu amaika pa intaneti zimangokhala zofuna kuti anthu ena aziwasirira? Zikuoneka kuti iwo amangofuna kuti anthu ena azichita nawo chidwi. Ena amalemba mawu achipongwe kapena otukwana pa zithunzi zimene iwowo kapena anthu ena aika pa intaneti. Kuchita zimenezi si kudzichepetsa komanso si kumvera ena chisoni omwe ndi makhalidwe amene Akhristu amalimbikitsidwa kukhala nawo.​—Werengani 1 Petulo 3:8.

Kodi zimene mumaika pa intaneti zimapangitsa ena kuona kuti ndinu wonyada kapena wodzichepetsa? (Onani ndime 15)

15. Kodi malangizo a m’Baibulo angatithandize bwanji kupewa mtima wodziona kuti ndife ofunika kwambiri?

15 Ngati mumagwiritsa ntchito intaneti, dzifunseni kuti: ‘Kodi zimene ndimalemba pa intaneti komanso zithunzi kapena mavidiyo amene ndimaikapo, zimapangitsa ena kuona kuti ndine wonyada? Kodi zingapangitse ena kuyamba kuchita nsanje?’ Baibulo limati: “Chilichonse cha m’dziko, monga chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizichokera kwa Atate, koma kudziko.” (1 Yoh. 2:16) Baibulo lina linamasulira mawu akuti “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake,” kuti “kufuna kumaoneka monga munthu wofunika.” Komatu Akhristu sayenera kumadziona kuti ndi ofunika kwambiri kapenanso kukhala ndi maganizo oti anthu ena aziwasirira. Iwo amatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.” (Agal. 5:26) Kudzichepetsa kungatithandize kupewa makhalidwe a anthu am’dzikoli omwe ndi onyada ndipo amafuna kuti ena aziwaona kuti ndi ofunika kwambiri.

‘MUZIGANIZA M’NJIRA YAKUTI MUKHALE MUNTHU WOGANIZA BWINO’

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kunyada?

16 Kudzichepetsa n’kofunika kwambiri chifukwa kunyada kumachititsa kuti munthu ‘asamaganize bwino.’ (Aroma 12:3) Anthu onyada amakhala odzikuza komanso sachedwa kukangana ndi ena. Nthawi zambiri zimene amaganiza ndiponso kuchita zimawabweretsera mavuto komanso zimavutitsa anthu ena. Ngati anthu oterewa sangasinthe, Satana akhoza kuchititsa khungu komanso kusokoneza maganizo awo. (2 Akor. 4:4; 11:3) Pamene munthu wodzichepetsa amakhala woganiza bwino. Iye amadziona moyenera ndipo amazindikira kuti anthu ena amamuposa m’njira zambiri. (Afil. 2:3) Amadziwanso kuti “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Pet. 5:5) Anthu amene amaganiza bwino safuna kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti adane ndi Yehova.

17. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipitirize kukhala odzichepetsa?

17 Kuti tipitirize kukhala odzichepetsa, tiyenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti ‘tivule umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndi kuvala umunthu watsopano.’ Kuchita zimenezi kumafuna khama. Tiyenera kuphunzira zimene Yesu ankachita ndi kuyesetsa kumutsanzira mosamala kwambiri. (Akol. 3:9, 10; 1 Pet. 2:21) Tikatero m’pamene zinthu zimatiyendera bwino. Tikamayesetsa kukhala odzichepetsa, tingathandize kuti banja lathu likhale losangalala, anthu mumpingo azigwirizana komanso tidzapewa kugwiritsa ntchito intaneti molakwika. Koposa zonse, Yehova adzasangalala nafe ndipo adzatidalitsa.

NYIMBO NA. 117 Ubwino wa Yehova

^ ndime 5 Anthu am’dzikoli ndi onyada ndiponso odzikonda. Ndiye tifunika kusamala kuti tisatengere makhalidwe amenewa. Munkhaniyi tikambirana mbali zitatu zomwe tingasonyezere kuti sitimadziganizira kuposa mmene tiyenera kudziganizira.

^ ndime 2 MATANTHAUZO A MAWU ENA: Munthu wonyada amaganizira kwambiri za iyeyo osati za anthu ena. Choncho munthu wonyada amakhalanso wodzikonda. Koma kudzichepetsa kumathandiza kuti munthu asakhale wodzikonda. Ngati munthu ndi wodzichepetsa, sakhala wonyada ndipo samadziona kuti ndi wofunika kwambiri kuposa ena.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mkulu yemwe ali ndi luso lokamba nkhani pamsonkhano komanso ali ndi udindo woyang’anira abale ena, amaonanso kuti ndi mwayi waukulu kutsogolera ena mu utumiki ndiponso kugwira nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu.